audio audio | raw_text string | normalized_text string | gender string |
|---|---|---|---|
Adawonjeza kuti abale ena sadachedwe, koma kuthotha gogoyo, ndipo adamuthira zikwapu, achitetezo a m’mudzi asadabwere kuwalanditsa. | Adawonjeza kuti abale ena sadachedwe, koma kuthotha gogoyo, ndipo adamuthira zikwapu, achitetezo a m’mudzi asadabwere kuwalanditsa. | female | |
Faston adati, maliro atayikidwa, aliyese adanjanja kuti azimitse gogoyo, koma zidakanika chifukwa nkuti gogoyo atathawitsidwa kale. | Fasitoni adati, maliro atayikidwa, aliyese adanjanja kuti azimitse gogoyo, koma zidakanika chifukwa nkuti gogoyo atathawitsidwa kale. | female | |
M’malo mwake anthu adakayatsa zovala za gogoyo kuphatikiza akatundu ake onse. Ifeyo gogoyo sitikumufunanso kuno, ngati a police akufuna amutulutse, ndiye apite kwina osati kuno. | M’malo mwake anthu adakayatsa zovala za gogoyo kuphatikiza akatundu ake onse. Ifeyo gogoyo sitikumufunanso kuno, ngati a polisi akufuna amutulutse, ndiye apite kwina osati kuno. | female | |
Akabwera kuno ndiye chomwe chidzachitike sindinena, chifukwa izizi adayamba kalekale kunena kuti atikukuta. Adatero Feston. | Akabwera kuno ndiye chomwe chidzachitike sindinena, chifukwa izizi adayamba kalekale kunena kuti atikukuta. Adatero Faston. | female | |
Mkazi wa malemu, Sella Byson wazaka 24, adati mwamuna wake amene adali ndi zaka 27, adakumana ndi ngozi tsiku lomwe adapita kuthengo, kukagwetsa mitengo, yoti awotchere makala. | Mkazi wa malemu, Sella Bayisoni wazaka tuwente folo, adati mwamuna wake amene adali ndi zaka tuwente-seveni, adakumana ndi ngozi tsiku lomwe adapita kuthengo, kukagwetsa mitengo, yoti awotchere makala. | female | |
Iye adati, atapita kuthengoko, sadachedwe kubwerera pamene amati mutu wake ukumuwawa, ati atangokhapa mtengo kuthengoko, adangomva ngati chinthu chamumenya ku mutu. | Iye adati, atapita kuthengoko, sadachedwe kubwerera pamene amati mutu wake ukumuwawa, ati atangokhapa mtengo kuthengoko, adangomva ngati chinthu chamumenya ku mutu. | female | |
Ndidakagula mankhwala koma sizidathandize, pakutha pamasiku adatupa mmutu, komaso diso lidatuluka m’malo mwake, tidathamangira kuchipatala koma sizidatheke, ndipo adamwalira. Adatero | Ndidakagula mankhwala koma sizidathandize, pakutha pamasiku adatupa mmutu, komaso diso lidatuluka m’malo mwake, tidathamangira kuchipatala koma sizidatheke, ndipo adamwalira. Adatero | female | |
Iye adati, chomwe akufuna nkuti anthu akufuna kwabwino amuthandize, chifukwa mwamuna wake wasiya ana awiri, omwe ndi ang’ono amene sangakwanitse kuwathandiza | Iye adati, chomwe akufuna nkuti anthu akufuna kwabwino amuthandize, chifukwa mwamuna wake wasiya ana awiri, omwe ndi ang’ono amene sangakwanitse kuwathandiza | female | |
Gogo Chabwera amasungidwa ndi mdzukulu wake Chifundo Suwiti, amena wakhala nawo kwa zaka zitatu, kumufusa za ufiti wa gogoyo, | Gogo Chabwera amasungidwa ndi mdzukulu wake Chifundo Suwiti, amena wakhala nawo kwa zaka zitatu, kumufusa za ufiti wa gogoyo, | female | |
Kumufunsa za ufiti wagogoyo, Suwiti adati, iye sadayambe wakhudzidwapo ndi gogoyo ngakhale ana ake onse 5 amene ali nawo. | Kumufunsa za ufiti wagogoyo, Suwiti adati, iye sadayambe wakhudzidwapo ndi gogoyo ngakhale ana ake onse fayifi amene ali nawo. | female | |
Ine nkhani ya ufiti, ndimayimva kwa abale awo, koma ineyo sindinganene kuti gogoyo adayamba wandilodzapo. adatero, | Ine nkhani ya ufiti, ndimayimva kwa abale awo, koma ineyo sindinganene kuti gogoyo adayamba wandilodzapo. adatero, | female | |
Ng’anga yina zayithina, itakana kudzutsa munthu wakufa. Ng’anga ina ku Balaka yapereka chindapusa cha 90,000 kwacha kupewa kukaseweza miyezi 15. | Ng’anga yina zayithina, itakana kudzutsa munthu wakufa. Ng’anga ina ku Balaka yapereka chindapusa cha nayinte sauzandi kwacha kupewa kukaseweza miyezi fifitini. | female | |
Imene adamugamula atapezeka wolakwa pamulandu woti adanamiza anthu kuti adzutsa mwana wakufa. | Imene adamugamula atapezeka wolakwa pamulandu woti adanamiza anthu kuti adzutsa mwana wakufa. | female | |
