audio
audioduration (s)
1.12
18.5
raw_text
stringlengths
1
297
normalized_text
stringlengths
1
267
gender
stringclasses
16 values
Wa pampando wa committee, a Raph Juma, adati committee yawo ili ndi chiyembekezo choti akuluakuluwo, akulongosola momwe zinthu ziliri, ndipo mitima ya a Malawi, ikhazikike.
Wa pampando wa Komiti, a Rafu Juma, adati Komiti yawo ili ndi chiyembekezo choti akuluakuluwo, akulongosola momwe zinthu ziliri, ndipo mitima ya a Malawi, ikhazikike.
female
Vuto lamafuta a galimoto, lomwe lanyanya tsopano, kamba ka kukwera kwa mtengo wagalimoto zonyamula anthu komaso zakweza
Vuto lamafuta a galimoto, lomwe lanyanya tsopano, kamba ka kukwera kwa mtengo wagalimoto zonyamula anthu komaso zakweza
female
Komaso zakweza nkhawa yoti izi zikhoza kusokoneza programme ya zipangizo za ulimi, zotsika mtengo ya AIP.
Komaso zakweza nkhawa yoti izi zikhoza kusokoneza purogiramu ya zipangizo za ulimi, zotsika mtengo ya eayepi.
female
Malingana ndi a Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) omwe amayang’anira zamafuta, vutoli lakula chifukwa dziko la Malawi lilibe ndalama zakunja zoyitanitsira mafuta kuchoka kunja.
Malingana ndi a Malawi Eneje Regulatare Othorite (MERA) omwe amayang’anira zamafuta, vutoli lakula chifukwa dziko la Malawi lilibe ndalama zakunja zoyitanitsira mafuta kuchoka kunja.
female
Mneneri wa MERA a Fitina Khonje, adatsimikiza polankhula ndi Zodiak Broadcasting Station, kuti ma company oyitanitsa mafuta.
Mneneri wa MERA a Fitina Khonje, adatsimikiza polankhula ndi Zodiyaki Burodikasiting'i Sitashoni, kuti ma kampani oyitanitsa mafuta.
female
Akulephera kutero chifukwa akufunika ndalama za kunja, kuti athe kugula mafuta kunjako nkubweretsa kuno.
Akulephera kutero chifukwa akufunika ndalama za kunja, kuti athe kugula mafuta kunjako nkubweretsa kuno.
femlae
Nkhaniyi ikuyha pafupifupi zaka ziwiri tsopano, kuyambira pomwe a MERA, a National Oil Company of Malawi NOCMA,
Nkhaniyi ikuyha pafupifupi zaka ziwiri tsopano, kuyambira pomwe a MERA, a Nashono Oyilo Kompany ofU Malawi NOKIMA,
female
Komaso ma company oyitanitsa mafuta a galimoto kunja, adayamba kusambira mmanja kusowa kwa ndalama za kunja.
Komaso ma kompani oyitanitsa mafuta a galimoto kunja, adayamba kusambira mmanja kusowa kwa ndalama za kunja.
female
Koma kadawulo wa bonding ku school ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources LUANAR a Christopher Mbukwa.
Koma kadawulo wa bonding ku sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe Univesite ofu Agirikacha andi Natchuro Risosesi (LUWANA) a Khirisitofa Mbukwa.
female
Ati boma likapanda kusaka ndalama zakunjazo nsanga, livutika kunyamula fetilizer wa AIP.
Ati boma likapanda kusaka ndalama zakunjazo nsanga, livutika kunyamula feteleza wa eayipi.
female
Vuto ilili ndilofunika njira yokhazikika kuthanirana nalo, osati zomwe zikuchitikazi, uno ndi October.
Vuto ilili ndilofunika njira yokhazikika kuthanirana nalo, osati zomwe zikuchitikazi, uno ndi Okotoba.
female
Ndipo boma limayenera kuyambapo kunyamula fetilizer wa AIP, koma m’malomwake, mpomwe mafuta afika povutitsitsa. Atero a Mbukwa.
Ndipo boma limayenera kuyambapo kunyamula feteleza wa eayipi, koma m’malomwake, mpomwe mafuta afika povutitsitsa. Atero a Mbukwa.
female
Mlembi wa unduna wa zamalimidwe a Dikis Kampani, adati, ma company 13, adasayina kale kuti agulitsa nawo fetilizer wa AIP.
Mlembi wa unduna wa zamalimidwe a Dikisi Kampani, adati, ma kompani fetini, adasayina kale kuti agulitsa nawo feteleza wa eayipi.
female
Koma akudikira unduna wa zachuma bank ya Reserve Bank of Malawi ndi ma Bank ena kuti athandize ndi ndalama za kunja.
Koma akudikira unduna wa zachuma banki ya Rezevu Banki ofu Malawi ndi ma Banki ena kuti athandize ndi ndalama za kunja.
female
Iwo adati pali fertilizer yemwe ali ku madoko a mayiko ena ofunika kukatengedwa, komaso fertilizer wina alikale m’dziko momwemuno, ndipo boma liyamba kumutumiza ku misika yomwe alimi angakagulire.
