audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Chipani cha AFORD chati kubwera kwa mamembala atsopano mchipanichi ndiumboni kuti anthu akumvesetsa mfundo za chipanichi komanso akugwilizana ndi utsogoleri wachipanichi | Chipani cha AFODI chati kubwera kwa mamembala atsopano mchipanichi ndiumboni kuti anthu akumvesetsa mfundo za chipanichi komanso akugwilizana ndi utsogoleri wachipanichi | Female | |
Mlembi wamkulu wa AFORD a Wakuda Kamanga polankhula lero ku ofesi yachipanichi ku Lilongwe lero pomwe amalandira mamembala atsopano 68 | Mlembi wamkulu wa AFODI a Wakuda Kamanga polankhula lero ku ofesi yachipanichi ku Lilongwe lero pomwe amalandira mamembala atsopano sikisite eiti | Female | |
wati izi zipeleka mangolomera ku chipanichi kuti chipitilize ntchito zolimbikitsa mbali zonse zachipanichi | wati izi zipeleka mangolomera ku chipanichi kuti chipitilize ntchito zolimbikitsa mbali zonse zachipanichi | Female | |
Ena mwa omwe awalandira mchipani cha AFORD a Evance Mtalamanja, a Chimango Mughogho komanso a Yankho Masina | Ena mwa omwe awalandira mchipani cha AFORDI a Evansi Mtalamanja, a Chimango Muwowo komanso a Yankho Masina | Female | |
ati alowa mchipanichi kambakoti ndichomwe chaonetsa kuti ndichokonzeka kutumikira a Malawi moyenera | ati alowa mchipanichi kambakoti ndichomwe chaonetsa kuti ndichokonzeka kutumikira a Malawi moyenera | Female | |
AFORD yatinso iika chidwi poonesetsa kuti anthu omwe akuzapikisana nawo pachisankho chamu 2025 mdzina la chipanichi ndioyenera | AFORDI yatinso iika chidwi poonesetsa kuti anthu omwe akuzapikisana nawo pachisankho chamu twente twente faifi mdzina la chipanichi ndioyenera | Female | |
Bungwe la FAM lalamula nthambi yoyendetsa mpira mchigawo cha pakati, ya Central Region Football Association- CRFA kuti ikonze masewero a Premier Division | Bungwe la FAMU lalamula nthambi yoyendetsa mpira mchigawo cha pakati, ya Sentilo lijoni futubo asosiyeshoni sialaefue kuti ikonze masewero a pulimiya divizyoni | Female | |
mu ligi ya Chipiku Stores, pakati pa ma timu a Kawinga FC ndi Namitete Zitha FC loweruka kapena la mulungu likudzali pa bwalo la Nankhaka kapena Civo ku Lilongwe | mu ligi ya Chipiku Sitozi, pakati pa ma timu a Kawinga efusi ndi Namitete Zitha efusi loweruka kapena la mulungu likudzali pa bwalo la Nankhaka kapena sivo ku Lilongwe | Female | |
Koma timu imene ipambane masewerowa si ndiye kuti yalowa Super League kapena yatenga ukatswiri kamba koti bungweli likhale likufufuza nkhani za chinyengo zimene zakhuza ma timu ena | Koma timu imene ipambane masewerowa si ndiye kuti yalowa supa ligi kapena yatenga ukatswiri kamba koti bungweli likhale likufufuza nkhani za chinyengo zimene zakhuza ma timu ena | Female | |
Bungwe la FAM lafunsa CRFA kuti ipereke zotsatira za masewero onse a ma timu a Leyman Panthers | Bungwe la FAMU lafunsa sialaefue kuti ipereke zotsatira za masewero onse a ma timu a Leyimani Panfazi | Female | |
Ngolowindo FC, Mangoni Warriors ndi Kamuzu Barracks Reserve kuti liphatikize pa kafuku-fuku wa zinyengo zimene zakhuza ligiyi | Ngolowindo efusi, Mangoni Waliyazi ndi Kamuzu Balakisi lizevu kuti liphatikize pa kafuku-fuku wa zinyengo zimene zakhuza ligiyi | Female | |
Mpungwe-pungwe okhuza katangale ndi ziphuphu wayimitsa ligi ya Chipiku kwa sabata zitatu tsopano kuyambira pamene munthu wina wa ku Salima, Rashid Likumbo | Mpungwe-pungwe okhuza katangale ndi ziphuphu wayimitsa ligi ya Chipiku kwa sabata zitatu tsopano kuyambira pamene munthu wina wa ku Salima, Rashidi Likumbo | Female | |
