audio
audio
raw_text
string
normalized_text
string
gender
string
Iwo adati, zitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika m'madera osiyanasiyananso, ndi umboni woti kupita kwa zaka tili pa ufulu, kukusintha zinthu.
Iwo adati, zitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika m'madera osiyanasiyananso, ndi umboni woti kupita kwa zaka tili pa ufulu, kukusintha zinthu.
female
Koma adandaula kuti anthu ena adyera ndiwo amabezeretsa dziko m'mbuyo pakuba ndalama za boma.
Koma adandaula kuti anthu ena adyera ndiwo amabezeretsa dziko m'mbuyo pakuba ndalama za boma.
female
A Suluhu omwe adali mlendo wolemekezeka pamwambowo adayamikira dziko la Malawi chifukwa chosunga bata ndi mtendere pa zaka zonsezo zomwe lakhala pa ufulu
A Suluhu omwe adali mlendo wolemekezeka pamwambowo adayamikira dziko la Malawi chifukwa chosunga bata ndi mtendere pa zaka zonsezo zomwe lakhala pa ufulu
female
Iwo adakhudza amalawi omwe adataya miyoyo kaamba ka namondwe wa Freddy, kupitiriza pa thandizo lomwe dziko lawo lidapereka namondweyo atangochitika kumene.
Iwo adakhudza amalawi omwe adataya miyoyo kaamba ka namondwe wa Freddy, kupitiriza pa thandizo lomwe dziko lawo lidapereka namondweyo atangochitika kumene.
female
koma pothirirapo ndemanga, a malawi ena adati chikondwerero cha tsikuli chimangochitika mwa chizolowezi chabe, chifukwa kuziyimira patokha komwe timakondwerera sikuoneka, mmalo mwake mavuto amangosinthana mdziko muno

A Precious Sinyangwe a mumzinda wa Lilongwe ati iwe atengapo gawo pa zikondwreo za mtunduwu koma palibe kusintha komwe angaloze kuti a malawi akuzimiradi pawokha.
A Pureshiyasi Sinyangwe a mumzinda wa Lilongwe ati iwe atengapo gawo pa zikondwreo za mtunduwu koma palibe kusintha komwe angaloze kuti a malawi akuzimiradi pawokha.
female
"Tikunena za zaka 59 koma zambiri timadalira zakunja. Zoona ndizakumunda zomwe, monga nthochi, mazira ndi zipatso zina ndi zina,
"Tikunena za zaka fifite-nayini koma zambiri timadalira zakunja. Zoona ndizakumunda zomwe, monga nthochi, mazira ndi zipatso zina ndi zina,
female
tizichita kuyitanitsa kuchoka kunja ngati tilibe nthaka ndi madzi, koma nkumati ndife oziyimirira patokha"? Adatero a Sinyangwe.
tizichita kuyitanitsa kuchoka kunja ngati tilibe nthaka ndi madzi, koma nkumati ndife oziyimirira patokha"? Adatero a Sinyangwe.
female
A Millium Chaona nawo adati, tsikuli limangokomera kuti anthu amakhala ndi mpata wopuma, koma tanthauzo lake limasemphana ndi momwe zinthu zikuyendera
A Miliyamu Chaona nawo adati, tsikuli limangokomera kuti anthu amakhala ndi mpata wopuma, koma tanthauzo lake limasemphana ndi momwe zinthu zikuyendera
female
ine ndi nenako pa zangongole zomwe tilinazo, kuchuluka kwa ngongolezo kukusonyezeratu kuti sife oyima patokhza ayi, timadalirabe ena
ine ndi nenako pa zangongole zomwe tilinazo, kuchuluka kwa ngongolezo kukusonyezeratu kuti sife oyima patokhza ayi, timadalirabe ena
female
Ana omwe akyubwera mtsogolo adzatifunsa mafunso oti tidzalephera kuyankha patanthauzo la tsikuli. Adatero a Chaona.
Ana omwe akyubwera mtsogolo adzatifunsa mafunso oti tidzalephera kuyankha patanthauzo la tsikuli. Adatero a Chaona.
female
Dziko la Malawi lidalandira ufulu wozilamulira mchaka cha 1964, ndipo kuchokera apo lidali pansi pa ulamuliro wa chipani chimodzi cha Malawi Congress Party (MCP).
Dziko la Malawi lidalandira ufulu wozilamulira mchaka cha nayintini sikisite-folo, ndipo kuchokera apo lidali pansi pa ulamuliro wa chipani chimodzi cha Malawi Kongeresi pate (EMU SIPI).
female
Mpaka chaka cha 1993, pomwe kudachitika refrendum nkusankha ulamuliro wa zipani zambiri
Mpaka chaka cha nayintin nayinte-firi, pomwe kudachitika rifurendamu nkusankha ulamuliro wa zipani zambiri
female
pansi pa ulamuliro wa zipani zambiri, dziko la Malawi lalamulidwako ndi ma president osiyanasiyana asanu, ndipo chaka chilichonse cha 6 July, dzikoli limakumbukira ufulu woziyimira palokha.
pansi pa ulamuliro wa zipani zambiri, dziko la Malawi lalamulidwako ndi ma purezidenti osiyanasiyana asanu, ndipo chaka chilichonse cha sikisi Julayi, dzikoli limakumbukira ufulu woziyimira palokha.
female
Chisankho cha 2025 chikhoza kudzakhala umboni wa ulamuliro weniweni wa democracy ngati bungwe la Malawi Electral Commissiona (MEC) lidzatsate malamulo atsopano.
