audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
A Kazembe, a Jooma komanso anthu ena anapikisana pa mpando-u pa chisankho cha mu 2019 | A Kazembe, a Joma komanso anthu ena anapikisana pa mpandowu pa chisankho cha mu twente naintini | Female | |
chomwe malingana ndi bungwe la zisankho la Mec, a Jooma ndi omwe anapambana Komatu Kazembe sanagwirizane ndi izi | chomwe malingana ndi bungwe la zisankho la Meki, a Joma ndi omwe anapambana Komatu Kazembe sanagwirizane ndi izi | Female | |
ndipo anatengera nkhaniyi ku bwalo la milandu pofuna kuti bwalolo ligamule kuti chisankhochi chichitikenso ponena kuti chinali ndi zolakwika | ndipo anatengera nkhaniyi ku bwalo la milandu pofuna kuti bwalolo ligamule kuti chisankhochi chichitikenso ponena kuti chinali ndi zolakwika | Female | |
Atamva nkhani yonse komanso umboni omwe unaperekedwa, oweruza Jack N’riva anati mbali yodandaula inalephera kutsimikizira kuti pa chisankhochi panali zolakwika | Atamva nkhani yonse komanso umboni omwe unaperekedwa, oweruza Jaki N’riva anati mbali yodandaula inalephera kutsimikizira kuti pa chisankhochi panali zolakwika | Female | |
A N’riva anatinso umboni omwe unaperekedwa sunatsimikizire ngati pa chisankhochi panali kubera kulikonse kumbali ya a Joma | A N’riva anatinso umboni omwe unaperekedwa sunatsimikizire ngati pa chisankhochi panali kubera kulikonse kumbali ya a Joma | Female | |
Poyankhula ndi atolankhani pambuyo pa chigamulocho, a Ralph Jooma anati ndi zosadabwitsa kuti bwalolo lapeza kuti chisankhochi chinalibe zolakwika zilizonse | Poyankhula ndi atolankhani pambuyo pa chigamulocho, a Rafu Joma anati ndi zosadabwitsa kuti bwalolo lapeza kuti chisankhochi chinalibe zolakwika zilizonse | Female | |
Mbali inayi, a Gerald Kazembe m’mau awo anati sanagwirizane ndi oweruza Jack N’riva ndipo akagwada ku bwalo la milandu la apilo kuti liunikenso chigamulochi | Mbali inayi, a Jeladi Kazembe m’mau awo anati sanagwirizane ndi oweruza Jaki N’riva ndipo akagwada ku bwalo la milandu la apilo kuti liunikenso chigamulochi | Female | |
Bwalo lalikuku la milandu mu mzinda wa Blantyre lero likupereka chigamulo chake pa nkhani yomwe a Gerald Kazembe a chipani cha Malawi Congress (MCP) akufuna kuti ligamule kuti a Ralph Jooma a chipani cha Democratic Progressive | Bwalo lalikuku la milandu mu mzinda wa Bulantaya lero likupereka chigamulo chake pa nkhani yomwe a Jeladi Kazembe a chipani cha Malawi kongelesi (emusipi) akufuna kuti ligamule kuti a Rafu Joma a chipani cha Demokilatiki puligilesivi | Female | |
sanasankhidwe moyenerera ngati phungu ku Dera la Mangochi Monkey Bay komwe awiriwa ndi anthu ena anapikisana pa chisankho Cha pa 21 May, 2019 | sanasankhidwe moyenerera ngati phungu ku Dera la Mangochi Monkibe komwe awiriwa ndi anthu ena anapikisana pa chisankho Cha pa twente wani meyi twnte naintini | Female | |
Oweruza Jack N'riva ndi yemwe pakadali pano akuwerenga chigamulo chake pa nkhaniyi. A Kazembe mu kalata yawo ya madandaulo kupita ku bwalo la milandu anati chisankhochi chinali ndi zolakwika ndipo chikuyenera kuchitikanso | Oweruza Jaki N'riva ndi yemwe pakadali pano akuwerenga chigamulo chake pa nkhaniyi. A Kazembe mu kalata yawo ya madandaulo kupita ku bwalo la milandu anati chisankhochi chinali ndi zolakwika ndipo chikuyenera kuchitikanso | Female | |
Inu mukutinji, maganizo anu ndi otani pa mnyamata wazaka 15, yemwe wazipha atapereka mimba kwa mwana mnzake ku Mangochi, pothawa mkwiyo wamakolo ake | Inu mukutinji, maganizo anu ndi otani pa mnyamata wazaka fifitini, yemwe wazipha atapereka mimba kwa mwana mnzake ku Mangochi, pothawa mkwiyo wamakolo ake | Female | |
Unduna wa za maphunziro wati ndondomeko yolimbikitsa maphunziro a science ndi masamu pakati pa ophunzira a msukulu za secondary ikuyenda bwino ngakhale pali zopsinja zina zomwe ntchitoyi ikukumana nawo | Unduna wa za maphunziro wati ndondomeko yolimbikitsa maphunziro a sayansi ndi masamu pakati pa ophunzira a msukulu za sekondale ikuyenda bwino ngakhale pali zopsinja zina zomwe ntchitoyi ikukumana nawo | Female | |
Wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro, Madalitso Kambauwa Wirima yayankhula izi dzulo m’boma la Ntcheu pomwe anakayendera maphunziro osula ukadaulo wa aphunzitsi a maphunziro a science ndi masamu | Wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro, Madalitso Kambauwa Wirima yayankhula izi dzulo m’boma la Ntcheu pomwe anakayendera maphunziro osula ukadaulo wa aphunzitsi a maphunziro a sayansi ndi masamu | Female | |
Malingana ndi a Wirima, sukulu zambiri pakadali pano zikukumana ndi vuto la kuchepa kwa zipangizo zophunzitsira komanso kuphunzilira msukulu za secondary | Malingana ndi a Wirima, sukulu zambiri pakadali pano zikukumana ndi vuto la kuchepa kwa zipangizo zophunzitsira komanso kuphunzilira msukulu za sekondale | Female | |
maka zoyendera koma anati boma lachilimika pofuna kuonetsetsa kuti vutoli lakonzedwa. Tikudziwa kuti zipangizo zophunzitsira komanso kuphunzilira ndi zosowa msukulu zambiri | maka zoyendera koma anati boma lachilimika pofuna kuonetsetsa kuti vutoli lakonzedwa. Tikudziwa kuti zipangizo zophunzitsira komanso kuphunzilira ndi zosowa msukulu zambiri | Female | |
ndipo izi zikukhuza kachitidwe ka ophunzira pa phunziroli atero a Wirima | ndipo izi zikukhuza kachitidwe ka ophunzira pa phunziroli atero a Wirima | Female | |
Wachiwiri kwa ndunayi yatinso boma likuzindikira bwino zakufunika kwa maphunziro a science komanso masamu choncho ndi koyenera kuti aphunzitsi ophunzitsa maphunzirowa akhale odziwa ntchito yawo | Wachiwiri kwa ndunayi yatinso boma likuzindikira bwino zakufunika kwa maphunziro a sayansi komanso masamu choncho ndi koyenera kuti aphunzitsi ophunzitsa maphunzirowa akhale odziwa ntchito yawo | Female | |
Ndipo m’mau ake m’modzi mwa aphunzitsi a science, Bandwell Msalanyama kuchokera ku sukulu ya Blantyre Secondary anati maphunzirowa awathandiza kuchita bwino kwambiri pa momwe angamaphunzitsire maphunzirowa | Ndipo m’mau ake m’modzi mwa aphunzitsi a sayansi, Bandiwelo Msalanyama kuchokera ku sukulu ya Bulantaya sekondale anati maphunzirowa awathandiza kuchita bwino kwambiri pa momwe angamaphunzitsire maphunzirowa | Female | |
Maphunziro wa anachitika pansi pa ntchito pa ndondomeko ya Equity with Quality and Learning at Secondary School | Maphunziro wa anachitika pansi pa ntchito pa ndondomeko ya ikwite wifi kwalite andi lening’i ati sekondale sukulu | Female | |
Usiku wapitiwu, moto olusa watentha ofesi ya za maphunziro m’boma la Rumphi, kuononga katundu wa nkhaninkhani | Usiku wapitiwu, moto olusa watentha ofesi ya za maphunziro m’boma la Rumphi, kuononga katundu wa nkhaninkhani | Female | |
Mneneri mu unduna wa za maphunziro, Chikondi Chimala watiuza kuti chomwe chayambitsa motowu sichikudziwika pakadali pano koma anati tiyankhule ndi a bwanamkubwa, a Fred Movete | Mneneri mu unduna wa za maphunziro, Chikondi Chimala watiuza kuti chomwe chayambitsa motowu sichikudziwika pakadali pano koma anati tiyankhule ndi a bwanamkubwa, a Fuledi Movete | Female | |
kapena mkulu wa za maphunziro, a MacPhine Mzumara m’boma la Rumphi kuti timve zambiri. A Fred Movete m’mau awo ati palibe chomwe akanachita | kapena mkulu wa za maphunziro, a Makifini Mzumara m’boma la Rumphi kuti timve zambiri. A Fuledi Movete m’mau awo ati palibe chomwe akanachita | Female | |
polingalira kuti motowu unali wa mphanvu komanso oopsa ndipo ofesiyi ilibe zipangizo zozimitsira moto | polingalira kuti motowu unali wa mphanvu komanso oopsa ndipo ofesiyi ilibe zipangizo zozimitsira moto | Female | |
Mbali inayi, MacPhine Mzumara ati ofesi yawo ikukaikira kuti motowu unayamba kaamba ka vuto la magetsi pomwenso adandaula kuti pakadali pano alibe mtengo ogwira | Mbali inayi, Makifini Mzumara ati ofesi yawo ikukaikira kuti motowu unayamba kaamba ka vuto la magetsi pomwenso adandaula kuti pakadali pano alibe mtengo ogwira | Female | |
Zithunzi za pa masamba a mchezo zimaonetsa anthu ena ozungulira ofesiyi akugwiritsa ntchito ndowa pofuna kuzimitsa motowu ngakhale sizinathandize konse | Zithunzi za pa masamba a mchezo zimaonetsa anthu ena ozungulira ofesiyi akugwiritsa ntchito ndowa pofuna kuzimitsa motowu ngakhale sizinathandize konse | Female | |
Ndemanga yanu ndi yotani nkhani ya kumangidwa kwa a namkungwi awiri ku Mulanje kaamba koganizilidwa kuti anakakamiza ana a zaka za pakati pa 14 ndi 16 kukavinidwa | Ndemanga yanu ndi yotani nkhani ya kumangidwa kwa a namkungwi awiri ku Mulanje kaamba koganizilidwa kuti anakakamiza ana a zaka za pakati pa fotini ndi sikisitini kukavinidwa | Female | |