anawulura kuti panachitika za chinyengo zimene zinalepheretsa timu ya Ngolowindo FC isapite ku Lilongwe kukasewera ndi Namitete Zitha FC pa bwalo la ku Kamuzu Barracks pa 7 January, 2024 | anawulura kuti panachitika za chinyengo zimene zinalepheretsa timu ya Ngolowindo efusi isapite ku Lilongwe kukasewera ndi Namitete Zitha efusi pa bwalo la ku Kamuzu Balakisi pa seveni januwale twente twente folo | Female | |
anthu atatu omwe anamangidwa kaamba kotchinga njira mtsogoleri wa dziko lino akudutsa pa HHI mu mzinda wa Blantyre lachisanu lapitali, akhalabe m'manja mwa apolisi mpaka lachisanu likudzali | anthu atatu omwe anamangidwa kaamba kotchinga njira mtsogoleri wa dziko lino akudutsa pa etchietchi ai mu mzinda wa bulantaya lachisanu lapitali, akhalabe m'manja mwa apolisi mpaka lachisanu likudzali | Female | |
Apolisi anasunga mwachinsinsi kumangidwa kwa atatuwa pofikira lero pomwe anatulukira pamaso pa Magistrate yemwe wati adzapeleka patsikulo chigamulo chake | Apolisi anasunga mwachinsinsi kumangidwa kwa atatuwa pofikira lero pomwe anatulukira pamaso pa majesitileti yemwe wati adzapeleka patsikulo chigamulo chake | Female | |
A Hector Ndawala, zaka 38, a Pearson Chimimba, a zaka 48 ndi a Lucy Namba, zaka 25, ndiwo akuzengedwa milandu ingapo | A Hekita Ndawala, zaka fete eiti, a Piyasoni Chimimba, a zaka fote eiti ndi a Luse Namba, zaka twente faifi, ndiwo akuzengedwa milandu ingapo | Female | |
Boma lakhazikitsa Sub T/A Msinde kukhala T/A Msinde, Sub T/A Chiwaula kukhala T/A Chiwaula ndipo agulupu Malembo kukhala Sub T/A m'boma la Lilongwe | Boma lakhazikitsa Subu tie Msinde kukhala tie Msinde, Sabu tie Chiwaula kukhala Tie Chiwaula ndipo agulupu Malembo kukhala Sabu Tie m'boma la Lilongwe | Female | |
Izi zikutsatira pomwe mtsogoleri wa dziko lino, malinga ndi mphamvu zomwe ali nazo kutengera malamulo a dziko lino anakweza mafumuwa pa udindo wawo | Izi zikutsatira pomwe mtsogoleri wa dziko lino, malinga ndi mphamvu zomwe ali nazo kutengera malamulo a dziko lino anakweza mafumuwa pa udindo wawo | Female | |
Nduna ya za maboma aang’ono, umodzi ndi chikhalidwe a Richard Chimwendo Banda yapempha mafumuwa kuti agwire ntchito zothandizila chitukuko cha dziko | Nduna ya za maboma aang’ono, umodzi ndi chikhalidwe a litchadi ichard Chimwendo Banda yapempha mafumuwa kuti agwire ntchito zothandizila chitukuko cha dziko | Female | |
ponena kuti mafumu akakhala patsogolo, chitukuko cha dziko chimayenda bwino. A Chimwendo Banda apemphanso mafumuwa kuti agwire ntchito limodzi popewa katangale | ponena kuti mafumu akakhala patsogolo, chitukuko cha dziko chimayenda bwino. A Chimwendo Banda apemphanso mafumuwa kuti agwire ntchito limodzi popewa katangale | Female | |
powachenjeza kuti apewe mchitidwe ogawa katundu monga wa mtukula pakhomo kwa omwe akufuna | powachenjeza kuti apewe mchitidwe ogawa katundu monga wa mtukula pakhomo kwa omwe akufuna | Female | |
Anthu a mdera la mfumu Chisinga ku Kasungu alanda matumba makumi asanu a feteleza otsika mtengo yemwe akuganizira kuti anthu ena amafuna kuzembetsa kuti akagulitse kwina | Anthu a mdera la mfumu Chisinga ku Kasungu alanda matumba makumi asanu a feteleza otsika mtengo yemwe akuganizira kuti anthu ena amafuna kuzembetsa kuti akagulitse kwina | Female | |
M'modzi mwa anthuwa, a Charles Dokera ati matumba makumi anayi anawapeza pa chipikisheni chomwe anthuwa anachita pa okha | M'modzi mwa anthuwa, a Tchalosi Dokera ati matumba makumi anayi anawapeza pa chipikisheni chomwe anthuwa anachita pa okha | Female | |
potsatira madandaulo oti adindo ena akuzembetsa fetelereza wa mderalo kumakagulitsa kwina | potsatira madandaulo oti adindo ena akuzembetsa fetelereza wa mderalo kumakagulitsa kwina | Female | |