Chisankho cha tuwente tuwente-fayifi chikhoza kudzakhala umboni wa ulamuliro weniweni wa dimokalase ngati bungwe la Malawi Elekitiro Komishoni (MEKI) lidzatsate malamulo atsopano.
female
Malinga ndi mneneri wa bungwelo a Sangwani Mwafulirwa, malamulo atsopanowa adzagwiritsidwa ntchito poperaka zilango kwa onse osakoneza kapena kuyambitsa ziwawa pa misonkhano ya campaign.
Malinga ndi mneneri wa bungwelo a Sangwani Mwafulirwa, malamulo atsopanowa adzagwiritsidwa ntchito poperaka zilango kwa onse osakoneza kapena kuyambitsa ziwawa pa misonkhano ya kampeni.
female
Sitidzasekelera aliyense wosokoneza chifukwa malamulo atsopano akutipatsa mphamvu. M'mbuyomu ndondomeko zimakhazikitsidwa koma padalibe lamulo lotipatsa mphamvu. Anatero a Mwafulirwa
Sitidzasekelera aliyense wosokoneza chifukwa malamulo atsopano akutipatsa mphamvu. M'mbuyomu ndondomeko zimakhazikitsidwa koma padalibe lamulo lotipatsa mphamvu. Anatero a Mwafulirwa
female
Malamulo atsopanowo akupereka mphamvu ku MEC zopereka chilango cha ndalama zokwana 5 000,000 kwacha
Malamulo atsopanowo akupereka mphamvu ku MEKI zopereka chilango cha ndalama zokwana fayifi miliyoni kwacha
female
malamulowo akuperekanso mphamvu ku MEC zochotsa candidate yemwe omutsatira ake apezeka akuyambitsa ziwawa
malamulowo akuperekanso mphamvu ku MEKI zochotsa candidate yemwe omutsatira ake apezeka akuyambitsa ziwawa
female
Izi zikutanthauza kuti onse ofuna kudzayimirira mmaudindo osiyanasiyana, ayambiretu kuphunzitsa owatsatira zokhuza malamulo atsopanowa chifukwa akhoza kudzawasokoneza
Izi zikutanthauza kuti onse ofuna kudzayimirira mmaudindo osiyanasiyana, ayambiretu kuphunzitsa owatsatira zokhuza malamulo atsopanowa chifukwa akhoza kudzawasokoneza
female
Tikhala tikukumana ndi zipani komanso onse okhuzidwa kuti tiwunikirane poyenera kusintha. Tikufuna kuti tikadzamafika 2025, zonse zizakhale zitakonzedwa. Atero a Mwafulirwa.
Tikhala tikukumana ndi zipani komanso onse okhuzidwa kuti tiwunikirane poyenera kusintha. Tikufuna kuti tikadzamafika tuwente tuwente-fayifi, zonse zizakhale zitakonzedwa. Atero a Mwafulirwa.
female
Pazisankho za m'mbuyomo, otsatira zipani amachitirana zipongwe ncholinga chofuna kuwopsezana ndi kugwetsana mphwayi. Ndipo pazipongwe zonsezi, ena adataya miyoyo ndi katundu wawo
azisankho za m'mbuyomo, otsatira zipani amachitirana zipongwe ncholinga chofuna kuwopsezana ndi kugwetsana mphwayi. Ndipo pazipongwe zonsezi, ena adataya miyoyo ndi katundu wawo
female
Ngakhale kuti bungwe la MEC limakhala ndi ndondomeko zolondoloza milandu, monga yoyambitsa ziwawa kapena kusokoneza kayendetsedwe ka zisankho, a Mwafulira ati mchitidwewo umachitikabe
Ngakhale kuti bungwe la MEKI limakhala ndi ndondomeko zolondoloza milandu, monga yoyambitsa ziwawa kapena kusokoneza kayendetsedwe ka zisankho, a Mwafulira ati mchitidwewo umachitikabe
female
Pazisankho za m'mbuyomu, ndondomeko zimenezi timakhala nazo, ndipo wina aliyense wopikisana nawo pa chisankho amasayinira kuti azikatsata zomwezo pamene akupanga campaign.
Pazisankho za m'mbuyomu, ndondomeko zimenezi timakhala nazo, ndipo wina aliyense wopikisana nawo pa chisankho amasayinira kuti azikatsata zomwezo pamene akupanga kampeni.
female
Vuto linali loti tinalibe mphavu zolangira amene waphwanya ndondomeko zimenezi. koma ulendo uno tabwera ndi moto, moti aliyense wozoloweza chisokonezo asamale. Iwo atero.
