audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
kuphatikizapo nyumba ndi katundu komanso mbewu zake. Banaba yemwe ndi mayi wa ana anayi, akuti anali atangofika kumene kuchokera kumunda ndipo ali mnyumba, anamva anthu akumukuwira kuti atuluke mnyumba athawe | kuphatikizapo nyumba ndi katundu komanso mbewu zake. Banaba yemwe ndi mayi wa ana anayi, akuti anali atangofika kumene kuchokera kumunda ndipo ali mnyumba, anamva anthu akumukuwira kuti atuluke mnyumba athawe | Female | |
kaamba koti madzi amalunjika kunyumba kwake. Pakali pano mayiyu pamodzi ndi anthu ena omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa mtsinjewu | kaamba koti madzi amalunjika kunyumba kwake. Pakali pano mayiyu pamodzi ndi anthu ena omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa mtsinjewu | Female | |
akupempha anthu akufuna kwabwino komanso boma kuti liwathandize ndi chakudya komanso malo okhala mongoyembekezera | akupempha anthu akufuna kwabwino komanso boma kuti liwathandize ndi chakudya komanso malo okhala mongoyembekezera | Female | |
Chaka chili chonse pa 15 January ndi tsiku la tchuthi kuno ku Malawi. Tsiku-li analikhazikitsa kuti likhale tsiku lokumbukira moyo wa malemu m’busa John Chilembwe | Chaka chili chonse pa fifitinii januwale ndi tsiku la tchuthi kuno ku Malawi. Tsiku-li analikhazikitsa kuti likhale tsiku lokumbukira moyo wa malemu m’busa Joni Chilembwe | Female | |
mtsogoleri wa mpingo yemwe anaimilira ndikusutsana ndi mchitidwe ochitira nkhanza anthu akuda panthawi ya ulamuliro wa atsamunda | mtsogoleri wa mpingo yemwe anaimilira ndikusutsana ndi mchitidwe ochitira nkhanza anthu akuda panthawi ya ulamuliro wa atsamunda | Female | |
Ndipo monga mwa nthawi zonse, zochitikachitika za tsikuli zikakhala ku likulu la mpingo wa PIM m’boma la Chiradzulu | Ndipo monga mwa nthawi zonse, zochitikachitika za tsikuli zikakhala ku likulu la mpingo wa Piayiemu m’boma la Chiradzulu | Female | |
M'modzi wa anthu omwe akutsogolera ntchito yokonza mwambo-wu a Steve Thamanda ati zonse zili mchimake. Boma latithandidza kwambiri | M'modzi wa anthu omwe akutsogolera ntchito yokonza mwambo-wu a Sitivi Thamanda ati zonse zili mchimake. Boma latithandidza kwambiri | Female | |
chaka chino kwa nthawi yoyamba boma lapanga nsalu ya tsikuli, atero a Thamanda. Mutu wa tsikuli chaka chino ndi Kuzani malire anga Ambuye | chaka chino kwa nthawi yoyamba boma lapanga nsalu ya tsikuli, atero a Thamanda. Mutu wa tsikuli chaka chino ndi Kuzani malire anga Ambuye | Female | |
M'busa Chilembwe ndi chizindikiro chakumenyera ufulu wa dziko lino ndipo boma limapitiliza kumpatsa ulemu pa 15 January chaka chilichonse komanso boma linasindikiza nkhope yake pa ndalama zapepala zingapo za dziko lino | M'busa Chilembwe ndi chizindikiro chakumenyera ufulu wa dziko lino ndipo boma limapitiliza kumpatsa ulemu pa fifitini Januwale chaka chilichonse komanso boma linasindikiza nkhope yake pa ndalama zapepala zingapo za dziko lino | Female | |
Mbiri ikuonetsa kuti M’busa Chilembwe anabadwa mchaka cha 1871, ndipo mwazina anali munthu olimbikitsa maphunziro. Iye anachita maphunziro ake aubusa m'dziko la America | Mbiri ikuonetsa kuti M’busa Chilembwe anabadwa mchaka cha eitini seventewani, ndipo mwazina anali munthu olimbikitsa maphunziro. Iye anachita maphunziro ake aubusa m'dziko la Amelikia | Female | |
Khonsolo ya boma la Lilongwe yati igwiritsa ntchito ndalama yokwana K2.5 miliyoni ya misonkho ya a Malawi pa ntchito yozula pholo la mbendera ndikukaliyika pa malo ena ku ma ofesi kwawo komweko | Khonsolo ya boma la Lilongwe yati igwiritsa ntchito ndalama yokwana thu pointi faifi miliyoni kwacha ya misonkho ya a Malawi pa ntchito yozula pholo la mbendera ndikukaliyika pa malo ena ku ma ofesi kwawo komweko | Female | |
Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe tsamba lino lawona chomwe chikuzungulira mmasamba a nchezo chomwe chikufotokoza mmene ndalama zigwilitsidwile pa ntchito yonseyi | Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe tsamba lino lawona chomwe chikuzungulira mmasamba a nchezo chomwe chikufotokoza mmene ndalama zigwilitsidwile pa ntchito yonseyi | Female | |