Iwo adati pali feteleza yemwe ali ku madoko a mayiko ena ofunika kukatengedwa, komaso feteleza wina alikale m’dziko momwemuno, ndipo boma liyamba kumutumiza ku misika yomwe alimi angakagulire.
female
Fertilizer apezeka, tuyembekeza wina yemwe ali m’madoko akunja, komaso kupatula apo tili ndi fertilizer wina m’dziko momwemuno yemwe tiyambirire kugawa. Adatero a Kampani.
feteleza apezeka, tuyembekeza wina yemwe ali m’madoko akunja, komaso kupatula apo tili ndi feteleza wina m’dziko momwemuno yemwe tiyambirire kugawa. Adatero a Kampani.
female
Koma a Mbukwa achenjeza kuti posachedwapa tikhala tikulowa mwenzi wa November, ndipo alimi amayenera kuti ayamba kale kugula fertilizer kapena wafika kale m’misika kuti alimi azikhala nchikhulupirilo.
Koma a Mbukwa achenjeza kuti posachedwapa tikhala tikulowa mwenzi wa November, ndipo alimi amayenera kuti ayamba kale kugula feteleza kapena wafika kale m’misika kuti alimi azikhala nchikhulupirilo.
female
Apapatu zikusonyeza kuti ngati tifike November ndi December, ndalama zakunja zisanawoneke, ndiyekuti mafuta a galimoto, akhalabe akuvuta, ndipo izi zikhudza kwambiri programme ya AIP. Atero a Mbukwa.
Apapatu zikusonyeza kuti ngati tifike Novemba ndi Disemba, ndalama zakunja zisanawoneke, ndiyekuti mafuta a galimoto, akhalabe akuvuta, ndipo izi zikhudza kwambiri purogiramu ya eayipi. Atero a Mbukwa.
female
Pozungulira zungulira m’mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu, atolankhani athu adapeza kuti galimoto zambiri, zinangoyimikidwa m’malo wogulitsa mafuta kudikira mwa chiyembekezo kuti mafuta akhoza kufika.
Pozungulira zungulira m’mizinda ya Bulantaya, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu, atolankhani athu adapeza kuti galimoto zambiri, zinangoyimikidwa m’malo wogulitsa mafuta kudikira mwa chiyembekezo kuti mafuta akhoza kufika.
female
Anthu ena adawuza atolankhaniwo kuti ntchito zawo zayima chifukwa akutaya nthawi nkudikirira mafuta, komaso ena adati, zikawavutitsitsa akugona m’malo ogulitsa mafutawo.
Anthu ena adawuza atolankhaniwo kuti ntchito zawo zayima chifukwa akutaya nthawi nkudikirira mafuta, komaso ena adati, zikawavutitsitsa akugona m’malo ogulitsa mafutawo.
female
Tidapezaso kuti eni agalimoto ozingwa, akukagula mafuta ku msika wambanda komwe akugula litre limodzi pa mtengo wa 5000 kwacha.
Tidapezaso kuti eni agalimoto ozingwa, akukagula mafuta ku msika wambanda komwe akugula lita limodzi pa mtengo wa fayifi sauzandi kwacha.
female
Mmalo mwa 1700 kwacha ndipo izi zachititsa kuti eni galimoto zonyamula anthu, akweze mitengo.
Mmalo mwa wani sauzandi seveni handiredi kwacha, ndipo izi zachititsa kuti eni galimoto zonyamula anthu, akweze mitengo.
female
Ena mwa eni galimoto zoterozo, akutha masiku angapo asadapite kumnsewu chifukwa chodikira mafuta kuti agule pa mtengo wovomelezeka ndi boma kuti mwina apangeko phindu.
Ena mwa eni galimoto zoterozo, akutha masiku angapo asadapite kumnsewu chifukwa chodikira mafuta kuti agule pa mtengo wovomelezeka ndi boma kuti mwina apangeko phindu.
female
Dziko la Malawi, likugwiritsa ntchito pafupifupi 3,000,000,000. kwacha pachaka kupereka thandizo kwa amayi amene anachotsa mimba pogwiritsa ntchito njira zosatetezeka.
Dziko la Malawi, likugwiritsa ntchito pafupifupi frir biliyoni kwacha pachaka kupereka thandizo kwa amayi amene anachotsa mimba pogwiritsa ntchito njira zosatetezeka.
female
Watero m’modzi mwa ma Doctor azawubereki, a Francis Makiya, polankhula pomwe bungwe la Centre for Solutions Journalism (CSJ)
Watero m’modzi mwa ma Dokotala azawubereki, a Furansisi Makiya, polankhula pomwe bungwe la Senta fo Solushonzi Jonalizimu (SI ESI JEYI)
female
Linachititsa maphunziro atolankhani pankhani zokhudza kuchotsa pathupi, a Makiya adati, zipatala za boma zimalola kuthandiza amayi amene anachotsa mimba njira zosavomerezeka.
Linachititsa maphunziro atolankhani pankhani zokhudza kuchotsa pathupi, a Makiya adati, zipatala za boma zimalola kuthandiza amayi amene anachotsa mimba njira zosavomerezeka.
female
Ngakhale malamulo amaletsa kuchotsa mimba, amayi ena amatero pa zifukwa zosiyanasiyana.
Ngakhale malamulo amaletsa kuchotsa mimba, amayi ena amatero pa zifukwa zosiyanasiyana.
female
Ena amakhala kuti akuwopa kuti maphunziro athera panjira, mwina mimbayo siyamuna awo, kapena akuwopa kutonzedwa komaso ena amawopa kutumbiza.