Kodi ndi bwino kukakamiza ana kukavinidwa. Inu Mukutinji ndiyo program yake ndi Ms. Mwaa mpaka nthawi ya 4 kololo | Kodi ndi bwino kukakamiza ana kukavinidwa. Inu Mukutinji ndiyo pulogilamu yake ndi Misi. Mwaa mpaka nthawi ya folo kololo | Female | |
Dalayivala wa galimoto ya mtundu wa Truck ali m’manja mwa apolisi ku Mzuzu pomuganizira kuti anasokoneza mdipiti wa galimoto za President Lazarus Chakwera | Dalayivala wa galimoto ya mtundu wa Thilaki ali m’manja mwa apolisi ku Mzuzu pomuganizira kuti anasokoneza mdipiti wa galimoto za Pulezidenti Lazalasi Chakwera | Female | |
Mneneri wa apolisi m’dziko muno, James Kadadzera watsimikiza za kumangidwa kwa darayivalayu yemwe akuziwika ndi dzina loti Lusungu Chirwa | Mneneri wa apolisi m’dziko muno, Jemusi Kadadzera watsimikiza za kumangidwa kwa darayivalayu yemwe akuziwika ndi dzina loti Lusungu Chirwa | Female | |
Malingana ndi a Kadadzera, mkuluyu yemwe nthawi yopalamula mlanduwu analibe chiphatso choyendesera galimoto, adasokoneza mdipiti wa President Chakwera dzulo la Mulungu mu mseu wa M1 ku Mzimba | Malingana ndi a Kadadzera, mkuluyu yemwe nthawi yopalamula mlanduwu analibe chiphatso choyendesera galimoto, adasokoneza mdipiti wa pulezidenti Chakwera dzulo la Mulungu mu mseu wa emu wani ku Mzimba | Female | |
Lusungu Chirwa akawonekera ku bwalo la Milandu posatchedwa komwe akayakhe mlanduwu. Anthu khumi ali m’manja mwa apolisi m’boma la Karonga | Lusungu Chirwa akawonekera ku bwalo la Milandu posatchedwa komwe akayakhe mlanduwu. Anthu khumi ali m’manja mwa apolisi m’boma la Karonga | Female | |
powaganizira kuti anamenya mpaka kupha munthu wina wa zaka 49 zakubadwa, a Mike Hauli, powaganizira kuti amakhuzidwa ndi imfa ya m’chimwene wake | powaganizira kuti anamenya mpaka kupha munthu wina wa zaka fote naini zakubadwa, a Maiki Hauli, powaganizira kuti amakhuzidwa ndi imfa ya m’chimwene wake | Female | |
Wofalitsa nkhani za apolisi ku Karonga, Enock Livasoni watsimikiza za kumangidwa kwa anthu khumiwa omwe apalamula mlanduwu m’mudzi mwa Malema 2 mfumu yaikulu Kyungu m’bomali | Wofalitsa nkhani za apolisi ku Karonga, Inoki Livasoni watsimikiza za kumangidwa kwa anthu khumiwa omwe apalamula mlanduwu m’mudzi mwa Malema thu mfumu yaikulu Kyungu m’bomali | Female | |
Nkhaniyi ikuti m’chimwene wawo wa a Mike Hauli, a Mwayiwowa anamwalira mosadziwika bwino ndipo anthu a m’mudzi anayamba kukayikira kuti a Hauli ndi omwe apha m’chimwene wawoyo mu masenga | Nkhaniyi ikuti m’chimwene wawo wa a Maiki Hauli, a Mwayiwowa anamwalira mosadziwika bwino ndipo anthu a m’mudzi anayamba kukayikira kuti a Hauli ndi omwe apha m’chimwene wawoyo mu masenga | Female | |
Ndipo anthuwa omwe ndi kuphatikizapo abale awo a Mike Hauli anakapanga m’bidikiro ku nyumba kwa Hauli komwe anayamba kuwamenya a Hauli mpaka kuwaotcha | Ndipo anthuwa omwe ndi kuphatikizapo abale awo a Maiki Hauli anakapanga m’bidikiro ku nyumba kwa Hauli komwe anayamba kuwamenya a Hauli mpaka kuwaotcha | Female | |
Anthu khumi-wa akuyembekezereka kuyamba kuyakha mlandu okupha munthu zomwe ndi zotsutsana ndi malamulo oyendetsera dziko lino, pomwe a polisi apempha anthu kuti asiye kutengera lamulo m’manja mwawo | Anthu khumiwa akuyembekezereka kuyamba kuyakha mlandu okupha munthu zomwe ndi zotsutsana ndi malamulo oyendetsera dziko lino, pomwe a polisi apempha anthu kuti asiye kutengera lamulo m’manja mwawo | Female | |
Anamkungwi awiri ali m’chitokosi cha a polisi m’boma la Mulanje kaamba kokakamiza atsikana awiri a zaka za pakati pa 14 ndi 16 kulowa Chinamwali | Anamkungwi awiri ali m’chitokosi cha a polisi m’boma la Mulanje kaamba kokakamiza atsikana awiri a zaka za pakati pa fotini ndi sikisitini kulowa Chinamwali | Female | |
Graciam Ngwira, yemwe ndi Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali, watsimikiza za kumangidwa kwa awiriwa omwe ndi a Lexa Chiphaso komanso Patricia Fyson | Gileshamu Ngwira, yemwe ndi Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali, watsimikiza za kumangidwa kwa awiriwa omwe ndi a Lekisa Chiphaso komanso Patilisha faisoni | Female | |