Chikalatachi chikusonyeza kuti gawo lokonzekera, lomwe ndikupeza kontalakita yemwe agwire ntchito yosamutsa phololi, igwiritsa ntchito ndalama yokwana K800,000 | Chikalatachi chikusonyeza kuti gawo lokonzekera, lomwe ndikupeza kontalakita yemwe agwire ntchito yosamutsa phololi, igwiritsa ntchito ndalama yokwana eiti handede sauzande kwacha | Female | |
Kuchoka apo, gawo la chiwiri la ntchito yozula pholo la mbendelali ndikukaliyika pa malo atsopano omwe akufunidwawo, akuti itenga ndalama za misonkho ya a Malawi zokwana K1,623,000 | Kuchoka apo, gawo la chiwiri la ntchito yozula pholo la mbendelali ndikukaliyika pa malo atsopano omwe akufunidwawo, akuti itenga ndalama za misonkho ya a Malawi zokwana wani miliyoni sikisi handede andi twentefilii kwacha | Female | |
Khonsoloyi yatiso ndalama yokwana K27,000 igwira ntchito mu gawo lachitatu la ntchitoyi yomwe akuti ndi kusamalira ngalande pamalowa | Khonsoloyi yatiso ndalama yokwana twente seveni sauzande kwacha igwira ntchito mu gawo lachitatu la ntchitoyi yomwe akuti ndi kusamalira ngalande pamalowa | Female | |
kuyiyeletsa kuti iwoneke mopatsa chikoka. Pakadali pano anthu osiyanasiyana m’dziko muno kuphatikizapo akatswiri azachuma, akudzudzula khonsoloyi kaamba kosalabadira kusamala ndalama za dziko lino | kuyiyeletsa kuti iwoneke mopatsa chikoka. Pakadali pano anthu osiyanasiyana m’dziko muno kuphatikizapo akatswiri azachuma, akudzudzula khonsoloyi kaamba kosalabadira kusamala ndalama za dziko lino | Female | |
Anthu ena ati nzodabwitsa kuti m’dziko losauka pazachuma ngati Malawi ndalama zochuluka chonchi zomwe ndi misonkho ya a Malawi, zitha kuwonongedwera pazinthu zosafunika kwenikweni ngati pholo la mbendelali | Anthu ena ati nzodabwitsa kuti m’dziko losauka pazachuma ngati Malawi ndalama zochuluka chonchi zomwe ndi misonkho ya a Malawi, zitha kuwonongedwera pazinthu zosafunika kwenikweni ngati pholo la mbendelali | Female | |
M’kati mwa nkhaniyi tinatchula kuti khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikufuna kugwiritsa ntchito K2.5 miliyoni kusamutsira pa malo ena pholo la mbendera. Apa tinalakwitsa | M’kati mwa nkhaniyi tinatchula kuti khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikufuna kugwiritsa ntchito thu pointi faifi miliyoni kwacha kusamutsira pa malo ena pholo la mbendera. Apa tinalakwitsa | Female | |
Ndi khonsolo ya boma la Lilongwe, Lilongwe District Council imene ikufuna kuwononga ndalama zankhaninkhanizi osati khonsolo ya mzinda wa Lilongwe , Lilongwe City Council | Ndi khonsolo ya boma la Lilongwe, Lilongwe Disitilikiti khanso imene ikufuna kuwononga ndalama zankhaninkhanizi osati khonsolo ya mzinda wa Lilongwe , Lilongwe site khanso | Female | |
Tikupepesa ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe chifukwa chakulakwitsa kwathu. Khwimbi latayira kamtengo Yobu Kachiwanda ndi DCCMS ulosi wamvula utapherezera | Tikupepesa ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe chifukwa chakulakwitsa kwathu. Khwimbi latayira kamtengo Yobu Kachiwanda ndi Disisiemuesi ulosi wamvula utapherezera | Female | |
Kutsatira ulosi omwe nthambi yoona za nyengo mdziko muno inachita ponena kuti mvula iyamba kugwa pa 1 February mwezi uno, tsopano a Malawi ambili ayamikila ulosi wanthambiyi | Kutsatira ulosi omwe nthambi yoona za nyengo mdziko muno inachita ponena kuti mvula iyamba kugwa pa wani febuluwale mwezi uno, tsopano a Malawi ambili ayamikila ulosi wanthambiyi | Female | |
pamene mvula yagwadi m’madera ochuluka ngati momwe nthambiyi inaloselela. Dzana mneneri wa ku nthambi yoona za nyengo a Yobu Kachiwanda anatsimikizira mtundu wa a Malawi | pamene mvula yagwadi m’madera ochuluka ngati momwe nthambiyi inaloselela. Dzana mneneri wa ku nthambi yoona za nyengo a Yobu Kachiwanda anatsimikizira mtundu wa a Malawi | Female | |