Ena amakhala kuti akuwopa kuti maphunziro athera panjira, mwina mimbayo siyamuna awo, kapena akuwopa kutonzedwa komaso ena amawopa kutumbiza.
female
Poti izi sizikuchitika, tikawona padziko lonse, mayiko amene ali ndi malamulo okhwima, ndikumene amayi amachotsa mimba mosadziteteza, Iwo adatero.
Poti izi sizikuchitika, tikawona padziko lonse, mayiko amene ali ndi malamulo okhwima, ndikumene amayi amachotsa mimba mosadziteteza, Iwo adatero.
female
A Makiya omwe ndi mlembi wankulu wabungwe lothana ndi kuchotsa mimba mosatetezeka la Cuallision for the prevention of unsafe abortion, anati nzovuta kuti amayi omwe amachotsa mimba mosayenera.
A Makiya omwe ndi mlembi wankulu wabungwe lothana ndi kuchotsa mimba mosatetezeka la kualishoni fo the purivenshoni ofu anisefu aboshoni anati nzovuta kuti amayi omwe amachotsa mimba mosayenera.
female
Pogwiritsa ntchito mitengo ya chinangwa kapena nsatsi, masipokosi, mabotolo a galasi ngakhalenso mankhwala ena akuchipatala, amapita kuchipatala komwe amathandizidwa.
Pogwiritsa ntchito mitengo ya chinangwa kapena nsatsi, masipokosi, mabotolo a galasi ngakhalenso mankhwala ena akuchipatala, amapita kuchipatala komwe amathandizidwa.
female
Ngakhale zikudziwika kuti amene achotsa mimba makamaka zipatala zomwe sizaboma, amagwiritsa ntchito ndalama zosaposa 20,000 kwacha.
Ngakhale zikudziwika kuti amene achotsa mimba makamaka zipatala zomwe sizaboma, amagwiritsa ntchito ndalama zosaposa tewente sauzandi kwacha.
female
Nzovuta kudziwa kuti amayi amene achotsa mimba mnjira zosatetezeka, amagwiritsa ntchito ndalama zingati, kuti athandizidwe kuchotsa zotsalira mzipatala za boma, chifukwa zimatengera kuti mimba inalipati nanga avulala motani.
Nzovuta kudziwa kuti amayi amene achotsa mimba mnjira zosatetezeka, amagwiritsa ntchito ndalama zingati, kuti athandizidwe kuchotsa zotsalira mzipatala za boma, chifukwa zimatengera kuti mimba inalipati nanga avulala motani.
female
Chinaso chimene ambiri sitiwerengera ndi nthawi imene amayi akhala mchipatala, kuti athandizidwe. Adatero iwo.
Chinaso chimene ambiri sitiwerengera ndi nthawi imene amayi akhala mchipatala, kuti athandizidwe. Adatero iwo.
female
Malinga ndi kafukufuku yemwe bungwe la Gas matcher mogwirizana ndi school ya madotolo ya college of medicine, adachita mu 2014,
Malinga ndi kafukufuku yemwe bungwe la Gasi matcha mogwirizana ndi sukulu ya madotolo ya Koleji ofu medisini, adachita mu tuwentr fotini,
female
Amayi azaka pakati ndi 16 ndi 18 mwa 100, amene ali ndi pathupi, amamwalira kamba kofuna kuchotsa pathupipo.
Amayi azaka pakati ndi sikisi ndi eyitini mwa wani handiredi, amene ali ndi pathupi, amamwalira kamba kofuna kuchotsa pathupipo.
female
Malinga ndi kafukufukuyo, amayi 141,000, adachotsa mimba mchaka cha 2015, ndipo 60 mwa amayi 100, amene anachotsa mimbawo, anakalandira thandizo mzipatala za boma.
Malinga ndi kafukufukuyo, amayi wani handiredi andi fote-wani sauszandi, adachotsa mimba mchaka cha tuwente fifitini, ndipo sikisite mwa amayi wani handiredi, amene anachotsa mimbawo, anakalandira thandizo mzipatala za boma.
female
Kafukufuku akusonyezaso kuti mwa amayi 100 aliwonse amene adachotsa mimba mnjira zosatetezeka,64.4, adali wokhala m’madera akumudzi.
Kafukufuku akusonyezaso kuti mwa amayi wani handiredi aliwonse amene adachotsa mimba mnjira zosatetezeka,sikisite-folo poyinti folo, adali wokhala m’madera akumudzi.
female
Potengera maphunziro,12.1 mwa 100 aliwonse adaphunzirapo ku primary,54.3 mwa 100, adalowako mkalasi za secondary pomwe 33.6, adapitirira apo.
Potengera maphunziro,thuwelofu poyinti wani mwa wani handiredi aliwonse adaphunzirapo ku purayimare,fifite-folo poyinti firi mwa wani handiredi, adalowako mkalasi za sekondare pomwe sete-firi poyinti sikisi, adapitirira apo.
female
Potengera chipembedzo, amayi 74.4 mwa 100 aliwonse ndi a chikhirisitu, amayi 10.3, a chisilamu, ndipo 14.6 ndi azipembedzo zina,pomwe 0.7, alibe chipembedzo.