Vuto linali loti tinalibe mphavu zolangira amene waphwanya ndondomeko zimenezi. koma ulendo uno tabwera ndi moto, moti aliyense wozoloweza chisokonezo asamale. Iwo atero.
female
Mkulu wa bungwe lowona kuti andale akutolerana ndikutsatira ndondomeko za dimokarase la Centre for Multiparty Democracy, a Kizito Tenthani, anati malamulo atsopanowa abwera nthawi yabwino.
Mkulu wa bungwe lowona kuti andale akutolerana ndikutsatira ndondomeko za dimokarase la Senta fo Matipate Dimokirase, a Kizito Tenthani, anati malamulo atsopanowa abwera nthawi yabwino.
female
Nkale lonse zipani komanso andale amasayina kuti sadzapanga mtopola kwa anzawo, ndipo adzaonetsa akuti chisankho chikuchitika mwa bata
Nkale lonse zipani komanso andale amasayina kuti sadzapanga mtopola kwa anzawo, ndipo adzaonetsa akuti chisankho chikuchitika mwa bata
female
koma chifukwa padalibe malamulo okhwimitsira, zimkavuta. Anatero a Tenthani. Iwo anati malamulo atsopanowo akunena chindunji
koma chifukwa padalibe malamulo okhwimitsira, zimkavuta. Anatero a Tenthani. Iwo anati malamulo atsopanowo akunena chindunji
female
zokhuza mchitidwe wonyozana kapena kunyazitsana ndi zilango zake kwa wopezeka wolakwa pa milandu yotero, makamaka pano pamwe anthu amatha kunyozana kapena kunyazitsana pa masamba a mchezo
zokhuza mchitidwe wonyozana kapena kunyazitsana ndi zilango zake kwa wopezeka wolakwa pa milandu yotero, makamaka pano pamwe anthu amatha kunyozana kapena kunyazitsana pa masamba a mchezo
female
MEC itati iyikepodi mtima ngati momwe akuneneramo, zikhoza kutichitira ubwino kwambiri. Atati alangeko angapo osokoneza, zisankho zitha kuyenda bwino. Atero a Tenthani
MEKI itati iyikepodi mtima ngati momwe akuneneramo, zikhoza kutichitira ubwino kwambiri. Atati alangeko angapo osokoneza, zisankho zitha kuyenda bwino. Atero a Tenthani
female
Mneneri Elason Zande akuti anafa nkudzukanso, pomwe anasala kudya kwa masiku 40 Mulungu atawawonekera.
Mneneri Elasoni Zande akuti anafa nkudzukanso, pomwe anasala kudya kwa masiku fote Mulungu atawawonekera.
female
A Zande omwe akuchita utumiki wawo m'boma la Chiradzulu, pa mpingo wa Nazareth Prophetic Church of all Nations, ati anatumidwa asanabadwe chifukwa mayi wawo anawauza kuti ngakhale ali mwana,
A Zande omwe akuchita utumiki wawo m'boma la Chiradzulu, pa mpingo wa Nazareti Purofetiki TChechi of all Neshonzi, ati anatumidwa asanabadwe chifukwa mayi wawo anawauza kuti ngakhale ali mwana,
female
bambo wawo amakana kuti simwana wawo chifukwa amachita zinthu zodabwitsa. Mpingowo uli msewu wa Midima pa Losa
bambo wawo amakana kuti simwana wawo chifukwa amachita zinthu zodabwitsa. Mpingowo uli msewu wa Midima pa Losa
female
A Zande omwe anabadwa chaka cha 1965, akuti Yesu anayamba kuwaonekera ali mwana, ndipo anakhala akumuuza wamsembe, panthawiyo nkuti ali a mpingo wa Katolika.
A Zande omwe anabadwa chaka cha nayintini sikisite-fayifi, akuti Yesu anayamba kuwaonekera ali mwana, ndipo anakhala akumuuza wamsembe, panthawiyo nkuti ali a mpingo wa Katolika.
female
Ndikamuuza wa msembeyu, amkandiyankha kui akumaona nyali yanga ikuwala kwambiri kumafikira kumalekezero a dziko lapansi. Yesuyu amandionekera chaka ndi chaka.
Ndikamuuza wa msembeyu, amkandiyankha kui akumaona nyali yanga ikuwala kwambiri kumafikira kumalekezero a dziko lapansi. Yesuyu amandionekera chaka ndi chaka.
female
koma mzaka za mma 1980, ndinayamba kudutsa nyengo zovuta kwambiri, ndipo 1984 Yesu anabwera masana kunditenga ndikupitanane kumwamba, komanso kukandionetsa ku gahena.
koma mzaka za mma nayintini eyite, ndinayamba kudutsa nyengo zovuta kwambiri, ndipo nayintini eyite-folo, Yesu anabwera masana kunditenga ndikupitanane kumwamba, komanso kukandionetsa ku gahena.
female
Anatero a Zande. Iwo anati, Yesu anawauza kuti achoke mpingo wawo wa katolika, mmawa wa tsiku lina chaka cha 1989, ali kumunda.