ponena kuti mvula iyamba kugwa mwezi uno pa 1 February pamene pachigawo cha pakati komanso kumwera kwa dziko lino kwakhala kopanda mvula pafupifupi masabata awili | ponena kuti mvula iyamba kugwa mwezi uno pa wani febuluwale pamene pachigawo cha pakati komanso kumwera kwa dziko lino kwakhala kopanda mvula pafupifupi masabata awili | Female | |
Kugwa kwa mvula pa 1 February a Salima ndi Kasungu kunafanana ndi zomwe nthambiyi inalosera zomwe zapangitsa a Malawi ambili kutayira ka mtengo nthambiyi | Kugwa kwa mvula pa wani febuluwale a Salima ndi Kasungu kunafanana ndi zomwe nthambiyi inalosera zomwe zapangitsa a Malawi ambili kutayira ka mtengo nthambiyi | Female | |
Pakadali pano alimi okhala mboma la Salima ati ndiwosangalala kamba kamvulayi popeza ng’ambayo ikadatha kuwononga mbewu zawo m’minda pamene zinayamba kuwuma | Pakadali pano alimi okhala mboma la Salima ati ndiwosangalala kamba kamvulayi popeza ng’ambayo ikadatha kuwononga mbewu zawo m’minda pamene zinayamba kuwuma | Female | |
Apolisi mu mzinda wa Lilongwe ati akusakasaka atsizinamtole omwe athyola ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ku Capital Hill ku Lilongwe | Apolisi mu mzinda wa Lilongwe ati akusakasaka atsizinamtole omwe athyola ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulosi Chilima ku kapiyo hilu ku Lilongwe | Female | |
momwe akuti abamo bisiketi ndi inki ya printer. A Salome Zgambo omwe ndi ofalitsa nkhani ku polisi ya Lingadzi munzindawu, awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno | momwe akuti abamo bisiketi ndi inki ya pulinta. A Salome Zyambo omwe ndi ofalitsa nkhani ku polisi ya Lingadzi munzindawu, awuza nyumba zina zofalitsa nkhani mdziko muno | Female | |
kuti akuganizira kuti akathyaliwa apanga chipongwechi pakati pa lachisanu komanso usiku wa Lolemba pa 15 January, 2024 | kuti akuganizira kuti akathyaliwa apanga chipongwechi pakati pa lachisanu komanso usiku wa Lolemba pa 1fifitini januwale twentetwente folo | Female | |
Iwo ati pali chisonyezo choti akubawa anagwiritsa ntchito zenera la ku bafa kwa ofesi ya mlembi wa mkulu wa ofesiyi | Iwo ati pali chisonyezo choti akubawa anagwiritsa ntchito zenera la ku bafa kwa ofesi ya mlembi wa mkulu wa ofesiyi | Female | |
ndipo atalowa mkatimo, mbavazi zabamo tonner yemwe amagwiritsidwa ntchito posindikiza kalata zosiyana siyana komanso ma bisiketi | ndipo atalowa mkatimo, mbavazi zabamo tona yemwe amagwiritsidwa ntchito posindikiza kalata zosiyana siyana komanso ma bisiketi | Female | |
Aka ndi kachiwiri kuti zoterezi zichitike kamba koti mzaka zitatu zapitazi, mu 2021, zoterezi zinachitikanso alonda angapo anamangidwa | Aka ndi kachiwiri kuti zoterezi zichitike kamba koti mzaka zitatu zapitazi, mu twentetwente wani, zoterezi zinachitikanso alonda angapo anamangidwa | Female | |
ndikuyimbidwa milandu ndipo ena mwa iwo akuseweza jele pano. Ogwira ntchito anayi pa kampani ya ETG awanjata kamba kogwinya feteleza | ndikuyimbidwa milandu ndipo ena mwa iwo akuseweza jele pano. Ogwira ntchito anayi pa kampani ya itiji awanjata kamba kogwinya feteleza | Female | |
Ogwira ntchito anayi apa kampani yogulitsa zipangizo za ulimi ya Export Trading Group, ETG awanjata ndikuwaponya mchitokosi cha apolisi ku Dowa | Ogwira ntchito anayi apa kampani yogulitsa zipangizo za ulimi ya ekisipoti thileding’i gulupu, Itiji awanjata ndikuwaponya mchitokosi cha apolisi ku Dowa | Female | |
kamba kowaganizira kuti adakwangwanula m’matumba afetereza pa kampanipo. Anthu anayi oganizilidwawa ndi a Sigele Selemani azaka 25, a Tionge Mazibuko azaka 37 | kamba kowaganizira kuti adakwangwanula m’matumba afetereza pa kampanipo. Anthu anayi oganizilidwawa ndi a Sigele Selemani azaka twente faifi, a Tionge Mazibuko azaka fete seveni | Female | |
a Gabriel Kayange azaka 31 komanso Fabiano Banda azaka 26 zakubadwa | a Gauliyeli Kayange azaka fetewani komanso Fabiuano Banda azaka twente sikisi zakubadwa | Female | |
Nkhani yonse ikuti sabata latha pa 20, yemwe ndi mkulu wakampaniyi mchigawo chapakati a Ivy Sinda anali paulendo oyendera malo ena ogulitsira zipangizo za ulimi akampaniyi | Nkhani yonse ikuti sabata latha pa tuwente, yemwe ndi mkulu wakampaniyi mchigawo chapakati a aive Sinda anali paulendo oyendera malo ena ogulitsira zipangizo za ulimi akampaniyi | Female | |