Malingana ndi a Ngwira, awiriwa anagwira ndikukakamiza atsikanawa omwe ndi a m’mudzi mwa Kandeu ndi Reuben mfumu yaikulu Chikumbu makolo awo a anawa asakudziwa | Malingana ndi a Ngwira, awiriwa anagwira ndikukakamiza atsikanawa omwe ndi a m’mudzi mwa Kandeu ndi Rubeni mfumu yaikulu Chikumbu makolo awo a anawa asakudziwa | Female | |
Pakadali pano, atsikana awiri-wa atulusidwa ku simbako pomwe anamkungwiwa akuyembekezereka kukawonekera ku bwalo la Milandu Posachedwapa | Pakadali pano, atsikana awiriwa atulusidwa ku simbako pomwe anamkungwiwa akuyembekezereka kukawonekera ku bwalo la Milandu Posachedwapa | Female | |
Anthu omwe sakudziwika athyola ndi kuba ndalama zopitilira K1 Million komanso lamya zam'manja zisanu ku bwalo la milandu la Mkukula First Grade Magistrate ku Lumbadzi m'boma la Dowa | Anthu omwe sakudziwika athyola ndi kuba ndalama zopitilira wani miliyoni kwacha komanso lamya zam'manja zisanu ku bwalo la milandu la Mkukula fesiiti giledi majesitileti ku Lumbadzi m'boma la Dowa | Female | |
Malingana ndi mlembi ku bwalolo, Isaac Atusaye, ndalama komanso lamya-zi ndi zomwe anthu ena anapereka ngati zikole pa milandu yosiyanasiyana yomwe akuyankha | Malingana ndi mlembi ku bwalolo, aizeki Atusaye, ndalama komanso lamyazi ndi zomwe anthu ena anapereka ngati zikole pa milandu yosiyanasiyana yomwe akuyankha | Female | |
Atusaye wati iwo adziwitsa kale apolisi ya Lumbazi za nkhaniyi omwe pakadali pano ayamba kufufuza | Atusaye wati iwo adziwitsa kale apolisi ya Lumbazi za nkhaniyi omwe pakadali pano ayamba kufufuza | Female | |
Mneneri wa polisi ya Lumbazi, Felix Kwinyani watiuza kuti ofesi yawo yalandiradi malipoti okhuza nkhaniyi koma pakadali pano, sangayankhule zambiri potengera kuti kafukufuku ofuna kugwira anthuwa ali mkati | Mneneri wa polisi ya Lumbazi, Felikisi Kwinyani watiuza kuti ofesi yawo yalandiradi malipoti okhuza nkhaniyi koma pakadali pano, sangayankhule zambiri potengera kuti kafukufuku ofuna kugwira anthuwa ali mkati | Female | |
Kutsatira kubedwa kwa katunduyu, zadziwikanso kuti pa bwalo la milanduli palibe alonda. Gulu lomwe likuzitchula kuti Blantyre Cyclists Crew mogwirizana ndi bungwe la EDUFUND | Kutsatira kubedwa kwa katunduyu, zadziwikanso kuti pa bwalo la milanduli palibe alonda. Gulu lomwe likuzitchula kuti Bulantaya saikilisiti khuluu mogwirizana ndi bungwe la Ejufandi | Female | |
akonza ulendo opalasa njinga omwe cholinga chake ndi kutolera ndalama zothandizira ophunzira ochepekedwa omwe akuchita maphunziro awo pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) | akonza ulendo opalasa njinga omwe cholinga chake ndi kutolera ndalama zothandizira ophunzira ochepekedwa omwe akuchita maphunziro awo pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi yunivesite ofu bizinezi andi apulayidi sayansezi (MUBASI) | Female | |
Ulendowu omwe uzachitike pa 3 September chaka chino akuti uzayambira mu mzinda wa Blantyre mpaka kukafika ku Zomba | Ulendowu omwe uzachitike pa fili sepitemba chaka chino akuti uzayambira mu mzinda wa Bulantaya mpaka kukafika ku Zomba | Female | |
Malingana ndi mneneri wa bungwe la EDUFUND, a Bester Kayaye, iwo akufuna atatolera ndalama zopitilira K35 Million ndi cholinga chofuna kufikira ophunzira 75 | Malingana ndi mneneri wa bungwe la Ejufandi, a Besita Kayaye, iwo akufuna atatolera ndalama zopitilira fete faifi miliyoni kwacha ndi cholinga chofuna kufikira ophunzira sevente faifi | Female | |
omwe ndi ena mwa ophunzira a nkhaninkhani omwe akusowekera thandizo pa sukuluyi. A Kayaye apempha anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino ndipo ali ndi kuthekera kuti athandizepo | omwe ndi ena mwa ophunzira a nkhaninkhani omwe akusowekera thandizo pa sukuluyi. A Kayaye apempha anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino ndipo ali ndi kuthekera kuti athandizepo | Female | |
Pakadali pano, mbali ziwirizi zati zili ndi malingaliro ofikira ophunzira ochuluka ndi thandizo koma zatsindika zakufunika koti mbali zokhuzidwa ziziwathandiza | Pakadali pano, mbali ziwirizi zati zili ndi malingaliro ofikira ophunzira ochuluka ndi thandizo koma zatsindika zakufunika koti mbali zokhuzidwa ziziwathandiza | Female | |