Ng’angayo Flezer Satha wa zaka 37 waboma la Ntcheu, wapereka chindapusacho, pa mulandu wobera munthu pomunamiza. | Ng’angayo Fuleza Satha wa zaka sete-seveni waboma la Ntcheu, wapereka chindapusacho, pa mulandu wobera munthu pomunamiza. | female | |
Mneneri wa police m’boma la Balaka a Gladson Mbumpha, ati izi zidachitika pa court la magistrate m’boma la Balaka, komwe ng’angayo idayitanidwa kuti ikagwire ntchito yomwe idalepherayo. | Mneneri wa polisi m’boma la Balaka a Giladisoni Mbumpha, ati izi zidachitika pa khoti la majisitireti m’boma la Balaka, komwe ng’angayo idayitanidwa kuti ikagwire ntchito yomwe idalepherayo. | female | |
Ng’angayo yapereka chindapusa chifukwa idapatsidwa mwayi wosankha pakati pokaseweza zaka 15 ku ndende kapena kupereka chindapusacho, moti pano yapita kwawo. | Ng’angayo yapereka chindapusa chifukwa idapatsidwa mwayi wosankha pakati pokaseweza zaka fifitini ku ndende kapena kupereka chindapusacho, moti pano yapita kwawo. | female | |
Adatero a Bumpha. Woyimilira boma pa milandu m’boma la Balaka a sub-insipector Mercy Chande adawuza court lo. | Adatero a Mbumpha. Woyimilira boma pa milandu m’boma la Balaka a sabu-insipekita Mese Chande adawuza khotilo. | female | |
Kuti a Satha adatenga 45,000 kwacha kwa a Yamikani Tobias, powawuza kuti adzutsa mwana wawo, yemwe adamwalira. | Kuti a Satha adatenga fite fayifi sauzandi kwacha kwa a Yamikani Tobiyasi, powawuza kuti adzutsa mwana wawo, yemwe adamwalira. | female | |
Chifundo wa zaka 18, yemwe adali mwana wa Tobias, adamwalira mu August 2022, atagwera pa chitsime, ndipo makolo ndi abale ake adayika malirowo. | Chifundo wa zaka eyitini, yemwe adali mwana wa Tobiyasi, adamwalira mu Ogasitituwente tuwente-thu, atagwera pa chitsime, ndipo makolo ndi abale ake adayika malirowo. | female | |
Koma a Chande adawuza Court kuti atayika malirowo, mulamu wa Tobias, adakatenga a Satha kuchoka ku Ntcheu kuti adzadzutse malemuyo, koma amafuna chipondamthengo cha 45,000 kwacha. | Koma a Chande adawuza khoti kuti atayika malirowo, mulamu wa Tobiyasi, adakatengaa a Satha kuchoka ku Ntcheu kuti adzadzutse malemuyo, koma amafuna chipondamthengo cha fote fayifi sauzandi kwacha. | female | |
Ng’angayo imayenera kugwira ntchito m’dera la Andiamo, pa mchombo pa boma la Balaka, Iyo idatsimikiza kuti ikwanitsa kudzutsa malemuyo, ndipo idalandiladi 45,000 kwacha. | Ng’angayo imayenera kugwira ntchito m’dera la Andiamo, pa mchombo pa boma la Balaka, Iyo idatsimikiza kuti ikwanitsa kudzutsa malemuyo, ndipo idalandiladi fote fayifi sauzandi kwacha. | ||
Koma idalephera kudzutsa wakufayo, adatero a Chande, powona kuti ndalama zapita koma palibe chizindikiro choti malemuyo adzuka, a Tobias adakamang’ala ku court. | Koma idalephera kudzutsa wakufayo, adatero a Chande, powona kuti ndalama zapita koma palibe chizindikiro choti malemuyo adzuka, a Tobiyasi adakamang’ala ku khoti. | female | |
Komwe a Satha adawatsegulira mulandu wobera munthu pomunamizira, a Satha adakana mulandu wakuba koma adavomera wonamiza munthu. | Komwe a Satha adawatsegulira mulandu wobera munthu pomunamizira, a Satha adakana mulandu wakuba koma adavomera wonamiza munthu. | female | |
Ndipo adawapeza wolakwa popanga zosemphana ndi gawo 319, la malamulo koma iwo adapempha kuti court liwapatse chilango chopepuka chifukwa ali ndi banja lomwe limadalira iwowo. | Ndipo adawapeza wolakwa popanga zosemphana ndi gawo firi handiredi andi nayintini, la malamulo koma iwo adapempha kuti khoti liwapatse chilango chopepuka chifukwa ali ndi banja lomwe limadalira iwowo. | Female | |
Koma a Chande adapempha court, kuti lipereke chilango chokhwima, kuti anthu ena amaganizo ndi mtima ngati wa Chatha, atengerepo phunziro kuti mchitidwewu uthe. | Koma a Chande adapempha khoti, kuti lipereke chilango chokhwima, kuti anthu ena amaganizo ndi mtima ngati wa Satha, atengerepo phunziro kuti mchitidwewu uthe. | female | |
Woweruza mayi Lucy Mukawa, adagwirizana ndi a Chande ndipo adalamula kuti a Satha alipire chindapusa cha 90,000 kwacha, kapena apo akaseweze zaka 15 kundende. | Woweruza mayi Luse Mukawa, adagwirizana ndi a Chande ndipo adalamula kuti a Satha alipire chindapusa cha nayinte sauzandi kwacha, kapena apo akaseweze zaka fifitini kundende. | female | |