ndicholinga chofuna kuwerengera katundu m’malowa koma anatutumuka ndizomwe ogwira ntchitowa anali kuchita pa Dowa | ndicholinga chofuna kuwerengera katundu m’malowa koma anatutumuka ndizomwe ogwira ntchitowa anali kuchita pa Dowa | Female | |
Pa 24 January, a Sinda anayenderanso pamalo ogulitsira zipangizozi pofuna kupitiliza ntchito yowelengera zipangizo za ulimizi koma nawo a Malawi Bureau of Standards anafikanso pamalopo | Pa twente folo januwale, a Sinda anayenderanso pamalo ogulitsira zipangizozi pofuna kupitiliza ntchito yowelengera zipangizo za ulimizi koma nawo a Malawi Byulo ofu sitandadzi anafikanso pamalopo | Female | |
Ogwira ntchitowa anadziwitsa a Sinda ponena kuti matumba a feteleza omwe akugulitsa pa malopa ndi osakwanira makilogalamu makumi asanu | Ogwira ntchitowa anadziwitsa a Sinda ponena kuti matumba a feteleza omwe akugulitsa pa malopa ndi osakwanira makilogalamu makumi asanu | Female | |
Izi zinapangitsa kuti ayeze matumbawo ndipo atayeza anapeza kuti matumba 15 ndi omwe samakwana makilogalamu 50 | Izi zinapangitsa kuti ayeze matumbawo ndipo atayeza anapeza kuti matumba fifitini ndi omwe samakwana makilogalamu fifite | Female | |
Akuluakulu pa kampaniyi anatsina khutu apolisi pa nkhaniyi ndipo apolisi sanachedwe koma kuchita kafukufuku pa zankhaniyi ndikumanga oganizilidwawa | Akuluakulu pa kampaniyi anatsina khutu apolisi pa nkhaniyi ndipo apolisi sanachedwe koma kuchita kafukufuku pa zankhaniyi ndikumanga oganizilidwawa | Female | |
Apa ogwira ntchito anayiwa anavomera kuti amapunguladi fetelezayu m’matumbamo. Pakadali pano, ogwira ntchito anayiwa akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu ndikuyankha mulandu wakuba pa malo a ntchito | Apa ogwira ntchito anayiwa anavomera kuti amapunguladi fetelezayu m’matumbamo. Pakadali pano, ogwira ntchito anayiwa akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu ndikuyankha mulandu wakuba pa malo a ntchito | Female | |
Apa ogwira ntchito anayiwa anavomera kuti amapunguladi fetelezayu m’matumbamo. Pakadali pano, ogwira ntchito anayiwa akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu ndikuyankha mulandu wakuba pa malo a ntchito | Apa ogwira ntchito anayiwa anavomera kuti amapunguladi fetelezayu m’matumbamo. Pakadali pano, ogwira ntchito anayiwa akuyembekezeka kukaonekela ku bwalo la milandu ndikuyankha mulandu wakuba pa malo a ntchito | Female | |
Mkumano wa nambala 19 wama Khansala komanso wa Phungu yekhayo wamu mzinda wa Zomba omwe pachingerezi umatchedwa Full Council walephereka chifukwa chachisokonedzo chomwe chidabuka munyumbayi | Mkumano wa nambala naintini wama Khansala komanso wa Phungu yekhayo wamu mzinda wa Zomba omwe pachingerezi umatchedwa fu khanso walephereka chifukwa chachisokonedzo chomwe chidabuka munyumbayi | Female | |
Makhansala achipani cha DPP komanso Phungu wachipani cha DPP Bester Awali adafunsa Mfumu ya Mzinda wa Zomba | Makhansala achipani cha Dipipi komanso Phungu wachipani cha Dipipi Besita Awali adafunsa Mfumu ya Mzinda wa Zomba | Female | |
Khansala Davie Maunde kuti ndichifikwa chiyani adalepheretsa mkumano womwe umayenera kuchitika Lachisanu pa 2 February Poyankhulapo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde | Khansala Devi Maunde kuti ndichifikwa chiyani adalepheretsa mkumano womwe umayenera kuchitika Lachisanu pa thu febuluwale Poyankhulapo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Devi Maunde | Female | |
adakumbutsa nyumbayi kuti zomwe akunena makhansalawo ndizotsamveka chifukwa nkhaniyi adayikambirana kale pa gulupu yawo lapa Whatsapp | adakumbutsa nyumbayi kuti zomwe akunena makhansalawo ndizotsamveka chifukwa nkhaniyi adayikambirana kale pa gulupu yawo lapa Watsapu | Female | |
lomwe makhansala ochuluka adamvomereza kuti mkumanowo uchitike Lolemba pa February. Apolisi angapo m'boma la Neno akulandira chithandizo pa chipatala chachikulu m'bomali | lomwe makhansala ochuluka adamvomereza kuti mkumanowo uchitike Lolemba pa faifi febuluwale. Apolisi angapo m'boma la Neno akulandira chithandizo pa chipatala chachikulu m'bomali | Female | |