Anatero a Zande. Iwo anati, Yesu anawauza kuti achoke mpingo wawo wa katolika, mmawa wa tsiku lina chaka cha nayintini eyite-nayini, ali kumunda.
female
Malinga ndi a Zande, adayamba kudutsa mmoyo wovuta ndi wowawa kuchokera mcaka cha 2006, pomwe Yesu anawatengeranso kumwamba kukawaonetsa zambiri.
Malinga ndi a Zande, adayamba kudutsa mmoyo wovuta ndi wowawa kuchokera mcaka cha tuwente ziro sikisi, pomwe Yesu anawatengeranso kumwamba kukawaonetsa zambiri.
female
koma iwo anati panali pa October 27 chaka cha 2009, pomwe Mulungu anawaonekera ndikuwauza kuti asadye komanso kumwa madzi kwa masiku 31.
koma iwo anati panali pa Okotoba tuwente-seveni chaka cha tuwente ziro nayini, pomwe Mulungu anawaonekera ndikuwauza kuti asadye komanso kumwa madzi kwa masiku sete-wani.
female
Anandiuza kuti ndikapempherere kuphiri komwe ndinapitadi. Ndipo ndinawauza ana anga kuti azikandiona pakadutsa masiku atatu kapena 5, chifukwa mwina ndikhoza kukafa
Anandiuza kuti ndikapempherere kuphiri komwe ndinapitadi. Ndipo ndinawauza ana anga kuti azikandiona pakadutsa masiku atatu kapena fayifi, chifukwa mwina ndikhoza kukafa
female
Ndinawapemphanso kuti azibweretsa madzi kuti ndizikachukuchira mkamwa. Koma ndinavutika nditafika tsiku lanambala 8, ndinafooka ndipo ndinamuuza Mulungu kuti basi ndifa.
Ndinawapemphanso kuti azibweretsa madzi kuti ndizikachukuchira mkamwa. Koma ndinavutika nditafika tsiku lanambala eyiti, ndinafooka ndipo ndinamuuza Mulungu kuti basi ndifa.
female
koma tsiku la chinayini, nditafookeratu ndinaona pakatali pakubwera anyamata awiri ovala zoyere, atatenga basket yomwe munali chakudya
koma tsiku la chinayini, nditafookeratu ndinaona pakatali pakubwera anyamata awiri ovala zoyere, atatenga basket yomwe munali chakudya
female
Ndipo anandiuza kuti atate anga ndiwomwe anawatuma. Analongosola a Zande. Ndipo anati atangodya, anthuwo komanso mbale zomwe anadyera zinasowa.
Ndipo anandiuza kuti atate anga ndiwomwe anawatuma. Analongosola a Zande. Ndipo anati atangodya, anthuwo komanso mbale zomwe anadyera zinasowa.
female
Ndipo kuchoka pomwepo anapeza mphamvu zochuluka. Kuchoka apo mapazi anga anatupa kwambiri, ndipo anthu anayamba kunditonza mpaka ndinamupempha mulungu kuti andiphe. Anatero a Zande.
Ndipo kuchoka pomwepo anapeza mphamvu zochuluka. Kuchoka apo mapazi anga anatupa kwambiri, ndipo anthu anayamba kunditonza mpaka ndinamupempha mulungu kuti andiphe. Anatero a Zande.
female
Koma iwo anati chinali chaka cha 2013, chomwe Mulungu anawauzanso kuti azikagona mtchalichowo chawo, ndipo Mulungu anawaphanso zilakolako za thupi.
Koma iwo anati chinali chaka cha tuwente setini, chomwe Mulungu anawauzanso kuti azikagona mtchalichowo chawo, ndipo Mulungu anawaphanso zilakolako za thupi.
female
Koma chifukwa chokhalitsa osamadya, thupi langa linayamba kuwola. moti mmiyendomu muli ziphsera ngati kuti ndinapsa, koma ndichikwa chokhalitsa mkachisi osamadya. Iwo analongosola.
Koma chifukwa chokhalitsa osamadya, thupi langa linayamba kuwola. moti mmiyendomu muli ziphsera ngati kuti ndinapsa, koma ndichikwa chokhalitsa mkachisi osamadya. Iwo analongosola.
female
Malinga ndi a Zande, Mulungu anawauzanso kuti asale kudya masiku 40 kuchokera pa 3 March kufika pa 11 April. Ndipo anati unali ulendo wovuta.
Malinga ndi a Zande, Mulungu anawauzanso kuti asale kudya masiku fote kuchokera pa firi Machi kufika pa ileveni epulo. Ndipo anati unali ulendo wovuta.
female
Chifukwa anafika pofooka ndikuziona kuti afa. "Nditafika tsiku la 25, ndinaona kuti mpweya umandithera komanso ndimavutika kupuma."
Chifukwa anafika pofooka ndikuziona kuti afa. "Nditafika tsiku la tuwente-fayifi, ndinaona kuti mpweya umandithera komanso ndimavutika kupuma."
female
Ndinali pakati pa imfa ndi moyo, koma ndinalimba mtima chifukwa ndi mulungu anandiuza. Kuchokera tsiku limenelo, ndiauza ana anga kuti azindijambula ngati umboni. Analongosola motero mneneriyo.