Potengera chipembedzo, amayi sevente folo poyinti folo mwa wani handiredi aliwonse ndi a chikhirisitu, amayi teni poyinti firi, a chisilamu, ndipo fotini poyinti sikisi ndi azipembedzo zina, pomwe ziro poyinti seveni, alibe chipembedzo.
female
Mkulu wabungwe la CSJ a Brian Ligomeka, adati ambiri amanena kuti mabungwe ndiomwe amaene akufuna kuti lamulolo lisinthe.
Mkulu wabungwe la si esi jeyi a Burayani Ligomeka, adati ambiri amanena kuti mabungwe ndiomwe amaene akufuna kuti lamulolo lisinthe.
female
Ndikulingana ndi momwe lirili dziko la Zambia, koma zowona kake nzoti Malawi Law Commission, ndilo lidapempha zoti lamulo lisinthe, litachita kafukufuku pakati pa a Malawi osiyanasiyana.
Ndikulingana ndi momwe lirili dziko la Zambia, koma zowona kake nzoti Malawi Lo komisoni, ndilo lidapempha zoti lamulo lisinthe, litachita kafukufuku pakati pa a Malawi osiyanasiyana.
female
Ena mwa amene adasayinira kuti lamulo litasintha, ndi mabungwe azipembedzo zikuluzikulu m’dzikomuno ndi mafumu. Chonchotu iyi si bill ya a mabungwe, koma nthambi ya boma. Adatero iwo.
Ena mwa amene adasayinira kuti lamulo litasintha, ndi mabungwe azipembedzo zikuluzikulu m’dzikomuno ndi mafumu. Chonchotu iyi si bilu ya a mabungwe, koma nthambi ya boma. Adatero iwo.
female
Nkhani imeneyo tidayimva, koma chodandawulitsa nchoti, plan yo yabwera nthawi yolakwika, pomwe fertilizer adakwera mtengo, komaso ndalama ikuvuta kupeza. Atero a Mazengela.
Nkhani imeneyo tidayimva, koma chodandawulitsa nchoti, pulaniyo yabwera nthawi yolakwika, pomwe feteleza adakwera mtengo, komaso ndalama ikuvuta kupeza. Atero a Mazengela.
female
Koma mfumu Mwabulawo ya ku Mzimba idati, nkofunika kulipatsa mpata boma, kuti ligwiritse ntchito ndondomeko yomwe lakoza, chifukwa zithandiza kuti magulu osiyanasiyana, apindule nawo.
Koma mfumu Mwabulawo ya ku Mzimba idati, nkofunika kulipatsa mpata boma, kuti ligwiritse ntchito ndondomeko yomwe lakoza, chifukwa zithandiza kuti magulu osiyanasiyana, apindule nawo.
female
Ngati mukumvetsetsa boma, plan ndiyoti anthu akhale m’magulu, kuti ena agule zipangizo za ma coupon.
Ngati mukumvetsetsa boma, pulani ndiyoti anthu akhale m’magulu, kuti ena agule zipangizo za ma kuponi.
female
Ndiye pali ena a mtukula pakhomo ndi ena akuthekera kochita ulimi wawukulu, omwe akuwayika pa Agriculture commercialization.
Ndiye pali ena a mtukula pakhomo ndi ena akuthekera kochita ulimi wawukulu, omwe akuwayika pa Agirikacha komesholayizeshoni.
female
Izi zithandiza chifukwa kale lija ena amapezeka m'ma category onse okha, komaso ena amalandira ma coupon, pomwe sangathe kulima chifukwa cha ukalamba kapena ulumali.
Izi zithandiza chifukwa kale lija ena amapezeka m'ma katigore onse okha, komaso ena amalandira ma kuponi, pomwe sangathe kulima chifukwa cha ukalamba kapena ulumali.
female
Kapenaso kusowa malo, ndiye amenewo kumva kwanga, alowa mma category ena, atero a Mwabulawo.
Kapenanso kusowa malo, ndiye amenewo kumva kwanga, alowa mma katigore ena, atero a Mwabulawo.
female
President wa bungwe la alimi la Famers Union of Malawi, a Manesi Nkhala, ati ndizomvetsa chisoni, kuti mwa alimi 3,000,000 oyenera kuthandizika mu AIP, theka lawo ndilo lithandizike chaka chino.
Purezidenti wa bungwe la alimi la Famazi Yuniyoni ofu Malawi, a Manesi Nkhala, ati ndizomvetsa chisoni, kuti mwa alimi firi miliyoni oyenera kuthandizika mu eayipi, theka lawo ndilo lithandizike chaka chino.
female
Kutanthawuza kuti ambiri adakali m’goli lanjala. Vuto loyamba ndiloti alimi ambiri, adalandira fertilizer, mochedwa dzinja lathali, zomwe zidachititsa kuti ambiri asakolole moyenera.
Kutanthawuza kuti ambiri adakali m’goli lanjala. Vuto loyamba ndiloti alimi ambiri, adalandira feteleza mochedwa dzinja lathali, zomwe zidachititsa kuti ambiri asakolole moyenera.
female
Vuto lachiwiri ndiloti mtengo wa fertilizer udakwera kwambiri, kutanthawuza kuti alimi 1.5000,000, ayenera kugula fertilizer wudulayo.