Chipwilikiti chabuka pa nkhani ya lamulo lokhudza chilango chonyonga munthu akalakwira ena mwa malamulo mdziko lino, pomwe oweruza ena a ku bwalo la milandu la lalikulu Supreme | Chipwilikiti chabuka pa nkhani ya lamulo lokhudza chilango chonyonga munthu akalakwira ena mwa malamulo mdziko lino, pomwe oweruza ena a ku bwalo la milandu la lalikulu Sapulimu | Female | |
akuti lamuloli lilipobe ngakhale kuti m’mbuyomu bwalo lomweli linati chilangochi chachotsedwa malingana ndi malamulo a dziko lino komanso mfundo za migwirizano ina yokhuza maufulu | akuti lamuloli lilipobe ngakhale kuti m’mbuyomu bwalo lomweli linati chilangochi chachotsedwa malingana ndi malamulo a dziko lino komanso mfundo za migwirizano ina yokhuza maufulu | Female | |
M’mbuyomu bwalo la Supreme lomweli mu chigamulo chake chomwe anasainira ndi oweruza opuma, Dunstain Mwaungulu chinati chilangochi chinachotsedwa | M’mbuyomu bwalo la Sapulimu lomweli mu chigamulo chake chomwe anasainira ndi oweruza opuma, Dasiteni Mwaungulu chinati chilangochi chinachotsedwa | Female | |
ponena kuti malamulo a dziko lino aakuli salaora chilango chonyonga munthu. Komatu oweruza asanu ndi awiri omwe amaunika chigamulochi ku Supreme Court, adzudzula oweruza Mwaungulu | ponena kuti malamulo a dziko lino aakuli salaora chilango chonyonga munthu. Komatu oweruza asanu ndi awiri omwe amaunika chigamulochi ku sapulimu khoti, adzudzula oweruza Mwaungulu | Female | |
ati kaamba kopeleka chigamulo pa nkhani yomwe sinali pamaso pa khothi kuti igamulidwe komanso kosafunsa maganizo a oweruza amnzake pa nthawi yomwe amachotsa lamuloli | ati kaamba kopeleka chigamulo pa nkhani yomwe sinali pamaso pa khothi kuti igamulidwe komanso kosafunsa maganizo a oweruza amnzake pa nthawi yomwe amachotsa lamuloli | Female | |
Koma poyankhapo pa nkhaniyi Sabata yatha, oweruza Mwaungulu anauza nyuzipepala ya Nation komanso wailesi ya Zodiak kuti iwo ndi odabwa ndi zomwe oweruza amnzakewa akunena | Koma poyankhapo pa nkhaniyi Sabata yatha, oweruza Mwaungulu anauza nyuzipepala ya neshoni komanso wailesi ya Zodiyaki kuti iwo ndi odabwa ndi zomwe oweruza amnzakewa akunena | Female | |
potsindika kuti chiweluzo chothetsa chilango chonyonga chinapangidwa atakambilana ndi oweruza anzao omwenso lero akutsutsa nkhaniyi | potsindika kuti chiweluzo chothetsa chilango chonyonga chinapangidwa atakambilana ndi oweruza anzao omwenso lero akutsutsa nkhaniyi | Female | |
A Mwangulu ati ali ndi umboni wa kalata za email zomwe oweruza omwe akutsutsana ndi izi analemba m’mbuyomu posonyeza kuti akugwirizana ndi chigamulo chochotsa lamuloli | A Mwangulu ati ali ndi umboni wa kalata za imelo zomwe oweruza omwe akutsutsana ndi izi analemba m’mbuyomu posonyeza kuti akugwirizana ndi chigamulo chochotsa lamuloli | Female | |
Mwa zina, malamulo amati munthu aliyense opezeka olakwa pa mlandu okupha munthu, ofuna kulanda boma komanso ogwilira, akuyenera kuphedwa | Mwa zina, malamulo amati munthu aliyense opezeka olakwa pa mlandu okupha munthu, ofuna kulanda boma komanso ogwilira, akuyenera kuphedwa | Female | |
Oweruza omwe anatenga nawo mbali kuunikanso chigamulo cha a Mwaungulu ndi a Edward Twea, a Anaclet Chipeta, a Lovemore Chikopa, a Frank Kapanda, a Andrew Nyirenda ndi a Razine Mzikamanda | Oweruza omwe anatenga nawo mbali kuunikanso chigamulo cha a Mwaungulu ndi a Ediwadi Twea, a Anakileti Chipeta, a Lavumo Chikopa, a Fulanki Kapanda, a Andulu Nyirenda ndi a Razini Mzikamanda | Female | |
ndipo adzudzula Mwaungulu kaamba kolemba za m’mutu mwawo. Pamenapa, oweruza opumayu wati aka sikoyamba kusemphana maganizo ndi oweruza enawa | ndipo adzudzula Mwaungulu kaamba kolemba za m’mutu mwawo. Pamenapa, oweruza opumayu wati aka sikoyamba kusemphana maganizo ndi oweruza enawa | Female | |
ponena kuti m’mbuyomu sanakondwenso ndi maganizo awo pa mlandu wa Chisankho cha mtsogoleri cha mu 2019 pomwe iwo anati sunayende bwino | ponena kuti m’mbuyomu sanakondwenso ndi maganizo awo pa mlandu wa Chisankho cha mtsogoleri cha mu twente naintini pomwe iwo anati sunayende bwino | Female | |
Unduna wa zamalo wati anthu omwe anauzidwa kuti asamuke ku mnyumba za bungwe la Malawi Housing (MHC) ku dera la Ngumbe mu mzinda wa Blantyre | Unduna wa zamalo wati anthu omwe anauzidwa kuti asamuke ku mnyumba za bungwe la Malawi Hauzing’i (emuetchisi) ku dera la Ngumbe mu mzinda wa Bulantaya | Female | |