Matumba ena khumi akuti awapeza atagwira galimoto yomwe inanyamula fetelezayo usiku ndipo sakudziwa kuti amapita naye kuti komanso cholinga chake | Matumba ena khumi akuti awapeza atagwira galimoto yomwe inanyamula fetelezayo usiku ndipo sakudziwa kuti amapita naye kuti komanso cholinga chake | Female | |
A Dokera ati anthu mderalo akapereka ku polisi ya Chisinga, mkulu yemwe amagulitsa feteleza mderalo komanso athetsa komiti yachitukuko ya mderalo | A Dokera ati anthu mderalo akapereka ku polisi ya Chisinga, mkulu yemwe amagulitsa feteleza mderalo komanso athetsa komiti yachitukuko ya mderalo | Female | |
poyiganizira kuti ikukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ntchito yogulitsa zipangizo zotsika mtengo mderalo. Apolisi akana kulankhulapo pa nkhaniyi | poyiganizira kuti ikukhudzidwa ndi kusokonekera kwa ntchito yogulitsa zipangizo zotsika mtengo mderalo. Apolisi akana kulankhulapo pa nkhaniyi | Female | |
Pali Kusamvana pa nkhani ya ma alawansi pakati pa adindo ndi aphunzitsi ophunzitsa chiyankhulo cha manja omwe pakadali pano | Pali Kusamvana pa nkhani ya ma alawansi pakati pa adindo ndi aphunzitsi ophunzitsa chiyankhulo cha manja omwe pakadali pano | Female | |
akuchita maphunziro a ntchitoyi pa koleji yosula aphunzitsi asukulu za pulayimale ku Mchinji | akuchita maphunziro a ntchitoyi pa koleji yosula aphunzitsi asukulu za pulayimale ku Mchinji | Female | |
Lolemba komanso lachiwiri sabata ino, aphunzitsiwa omwe alipo oposa 80, ananyanyala maphunzirowa | Lolemba komanso lachiwiri sabata ino, aphunzitsiwa omwe alipo oposa eite, ananyanyala maphunzirowa | Female | |
ati pokwiya ndi K4,200 yomwe akuwapatsa pa tsiku ponena kuti ndi chitonzo | ati pokwiya ndi fo sauzande thu handiledi kwacha yomwe akuwapatsa pa tsiku ponena kuti ndi chitonzo | Female | |
Aphunzitsiwa omwe achokera m'maboma a Lilongwe ndi Mchinji atiwuza kuti amayembekeza kuti adzilandira K45,000 pa tsiku kapena K31,000 yomwe ndi yovomerezeka ndi boma | Aphunzitsiwa omwe achokera m'maboma a Lilongwe ndi Mchinji atiwuza kuti amayembekeza kuti adzilandira fote faifi sauzande kwacha pa tsiku kapena fete wani sauzande kwacha yomwe ndi yovomerezeka ndi boma | Female | |
M'modzi mwa akuluakulu ku unduna wa za maphunziro a Lucy Magagula, omwe anakumana ndi anthuwa pamodzi ndi akuluakulu ena akana kulankhulapo pankhaniyi | M'modzi mwa akuluakulu ku unduna wa za maphunziro a Luse Magagula, omwe anakumana ndi anthuwa pamodzi ndi akuluakulu ena akana kulankhulapo pankhaniyi | Female | |
Bwalo lamilandu la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe lero likupitilira kumva mulandu okhudza katangale | Bwalo lamilandu la tchifi lezidenti Majesitileti ku Lilongwe lero likupitilira kumva mulandu okhudza katangale | Female | |
omwe nduna yakale yoona zamphamvu zamagetsi a Newton Kambala ndi akuluakulu ena awiri akuyankha | omwe nduna yakale yoona zamphamvu zamagetsi a Nyutoni Kambala ndi akuluakulu ena awiri akuyankha | Female | |
Pakadalipano oimira mmodzi mwa oganizilidwa mulandu a Chris Chaima Banda, a Wapona Kita akufunsa mafunso mboni yaboma pamulanduwu a Hellen Buluma | Pakadalipano oimira mmodzi mwa oganizilidwa mulandu a khilisi Chaima Banda, a Wapona Kita akufunsa mafunso mboni yaboma pamulanduwu a Heleni Buluma | Female | |
omwe anali ogwilizira udindo wa wachiwiri wakale wamkulu wabungwe loona za mafuta la NOCMA | omwe anali ogwilizira udindo wa wachiwiri wakale wamkulu wabungwe loona za mafuta la NOKIMA | Female | |
Mwazina, a Kita afunsa a Buluma ngati akudziwa za lamya yomwe inaimbidwa pogwilitsa ntchito foni ya a Buluma yomwe inaipeleka kale mmanja mwa bungwe la ACB | Mwazina, a Kita afunsa a Buluma ngati akudziwa za lamya yomwe inaimbidwa pogwilitsa ntchito foni ya a Buluma yomwe inaipeleka kale mmanja mwa bungwe la Esibi | Female | |