atavulazidwa ndi anthu olusa pomwe amakhazikitsa bata pazipolowe zomwe zimachitika m'mudzi mwa Kalioni m'bomali | atavulazidwa ndi anthu olusa pomwe amakhazikitsa bata pazipolowe zomwe zimachitika m'mudzi mwa Kalioni m'bomali | Female | |
Anthu omwe achita zipolowezi ati anali okwiya ndi mkulu wina otchedwa Kamfumu yemwe akumuganizira kuti akukhudzidwa ndi kusowa kwa mwana yemwe wakhala asakuoneka masiku angapo tsopano mmudzimo | Anthu omwe achita zipolowezi ati anali okwiya ndi mkulu wina otchedwa Kamfumu yemwe akumuganizira kuti akukhudzidwa ndi kusowa kwa mwana yemwe wakhala asakuoneka masiku angapo tsopano mmudzimo | Female | |
Malingana ndi m'neneri wapolisi ku Neno, Austin Kamwendo, wati apolisi akwanitsa kumuthawitsa munthu oganiziridwayu, koma anthu okwiyawa, aononga nyumba komanso minibus za a Kamfumu | Malingana ndi m'neneri wapolisi ku Neno, Ositini Kamwendo, wati apolisi akwanitsa kumuthawitsa munthu oganiziridwayu, koma anthu okwiyawa, aononga nyumba komanso minibasi za a Kamfumu | Female | |
Myamata wa zaka 15 yemwe amabilsala kamba kokupha mchemwali wake fyness Chapweteka, chifukwa chosemphana pa nkhani ya poto wapezeka m'boma la Balaka ndipo wamangidwa | Myamata wa zaka fifitini yemwe amabilsala kamba kokupha mchemwali wake fainesi Chapweteka, chifukwa chosemphana pa nkhani ya poto wapezeka m'boma la Balaka ndipo wamangidwa | Female | |
Malinga ndi mneneri wapolisi m'boma la Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati oganiziridwayu ayimbidwa mulandu okupha | Malinga ndi mneneri wapolisi m'boma la Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati oganiziridwayu ayimbidwa mulandu okupha | Female | |
omwe umatsutsana ndi malamulo a dziko lino a gawo 209 ndipo akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa ndondomeko zonse zikamalizidwa | omwe umatsutsana ndi malamulo a dziko lino a gawo thuzilonaini ndipo akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa ndondomeko zonse zikamalizidwa | Female | |
Pa 11 January chaka chomwe chino, oganiziridwayu anathawa atabaya m'chemwali wake pakhosi chifukwa cha poto omwe amamukaniza kuti asakazingiremo chimanga | Pa ileveni Januwale chaka chomwe chino, oganiziridwayu anathawa atabaya m'chemwali wake pakhosi chifukwa cha poto omwe amamukaniza kuti asakazingiremo chimanga | Female | |
Oganiziridwayu amachokera m'mudzi wa Mtendere, mfumu yaikulu Chilipa, m'boma la Mangochi. Apolisi kwa Jenda m'boma la Mzimba amanga bambo wina Chikondi Muwa wazaka 24 | Oganiziridwayu amachokera m'mudzi wa Mtendere, mfumu yaikulu Chilipa, m'boma la Mangochi. Apolisi kwa Jenda m'boma la Mzimba amanga bambo wina Chikondi Muwa wazaka twente folo | Female | |
pomuganizira kuti wakhala akusunga komanso kugwililira atsikana awiri azaka 15 ndi 16 | pomuganizira kuti wakhala akusunga komanso kugwililira atsikana awiri azaka fifitini ndi sikisitini | Female | |
Malingana ndi m'neneri wapolisi ya Jenda, MacFarlen Mseteka, wati bamboyu anayamba kusunga komanso kuchita zadama ndi mtsikana wazaka 16 yo pa 24 December, chaka chatha | Malingana ndi m'neneri wapolisi ya Jenda, Makifaleni Mseteka, wati bamboyu anayamba kusunga komanso kuchita zadama ndi mtsikana wazaka sikisitini yo pa twente folo Disemba, chaka chatha | Female | |
pomwe wachiwiriyo anayamba kukhala naye pa 10 January chaka chomwe chino. Mtseteka watinso apolisi anayamba kufufuza za kusowa kwa mwana wazaka 16 | pomwe wachiwiriyo anayamba kukhala naye pa teni Januwale chaka chomwe chino. Mtseteka watinso apolisi anayamba kufufuza za kusowa kwa mwana wazaka sikisitini | Female | |
bambo ake atakadandaula zakusowa kwa mwana wawo kupolisi yemwe anasiya kuoneka pa 24 December. Apolisi atafufuza, anakamupeza mwanayu komanso ali ndi mnzake wina m'nyumba mwa Muwa | bambo ake atakadandaula zakusowa kwa mwana wawo kupolisi yemwe anasiya kuoneka pa twente folo Disemba . Apolisi atafufuza, anakamupeza mwanayu komanso ali ndi mnzake wina m'nyumba mwa Muwa | Female | |