Ndinali pakati pa imfa ndi moyo, koma ndinalimba mtima chifukwa ndi mulungu anandiuza. Kuchokera tsiku limenelo, ndiauza ana anga kuti azindijambula ngati umboni. Analongosola motero mneneriyo.
female
iwo anati, akhalanso akugona pa chiguduli kuchoka 2013 kufikira chaka cha mwezi wa May.
iwo anati, akhalanso akugona pa chiguduli kuchoka tuwente setini kufikira chaka cha mwezi wa May.
female
Malinga ndi mkuku wa mpingo wawo a Joseph Pensulu, anati zimakhala zomvetsa chisoni anthu akamaona akamaliza kusala kudya kwa masiku ambiri osadya komanso kumwa madzi.
Malinga ndi mkuku wa mpingo wawo a Jozefe Pensulu, anati zimakhala zomvetsa chisoni anthu akamaona akamaliza kusala kudya kwa masiku ambiri osadya komanso kumwa madzi.
female
Koma kusala kudya kwa ulendo uno kwa masiku 40, sikunali kophweka monga mungaonaere muzithunzimo. Kusala kudyaku sikunali kozisangalatsa woka, koma mulungu anawatuma.
Koma kusala kudya kwa ulendo uno kwa masiku 40, sikunali kophweka monga mungaonaere muzithunzimo. Kusala kudyaku sikunali kozisangalatsa woka, koma mulungu anawatuma.
female
Koma anthu amaona ngati ndizopanda pake. Anatero a Pensulo. Iwo anati patatsala masiku anayi kuti amalize, anapita kukawaona ndipo chisoni chachikulu chinawagwira.
Koma anthu amaona ngati ndizopanda pake. Anatero a Pensulo. Iwo anati patatsala masiku anayi kuti amalize, anapita kukawaona ndipo chisoni chachikulu chinawagwira.
female
Malinga ndi a Pensulo, mpingo wawo unalibe choyankhula panthawiyi, koma kuvomereza kuti zitero. Mneneri Rex Kalolo omwe ndi wamkulu wa bungwe la Prophetic Association of Malawi,
Malinga ndi a Pensulo, mpingo wawo unalibe choyankhula panthawiyi, koma kuvomereza kuti zitero. Mneneri Rekisi Kalolo omwe ndi wamkulu wa bungwe la Purofetiki Asosiyeshoni ofu Malawi,
female
Anati ndi bodza kuti munthu akhoza kukhala kwa masiku 40 osadya komanso osamwa, chifukwa thupi lili ndi kapangidwe kake.
Anati ndi bodza kuti munthu akhoza kukhala kwa masiku fote osadya komanso osamwa, chifukwa thupi lili ndi kapangidwe kake.
female
Masiku omwe munthu angadutse malinga ndi achipatala ndi atatu, ndipo lachinayi limakhala lovuta. Timadziwa Mose komanso Yesu.
Masiku omwe munthu angadutse malinga ndi achipatala ndi atatu, ndipo lachinayi limakhala lovuta. Timadziwa Mose komanso Yesu.
female
Ndipo sitinganene zambiri chifukwa buku ;lopatulika sililongosola zambiri. Anatero a Kalolo.
Ndipo sitinganene zambiri chifukwa buku ;lopatulika sililongosola zambiri. Anatero a Kalolo.
female
Iwo anati akukaikira zoti a Zande anasala kwa masiku 40. Akukaikira pokhapokha atayankha mafunso ena.
Iwo anati akukaikira zoti a Zande anasala kwa masiku fote. Akukaikira pokhapokha atayankha mafunso ena.
female
Zimapwetekesa anthu, ndichifukwa chimazikana nkhani zimenezi. Anthu ena amangotengera, ndipo apweteketsa anthu.
Zimapwetekesa anthu, ndichifukwa chimazikana nkhani zimenezi. Anthu ena amangotengera, ndipo apweteketsa anthu.
female
Palibe angakhale kwa masiku 40 osadya komanso kumwa. Anatero a Kalolo. Iwo anati nkhanizi zikuchuluka chifukwa choti anthu ambiri alibe chidziwitsa chenicheni.
Palibe angakhale kwa masiku fote osadya komanso kumwa. Anatero a Kalolo. Iwo anati nkhanizi zikuchuluka chifukwa choti anthu ambiri alibe chidziwitsa chenicheni.
female
Sindikukhulupilira zimenezo malire andipatse umboni, onse omwe anayeserapo amafa. Anatero a Kalolo.
Sindikukhulupilira zimenezo malire andipatse umboni, onse omwe anayeserapo amafa. Anatero a Kalolo.
female
Ndipo anati bungwe lawo likuyesetsa kulangiza anthu kuti asamachite izi, chifukwa akupwetekeka nazo
Ndipo anati bungwe lawo likuyesetsa kulangiza anthu kuti asamachite izi, chifukwa akupwetekeka nazo
female
Apostle Criford Kawinga walengeza kuti timu yake yomwe imadziwika kuti Kawinga FC, tsopano izidziwika ndi dzina loti Crek Sporting Club
Aposito khirifodi Kawinga walengeza kuti timu yake yomwe imadziwika kuti Kawinga EFUSI, tsopano izidziwika ndi dzina loti Khireki Sipoting'i kilabu
female
Apostle Kawinga alengeza izi mu mzinda wa Lilongwe ku hotela ya sunbird Capital, komwe akonza mgonero wa timuyi kukondwerera kuti yalowa mu ligi yayikulu ya TNM super league.