panthawiyi ndipo a Buluma anati sakudziwa za lamya yomwe inaimbidway | panthawiyi ndipo a Buluma anati sakudziwa za lamya yomwe inaimbidway | Female | |
A Kambala, a Chaima komanso a Enoch Chihana akuwaganizira kuti amafuna kuchita zakatangale pantchito yomweletsa mafuta a galimoto mdziko lino | A Kambala, a Chaima komanso a Enoki Chihana akuwaganizira kuti amafuna kuchita zakatangale pantchito yomweletsa mafuta a galimoto mdziko lino | Female | |
Abambo 90,000 ndi omwe achita m'dulidwe m'dziko muno m'malo mwa abambo okwana 200,000 omwe amayenela kudulidwa chaka chapitachi | Abambo nainte sauzande ndi omwe achita m'dulidwe m'dziko muno m'malo mwa abambo okwana thu handiledi sauzande omwe amayenela kudulidwa chaka chapitachi | Female | |
Mkulu woyang'anira ntchitoyi m'dziko muno a Martin Kapito wauza Zodiak kuti namondwe wa Freedy analepheretsa kuti afikire anthu omwe amafuna kuti awafikire mu ntchitoyi kaamba koti inayima kwa miyezi ingapo | Mkulu woyang'anira ntchitoyi m'dziko muno a Matini Kapito wauza Zodiyaki kuti namondwe wa fulede analepheretsa kuti afikire anthu omwe amafuna kuti awafikire mu ntchitoyi kaamba koti inayima kwa miyezi ingapo | Female | |
Iwo ati pakadali pano zipatala 200 zikupereka thandizo la m'dulidwe wa abambo ndipo Chaka chino akufuna afikire amuna 200,000 | Iwo ati pakadali pano zipatala thu handiledi zikupereka thandizo la m'dulidwe wa abambo ndipo Chaka chino akufuna afikire amuna thu handiledi sauzande | Female | |
Bwalo la milandu la First Grade magistrate ku Neno lalamula a Benito Mpapa azaka 63 kuti akhale ku ndende zaka khumi pogonana ndi mwana wazaka 16 | Bwalo la milandu la fesiti giledi majesitileti ku Neno lalamula a Benito Mpapa azaka sikisite fili kuti akhale ku ndende zaka khumi pogonana ndi mwana wazaka sikisitini | Female | |
A Mpapa omwe anali mlangizi wakale wamaphunziro a pulaimale m'bomali, ati awapatsa chilangochi kamba ka zaka zawo komanso kuti ndikoyamba kupalamula mlandu | A Mpapa omwe anali mlangizi wakale wamaphunziro a pulaimale m'bomali, ati awapatsa chilangochi kamba ka zaka zawo komanso kuti ndikoyamba kupalamula mlandu | Female | |
Mchigamulo chake, First Grade Magistrate Margret Khobili wati zomwe anachita a Mpapa nzosemphana ndi malamulo kotero apereka chilangochi kuti anthu ena atengelepo phunziro | Mchigamulo chake, fesiti giledi majesitileti magileti Khobili wati zomwe anachita a Mpapa nzosemphana ndi malamulo kotero apereka chilangochi kuti anthu ena atengelepo phunziro | Female | |
A Mpapa adawamanga m'mwezi wa June chaka chatha. Mvula ya mphamvu komanso mphepo yasasula malata pa chipinda chochilira amayi pa chipatala cha M'deza | A Mpapa adawamanga m'mwezi wa Juni chaka chatha. Mvula ya mphamvu komanso mphepo yasasula malata pa chipinda chochilira amayi pa chipatala cha M'deza | Female | |
komanso Chipinda chothandizira odwala pa chipatala cha Maonde ku Dedza. M'neneri wa za umoyo m'bomali a Mwai Liabunya | komanso Chipinda chothandizira odwala pa chipatala cha Maonde ku Dedza. M'neneri wa za umoyo m'bomali a Mwai Liyabunya | Female | |
watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti ntchito yopereka thandizo la za umoyo mzipatalazi yakhudzika kamba Ka ichi | watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti ntchito yopereka thandizo la za umoyo mzipatalazi yakhudzika kamba Ka ichi | Female | |
Iwo apemphanso mabungwe kuti awathandize ndi zipangizo zokonzera zipatalazi. Khwimbi la anthu lasonkhana pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe | Iwo apemphanso mabungwe kuti awathandize ndi zipangizo zokonzera zipatalazi. Khwimbi la anthu lasonkhana pa bwalo la ndege la Kamuzu ku Lilongwe | Female | |