Achipatala atsimikiza kuti anawa amagwiliridwa. Padakali pano, oganiziridwayu watseguliridwa mulandu ogonana ndi ana | Achipatala atsimikiza kuti anawa amagwiliridwa. Padakali pano, oganiziridwayu watseguliridwa mulandu ogonana ndi ana | Female | |
zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino a gawo 138, ndipo Muwa akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa | zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino a gawo wani fili eiti, ndipo Muwa akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa | Female | |
Mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa, yachititsa kuti madzi ochuluka, awononge msewu wa M5 ochokera pa Salima Turn Off kupita ku Salima pamalo odziwika kuti Mwalawoyera | Mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa, yachititsa kuti madzi ochuluka, awononge msewu wa emu faifi ochokera pa Salima Theni ofu kupita ku Salima pamalo odziwika kuti Mwalawoyera | Female | |
Ofalitsa nkhani za bungwe loona za misewu la Roads Authority, a Portia Kajanga, ati msewu wadukilatu pamalowa | Ofalitsa nkhani za bungwe loona za misewu la Lodzi ofolite, a Potiya Kajanga, ati msewu wadukilatu pamalowa | Female | |
kambanso koti anthu ena anaba zipangizo pamlathowo, kotero kuti palibe galimoto yomwe ingadutse pamalopo | kambanso koti anthu ena anaba zipangizo pamlathowo, kotero kuti palibe galimoto yomwe ingadutse pamalopo | Female | |
A Kajanga apempha anthu kuti agwiritse ntchito msewu wa Golomoti kapena kuti Khwekhwelele pofuna kupita mbali ya Salima kuchokera ku Balaka kapena Ntcheu | A Kajanga apempha anthu kuti agwiritse ntchito msewu wa Golomoti kapena kuti Khwekhwelele pofuna kupita mbali ya Salima kuchokera ku Balaka kapena Ntcheu | Female | |
Pakadali pano, iwo ati kontarakita ali pamalopo kubwezeretsa mlathowo mchimake. Apolisi ku Area 3 ku Lilongwe agwira anthu asanu ndi anayi, 9 | Pakadali pano, iwo ati kontarakita ali pamalopo kubwezeretsa mlathowo mchimake. Apolisi ku Eliya fili ku Lilongwe agwira anthu asanu ndi anayi, naini | Female | |
omwe amafuna kuba chimanga ndi fetereza ku bungwe la Agricultural Research and Extension Trust, ARET. Apolisiwo akusunganso galimoto yonyamula katundu yomwe mbavazo zimafuna kunyamulira katunduyo | omwe amafuna kuba chimanga ndi fetereza ku bungwe la Agilikachulo Lisetchi ekisitenshoni thilasiti, ARETI. Apolisiwo akusunganso galimoto yonyamula katundu yomwe mbavazo zimafuna kunyamulira katunduyo | Female | |
Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati anthu ena anatsina khutu apolisi kuti anthu ena akukonza zokaba ku bungwelo. Apa, apolisiwo anafika msanga pamalopo ndikubisala | Mneneri wapolisi ku Lilongwe, hasiting’izi Chigalu, wati anthu ena anatsina khutu apolisi kuti anthu ena akukonza zokaba ku bungwelo. APA, apolisiwo anafika msanga pamalopo ndikubisala | Female | |
Kenako anawona anthuwo omwe anabwera pa galimoto ndikuyamba kutsegula pa chipata cholowera mkati mwa maofesi abungwelo pogwiritsa ntchito zitsulo | Kenako anawona anthuwo omwe anabwera pa galimoto ndikuyamba kutsegula pa chipata cholowera mkati mwa maofesi abungwelo pogwiritsa ntchito zitsulo | Female | |
Apolisiwo anagwira anthuwo omwe ananyamulanso zikwanje ndipo atawafunsa, anaulula kuti amafuna kuba fetereza komanso chimanga | Apolisiwo anagwira anthuwo omwe ananyamulanso zikwanje ndipo atawafunsa, anaulula kuti amafuna kuba fetereza komanso chimanga | Female | |
Bungwe la Water and Environmental Sanitation Network, WESNET lapempha boma kuti liyike ndalama zokwanira ku ntchito za madzi ndi ukhondo | Bungwe la wota andi invailomento saniteshoni tetiweki , WESINETI lapempha boma kuti liyike ndalama zokwanira ku ntchito za madzi ndi ukhondo | Female | |
Mkulu wa bungwe la WESNET, a Willes Mwandira, apereka pempholi mu mzinda wa Lilongwe. Iwo ati pamene boma likutolera maganizo osiyanasiyana pa chikonzero cha chuma chaboma cha 2024 | Mkulu wa bungwe la WESINETI, a Willes Mwandira, apereka pempholi mu mzinda wa Lilongwe. Iwo ati pamene boma likutolera maganizo osiyanasiyana pa chikonzero cha chuma chaboma cha Twente twente folo | Female | |