Anthu ambiri odzichemerera kuti ndi ng’anga m’dzikomuno, amadzinenera kuti ali ndi mankhawala othana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo nthenda za mgonagona. | Anthu ambiri odzichemerera kuti ndi ng’anga m’dzikomuno, amadzinenera kuti ali ndi mankhawala othana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo nthenda za mgonagona. | female | |
Ena mwa anthu otere amakakamiza amayi kugona wawo powawuza kuti akatero awatsegula njira ya chiberekero ndipo alandira mphatso ya mwana ngati ali wosabereka. | Ena mwa anthu otere amakakamiza amayi kugona wawo powawuza kuti akatero awatsegula njira ya chiberekero ndipo alandira mphatso ya mwana ngati ali wosabereka. | female | |
Enanso mwa anthu oterewa, amabera anthu powanamiza kuti iwo amachulukitsa ndalama koma mapeto ake amawabera ndalama zomwe iwo amapereka kuti awachulukitsirezo. | Enanso mwa anthu oterewa, amabera anthu powanamiza kuti iwo amachulukitsa ndalama koma mapeto ake amawabera ndalama zomwe iwo amapereka kuti awachulukitsirezo. | female | |
Kufuna kuthana ndi vutolo, nthambi yowona za mankhwala mogwirizana ndi nthambi yowona za zowulutsa mawu ndi kufalitsa nkhani ya MACRA. | Kufuna kuthana ndi vutolo, nthambi yowona za mankhwala mogwirizana ndi nthambi yowona za zowulutsa mawu ndi kufalitsa nkhani ya MAKIRA. | female | |
Adayika lamulo loletsa kugwiritsa ntchito mankhwala achikuda, pokhapokha nthambi yowona za mankhwala yitavomereza. A Satha amachokera m’mudzi mwa Madzenje kwa mfumu yayikulu Kwataine m’boma la Ntcheu. | Adayika lamulo loletsa kugwiritsa ntchito mankhwala achikuda, pokhapokha nthambi yowona za mankhwala yitavomereza. A Satha amachokera m’mudzi mwa Madzenje kwa mfumu yayikulu Kwataine m’boma la Ntcheu. | female | |
Pamene aphungu anyumba ya malamulo amayembekezera kukwangula zokambirana zawo dzulo, mkulu wabungwe lowona za ufulu wa anthu la SED | Pamene aphungu anyumba ya malamulo amayembekezera kukwangula zokambirana zawo dzulo, mkulu wabungwe lowona za ufulu wa anthu la SEDI | female | |
a Sylvester Namiwa, ati nkumanowu sudathandize a Malawi pa nkhani ya njala. Iwo ati, polingalira momwe njala ikukolerera mdziko muno, bill ya chimanga ikadakhala koyambilira. | a Silivesita, Namiwa ati nkumanowu sudathandize a Malawi pa nkhani ya njala. Iwo ati, polingalira momwe njala ikukolerera mdziko muno, bilu ya chimanga ikadakhala koyambilira. | female | |
Kuti ikambidwe ndi kutha msanga kuti zina za ma bill wo zothandiza kuchepetsa njala ziyambike. | Kuti ikambidwe ndi kutha msanga kuti zina za ma biluwo zothandiza kuchepetsa njala ziyambike. | female | |
Mwazina iwo adati, biluyo ndiyothandiza kuti boma likhoza kupereka ma contract olima chimanga cha mthilira kwa ma company akuluakulu, kuti chizisokerera miyezi ya njala. | Mwazina iwo adati, biluyo ndiyothandiza kuti boma likhoza kupereka ma kontirakiti olima chimanga cha mthilira kwa ma kampani akuluakulu, kuti chizisokerera miyezi ya njala. | female | |
Akadakambirana ndikuvomereza bill imeneyi, bwezi pano akukonzekera kuti ma contract ayenda bwanji? Ndiye kuti potengera ndi momwe njala ilili, pofika December bwezi tikuyembekezera chimanga cha mthirira. Adatero a Namiwa. | Akadakambirana ndikuvomereza bilu imeneyi, bwezi pano akukonzekera kuti ma kontirakiti ayenda bwanji? Ndiye kuti potengera ndi momwe njala ilili, pofika Disemba bwezi tikuyembekezera chimanga cha mthirira. Adatero a Namiwa. | female | |
Koma iwo ati ndizodandawulitsa kuti ngakhale mabungwe ndi akadawulo adayesetsa kupanga phokoso za biluyo, nyumbayi idasankha kutseka makutu, mpakana yamaliza mkumano wake. | Koma iwo ati ndizodandawulitsa kuti ngakhale mabungwe ndi akadawulo adayesetsa kupanga phokoso za biluyo, nyumbayi idasankha kutseka makutu, mpakana yamaliza mkumano wake. | female | |
Mkumanowo uli nkati, aphungu adakwekwesa nduna ya zamalimidwe a Sam Kawale, kuti alongosole bwino, zomwe boma likuchita pofuna kuti njala isapweteke anthu mdzikomuno | Mkumanowo uli nkati, aphungu adakwekwesa nduna ya zamalimidwe a Samu Kawale, kuti alongosole bwino, zomwe boma likuchita pofuna kuti njala isapweteke anthu mdzikomuno | female | |