komwe kuli mwambo olandira katswiri wa ku tsogolo mu timu ya mpira wa miyendo ya asungwana ya dziko lino, ya Scorchers, komanso Inter Milan Tabitha Chawinga | komwe kuli mwambo olandira katswiri wa ku tsogolo mu timu ya mpira wa miyendo ya asungwana ya dziko lino, ya sikochazi, komanso inta milani Tabitha Chawinga | Female | |
Chawinga wafika kuchokera ku Italy kumene watenga mphoto ya katswiri ogoletsa zigoli zambiri Golden Boot | Chawinga wafika kuchokera ku itale kumene watenga mphoto ya katswiri ogoletsa zigoli zambiri godeni buti | Female | |
Anthu ochuluka omwe ali ku bwalo la ndegeli akuyimba nyimbo zomutamanda kwatswiriyu komanso zosonyeza chimwemwe | Anthu ochuluka omwe ali ku bwalo la ndegeli akuyimba nyimbo zomutamanda kwatswiriyu komanso zosonyeza chimwemwe | Female | |
Ku Chiradzulu, a polisi amanga abambo awiri omwe akuwaganizira kuti apha nzawo, a Mavuto Liphama a zaka 20 zakubadwa ati kamba kolimbilana hule | Ku Chiradzulu, a polisi amanga abambo awiri omwe akuwaganizira kuti apha nzawo, a Mavuto Liphama a zaka twente zakubadwa ati kamba kolimbilana hule | Female | |
M’neneri wapolisi m'bomali a Cosmas Kagulo wauza Zodiak Online kuti awiriwa ndi a Mphatso Labana a zaka 18 | M’neneri wapolisi m'bomali a kosimasi Kagulo wauza Zodiyaki Onilaini kuti awiriwa ndi a Mphatso Labana a zaka eitini | Female | |
komanso a Maxwell Kadaya a zaka 20 onse ochokera m'dera la mfumu yaikuli Likoswe m'bomali | komanso a Makisiwelo Kadaya a zaka twente onse ochokera m'dera la mfumu yaikuli Likoswe m'bomali | Female | |
Malinga ndi a polisi malemuwa sabata latha anapita ku malo ena omwela mowa, komwe anapalanako ubwenzi ndi mtsikana oyendayendayu ndipo abambo awiriwa anawamenya mpaka Ku wasiya ali chikomokere | Malinga ndi a polisi malemuwa sabata latha anapita ku malo ena omwela mowa, komwe anapalanako ubwenzi ndi mtsikana oyendayendayu ndipo abambo awiriwa anawamenya mpaka Ku wasiya ali chikomokere | Female | |
Anthu akufuna kwabwino anathamangira ndimalemuwa ku chipatala cha Nguludi Mission asanawatumiza ku chipatala cha Queens komwe amwalira dzuro | Anthu akufuna kwabwino anathamangira ndimalemuwa ku chipatala cha Nguludi Mishoni asanawatumiza ku chipatala cha kwinzi komwe amwalira dzuro | Female | |
Aphunzitsi omwe anamaliza maphunziro awo m'sukulu zosiyanasiyana kuchokera m'chaka cha 2020, adandaula kaamba kakupitilira kuchedwa kwaboma kuti awalembe ntchito | Aphunzitsi omwe anamaliza maphunziro awo m'sukulu zosiyanasiyana kuchokera m'chaka cha twente twente, adandaula kaamba kakupitilira kuchedwa kwaboma kuti awalembe ntchito | Female | |
Ena mwa aphunzitsiwa a Damiano Kapito komanso a Moses Fabiano auza Zodiak kuti onse omwe anamaliza maphunziro | Ena mwa aphunzitsiwa a Damiano Kapito komanso a Mozesi fabiyano auza Zodiyaki kuti onse omwe anamaliza maphunziro | Female | |
kuyambira IPTE 13,14,15,16 ndi 17 sanawalembebe ntchito | kuyambira IPITE fetini, fotini, fifitini, sikisitini ndi seventini sanawalembebe ntchito | Female | |
M'neneri mu unduna wa zamaphunziro a Mphatso Nkuonera wati aphunzitsi wa adekhe poti ndalama zinayikidwa kale mu ndondomeko ya za chuma ya chaka chino | kuyambira IPTE 13,14,15,16 ndi 17 sanawalembebe ntchito | Female | |
kuti awalembe ntchito ndipo akutsatira ndondomeko zoikika kuti izi zitheke. Katswiri pa nkhani za ulimi a Ronald Chilumpha | kuti awalembe ntchito ndipo akutsatira ndondomeko zoikika kuti izi zitheke. Katswiri pa nkhani za ulimi a lonadi Chilumpha | Female | |