mpaka 2025 nkofunika kuyika chidwi pa ntchito za madzi komanso ukhondo. Chaka ndi chaka ngati dziko tikumakumana ndi mavuto a zaumoyo monga mliri wa cholera | mpaka twente twente faifi nkofunika kuyika chidwi pa ntchito za madzi komanso ukhondo. Chaka ndi chaka ngati dziko tikumakumana ndi mavuto a zaumoyo monga mliri wa cholera | Female | |
kaamba ka kusoweka kwa madzi abwino komanso ntchito za ukhondo. Mwazina mavutowa amakula kaamba ka kuchepa kwa ndalama zomwe zimayikidwa ku ntchito za madzi komanso ukhondo. | kaamba ka kusoweka kwa madzi abwino komanso ntchito za ukhondo. Mwazina mavutowa amakula kaamba ka kuchepa kwa ndalama zomwe zimayikidwa ku ntchito za madzi komanso ukhondo. | Female | |
Tikufuna boma likwaniritse lonjezo lomwe limalimbikitsika maiko kuti adziika K5 pa K100 iliyonse ya ndondomeko ya chuma chaboma ku ntchito za madzi ndi ukhondo | Tikufuna boma likwaniritse lonjezo lomwe limalimbikitsika maiko kuti adziika faifi kwacha pa wanihandede kwacha iliyonse ya ndondomeko ya chuma chaboma ku ntchito za madzi ndi ukhondo | Female | |
Ngati tikwaniritse izi, ntchito zilizonse kaya ndi zaumoyo, sukulu kaya chitukuko zidziyenda bwino. Anatero a Mwandira | Ngati tikwaniritse izi, ntchito zilizonse kaya ndi zaumoyo, sukulu kaya chitukuko zidziyenda bwino. Anatero a Mwandira | Female | |
Unduna wa zachuma ukuyenda mzigawo za mdziko lino kumva maganizo a anthu osiyanasiyana pa za ndondomeko ya chuma chaboma ya chaka cha 2024 mpaka 2025 | Unduna wa zachuma ukuyenda mzigawo za mdziko lino kumva maganizo a anthu osiyanasiyana pa za ndondomeko ya chuma chaboma ya chaka cha twente twente folo mpaka twente twente faifi | Female | |
Mayi wina ku Kasungu walamulidwa kukhala ku ndende kwa zaka 16 pogonana kawiri ndi mnyamata wazaka 16 yemwe wamupatsiranso chindoko | Mayi wina ku Kasungu walamulidwa kukhala ku ndende kwa zaka sikisitini pogonana kawiri ndi mnyamata wazaka sikisitini yemwe wamupatsiranso chindoko | Female | |
Malingana ndi mneneri wapolisi ku Kasungu, Joseph Kachikho, wati ulendo oyamba, mayiyu anamuyitanira mwanayu kuchipinda kwake komwe anakamunyengelera ndi mafilimu olaula | Malingana ndi mneneri wapolisi ku Kasungu, Jozefe Kachikho, wati ulendo oyamba, mayiyu anamuyitanira mwanayu kuchipinda kwake komwe anakamunyengelera ndi mafilimu olaula | Female | |
panthawi yomwe mwanayu amakhala m'nyumba mwake ngati wantchito. Ndipo atagonana nayenso kachiwiri pa tchire, ndi pomwe mwanayu amakaulula za nkhaniyi kwa mayi ake | panthawi yomwe mwanayu amakhala m'nyumba mwake ngati wantchito. Ndipo atagonana nayenso kachiwiri pa tchire, ndi pomwe mwanayu amakaulula za nkhaniyi kwa mayi ake | Female | |
Atakayezedwa kuchipatala, mwanayu anapezeka ndi matenda achindoko omwe mayiyu anapezeka nawonso. Bwalo lamilandu la Magistrate linapereka chilango chokhwimachi ndi cholinga choti ena apezerepo phunziro | Atakayezedwa kuchipatala, mwanayu anapezeka ndi matenda achindoko omwe mayiyu anapezeka nawonso. Bwalo lamilandu la Majasitileti linapereka chilango chokhwimachi ndi cholinga choti ena apezerepo phunziro | Female | |
Bwalo la milandu ku Mulanje lalamula Zagwa Hamilton wazaka 37 kukakhala kundende kwa chaka chimodzi | Bwalo la milandu ku Mulanje lalamula Zagwa Hamitoni wazaka fete seveni kukakhala kundende kwa chaka chimodzi | Female | |
chifukwa chothawa panthawi yomwe amafuna kuti akatsekeredwe. Wachiwiri kwa m'neneri wapolisi ku Mulanje, Lea Kambalame, wati pa 1 November 2023, Hamilton anathawa m'manja mwa apolisi | chifukwa chothawa panthawi yomwe amafuna kuti akatsekeredwe. Wachiwiri Kwa m'neneri wapolisi ku Mulanje, Leya Kambalame, wati pa wani novemba twente twente fili, Hamitoni anathawa m'manja mwa apolisi | Female | |
akuchokera kubwalo lamilandu bwalolo litalamula kuti lipitiriza kumva mlanduwo tsiku lina. Hamilton anagwidwa ndi apolisi am'mudzi pakhonde la nyumba yawo ndikukaperekedwanso kupolisi patadutsa sabata imodzi | akuchokera kubwalo lamilandu bwalolo litalamula kuti lipitiriza kumva mlanduwo tsiku lina. Hamitoni anagwidwa ndi apolisi am'mudzi pakhonde la nyumba yawo ndikukaperekedwanso kupolisi patadutsa sabata imodzi | Female | |