Vuto lachiwiri ndiloti mtengo wa feteleza udakwera kwambiri, kutanthawuza kuti alimi wani poyinti fayifi miliyoni otsalawo, ayenera kugula feteleza wudulayo.
female
Zomwe zikukayikitsa ngati angakwanitse, adatero a Nkhata. Koma a Kampani adati, zonse zitengera kuti boma liyika fertilizer wa AIP pa mtengo wanji, ndipo akapanga masamu ndi budget ya chaka chino.
Zomwe zikukayikitsa ngati angakwanitse, adatero a Nkhata. Koma a Kampani adati, zonse zitengera kuti boma liyika feteleza wa eayipi pa mtengo wanji, ndipo akapanga masamu ndi bajeti ya chaka chino.
female
Apeza chiwerengero chenicheni. Chiwerengero chomaliza chidzatuluka boma likakhazikitsa mtengo wa fertilizer wa AIP.
Apeza chiwerengero chenicheni. Chiwerengero chomaliza chidzatuluka boma likakhazikitsa mtengo wa feteleza wa eayipi.
female
Koma likuyembekezeka pakati pa alimi wokwana 1.3.000,000 ndi 1.5.000,000 mu programme ya chaka chino. Adatero a Kampani.
Koma likuyembekezeka pakati pa alimi wokwana wani poyinti firi miliyoni ndi wani poyinti fayifi mliyoni, mu purogiramu ya chaka chino. Adatero a Kampani.
female
Panthawi ya campaign, mgwirizano wa Tonse Alliance, unkalonjeza fertilizer otsika mtengo kwa aliyense, Universal subsidy.
Panthawi ya kampeni, mgwirizano wa Tonse Alayansi, unkalonjeza feteleza otsika mtengo kwa aliyense, Univeso sabuside.
female
Pa mtengo wa 14,500 kwacha, ndipo mchaka chake choyamba alimi okwana 3.7.000,000, adapindula.
Pa mtengo wa fotini sauzandi fayifi handiredi kwacha, ndipo mchaka chake choyamba alimi okwana firi poyinti seveni miliyoni, adapindula.
female
Kuchoka apo mchaka chotsatira cha 2022-2023, chiwerengerocho chidatsika kufika pa 2.5.000,000, ndipo pano mpomwe pabwera ganizo lotsitsaso chiwerengero kufika pa 1.5.000,000.
Kuchoka apo mchaka chotsatira cha tuwente tuwente thu-tewente tuwente firi, chiwerengerocho chidatsika kufika pa thu poyinti fiyafi miliyoni, ndipo pano mpomwe pabwera ganizo lotsitsanso chiwerengero kufika pa wani poyinti fayifi miliyoni.
female
Bwalo la Nsanje First Grade Magistrate, lalamula amuna awiri, kukagwira ukayidi kwa miyezi 24, atawapeza wolakwa pa mulandu woba ma phone.
Bwalo la Nsanje Fesiti Giredi Majisitireti, lalamula amuna awiri, kukagwira ukayidi kwa miyezi tuwente folo, atawapeza wolakwa pa mulandu woba ma foni.
female
Yemwe amayimira boma pa mulanduwu a Innocent Banda, anawuza bwalolo, kuti awiriwa White Potifara ndi Nkhonde Wisted.
Yemwe amayimira boma pa mulanduwu a Inosenti Banda, anawuza bwalolo, kuti awiriwa Wayiti Potifara ndi Nkhonde Wisitedi,
female
Pa 12 July,2023, anafika pa msika wa Tengani m’bomalo ngati ofuna kutchajitsa ma phone komaso kuti ametedwe malo ometera a Shadreck Mussa.
Pa thuwelofu Julayi, tuwente tuwente-firi, anafika pa msika wa Tengani m’bomalo ngati ofuna kutchajitsa ma foni komaso kuti ametedwe malo ometera a Shadireki Musa.
female
Sargent Banda anati, kenako Potifara anatuma a Mussa kuti akamugulire chakumwa cha mtundu wa Frozy, ndipo iwo adanakwanitsa kuba ma lamya wokwanira 7.
Sajenti Banda anati, kenako Potifara anatuma a Musa kuti akamugulire chakumwa cha mtundu wa Furoze, ndipo iwo adanakwanitsa kuba ma lamya wokwanira seveni.
female
A 700,000 kwacha ndipo anathawira ku Blantyre, iwo anati, a Potifara anagwidwa pa msika wa Thabwa ndi lamya imodzi ya mtundu wa Samsung Galaxy.
A seveni handiredi sauzandi kwacha ndipo anathawira ku Bulantaya, iwo anati, a Potifara anagwidwa pa msika wa Thabwa ndi lamya imodzi ya mtundu wa Samusung'i Galakise.
female
Yandalama zokwanira 250,000 kwacha, ya a Kenedy Petrol Yohane. Pabwalo la milandu awiriwa anawukana mulandu wakuba mosemphana ndi gawo 278 la malamulo akulu a dzikolino.
Yandalama zokwanira thu handiredi fifite sauzandi kwacha, ya a Kenede Peturo Yohane. Pabwalo la milandu awiriwa anawukana mulandu wakuba mosemphana ndi gawo thu handiredi sevente eyiti la malamulo akulu a dzikolino.
female
Ndipo woyimira boma, anabweretsa mboni zake zitatu, zomwe zinapherezera kuti mulanduwu, unapalamulidwadi.