wapempha alimi kuti asamale bwino mbatata zomwe akolora pomwe pali chiopsezo kuti njala itha kugwa m’dziko muno | wapempha alimi kuti asamale bwino mbatata zomwe akolora pomwe pali chiopsezo kuti njala itha kugwa m’dziko muno | Female | |
A Chilumpha ati alimi atha kuchita izi popala makaka a mbatata zomwe ndi zochuluka zedi m’madera ena a dziko lino kuti adzathe kugwiritsa ntchito mtsogolo | A Chilumpha ati alimi atha kuchita izi popala makaka a mbatata zomwe ndi zochuluka zedi m’madera ena a dziko lino kuti adzathe kugwiritsa ntchito mtsogolo | Female | |
Iwo aonjezeranso kuti kuchuluka kwa mbatatazi kupereke phunziro kwa adindo kuti pakhale ndondomeko zabwino zokonzera katundu osiyanasiyana | Iwo aonjezeranso kuti kuchuluka kwa mbatatazi kupereke phunziro kwa adindo kuti pakhale ndondomeko zabwino zokonzera katundu osiyanasiyana | Female | |
kuchokera ku mbewu ngati izi monga ufa wa mbatata ndi zina zomwe zingathe kugulitsidwa ngakhale m’maiko a kunja | kuchokera ku mbewu ngati izi monga ufa wa mbatata ndi zina zomwe zingathe kugulitsidwa ngakhale m’maiko a kunja | Female | |
Apolisi ku Mwanza achenjeza anthu okhala moyandikana ndi mtsinje wa Nkhwivi kuti akhale osamala kaamba ka ng'ona yomwe akuiganizira kuti ndiyolusa yomwe ati itha kuvulaza anthu | Apolisi ku Mwanza achenjeza anthu okhala moyandikana ndi mtsinje wa Nkhwivi kuti akhale osamala kaamba ka ng'ona yomwe akuiganizira kuti ndiyolusa yomwe ati itha kuvulaza anthu | Female | |
Ofalitsa nkhani zapolisi ya Mwanza, a Hope Kasakula ati iwo pamodzi ndi ogwira ntchito azachilengedwe akusaka chirombo chi | Ofalitsa nkhani zapolisi ya Mwanza, a Hopu Kasakula ati iwo pamodzi ndi ogwira ntchito azachilengedwe akusaka chirombo chi | Female | |
A Kasakula ati nkofunika kuti anthu ayesetse kupewa kufikira ng'onayi mpaka ataigwira | A Kasakula ati nkofunika kuti anthu ayesetse kupewa kufikira ng'onayi mpaka ataigwira | Female | |
Apolisi m'boma la Phalombe amanga bambo wa zaka 29, pomuganizira kuti anadula ziwalo zobisika za mwana wake wa m'muna wa zaka zisanu ndi zinayi (9) | Apolisi m'boma la Phalombe amanga bambo wa zaka twente naini, pomuganizira kuti anadula ziwalo zobisika za mwana wake wa m'muna wa zaka zisanu ndi zinayi (naini) | Female | |
M'neneri wa apolisi, mbomali, a Jimmy Kapanja, ati bamboyo ndiwa m'mudzi wa Mwalala, mfumu yaikulu Nazombe m'bomali | M'neneri wa apolisi, mbomali, a Jime Kapanja, ati bamboyo ndiwa m'mudzi wa Mwalala, mfumu yaikulu Nazombe m'bomali | Female | |
A Kapanja ati bamboyu ananyengelera mayi a mwanayu omwe adasiyana nawo banja m'chaka cha 2018 | A Kapanja ati bamboyu ananyengelera mayi a mwanayu omwe adasiyana nawo banja m'chaka cha twente eitini | Female | |
kuti azikakhala ndi mwanayu m'dziko la Mozambique koma mayiyu anapempha mkuluyu kuti akumane ndi malume awo asanamutenge | kuti azikakhala ndi mwanayu m'dziko la Mozambiki koma mayiyu anapempha mkuluyu kuti akumane ndi malume awo asanamutenge | Female | |
Malinga ndi a Kapanja, bamboyo ananyengeleranso mayiyo kuti apite ndi mwanayu pa sitolo ina kuti akamugulire zinthu | Malinga ndi a Kapanja, bamboyo ananyengeleranso mayiyo kuti apite ndi mwanayu pa sitolo ina kuti akamugulire zinthu | Female | |
koma m'malo mwake anamutengera ku mtsinje komwe anamudula ziwalo zobisika ndikuthawa. Bamboyu akaonekera mbwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wovulaza munthu, malinga ndi apolisi | koma m'malo mwake anamutengera ku mtsinje komwe anamudula ziwalo zobisika ndikuthawa. Bamboyu akaonekera mbwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wovulaza munthu, malinga ndi apolisi | Female | |