sasamuka ngakhale eni malo omwe nyumbazi zinamangidwa anakatenga chilolezo ku bwalo la milandu chotulutsa anthuwa | sasamuka ngakhale eni malo omwe nyumbazi zinamangidwa anakatenga chilolezo ku bwalo la milandu chotulutsa anthuwa | Female | |
Nduna mu undunawu, Kezzie Msukwa yati pakadali pano boma layamba kuchita zokambirana ndi mbali zokhuzidwa pa nkhaniyi | Nduna mu undunawu, Kezi Msukwa yati pakadali pano boma layamba kuchita zokambirana ndi mbali zokhuzidwa pa nkhaniyi | Female | |
A Msukwa ayankhula izi lero pomwe anakayendera anthuwa omwe anauzidwa kuti pofika loweruka nthawi ya 9 koloko m’mawa akhale atasamuka chifukwa malowa eni wake akuwafuna | A Msukwa ayankhula izi lero pomwe anakayendera anthuwa omwe anauzidwa kuti pofika loweruka nthawi ya naini koloko m’mawa akhale atasamuka chifukwa malowa eni wake akuwafuna | Female | |
Lawyer yemwe akuimira eni malowa, Kuleza Phokoso wati bungwe la MHC linanyozera langizo loti lisamange nyumba pa malopa chifukwa siaboma | Loya yemwe akuimira eni malowa, Kuleza Phokoso wati bungwe la emuetchisi linanyozera langizo loti lisamange nyumba pa malopa chifukwa siaboma | Female | |
Phokoso waonjezeranso kuti bungweli litamalizitsa kumanga nyumba-i, linayamba kuikamo anthu okhala ngakhale nkhani-yi inali ili ku bwalo la milandu, zomwe zawachititsa kuti akatenga chilolezo chothamangitsa anthuwa | Phokoso waonjezeranso kuti bungweli litamalizitsa kumanga nyumbazi, linayamba kuikamo anthu okhala ngakhale nkhaniyi inali ili ku bwalo la milandu, zomwe zawachititsa kuti akatenga chilolezo chothamangitsa anthuwa | Female | |
Pakadali pano pali nkhawa kuti nyumbazi zomwe zonse ndi 65 ndipo ndi zapamwamba, zitha kugumulidwa | Pakadali pano pali nkhawa kuti nyumbazi zomwe zonse ndi sikisite faifi ndipo ndi zapamwamba, zitha kugumulidwa | Female | |
Ndalama zokwana 3.5 billion kwacha zomwe MHC inachita kubwereka ku bank ina, ndi zomwe zinagwiritsidwa ntchito pomanga nyumbazi | Ndalama zokwana fili pointi faifi biliyoni kwacha zomwe emuetchisi inachita kubwereka ku banki ina, ndi zomwe zinagwiritsidwa ntchito pomanga nyumbazi | Female | |
Apolisi m'boma la Dedza atsekera mchitokosi mphunzitsi wina wa zaka 27 zakubadwa pomuganizira kuti wakhala akugwililira komanso kupereka mimba kwa ophunzira wa zaka 15 yemwe ali mu form one pa sukulu ina kumeneko | Apolisi m'boma la Dedza atsekera mchitokosi mphunzitsi wina wa zaka twente seveni zakubadwa pomuganizira kuti wakhala akugwililira komanso kupereka mimba kwa ophunzira wa zaka fifitiini yemwe ali mu fomu wani pa sukulu ina kumeneko | Female | |
Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Dedza, Cassim Manda wati oganizilidwayu ndi Collings Chikaphonya yemwe wakhala ali pa chibwenzi ndi mwanayu | Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Dedza, kasimu Manda wati oganizilidwayu ndi koling’izi Chikaphonya yemwe wakhala ali pa chibwenzi ndi mwanayu | Female | |
kuyambira chaka chatha. Manda wati Chikaphonya anagwa naye mchikondi mwanayu atamuona umo amavinira pa ukwati wina omwe anagwilizira ndipo n’kuti pa nthawiyi anali ali mu standard 8 | kuyambira chaka chatha. Manda wati Chikaphonya anagwa naye mchikondi mwanayu atamuona umo amavinira pa ukwati wina omwe anagwilizira ndipo n’kuti pa nthawiyi anali ali mu sitandade eiti | Female | |
Ubwenzi wawo utafumbira, mwanayu anayamba kuonetsa zizindikiro zoti ndi oyembekezera ndipo apa sanachedwe koma anapita ku nyumba ya mphunzitsiyu yemwe pakupita pa nthawi, anayamba kumuchita nkhanza | Ubwenzi wawo utafumbira, mwanayu anayamba kuonetsa zizindikiro zoti ndi oyembekezera ndipo apa sanachedwe koma anapita ku nyumba ya mphunzitsiyu yemwe pakupita pa nthawi, anayamba kumuchita nkhanza | Female | |
Mabungwe osiyana-siyana akupitilira kuyankhulapo pa kumangidwa kwa akuluakulu komanso mamembala ena a bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiative (CDEDI) lachitatu lapitali mu mzinda wa Lilongwe | Mabungwe osiyanasiyana akupitilira kuyankhulapo pa kumangidwa kwa akuluakulu komanso mamembala ena a bungwe la senta fo demolilase andi ikonomiki divelopumenti inishetivi (SIDEDI) lachitatu lapitali mu mzinda wa Lilongwe | Female | |