Wapampando wa committee yowona za malimidwe, a Samir Suleman, adachenjeza boma kuti likangowodzera pang’ono, ntchito zambiri zidzayima chifukwa boma lidzakhala likulimbana ndi njala. | Wapampando wa komiti yowona za malimidwe, a Samiye Sulemani, adachenjeza boma kuti likangowodzera pang’ono, ntchito zambiri zidzayima chifukwa boma lidzakhala likulimbana ndi njala. | female | |
Zomwe tikunena nzoti, ngati akunena chilungamo, kuti chimanga chilipo chokwanira, achimwaze mmisika, kuti anthu akagule, chifukwa komwe tikuloweraku, ntchito idzakula mapeto ake zina zidzayima. | Zomwe tikunena nzoti, ngati akunena chilungamo, kuti chimanga chilipo chokwanira, achimwaze mmisika, kuti anthu akagule, chifukwa komwe tikuloweraku, ntchito idzakula mapeto ake zina zidzayima. | female | |
Adatero a Suleman. A Kawale adabwereza mawu awo kuti chimanga chilipo, koma aphungu adawonetsa kusagwirizananazo, pong’ung’udza iwo akuwerenga statement yawo mnyumbayo. | Adatero a Sulemani. A Kawale adabwereza mawu awo kuti chimanga chilipo, koma aphungu adawonetsa kusagwirizananazo, pong’ung’udza iwo akuwerenga sitetementi yawo mnyumbayo. | female | |
Panopa ku nkhokwe za boma kuli chimanga chokwana ma tone 68,000. Ma tone 52,000 ndi a NFRA pomwe ma tone 15,000 ndi cha ADMARC. | Panopa ku nkhokwe za boma kuli chimanga chokwana ma tani sikisite eyiti sauzandi. Ma tani fifite-thu sauzandi ndi a ENI EFU ARAE pomwe ma tani fifitini sauzandi ndi cha ADIMAKI. | female | |
Kuwonjenzera apo boma ligula chimanga chokwana ma tone 42,000 ndi 12,000,000,000 ya mu budget. Adatero a Kawale. | Kuwonjenzera apo boma ligula chimanga chokwana ma tani fote-thu sauzandi ndi thuwelofu biliyoni kwacha ya mu bajeti. Adatero a Kawale. | female | |
Pa mkumanowo, nyumbayi idavomereza ma bill anayi wokhudza ngongole zoti boma libwereke nkuthandizira kulimbikitsa ntchito za ulimi makamaka wa m’thilira. | Pa mkumanowo, nyumbayi idavomereza ma bilu anayi wokhudza ngongole zoti boma libwereke nkuthandizira kulimbikitsa ntchito za ulimi makamaka wa m’thilira. | female | |
Ena mwa ma biluwa ndi ngongole zokwana 276,000,000,000, kwacha zoti boma libwereke ku International Development Association ya World Bank. | Ena mwa ma biluwa ndi ngongole zokwana thu handiredi andi sevente sikisi biliyoni kwacha zoti boma libwereke ku Intanashono Divelopumenti Asosiyeshoni ya Walodi Banki. | female | |
Ndi International Bank for Reconstruction, za gawo lachiwiri ya project ya AGCOM. Nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe, adati mabiluwa athandiza kulimbikitsa ntchito yothana ndi njala. | Ndi Intanashono Banki fo Rikonsitirakishoni, za gawo lachiwiri ya purojekiti ya AGIKOMU. Nduna ya zachuma a Sositeni Gwengwe, adati mabiluwa athandiza kulimbikitsa ntchito yothana ndi njala. | female | |
Makamaka podzera mu ulimi wa m’thilira ndi ma project ena wothandiza anthu kuti azikhala ndi chakudya chokwanira. | Makamaka podzera mu ulimi wa m’thilira ndi ma purojekiti ena wothandiza anthu kuti azikhala ndi chakudya chokwanira. | female | |
Dziko lililonse loganizira za anthu ake, limayenera kuwonetsetsa kuti pali njira zokhazikika zoti anthu a m’dzikolo azikhala ndi chakudya. | Dziko lililonse loganizira za anthu ake, limayenera kuwonetsetsa kuti pali njira zokhazikika zoti anthu a m’dzikolo azikhala ndi chakudya. | female | |
Ma bill amene avomerezedwawa, ntchito yake ndi imeneyo, ndipo atithandiza kwambiri. Adatero a Gwengwe. | Ma bilu amene avomerezedwawa, ntchito yake ndi imeneyo, ndipo atithandiza kwambiri. Adatero a Gwengwe. | female | |
Ma plan a boma a Malawi 2063, nkhani imodzi yayikulu ndiyolimbikitsa ulimi wa makono monga mthilira, kugwititsa ntchito makina apamwamba pawulimi, komaso kutsegula misika ya zokolola ya mphavu. | Ma pulani a boma a Malawi tuwente sikisite-firi, nkhani imodzi yayikulu ndiyolimbikitsa ulimi wa makono monga mthilira, kugwititsa ntchito makina apamwamba pawulimi, komaso kutsegula misika ya zokolola ya mphavu. | female | |