Aposito Kawinga alengeza izi mu mzinda wa Lilongwe ku hotela ya sanibedi Kapito, komwe akonza mgonero wa timuyi kukondwerera kuti yalowa mu ligi yayikulu ya TI ENI EMU super ligi.
female
Tachita izi kuti enanso athe kuthandizana nafe poyendetsa timuyi. Watero Kawinga.
Tachita izi kuti enanso athe kuthandizana nafe poyendetsa timuyi. Watero Kawinga.
female
Mwazina a Kawinga ati apitiliza kuthandiza timuyi mu ligi yayikulu, pomwenso waonetsera bus yomwe timuyi izigwiritsa ntchito.
Mwazina a Kawinga ati apitiliza kuthandiza timuyi mu ligi yayikulu, pomwenso waonetsera bus yomwe timuyi izigwiritsa ntchito.
female
Kuli kuimba mwa mavume, pomwe a Kawinga apereka 250,000 kwacha kwa wosewera aliyense mu timuyi.
Kuli kuimba mwa mavume, pomwe a Kawinga apereka 250,000 kwacha kwa wosewera aliyense mu timuyi.
female
Makhansala awiri a chipani cha Democratic Progressive (DPP) atuluka mchipanichi, ndipo alowa chipani cha Malawi Congress (MCP).
Makhansala awiri a chipani cha Dimokaratiki Purogiresivi (DIPIPI) atuluka mchipanichi, ndipo alowa chipani cha Malawi Kongiresi (EMU SIPI).
female
Mkulu wokopa anthu mu MCP, a Moses Kumkuyu, alandira makhansala awiriwa pa msonkhano omwe anachititsa pa school ya Chilayeni, mdera la sub T/A Nyambalo, ku Phalombe.
Mkulu wokopa anthu mu EMU SIPI, a Mozesi Kumkuyu, alandira makhansala awiriwa pa msonkhano omwe anachititsa pa sukulu ya Chilayeni, mdera la sabu Tiyee Nyambalo, ku Phalombe.
female
Makhansalawa ndi a Felix Blayer Jumbe a Mauzi ward, mdera la Phalombe North East komanso a Fedson Thomas a dera la Likulezi ward kumwera kwa Phalombe.
Makhansalawa ndi a Felikisi Buleya Jumbe a Mauzi waadi, mdera la Phalombe Nofi Isiti komanso a Fedisoni Thomasi a dera la Likulezi waadi kumwera kwa Phalombe.
female
Makhansalawa omwe anabwera ndi mafumu a m'maderawa, ati achita izi kamba president Dr Lazarus Chakwera ndiokhululuka komanso chipani chawo ndi cha mtendere ndipo akufuna chitukuko
Makhansalawa omwe anabwera ndi mafumu a m'maderawa, ati achita izi kamba purezidenti Dokota Lazarasi Chakwera ndiokhululuka komanso chipani chawo ndi cha mtendere ndipo akufuna chitukuko
female
Kodi chikuchitika ndi chani pakati pa oyimba ndi oyang'anira oyimbawa? K. Banton wadza ndi thumba lonse pamene akhale akucheza ndi Emmanuel Chokoso mu Programme ya Ngamo The truth, pa MBC.
Kodi chikuchitika ndi chani pakati pa oyimba ndi oyang'anira oyimbawa? Keyi Bantoni wadza ndi thumba lonse pamene akhale akucheza ndi Imanuwelo Chokoso mu Purogiramu ya Ngamo dhe thurufi, pa EMUBISI.
female
k. Banton wafotokozanso za mpungwepungwe womwe ukuchitika pakati pa oyimba ena pa masamba a mchezo. porogiramuyi iwulutsidwa nthawi ya 8 o'clock usiku la mulungu pa 4 February.
keyi Bantoni wafotokozanso za mpungwepungwe womwe ukuchitika pakati pa oyimba ena pa masamba a mchezo. porogiramuyi iwulutsidwa nthawi ya eyiti koloko usiku, la mulungu pa folo Feburuware.
female
Mtsogoleri wachitatu wa dziko la Namibia, Hage Geingob wamwalira ali ndi zaka 82. A Geingob amwalilira ku chipatala china mu mzinda wa windhoke mdzikoli
Mtsogoleri wachitatu wa dziko la Namibia, Heji Genko wamwalira ali ndi zaka eyite thu. A Genko amwalilira ku chipatala china mu mzinda wa windihoko mdzikoli
female
Otsatira kwa a Geingob, a Nangolo Mbumba, alengeza za imfayi. Malemuwa asiya mkazi komanso ana awiri. Anatero a Mbumba.