Mwa omangidwawa ndi a Sylvester Namiwa yemwe ndi mtsogoleri wa bungweli komanso a Edwin Mauluka omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu a CDEDI ndi anthu ena pafupifupi khumi | Mwa omangidwawa ndi a Silivesita Namiwa yemwe ndi mtsogoleri wa bungweli komanso a Ediwini Mauluka omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu a SIDEDI ndi anthu ena pafupifupi khumi | Female | |
Bungwe la Human Rights Consultative Committee (HRCC) lati palibe zifukwa zenizeni zomwe khonsolo inakanikanizira bungweli kuchita m’bindikiro komanso apolisi anamangira anthuwa | Bungwe la Hyumani laitsi konzatetivi komitii (etchi alasisi) lati palibe zifukwa zenizeni zomwe khonsolo inakanikanizira bungweli kuchita m’bindikiro komanso apolisi anamangira anthuwa | Female | |
Zifukwa zomwe adindo analepheretsera m’bindikiro wa CDEDI ndi zosamveka komanso zoseketsa, watero mtsogoleri wa HRCC, Robert Mkwezalamba kudzera mkalata yomwe bungwe lawo latulutsa | Zifukwa zomwe adindo analepheretsera m’bindikiro wa SIDEDI ndi zosamveka komanso zoseketsa, watero mtsogoleri wa Etchialasisi, Robati Mkwezalamba kudzera mkalata yomwe bungwe lawo latulutsa | Female | |
Mbali inayi, bungwe la Center for Mindset Change (CMC) kudzera mwa mkulu wake, Philip Kamangirah lati nkhani ya ufulu ochita zionetsero za bata zosonyeza kusakondwa ndi zinthu zina | Mbali inayi, bungwe la senta fo maindiseti chenji (siemusi) kudzera mwa mkulu wake, filipi Kamangira lati nkhani ya ufulu ochita zionetsero za bata zosonyeza kusakondwa ndi zinthu zina | Female | |
siyokambirana choncho ndi zosamveka kuti anthuwa ali mchitokosi cha apolisi. Apa iwo apempha apolisi kuti awatulutse mchitokosimu | siyokambirana choncho ndi zosamveka kuti anthuwa ali mchitokosi cha apolisi. Apa iwo apempha apolisi kuti awatulutse mchitokosimu | Female | |
Pakadali pano, mneneri wa apolisi m’dziko muno James Kadazera wati anthuwa atengeredwa ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akauzidwe milandu yomwe apalamula komanso kukapempha bail ya court | Pakadali pano, mneneri wa apolisi m’dziko muno Jemusi Kadazera wati anthuwa atengeredwa ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akauzidwe milandu yomwe apalamula komanso kukapempha belo ya khoti | Female | |
Bwanamkubwa wa boma la Nkhotakota, a Blessings Nkhoma amwalira m’mawa wa Lero la Chinayi. Mneneri mu unduna wa maboma aang'ono, Anjoya Mwanza | Bwanamkubwa wa boma la Nkhotakota, a Bulesing’izi Nkhoma amwalira m’mawa wa Lero la Chinayi. Mneneri mu unduna wa maboma aang'ono, Anjoya Mwanza | Female | |
watsimikiza za ku mwalira Kwa a Nkhoma koma wati sangafotokoze zambiri panopa | watsimikiza za ku mwalira Kwa a Nkhoma koma wati sangafotokoze zambiri panopa | Female | |
Bwalo la milandu la Mangochi First Grade Magistrate lalamuka Willard Chimwaza wa zaka 28 kukakhala ku ndende kwa zaka 42 | Bwalo la milandu la Mangochi fesiti giledi majesitileti lalamuka Wiladi Chimwaza wa zaka twente eiti kukakhala ku ndende kwa zaka fote thu | Female | |
atamupeza olakwa pa milandu yozembetsa komanso kugwilira atsikana awiri a zaka zapakati pa 18 ndi 22 | atamupeza olakwa pa milandu yozembetsa komanso kugwilira atsikana awiri a zaka zapakati pa eitini ndi twente thu | Female | |
Yemwe amayimira boma pa milanduwu Amos Mwase anawuza bwaloli kuti pa 3 July mkuluyu anapita m’mudzi mwa Mpita kwa mfumu yaikulu Katuli | Yemwe amayimira boma pa milanduwu Amosi Mwase anawuza bwaloli kuti pa fili julayi mkuluyu anapita m’mudzi mwa Mpita kwa mfumu yaikulu Katuli | Female | |
komwe ananamiza anthu kuti amagwira ntchito ku YONECO ndipo akufuna atsikana omwe anasiyira sukulu pa njira kuti awapatse ngongole yoyambira business | komwe ananamiza anthu kuti amagwira ntchito ku YONECO ndipo akufuna atsikana omwe anasiyira sukulu pa njira kuti awapatse ngongole yoyambira bizinezi | Female | |
Mkuluyu ati anatenga atsikana awiriwa kupita nayo pa Mangochi boma komwe anawanamiza kuti akukapanga maphunziro apa dera a momwe angayendesere business | Mkuluyu ati anatenga atsikana awiriwa kupita nayo pa Mangochi boma komwe anawanamiza kuti akukapanga maphunziro apa dera a momwe angayendesere bizinezi | Female | |
Kenako mkuluyu ati anawatengera atsikana awiriwa ku malo ena ogona alendo komwe anawagwilira ndikuwasiya komweko. Bungwe la zisankho la Mec | Kenako mkuluyu ati anawatengera atsikana awiriwa ku malo ena ogona alendo komwe anawagwilira ndikuwasiya komweko. Bungwe la zisankho la Meki | Female | |