Malingana ndi a Gwengwe, masomphenya amenewa akhoza kutheka ndi project ya AGCOM yomwe aphungu pa nkumano wapitawu, anavomereza ndalama zake za gawo lachiwiri. | Malingana ndi a Gwengwe, masomphenya amenewa akhoza kutheka ndi purojekiti ya AGIKOMU yomwe aphungu pa nkumano wapitawu, anavomereza ndalama zake za gawo lachiwiri. | female | |
Pa mkomanowu, nkhani ina yomwe idamanga nthenje, idali yokhudza ndalama zomwe anthu anapereka pobwezeretsa ziphaso za uzika. | Pa mkomanowu, nkhani ina yomwe idamanga nthenje, idali yokhudza ndalama zomwe anthu anapereka pobwezeretsa ziphaso za uzika. | female | |
Nthawi yomwe ziphaso imatenga kuti zituluke, komaso nkhani yokhudza tsiku lothera mphavu ya chiphaso. Nduna ya zachitetezo cha dziko a Ken Zikhale Ng’oma. | Nthawi yomwe ziphaso imatenga kuti zituluke, komaso nkhani yokhudza tsiku lothera mphavu ya chiphaso. Nduna ya zachitetezo cha dziko a Keni Zikhale Ng’oma. | female | |
Adalonjeza nyumbayi kuti akoza zonsezo, ndipo pano nthambi yopanga ziphaso ya NRB yalengeza kuti munthu saziperekaso ndalama pobwezeretsa zitupa. | Adalonjeza nyumbayi kuti akoza zonsezo, ndipo pano nthambi yopanga ziphaso ya ENI ARABI yalengeza kuti munthu saziperekaso ndalama pobwezeretsa zitupa. | female | |
Komaso zitupa zonse zizigwira ntchito mpaka pa 1 January. A police m’boma la Lilongwe amanga abambo atatu abanja limodzi. | Komaso zitupa zonse zizigwira ntchito mpaka pa wani Januware. A polisi m’boma la Lilongwe amanga abambo atatu abanja limodzi. | female | |
Powaganizira kuti adapha m’balewawo, polimbirana malo m’mudzi mwa Maliseni kwa mfumu yayikuli Chadza. | Powaganizira kuti adapha m’balewawo, polimbirana malo m’mudzi mwa Maliseni kwa mfumu yayikuli Chadza. | female | |
Mneneri wa police m’boma la Lilongwe a Hastings Chigalu, atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati, kupatula kupha a Moffat Kamunthu azaka 39. | Mneneri wa polisi m’boma la Lilongwe a Hesiting'izi Chigalu, atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati, kupatula kupha a Mofati Kamunthu azaka sete nayini. | female | |
Abambo atatuwa, akuzengedwanso mlandu wovulaza anthu ena ochokera kubanja la malemuwo, anthuwo ndi a mabanja awiri, koma pa chisuweni. | Abambo atatuwa, akuzengedwanso mlandu wovulaza anthu ena ochokera kubanja la malemuwo, anthuwo ndi a mabanja awiri, koma pa chisuweni. | female | |
Ndiye amalimbirana malo, koma kamba kosamvana ngakhale mafumu adalowererapo, adamenyana kwambiri pa 24 June 2023, pomwe malemuwo adafera pomwepo. | Ndiye amalimbirana malo, koma kamba kosamvana ngakhale mafumu adalowererapo, adamenyana kwambiri pa tuwente folo Juni tuwente tuwente-firi, pomwe malemuwo adafera pomwepo. | female | |
Ndipo ena adavulazidwa. Atero a Chigalu. Iwo ati nkhaniyo itafika povuta, idapita kubwalo la nyakwawa Nsabwe, komwe adagamula mokomera banja la malemulo, koma sidathere pompo. | Ndipo ena adavulazidwa. Atero a Chigalu. Iwo ati nkhaniyo itafika povuta, idapita kubwalo la nyakwawa Nsabwe, komwe adagamula mokomera banja la malemulo, koma sidathere pompo. | female | |
Chifukwa banja linalo, lidatengera nkhaniyo ku ma bwalo ena, koma konseko nkhani imakomera banja la malemulo. | Chifukwa banja linalo, lidatengera nkhaniyo ku ma bwalo ena, koma konseko nkhani imakomera banja la malemulo. | female | |
Iwo ati chifukwa chowonetsa kusakhutirabe, mafumuwo adawawuza kuti akachite appeal ku bwalo la mfumu yayikulu Chadza. | Iwo ati chifukwa chowonetsa kusakhutirabe, mafumuwo adawawuza kuti akachite apilu ku bwalo la mfumu yayikulu Chadza. | female | |
Nthawi ili mma 7 madzulo pa 24 June pomwepo, woganiziridwawo adazingira mwana wochokera ku banja la malemu, akuchoka ku msika, ndiye poti abale ake akamulanditse, ndewu ya zida idayamba. | Nthawi ili mma seveni madzulo pa tuwente folo Juni pomwepo, woganiziridwawo adazingira mwana wochokera ku banja la malemu, akuchoka ku msika, ndiye poti abale ake akamulanditse, ndewu ya zida idayamba. | female | |