Anthu omwe chiwelengelo chawo sichikudziwika akuganizilidwa kuti amwalira pomwe enanso ambiri amvulara potsatira ngozi ya galimoto | Anthu omwe chiwelengelo chawo sichikudziwika akuganizilidwa kuti amwalira pomwe enanso ambiri amvulara potsatira ngozi ya galimoto | Female | |
imene yachitika pa Tenenthe, pakati pa nseu wa Chitipa ndi Karonga pamene amachokera ku mpira. Anthuwa anakwera galimoto la mtundu wa lorry, nambala yake NA 6449 | imene yachitika pa Tenenthe, pakati pa nseu wa Chitipa ndi Karonga pamene amachokera ku mpira. Anthuwa anakwera galimoto la mtundu wa lore, nambala yake enie sikisite folo fote naini | Female | |
ndipo ndi a timu ya Nyungwe United ya ku Karonga imene inakasewera ndi timu ya Chitipa Hammers pa bwalo la Jombajomba mu mpikisano wa Northern Region Football Association and FAM Moto Division 1 | ndipo ndi a timu ya Nyungwe yunaitedi ya ku Karonga imene inakasewera ndi timu ya Chitipa Hamazi pa bwalo la Jomba jomba mu mpikisano wa noveni lijoni futubo asosiyeshoni andi famu moto Divizyoni wani | Female | |
A polisi ndi a chipatala akuyembekezeka kutulutsa lipoti la chimene chachititsa ngoziyi komanso chiwerengero chenicheni. Pakadali pano, mlembi wamkulu wa Northern Region Football Association, Masiya Nyasulu | A polisi ndi a chipatala akuyembekezeka kutulutsa lipoti la chimene chachititsa ngoziyi komanso chiwerengero chenicheni. Pakadali pano, mlembi wamkulu wa Noveni lijoni futubo asosiyeshoni, Masiya Nyasulu | Female | |
wati masewero onse a mpikisanowu komanso a ligi ya Simama and Sons-SIMSO and Innobuild Premier Division, a la mulungu pa 4 June, 2023, awayimitsa | wati masewero onse a mpikisanowu komanso a ligi ya Simama and Sanzi-Simuso andi inobyudi pulimiya divizyoni , a la mulungu pa folo juni, twente twente fili, awayimitsa | Female | |
Anthu okhala m'mudzi wa Mpokonyola kwa mfumu yaikulu Katunga m'boma la Chikwawa adzudzura bungwe logulitsa magetsi la ESCOM | Anthu okhala m'mudzi wa Mpokonyola kwa mfumu yaikulu Katunga m'boma la Chikwawa adzudzura bungwe logulitsa magetsi la Esikomu | Female | |
kaamba kochedwa kubwezeretsa makina a magetsi a Transformer omwe adawonongeka pa msika wa pa Dembo kumapeto a chaka chatha | kaamba kochedwa kubwezeretsa makina a magetsi a Thilansifoma omwe adawonongeka pa msika wa pa Dembo kumapeto a chaka chatha | Female | |
Gulupu Mpokonyola yauza Zodiak Online kuti izi zachititsa anthu okhala mozungulira msikawu komanso madela ena omwe amadalira makinawa kukumana ndi mavuto osiyanasiyana | Gulupu Mpokonyola yauza Zodiyaki Onilaini kuti izi zachititsa anthu okhala mozungulira msikawu komanso madela ena omwe amadalira makinawa kukumana ndi mavuto osiyanasiyana | Female | |
maka amayi omwe akuti akuyenda mtunda wautali kupita ku chigayo | maka amayi omwe akuti akuyenda mtunda wautali kupita ku chigayo | Female | |
A Limitedi Chapalapata, omwe amachita bizinezi yogulitsa zakumwa ndi katundu wina ati bizinesi yawo yalowa pansi kwambiri kamba kavutoli | A Limitedi Chapalapata, omwe amachita bizinezi yogulitsa zakumwa ndi katundu wina ati bizinesi yawo yalowa pansi kwambiri kamba kavutoli | Female | |
Iwo ati ntchito zina za malonda ngati kutchaja mafoni komanso kumeta m'mutu za sokonekelera | Iwo ati ntchito zina za malonda ngati kutchaja mafoni komanso kumeta m'mutu za sokonekelera | Female | |
Pakadali pano, m'neneri wa bungweli, a Kity Chingota ati vutoli akulidziwa ndipo akuyetsetsa kuti abwezeretse makinawa mdelari | Pakadali pano, m'neneri wa bungweli, a Kite Chingota ati vutoli akulidziwa ndipo akuyetsetsa kuti abwezeretse makinawa mdelari | Female | |
Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo m'dziko muno la FAM lero lakhazikitsa ntchito yomwe cholinga chake ndikutukula masewero a mpira wa miyendo | Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo m'dziko muno la FAMU lero lakhazikitsa ntchito yomwe cholinga chake ndikutukula masewero a mpira wa miyendo | Female | |
wa asungwana m'dziko muno ndi thandizo la bungwe la FIFA. M'modzi mwa akuluakulu a bungweli a Chimango Munthali | wa asungwana m'dziko muno ndi thandizo la bungwe la FIFA. M'modzi mwa akuluakulu a bungweli a Chimango Munthali | Female | |
wauza Zodiak kuti iyi ndi imodzi mwa ndondomeko za bungwe la FIFA yomwe cholinga chake ndikupititsa patsogolo masewerowa | wauza Zodiyak kuti iyi ndi imodzi mwa ndondomeko za bungwe la FIFA yomwe cholinga chake ndikupititsa patsogolo masewerowa | Female | |
Wapampando wa bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo wa asungwana m'dziko muno a Adelaide Migogo, wati ndondomekoyi ithandizila kutukula masewerowa | Wapampando wa bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo wa asungwana m'dziko muno a Adelaide Migogo, wati ndondomekoyi ithandizila kutukula masewerowa | Female | |
Ntchitoyi ayikhazikitsa lero pa bwalo la Civo ku Lilongwe ndipo cholinga chake ndikuwadziwitsa anthu za masewerowa komanso kulimbikitsa asungwana kutenga mbali m'masewerowa | Ntchitoyi ayikhazikitsa lero pa bwalo la Civo ku Lilongwe ndipo cholinga chake ndikuwadziwitsa anthu za masewerowa komanso kulimbikitsa asungwana kutenga mbali m'masewerowa | Female | |
Kampani ya Sycamore Consult Limited yati ndalama zili pa dziko pompano osati kwina, chofunika n'kupeza njira kuti zikhale ndi anthu ambiri | Kampani ya Sikamo konzati limitedi yati ndalama zili pa dziko pompano osati kwina, chofunika n'kupeza njira kuti zikhale ndi anthu ambiri | Female | |
Mkulu wa bungweli a Audrey Mwala wati ngakhale chuma sichikuyenda bwino, ndi zotheka anthu kupeza njira zopezera ndalama | Mkulu wa bungweli a Odile Mwala wati ngakhale chuma sichikuyenda bwino, ndi zotheka anthu kupeza njira zopezera ndalama | Female | |
Iwo auza atolankhani ku Blantyre lero kuti akonza msonkhano umene udzasonkhanitse akatswiri pa za malonda komanso chuma kuti adzafotokoze njirazi ku Blantyre mu August chaka chino | Iwo auza atolankhani ku Bulantaya lero kuti akonza msonkhano umene udzasonkhanitse akatswiri pa za malonda komanso chuma kuti adzafotokoze njirazi ku Bulantaya mu Ogasiti chaka chino | Female | |
Mmodzi mwa oyimbira mpira wa miyendo mdziko lino Godfrey Nkhakananga amusankha pa mndandanda wa ma referee amene ayimbire mpikisano wa chaka chino wa COSAFA Senior Men's Challenge | Mmodzi mwa oyimbira mpira wa miyendo mdziko lino Godifule Nkhakananga amusankha pa mndandanda wa ma lifali amene ayimbire mpikisano wa chaka chino wa KOSAFA Seniyo Menzi Tchalenji | Female | |
umene uchitikire mu mzinda wa Durban ku South Africa kuyambira pa 5 mpaka pa 17 July | umene uchitikire mu mzinda wa Dabeni ku saufi afilika kuyambira pa faifi mpaka pa seventini julai | Female | |
Kalata ya bungwe la Council of Southern African Football Associations( COSAFA) imene wasayinira mkulu oyendetsa ntchito za bungweli Sue Destombes kupita ku bungwe la FAM | Kalata ya bungwe la Khanso of sauveni afulikani futubo asosiyeshoni ( KOSAFA) imene wasayinira mkulu oyendetsa ntchito za bungweli Su Desitombesi kupita ku bungwe la FAMU | Female | |
yati Nkhakananga amene ndi mphunzitsi pa sukulu ya sekondale ya Chipoka ku Salima akapezeke ku South Africa pomafika pa 30 June | yati Nkhakananga amene ndi mphunzitsi pa sukulu ya sekondale ya Chipoka ku Salima akapezeke ku Saufi afilika pomafika pa fete juni | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.