Ndipo woyimira boma, anabweretsa mboni zake zitatu, zomwe zinapherezera kuti mulanduwu, unapalamulidwadi.
female
Popereka madandawulo awo atawapeza wolakwa, Potifara ndi Wistedi, anapempha chifundo kunena kuti nkuyamba kupalamula mulandu, komaso amayang’anira mabanja awo, omwe avutike akatumizidwa kundende.
Popereka madandawulo awo atawapeza wolakwa, Potifara ndi Wisitedi, anapempha chifundo kunena kuti nkuyamba kupalamula mulandu, komaso amayang’anira mabanja awo, omwe avutike akatumizidwa kundende.
female
Koma sargent Banda, anatsutsa izi ponena kuti amunawa kupalamula mulandu ngati uwu ndikachitatu. Iye anapempha chilango chokhwima chomwe chingachititse anthu ena kuwopa kupalamula milandu ya mtunduwu.
Koma sajenti Banda, anatsutsa izi ponena kuti amunawa kupalamula mulandu ngati uwu ndikachitatu. Iye anapempha chilango chokhwima chomwe chingachititse anthu ena kuwopa kupalamula milandu ya mtunduwu.
female
Sargent Banda anati, zikuwonetsa kuti amuna awiriwa, anachita kukonzekera bwinolomwe kupalamula mulanduwu, popeza anachita kuchoka ku Blantyre ndi kufika ku Nsanje kukapalamula mulanduwu.
Sajenti Banda anati, zikuwonetsa kuti amuna awiriwa, anachita kukonzekera bwinolomwe kupalamula mulanduwu, popeza anachita kuchoka ku Bulantaya ndi kufika ku Nsanje kukapalamula mulanduwu.
female
Oweruza Hanif Ngundende, anagwirizana ndi woyimira boma, ponena kuti anthu ngati awa, ndiwoyipa kwambiri, popeza amachititsa kuti anthu omwe ali ndi malo otchajira lamya.
Oweruza Hanifu Ngundende, anagwirizana ndi woyimira boma, ponena kuti anthu ngati awa, ndiwoyipa kwambiri, popeza amachititsa kuti anthu omwe ali ndi malo otchajira lamya.
female
Akhale ndi milandu ya ndalama zochuluka, pofuna kubweza ma lamya omwe amakhala akubedwa. Mwa ichi Ngundende analamula Potifara ndi Wistedi kuti akagwire ukayidi kwazaka ziwiri.
Akhale ndi milandu ya ndalama zochuluka, pofuna kubweza ma lamya omwe amakhala akubedwa. Mwa ichi Ngundende analamula Potifara ndi Wisitedi kuti akagwire ukayidi kwazaka ziwiri.
female
Kuti andipsyi ena atengerepo phunziro. Potifara wazaka 23 amachokera kwa Nyenyezi T/A Mlolo, pomwe Wistedi wazaka 25, kwawo ndi kwa Soljeni, T/A Mbenje, m’boma la Nsanje.
Kuti andipsyi ena atengerepo phunziro. Potifara wazaka tuwente-firi amachokera kwa nyenyezi tiye Mlolo, pomwe Wisitedi wazaka tuwente, kwawo ndi kwa Sojeni, tiye Mbenje, m’boma la Nsanje.
female
Alimi ena amene afika kuchiwonetsero cha ulimi chimene nduna ya zamalimidwe a Sam Kawale adatsegulira dzulo mu mzinda wa Blantyre, ati akukhutira ndi chiwonetserochi.
Alimi ena amene afika kuchiwonetsero cha ulimi chimene nduna ya zamalimidwe a Samu Kawale adatsegulira dzulo mu mzinda wa Bulantaya, ati akukhutira ndi chiwonetserochi.
female
Chiwonetserochi ndi cha number 19, ndipo chabweretsa pamodzi alimi, nthambi za boma, ogulitsa mbeu ndi zipangizo.
Chiwonetserochi ndi cha nambala nayintini, ndipo chabweretsa pamodzi alimi, nthambi za boma, ogulitsa mbeu ndi zipangizo.
female
Mabungwe komaso ma company okonza katundu kuchokera ku zakumunda komaso ziweto ndi nsomba. M’modzi mwa alimiwo, mayi Alice Mbayo, ochokera ku Mafinga Irrigation ku Chisenga EPA, m’boma la Chitipa.
Mabungwe komaso ma kampani okonza katundu kuchokera ku zakumunda komaso ziweto ndi nsomba. M’modzi mwa alimiwo, mayi Alisi Mbale, ochokera ku Mafinga Irigeshoni ku Chisenga ipie, m’boma la Chitipa.
female
Adati apindula kwambiri, chifukwa Nthochi zonse zomwe zinabwera zagulitsidwa, ndipo ambiri akufuna kuti azilumikizana nawo pa Nyemba zawo zimene amachulukitsa ndi kugulitsa kuti alimi akadzale.
Adati apindula kwambiri, chifukwa Nthochi zonse zomwe zinabwera zagulitsidwa, ndipo ambiri akufuna kuti azilumikizana nawo pa Nyemba zawo zimene amachulukitsa ndi kugulitsa kuti alimi akadzale.
female
Ambiri akuchita chidwi ndi mbeu ya Nyemba yamakono ya NOWA 45, imene timachulukitsa kuti alimi adzale, mbewuyi, ili ndi m’chere wa Zinc umene umathandiza kuti munthu aziwona bwino.