Mkatikati mwa ndewu, a banja linalo adakhapa akubanja la malemuwo, koma pamwe ena onse adakwanitsa kuthawa, malemuwo adawumbiliridwa mpaka kukomoledwa pomwepo nkukafera ku chipatala cha Mitundu. | Mkatikati mwa ndewu, a banja linalo adakhapa akubanja la malemuwo, koma pomwe ena onse adakwanitsa kuthawa, malemuwo adawumbiliridwa mpaka kukomoledwa pomwepo nkukafera ku chipatala cha Mitundu. | female | |
A dolongosola choncho a Chigalu Abambo woganiziridwawo ndi a Marko Kambiya a zaka 31, a Innocent Kambiya a zaka 20 ndi a Benard Kambiya a zaka 19. | A dolongosola choncho a Chigalu. Abambo woganiziridwawo ndi a Mariko Kambiya a zaka fote wani, a Inosenti Kambiya a zaka tuwente ndi a Benadi Kambiya a zaka nayintini. | female | |
Ndipo pomwe nkhaniyo imatipeza, nkuti a police akudikira zotsatira za chomwe chidapha malemuyo, kuti atsegule mulandu. | Ndipo pomwe nkhaniyo imatipeza, nkuti a polisi akudikira zotsatira za chomwe chidapha malemuyo, kuti atsegule mulandu. | female | |
Pa 7 June, 2023. Apolice a Ntchisi nawo, adamanga a Daniel Clifford a zaka 29, a Andison Clifford a zaka 29 ndi a Joseph Sajiwa a zaka 39. | Pa seveni Juni, tuwente tuwente firi, a police a Ntchisi nawo, adamanga a Daniyelo khilifodi a zaka tuwente nayini, a Andisoni khilifodi a zaka tuwente nayini ndi a Josefe Sajiwa a zaka sete nayini. | female | |
Powaganizira kuti adapha a Peter David a zaka 22 pankhaniso yolimbirana malo. M’boma la Mchinji, mudzi wonse wa Chikatupa kwa T/A Mlonyeni, anthu onse adathawapo atavulazana. | Powaganizira kuti adapha a Pita Devidi a zaka tuwente-thu pankhaniso yolimbirana malo. M’boma la Mchinji, mudzi wonse wa Chikatupa kwa Tiyee Mlonyeni, anthu onse adathawapo atavulazana. | female | |
Kugumulirana nyumba, kupherana ziweto ndi kutentherana nkhokwe patabuka mkangano wa malo, zomwe zidapangitsa kuti boma liyambitse program yoti anthu azilembetsa malo a banja kuti azikhala ndi umboni wa umwini. | Kugumulirana nyumba, kupherana ziweto ndi kutentherana nkhokwe patabuka mkangano wa malo, zomwe zidapangitsa kuti boma liyambitse purogiramu yoti anthu azilembetsa malo a banja kuti azikhala ndi umboni wa umwini. | female | |
Mkulu woyang’anira ntchito yowunika malamulo okhudza malo ku unduna wa zamalo, a Masida Mbano, adati program yoti anthu azilembetsa malo a banja, idakhazikitsidwa ncholinga choteteza anthu ochepekedwa mphavu. | Mkulu woyang’anira ntchito yowunika malamulo okhudza malo ku unduna wa zamalo, a Masida Mbano, adati purogiramu yoti anthu azilembetsa malo a banja, idakhazikitsidwa ncholinga choteteza anthu ochepekedwa mphavu. | female | |
Anthuwo ndi monga ana amasiye, wokalamba, awulumali, akamwini ndi atengwa, omwe munthu yemwe amadalira akamwalira amalandidwa malo mosavuta. | Anthuwo ndi monga ana amasiye, wokalamba, awulumali, akamwini ndi atengwa, omwe munthu yemwe amadalira akamwalira amalandidwa malo mosavuta. | female | |
Cholinga choyamba nchoti titeteze anthu opanda mphavuwa, chifukwa anthu adyera amadyera masuku pamutu. | Cholinga choyamba nchoti titeteze anthu opanda mphavuwa, chifukwa anthu adyera amadyera masuku pamutu. | female | |
Ndiye tikufuna azikhala ndi umboni wokwanira woti olo ku court, akhoza kukapeza chilungamo. Adatero a Mbano. | Ndiye tikufuna azikhala ndi umboni wokwanira woti olo ku khoti, akhoza kukapeza chilungamo. Adatero a Mbano. | female | |
Iwo adati ndi ndondomekoyi, milandu ya malo, ikhoza kuchepa chifukwa anthu ena amayamba dala milandu akudziwa chowona, koma amatengera danga kuti palibe umboni. | Iwo adati ndi ndondomekoyi, milandu ya malo, ikhoza kuchepa chifukwa anthu ena amayamba dala milandu akudziwa chowona, koma amatengera danga kuti palibe umboni. | female | |
T/A Mwansambo ya ku Nkhotakota yathirira umboni kuti kulembetsa malo a banja nkothandiza, komaso kumapeputsa mafumu ku ntchito yoweruza milandu ya malo. | Tiyee Mwansambo ya ku Nkhotakota yathirira umboni kuti kulembetsa malo a banja nkothandiza, komaso kumapeputsa mafumu ku ntchito yoweruza milandu ya malo. | female | |
Iwo ndi m’modzi mwa mafumu omwe adapanga kale program yo m’madera mwawo, ndipo adati m’miyezi 8 program yo isadabwere. | Iwo ndi m’modzi mwa mafumu omwe adapanga kale purogiramuyo m’madera mwawo, ndipo adati m’miyezi eyiti purogiramuyo isadabwere. | female | |