lati anthu omwe akufuna kutenga nawo mbali pa ntchito ya zisankho za chibwereza zomwe zichitike posachedwapa komanso ntchito younikanso malire a Madera a aphungu, akuyenera kulandira katemera oteteza ku mliri wa COVID-19 | lati anthu omwe akufuna kutenga nawo mbali pa ntchito ya zisankho za chibwereza zomwe zichitike posachedwapa komanso ntchito younikanso malire a Madera a aphungu, akuyenera kulandira katemera oteteza ku mliri wa kovidi-naintini | Female | |
Ganizoli ladza patangopita sabata pafupifupi ziwiri bungweli litauza ogwira ntchito ku ofesi zake zonse kuti abaitse katamerayu kupanda kutero asamapite ku ofesi | Ganizoli ladza patangopita sabata pafupifupi ziwiri bungweli litauza ogwira ntchito ku ofesi zake zonse kuti abaitse katamerayu kupanda kutero asamapite ku ofesi | Female | |
Koma malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa ndipo wasainira ndi mkulu wa zisankho ongogwilizira, Haris Potani | Koma malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa ndipo wasainira ndi mkulu wa zisankho ongogwilizira, Harisi Potani | Female | |
polingalira kuti zisankho za chibwereza komanso kuunikira malire a aphungu kumakhuza kuyenda komanso kukumana ndi anthu osiyanasiyana, ndi koyenera kubayitsa katemera wa COVID-19 | polingalira kuti zisankho za chibwereza komanso kuunikira malire a aphungu kumakhuza kuyenda komanso kukumana ndi anthu osiyanasiyana, ndi koyenera kubayitsa katemera wa kovidi-naintini | Female | |
President Lazarus Chakwera wachotsa a Newton Kambala ngati nduna ya za magetsi komanso mlangizi wawo pa nkhani za mfundo za chitukuko, manifesto pachingerezi, Chris Chaima Banda | pulezidenti lazalasi Chakwera wachotsa a Nyutoni Kambala ngati nduna ya za magetsi komanso mlangizi wawo pa nkhani za mfundo za chitukuko, manifesto pachingerezi, khilisi Chaima Banda | Female | |
A Kambala ndi a Banda achotsedwa kutsatira kumangidwa kwawo kuphatikizaponso mtsogoleri wa chipani cha Alliance for Democracy (AFORD), a Enoch Chihana | A Kambala ndi a Banda achotsedwa kutsatira kumangidwa kwawo kuphatikizaponso mtsogoleri wa chipani cha Alayansi fo demokilase (AFODI), a Inoki Chihana | Female | |
ndi bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la ACB powaganizira kuti amapanga upo ofuna kupereka ziphuphu kwa akuluakulu a kampani yoona za mafuta ya NOCMA kuti iwakondere pa kaperekedwe ka makontilakiti | ndi bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la esibi powaganizira kuti amapanga upo ofuna kupereka ziphuphu kwa akuluakulu a kampani yoona za mafuta ya NOKUMA kuti iwakondere pa kaperekedwe ka makontilakiti | Female | |
Kuchotsedwa kwa a Kambala kukutanthauza kuti dziko lino, tsopano lilibe nduna m'maunduna anai a boma omwe ndi kuphatikizapo unduna wa za mayendedwe , unduna wa maboma ang'ono komanso unduna wa za ntchito | Kuchotsedwa kwa a Kambala kukutanthauza kuti dziko lino, tsopano lilibe nduna m'maunduna anai a boma omwe ndi kuphatikizapo unduna wa za mayendedwe , unduna wa maboma ang'ono komanso unduna wa za ntchito | Female | |
A Polisi ku Lilongwe amanga mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), a Sylvester Namiwa | A Polisi ku Lilongwe amanga mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Senta Fo Demokilase Andi Ikonomiki Divelopumenti Inishetivi (SIDEDI), a Silivesita Namiwa | Female | |
A Namiwa amangidwa panja pa Nyumba ya Malamulo komwe amayembekezera kutsogolera a Malawi kuchita m’bindikiro pofuna kukakamiza kalariki wa nyumba ya Malamulo, a Fiona Kalemba | A Namiwa amangidwa panja pa Nyumba ya Malamulo komwe amayembekezera kutsogolera a Malawi kuchita m’bindikiro pofuna kukakamiza kalariki wa nyumba ya Malamulo, a Fiyona Kalemba | Female | |
sipikala Gotani Hara komanso Nduna ya za m’dziko a Richard Chimwendo Banda kuti afotokoze bwino paza momwe bilu yopempha ngongole ku maiko a kunja inazembetsedwera kupita ku nyumba ya malamulo | sipikala Gotani Hara komanso Nduna ya za m’dziko a litchadi Chimwendo Banda kuti afotokoze bwino paza momwe bilu yopempha ngongole ku maiko a kunja inazembetsedwera kupita ku nyumba ya malamulo | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.