Otsatira kwa a Genko, a Nangolo Mbumba, alengeza za imfayi. Malemuwa asiya mkazi komanso ana awiri. Anatero a Mbumba.
female
A Geingob anasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko la Namibia, muchaka cha 2015 ndipo atisiuya akulamulira term yawo yachiwiri.
A Genko anasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko la Namibia, muchaka cha tuwente fifitini ndipo atisiuya akulamulira teremu yawo yachiwiri.
female
Boma latsimikiza kuti makalabu alimi, ayambanso mdziko muno ngati njira imodzi yopititsira patsogol ulimi
Boma latsimikiza kuti makalabu alimi, ayambanso mdziko muno ngati njira imodzi yopititsira patsogol ulimi
female
Nduna yaza ulimi a Sam Kawale pamodzi ndi nduna yaza chuma a Simplex Chithyola Banda, ati izi zili chimwechi chifukwa mtsogoleri wa dziko lino a Dr Lazarus Chakwera
Nduna yaza ulimi a Samu Kawale pamodzi ndi nduna yaza chuma a Simpulekisi Chithyola Banda, ati izi zili chimwechi chifukwa mtsogoleri wa dziko lino a Dokota Lazarasi Chakwera,
female
anayika chidwi kwambiri poyambitsanso makalabu amenewa, monga momwe zinali kale nthawi ya Dr Kamuzu Banda.
anayika chidwi kwambiri poyambitsanso makalabu amenewa, monga momwe zinali kale nthawi ya Dokota Kamuzu Banda.
female
Izi zadziwika paulendo woyendera alimi omwe apindula ndi ngongole za NEEF zogulira zipangizo za ulimi m'maboma asanu ndi awiri omwe atenga ngongole zokwana 30,000,000 kwacha.
Izi zadziwika paulendo woyendera alimi omwe apindula ndi ngongole za NIFI zogulira zipangizo za ulimi m'maboma asanu ndi awiri omwe atenga ngongole zokwana sete miliyoni kwacha.
female
Ndipo ambiri mwa iwo anakwanitsa kulima mahekitala oposa khumi ndi anayi. pothirirapo ndemanga a Kawale anati, bungwe la AGCOM ndi mabundwe ena,
Ndipo ambiri mwa iwo anakwanitsa kulima mahekitala oposa khumi ndi anayi. pothirirapo ndemanga a Kawale anati, bungwe la AGIKOMU ndi mabundwe ena,
female
aziperekanso ngongole ku makalabuwa, ndipo atinso zimenezi zichepetsa chiwerengero cha alimi okatenga zipanmgizo zaulimi zotsika mtengo.
aziperekanso ngongole ku makalabuwa, ndipo atinso zimenezi zichepetsa chiwerengero cha alimi okatenga zipanmgizo zaulimi zotsika mtengo.
female
Thupi la mnyamata wina lapezeka m'mawa uno likuyandama pa dziwe la Gele, m'mudzi wa Chibwana, kwa mfumu yaikulu Sitolo ku Machinga.
Thupi la mnyamata wina lapezeka m'mawa uno likuyandama pa dziwe la Gele, m'mudzi wa Chibwana, kwa mfumu yaikulu Sitolo ku Machinga.
female
Malume a mnyamatayu, a Aubrey Songeya, ati mzukulu wawoyi yemwe ndi Denford Mbulanje wa zaka 9, anasowa dzulo la mulungu
Malume a mnyamatayu, a Obure Songeya, ati mzukulu wawoyi yemwe ndi Denifodi Mbulanje wa zaka nayini, anasowa dzulo la mulungu
female
pomwe amasewera ndi anzake ndipo sanabwerere kunyumba komwe amakhal ndi bambo ake. A Songeya anati, anthu ena nayamba kusaka mwanayu, ndipo anapeza zovala zake zili mmbali mwa dziweli.
pomwe amasewera ndi anzake ndipo sanabwerere kunyumba komwe amakhal ndi bambo ake. A Songeya anati, anthu ena nayamba kusaka mwanayu, ndipo anapeza zovala zake zili mmbali mwa dziweli.
female
Ndipo anazindikiranso thupi lake likuyandama. Pakanali pano thipuli likanali pamalowa kudikirira apolice kuti afike pamalowo.
Ndipo anazindikiranso thupi lake likuyandama. Pakanali pano thipuli likanali pamalowa kudikirira apolisi kuti afike pamalowo.
female
A Police ku Lilonge amanga bambo wina wazaka 30, yemwe wakhala akubisala kwa miyezi iwiri, pomuganizira kuti anatsogolera kotchola kwa nyumba yosungiramo katundu
A Polisi ku Lilonge amanga bambo wina wazaka sete, yemwe wakhala akubisala kwa miyezi iwiri, pomuganizira kuti anatsogolera kotchola kwa nyumba yosungiramo katundu
female
ndikuba njinga zamoto 61, komanso ma bello a zovala zakaunjika, zonse za ndalama zokwana 229,000,000 kwacha.