Adaweruza milandu 66 yokhudza malo, koma pano milanduyo idatha. Mlandu wa prophet Shepherd Bushiri ndi akazi awo a Mary, udalephereka kuyamba lachiwiri. | Adaweruza milandu sikisite-sikisi yokhudza malo, koma pano milanduyo idatha. Mlandu wa purofeti Shepadi Bushiri ndi akazi awo a Mere, udalephereka kuyamba lachiwiri. | female | |
Kamba ka kusagwirizana kumene kunalipo pakati pa ma Lawyer awo ndi a boma, pachifukwa chimenecho, oweruza milandu a Madalitso Chimwanza, | Kamba ka kusagwirizana kumene kunalipo pakati pa ma Loya awo ndi a boma, pachifukwa chimenecho, oweruza milandu a Madalitso Chimwanza, | female | |
Adawuyimitsa ndi kulamula kuti udzapitirire pa 10 July, 2023. Lawyer wa a Bushiri a Wapona Kitta adati mulanduwu sungayambe chifukwa mbari yoyimira boma idali isanaperekeke umboni wonse wofunika. | Adawuyimitsa ndi kulamula kuti udzapitirire pa teni Julayi, tuwente tuwente-firi. Loya wa a Bushiri a Wapona Kita adati mulanduwu sungayambe chifukwa mbari yoyimira boma idali isanaperekeke umboni wonse wofunika. | female | |
Mukudziwa kuti bwalo lino lidakumananso pa 16 February, 2023, pomwe court lidagamula kuti boma litipatse umboni omwe lilinawo koma sitidalandire. Iwo adatero. | Mukudziwa kuti bwalo lino lidakumananso pa sikiistini Feburuware, tuwente tuwente-firi, pomwe khoti lidagamula kuti boma litipatse umboni omwe lilinawo koma sitinalandire. Iwo adatero. | female | |
Koma woyimira boma a Dziko ndi anthu Malunda adati a Kitta adawadzidzimutsa, chifukwa zomwe adanena mu court zo amayenera kuwadziwitsa powalembera tsiku la ku court lisadafike. | Koma woyimira boma a Dziko ndi anthu Malunda adati a Kita adawadzidzimutsa, chifukwa zomwe adanena mu khotizo amayenera kuwadziwitsa powalembera tsiku la ku khoti lisadafike. | female | |
Mukuona kwanga, zomwe abweretsa azathuwa ndiye mutu wa mlandu wonse, choncho amayenera kutidziwitsa ndondomeko yake kuti tikonzekere bwino tisanabwere ku court. | Mukuona kwanga, zomwe abweretsa azathuwa ndiye mutu wa mlandu wonse, choncho amayenera kutidziwitsa ndondomeko yake kuti tikonzekere bwino tisanabwere ku khoti. | female | |
A Chimwaza atamva mbali zonse anagamula kuti payenera kutsatidwa malamulo a court, iwo anapereka masiku 14 kuti achite zofunikira komanso masiku ena 14 oti ma lawyer a boma awunike mfundozo. | A Chimwaza atamva mbalizonse anagamula kuti payenera kutsatidwa malamulo a khoti, iwo adapereka masiku fotini kuti achite zofunikira komanso masiku ena fotini oti ma loya a boma awunike mfundozo. | female | |
Izi zidachititsa kuti mboni yochokera m’dziko la South Africa a Sibongile Zinyathi asathe kupereka umboni. | Izi zidachititsa kuti mboni yochokera m’dziko la Sowufi Afirika a Sibongile Zinyathi asathe kupereka umboni. | female | |
A Kitta amafuna kuti court lingothetsa mulanduwo osamva nkomwe umboni uliwonse, chifukwa adati mbali ya boma idalephera kupereka zofunikira. | A Kita amafuna kuti khoti lingothetsa mulanduwo osamva nkomwe umboni uliwonse, chifukwa adati mbali ya boma idalephera kupereka zofunikira. | female | |
Mwezi wa November 2020, a Bushiri ndi akazi awo, adathawa ku South Africa nkubwera ku Malawi ati chifukwa amawopsyezedwa pomwe dzikolo linkawazenga milandu. | Mwezi wa Novembala tuwente tuwente, a Bushiri ndi akazi awo, adathawa ku Sowufi Afirika nkubwera ku Malawi ati chifukwa amawopsyezedwa pomwe dzikolo linkawazenga milandu. | female | |
Mulanduwo ukadali pa stage yofuna kupeza ngati ungakambidwe kapena ayi, ma lawyer a Bushiri adapempha court kuti ngati nkukambidwa ndiye kuti mboni za ku South Africa. | Mulanduwo ukadali pa siteji yofuna kupeza ngati ungakambidwe kapena ayi, ma loya a Bushiri adapempha khoti kuti ngati nkukambidwa ndiye kuti mboni za ku Sowufi Afirika. | female | |
Ziyenera kubwera ku Malawi. Koma panthawiyo oweruza milandu a Redson Kapindu adati mbonizo zikhoza kuperekera umboni kudzera pa makina a internet. | Ziyenera kubwera ku Malawi. Koma panthawiyo oweruza milandu a Redisoni Kapindu adati mbonizo zikhoza kuperekera umboni kudzera pa makina a intaneti. | femae | |