Ambiri akuchita chidwi ndi mbeu ya Nyemba yamakono ya NEWA fote fayifi, imene timachulukitsa kuti alimi adzale, mbewuyi, ili ndi m’chere wa Zinki umene umathandiza kuti munthu aziwona bwino.
female
Komaso kwa amene ali ndi chilonda chimapola msanga, anatero mayi wa ana anayiyo, amena ali m’gulu la Tiyezye seed multiplication.
Komaso kwa amene ali ndi chilonda chimapola msanga, anatero mayi wa ana anayiyo, amena ali m’gulu la Tiyeziye seed matipulikeshoni.
female
Mlimi wina mayi Nancy Chidzalo wa Hotnet Foods Limited, adati chiwonetserochi, chathandiza kuti afikire misika ina ndi zimene amakoza kuchokera ku nthochi.
Mlimi wina mayi Nanse Chidzalo wa Hotinet Fudzi Limitedi, adati chiwonetserochi, chathandiza kuti afikire misika ina ndi zimene amakoza kuchokera ku nthochi.
female
Tikusanduliza Nthochi nkukonza Banana crisps, cheeps cha nthochi komanso ufa wa nthochi. Ufawu timawukonza bwino.
Tikusanduliza Nthochi nkukonza Banana khirisipisi, chipisi cha nthochi komanso ufa wa nthochi. Ufawu timawukonza bwino.
female
Zonsezi timazipakira bwino, ndipo tikugulitsa kwambiri ku Lilongwe, koma tsopano tifalikira madera enanso. Adatero iwo.
Zonsezi timazipakira bwino, ndipo tikugulitsa kwambiri ku Lilongwe, koma tsopano tifalikira madera enasno. Adatero iwo.
female
Ndipo mkulu wa bungwe la Centre for Agriculture Transformation, CAT, a Macloud Nkhoma, adati adasangalala chifukwa abwera ku chiwonetserocho ndi alimi amene amagwira nawo ntchito m’dziko muno ndi ulimi wawo wosiyanasiyana.
Ndipo mkulu wa bungwe la Senta fo Agirikacha Thiransifomeshoni (KATI), a Makilawudi Nkhoma, adati adasangalala chifukwa abwera ku chiwonetserocho ndi alimi amene amagwira nawo ntchito m’dziko muno ndi ulimi wawo wosiyanasiyana.
female
Tabwera ndi alimi amene akusandulitsa zosiyanasiyana kuchokera kumunda. Ena akuchulukitsa mbewu, komaso ena akukonza zakudya za Nsomba zimene m’mbuyomu alimi a nsomba amagula ku Zambia.
Tabwera ndi alimi amene akusandulitsa zosiyanasiyana kuchokera kumunda. Ena akuchulukitsa mbewu, komaso ena akukonza zakudya za Nsomba zimene m’mbuyomu alimi a nsomba amagula ku Zambia.
female
Izi zithandiza kuti ndalama zizikhalira m’dziko lomwelino adatero iwo. A Nkhoma adati, iwo ndi wokondwa kuti bungwe lawo, lidapeza imodzi mwa mphoto 6, zimene zidaperekedwa ku chiwonetserochi.
Izi zithandiza kuti ndalama zizikhalira m’dziko lomwelino adatero iwo. A Nkhoma adati, iwo ndi wokondwa kuti bungwe lawo, lidapeza imodzi mwa mphoto sikisi, zimene zidaperekedwa ku chiwonetserochi.
female
Polankhula potsegulira chiwonetserochi, a Kawale adati, pakadali pano, nkhani yoti ulimi ufike pena ngati business, ikadali mokwawa.
Polankhula potsegulira chiwonetserochi, a Kawale adati, pakadali pano, nkhani yoti ulimi ufike pena ngati bizinesi, ikadali mokwawa.
female
Koma unduna wawo mogwirizana ndi magulu ena akuyesetsa kuti zinthu zipite patsogolo. Tikudziwa kuti makina othandiza kutukula ulimi ngokwera mtengo.
Koma unduna wawo mogwirizana ndi magulu ena akuyesetsa kuti zinthu zipite patsogolo. Tikudziwa kuti makina othandiza kutukula ulimi ngokwera mtengo.
female
Nchifukwa chake tikubweretsa njira zoti izi zisinthe, kuti alimi ang’ono, azitha kupeza makinawa bwinolomwe.
Nchifukwa chake tikubweretsa njira zoti izi zisinthe, kuti alimi ang’ono, azitha kupeza makinawa bwinolomwe.
female
Chiwonetserochi chimene chimachitika chaka ndi chaka chitha loweruka, ndipo chikuchitikira ku Chichiri Trade Fare Grounds mu m’zinda wa Blantyre. Mutu wake ndi Kudzidalira potenga ulimi ngati business.