ndikuba njinga zamoto sikisite-wani, komanso mabelo a zovala zakaunjika, zonse za ndalama zokwana thu handiredi andi tuwente-nayini miliyoni kwacha.
female
Mneneri wa police ya Lilongwe a Hastings Chigalu, wati bamboyu yemwe amadziwika ndi dzina loti Nana, koma lake lenileni ndi Manuel Jona,
Mneneri wa police ya Lilongwe a Hesiting'izi Chigalu, wati bamboyu yemwe amadziwika ndi dzina loti Nana, koma lake lenileni ndi Manuwelo Jona
female
amupeza dzulo ku estate ya Lowani ku Neno, komwe wakhala akubisala. A Chigalu anawonjezera kunena kuti apolice azofufuzafufuza,
amupeza dzulo ku esiteti ya Lowani ku Neno, komwe wakhala akubisala. A Chigalu anawonjezera kunena kuti apolisi azofufuzafufuza,
female
agwiranso mayi wa zaka 30 a Lilian Manda aku area 49, powaganizira kuti akhala akulandira ndikugulitsa katundu wakuba kuchokela kwa a Jona
agwiranso mayi wa zaka sete a Liliyani Manda aku eriya fote-nayini, powaganizira kuti akhala akulandira ndikugulitsa katundu wakuba kuchokela kwa a Jona
female
Malipoti akusonyeza kuti mwezi wa December chaka chatha, woganiziridwayu limodzi ndi anzake, anaba katunduyo, atagwiriza ndi mulonda yemwe amagwira ntchito pamalopo.
Malipoti akusonyeza kuti mwezi wa Disemba chaka chatha, woganiziridwayu limodzi ndi anzake, anaba katunduyo, atagwiriza ndi mulonda yemwe amagwira ntchito pamalopo.
female
Boma latsimikizila alimi mdziko muno kuti asade nkhawa za misika komwe akagulitse mbewu zao. Nduna ya zaulimi a Sam Kawale anena izi atayendela alimi omwe apindula ndi ngongole za ulimi za NEEF
Boma latsimikizila alimi mdziko muno kuti asade nkhawa za misika komwe akagulitse mbewu zao. Nduna ya zaulimi a Samu Kawale anena izi atayendela alimi omwe apindula ndi ngongole za ulimi za Nifi
Female
A Kawale ati kampani zambili kuphatikizapo ya Pyxus ndi Paramount Holdings zatsimikizila boma kuti agula mbewu zochuluka kuchokera kwa alimi chaka chino
A Kawale ati kampani zambili kuphatikizapo ya Paisasi ndi paramaunti hoding’izi zatsimikizila boma kuti agula mbewu zochuluka kuchokera kwa alimi chaka chino
Female
Iwo ati pali mwai waukulu kuti nalo bungwe la ADMARC liyamba kugula mbewu mu nthawi yake kaamba koti nduna yoona zachuma yawatsimikila zakuthekera kopereka ndalama zokwanira ku bungweli
wo ati pali mwai waukulu kuti nalo bungwe la Adimaki liyamba kugula mbewu mu nthawi yake kaamba koti nduna yoona zachuma yawatsimikila zakuthekera kopereka ndalama zokwanira ku bungweli
Female
Alimi ambiri omwe awayendera kale m'maboma a Lilongwe, Mchinji ndi Ntchisi akuyamika boma chifukwa chopereka ngongole za NEEF
Alimi ambiri omwe awayendera kale m'maboma a Lilongwe, Mchinji ndi Ntchisi akuyamika boma chifukwa chopereka ngongole za Nifi
Female
kwa alimi ponena kuti zikuwapatsa mwai wogula zipangizo zambiri zaulimi poyerekeza ndi ndondomeko ya AIP
kwa alimi ponena kuti zikuwapatsa mwai wogula zipangizo zambiri zaulimi poyerekeza ndi ndondomeko ya Eayipi
Female
M'modzi mwa alimiwa, a Bonface Puye, m'boma la Mchinji ati ngongole za NEEF zitafikila alimi ambili mdziko muno nkhani ya njala itha kukhala mbili ya makedzana
M'modzi mwa alimiwa, a Bonifesi Puye, m'boma la Mchinji ati ngongole za Nifi zitafikila alimi ambili mdziko muno nkhani ya njala itha kukhala mbili ya makedzana
Female
Ndipo poyankhula kwa Mkanda a Kawale atsimikira alimi omwe sanagule fetereza kuti aonetsetsa kuti akupezeka mosavuta
Ndipo poyankhula kwa Mkanda a Kawale atsimikira alimi omwe sanagule fetereza kuti aonetsetsa kuti akupezeka mosavuta
Female
Phungu wadera la kumpoto m'boma la Mchinji, a Rachel Mazombwe Zulu, ayamika boma la Dr Lazarus Chakwera chifukwa choika chidwi pa ulimi zomwe ati zithandiza kuthetsa vuto la njala
Phungu wadera la kumpoto m'boma la Mchinji, a Recho Mazombwe Zulu, ayamika boma la Dokota Lazalasi Chakwera chifukwa choika chidwi pa ulimi zomwe ati zithandiza kuthetsa vuto la njala
Female