Kapena dziko la Malawi likhoza kupempha court lapadera ku South Africa kuti limve umboni. A Bushiri omwe adayambitsa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), | Kapena dziko la Malawi likhoza kupempha khoti lapadera ku Sowufi Afirika kuti limve umboni. A Bushiri omwe adayambitsa mpingo wa inlayitenidi khirisitiyani Gadharing'i (ISIJI), | female | |
Apangapo utumiki wa Mulungu maiko osiyanasiyana, koma adakhazikika ku South Africa, komwe amkayendetsera business zawo. | Apangapo utumiki wa Mulungu maiko osiyanasiyana, koma adakhazikika ku Sowufi Afirika, komwe amkayendetsera bizinesi zawo. | female | |
Kadaulo pa ndale a George Phiri, ati palibe chifukwa chomveka choti dziko la Malawi lizikondwerera ufulu wodziyimirira palokha chifukwa mzambiri limadalira maiko ndi mabungwe ena. | Kadaulo pa ndale a Joji Phiri, ati palibe chifukwa chomveka choti dziko la Malawi lizikondwerera ufulu wodziyimirira palokha chifukwa mzambiri limadalira maiko ndi mabungwe ena. | female | |
lachinayi lapitali, dziko la malawi limakondwerera kuti lakwanitsa zaka 59 zoziyimirira palokha, ndipo budget ya chikondwererochi idali 320 000,000 kwacha | lachinayi lapitali, dziko la malawi limakondwerera kuti lakwanitsa zaka fifite-nayini zoziyimirira palokha, ndipo bajeti ya chikondwererochi idali firi handiredi andi tuwente miliyoni kwacha | female | |
Chikondwererochi chidayamba ndi mwambo wa mapemphero ku Bingu International Convertional Centre (BICC), ndipo chikondwerero chidachika ku bwalo la Bingu National Stadium. | Chikondwererochi chidayamba ndi mwambo wa mapemphero ku Bingu Intanashono Konveshono Senta (BI AYI SISI), ndipo chikondwerero chidachika ku bwalo la Bingu Nashono Sitediyamu | female | |
kumene mlendo wolemekezeka kwambiri, adali mtsogoleri wa dziko la Tanzania, mayI Samia Suluhu Hassan. koma a Phiri ati; "zikutanthauzanji kusakaza ndalama zocholuka choncho?" | kumene mlendo wolemekezeka kwambiri, adali mtsogoleri wa dziko la Tanzania, mayi Samiya Suluhu Hasani. koma a Phiri ati; "zikutanthauzanji kusakaza ndalama zocholuka choncho?" | female | |
Kupanga chikondwerero chomwe tanthauzo lake silioneka, poti zambiri timapanga ndi thandizo la mabungwe ndi mayiko ena. | Kupanga chikondwerero chomwe tanthauzo lake silioneka, poti zambiri timapanga ndi thandizo la mabungwe ndi mayiko ena. | female | |
Zowona tingaononge 320 000,000 kwacha kukondwerera ufulu wozilamulira chonsecho mtsogoleri wathu akulowera uku ndi uku kukapempha thandizo? Tikuyendetsa dziko ndi thandizo, koma nkumati ndife oziyimirira patokha zoona? | Zowona tingaononge firi handiredi andi tuwente miliyomi kwacha kukondwerera ufulu wozilamulira chonsecho mtsogoleri wathu akulowera uku ndi uku kukapempha thandizo? Tikuyendetsa dziko ndi thandizo, koma nkumati ndife oziyimirira patokha zoona? | female | |
Tikuchita kusowa ndalama za kunja, koma nkumati tili pa ufulu wozilamulira. Tisinthe kaye, othandiza azibwera tokha tili npogwira. Atero a Phiri. | Tikuchita kusowa ndalama za kunja, koma nkumati tili pa ufulu wozilamulira. Tisinthe kaye, othandiza azibwera tokha tili npogwira. Atero a Phiri. | female | |
Ndipo polankhula pa mwambo wa lachinayi, a Chakwera adati; "Chifukwa cha ufulu woziyimilira, dziko la Malawi | Ndipo polankhula pa mwambo wa lachinayi, a Chakwera adati; "Chifukwa cha ufulu woziyimilira, dziko la Malawi | female | |
ladutsa muzambiri koma lidapilira muzonsezo ndipo likuyesetsa palokha kuchilimika kuti litukuke" | ladutsa muzambiri koma lidapilira muzonsezo ndipo likuyesetsa palokha kuchilimika kuti litukuke" | female | |
Ngakahale takumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana, sizidatibwezerem'mbuyo pamaso mphenya athu a Malawi 2063, ofuna kuti dziko lathu likwera kuchoka pomwe lili. Adatero a Chakwera. | Ngakahale takumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana, sizidatibwezerem'mbuyo pamaso mphenya athu a Malawi tuwente sikisite-firi, ofuna kuti dziko lathu likwera kuchoka pomwe lili. Adatero a Chakwera. | female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.