Chiwonetserochi chimene chimachitika chaka ndi chaka chitha loweruka, ndipo chikuchitikira ku Chichiri Thiredi Feya Girawunzi mu m’zinda wa Bulantaya. Mutu wake ndi Kudzidalira potenga ulimi ngati bizinesi.
female
Abale a gogo Binwell Chabwera amene adathawitsidwa, pomuganizira kuti adapha mdzukulu wake m'matsenga, anenetsa kuti iwo sakufunanso kuwona gogoyo.
Abale a gogo Biniwelo Chabwera amene adathawitsidwa, pomuganizira kuti adapha mdzukulu wake m'matsenga, anenetsa kuti iwo sakufunanso kuwona gogoyo.
feamle
Gogo Chabwera, wakhala m’manja mwa a police ya Zalewa m’boma la Neno kwa sabata zitatu, iye atathawitsidwa kumudzi kwawo, pofuna moyo wake kutsatira imfa ya mdzukulu wake.
Gogo Chabwera, wakhala m’manja mwa a polisi ya Zalewa m’boma la Neno kwa sabata zitatu, iye atathawitsidwa kumudzi kwawo, pofuna moyo wake kutsatira imfa ya mdzukulu wake.
female
Pamene timasindikiza nkhaniyi nkuti gogoyu atatengedwa ndi akufuna kwabwino, Amayi Mbambande Foundation mu mzinda wa Lilongwe.
Pamene timasindikiza nkhaniyi nkuti gogoyu atatengedwa ndi akufuna kwabwino, Amayi Mbambande Fawundeshoni mu mzinda wa Lilongwe.
female
Koma gogoyu adakana kuti iye satamba ndipo nayenso adali wodabwa kuti akumuganizira kuti ndamene wazimitsa mdzukuluwake, Chiyembekezo Bysod.
Koma gogoyu adakana kuti iye satamba ndipo nayenso adali wodabwa kuti akumuganizira kuti ndamene wazimitsa mdzukuluwake, Chiyembekezo Bayisoni.
female
Ine sinditamba, ndipo ndikadakhala ndimapanga zimenezo, bwezi nditatha anaanga amene mpaka lero alimoyo. Adatero.
Ine sinditamba, ndipo ndikadakhala ndimapanga zimenezo, bwezi nditatha anaanga amene mpaka lero alimoyo. Adatero.
female
Lachisanu masana, msangulutso udafika m’mudzi mwa Kasamba 1 kwa T/A Symon kwawo kwa gogoyu m’bomalo.
Lachisanu masana, msangulutso udafika m’mudzi mwa Kasamba wani kwa Tiyee Sayimoni kwawo kwa gogoyu m’bomalo.
female
Kumeneko tidapeza ana 5 agogoyo, omwe ndi amayi anayi ndi mwamuna m'modzi. Gogoyu amasungidwa ndi chidzukulu chake Chifundo Suwiti.
Kumeneko tidapeza ana fayifi agogoyo, omwe ndi amayi anayi ndi mwamuna m'modzi. Gogoyu amasungidwa ndi chidzukulu chake Chifundo Suwiti.
female
Faston Chabwera ndi mwana wake wa m’mudzi yekhayo amene ali moyo. Iye adati zochita za gogoyo, ndi zomwe zidapereka uthenga woyipa, kuti anthu amuganizire kuti ndamene wakoza mdzukukulu wakeyo.
Fasitoni Chabwera ndi mwana wake wa m’mudzi yekhayo amene ali moyo. Iye adati zochita za gogoyo, ndi zomwe zidapereka uthenga woyipa, kuti anthu amuganizire kuti ndamene wakoza mdzukukulu wakeyo.
female
Iye adati, gogoyo adayamba pakale kunena kuti athana ndi mdzukulu wakeyo komaso ana ena, koma izi amalankhula popanda kumuyamba.
Iye adati, gogoyo adayamba pakale kunena kuti athana ndi mdzukulu wakeyo komaso ana ena, koma izi amalankhula popanda kumuyamba.
female
Ifa ya mdzukulu wa gogoyo, ndiyomwe idachititsa a banja kuti aloze zala gogoyo, kuti ndamene wakonza.
Ifa ya mdzukulu wa gogoyo, ndiyomwe idachititsa a banja kuti aloze zala gogoyo, kuti ndamene wakonza.
female
Sabata idatha mdzukulu wakeyo akudwala, koma gogoyo sadafune kudzamuzonda. Tsikulina tidachita kumukakamiza kuti adzamuwone, ndipo anabwera, koma zomwe adachita, zidatidabwitsa.
Sabata idatha mdzukulu wakeyo akudwala, koma gogoyo sadafune kudzamuzonda. Tsikulina tidachita kumukakamiza kuti adzamuwone, ndipo anabwera, koma zomwe adachita, zidatidabwitsa.
female
Podzamuwona adati, titenge chitosi cha nkhuku ndi kuchisungunura ndiye madziwo adamuwaza kumutu, ati akhalabwino koma sizidathandize. Adatero.
Podzamuwona adati, titenge chitosi cha nkhuku ndi kuchisungunura ndiye madziwo adamuwaza kumutu, ati akhalabwino koma sizidathandize. Adatero.
female
Iye adati pofika pa August 26, mdzukuluyo adatsazika, ndipo aliyese adaganizira kuti wachita izi ndi gogoyo.
Iye adati pofika pa Ogasitituwente-sikisi, mdzukuluyo adatsazika, ndipo aliyese adaganizira kuti wachita izi ndi gogoyo.
female