Hamilton amachokera m'mudzi wa Gulumba, mfumu yaikulu Chikumbu, m'boma la Mulanje. Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission, MEC | Hamitoni amachokera m'mudzi wa Gulumba, mfumu yaikulu Chikumbu, m'boma la Mulanje. Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Elekititolo komishoni, MEKI | Female | |
lati sizowona kuti Bungweli lalamulidwa ndi bungwe la International Monetory Fund (IMF) kuthetsa madera atsopano a aphungu a Nyumba ya Malamulo | lati sizowona kuti Bungweli lalamulidwa ndi bungwe la Intaneshono monetale fandi Aiemuefu kuthetsa madera atsopano a aphungu a Nyumba ya Malamulo | Female | |
Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati dongosolo lonse la ndondomeko za madera atsopano a aphungu liri mchimake | Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati dongosolo lonse la ndondomeko za madera atsopano a aphungu liri mchimake | Female | |
Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati dongosolo lonse la ndondomeko za madera atsopano a aphungu liri mchimake | Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati dongosolo lonse la ndondomeko za madera atsopano a aphungu liri mchimake | Female | |
Associate Professor Betchani Tchereni wasankhidwa kukhala mlembi woona zachuma ku Unduna wa Zachuma. A Tchereni akulowa m'malo mwa a MacDonald Mafuta Mwale | Asosiyeti Pulofesa Betchani Tchereni wasankhidwa kukhala mlembi woona zachuma ku Unduna wa Zachuma. A Tchereni akulowa m'malo mwa a Makidonadi Mafuta Mwale | Female | |
omwe tsopano asankhidwa kukhala wachiwiri kwa gavanala wa Reserve Bank. Kusintha kwa maudindoku kwadza pa nthawi yomwe ndondomeko ya zachuma cha dziko lino ikuunikidwanso | omwe tsopano asankhidwa kukhala wachiwiri kwa gavanala wa Lizevu Banki. Kusintha kwa maudindoku kwadza pa nthawi yomwe ndondomeko ya zachuma cha dziko lino ikuunikidwanso | Female | |
ndipo a Tchereni akuyembekezeka kupitiliza kayendetsedwe kabwino kachuma komwe kalipo kale. Mkulu wofalitsa nkhani muofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna zaboma, a Robert Kalindiza, atsimikiza za nkhaniyi | ndipo a Tchereni akuyembekezeka kupitiliza kayendetsedwe kabwino kachuma komwe kalipo kale. Mkulu wofalitsa nkhani muofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna zaboma, a Lobati Kalindiza, atsimikiza za nkhaniyi | Female | |
Apolisi ku Mangochi akufunafuna m'nyamata wazaka 15 amene akuganizilidwa kuti wapha mlongo wake Fyness Chapweteka wa zaka 26 | Apolisi ku Mangochi akufunafuna m'nyamata wazaka fifitini amene akuganizilidwa kuti wapha mlongo wake Fainesi Chapweteka wa zaka twente sikisi | Female | |
chifukwa chosemphana maganizo pankhani yokhudza poto watsopano. Mneneri wapolisi ku Mangochi, Amina Tepani Daudi, watsimikizira MBC Online, kuti izi zinachitika pa 11 January 2024 | chifukwa chosemphana maganizo pankhani yokhudza poto watsopano. Mneneri wapolisi ku Mangochi, Amina Tepani Daudi, watsimikizira Emubisi onilaini , kuti izi zinachitika pa leveni januwale twente twente folo | Female | |
m'mudzi wa Mtendere, Mfumu yaikulu Chilipa, m'boma la Mangochi. Malingana ndi mayi a malemuwa, mkangano unabuka pakati pa awiriwa | m'mudzi wa Mtendere, Mfumu yaikulu Chilipa, m'boma la Mangochi. Malingana ndi mayi a malemuwa, mkangano unabuka pakati pa awiriwa | Female | |
chifukwa cha poto watsopano omwe malemuwa anagula kuti aziphikira ndiwo koma mnyamatayu anawutenga ndikukazingira chimanga zomwe zinapangitsa malemuwa kuti amudzudzule | chifukwa cha poto watsopano omwe malemuwa anagula kuti aziphikira ndiwo koma mnyamatayu anawutenga ndikukazingira chimanga zomwe zinapangitsa malemuwa kuti amudzudzule | Female | |
Mkatimkati momudzudzula, ndewu inayambika pomwe m'nyamatayu anatenga mpeni n'kubaya nawo m'chemwali wake | Mkatimkati momudzudzula, ndewu inayambika pomwe m'nyamatayu anatenga mpeni n'kubaya nawo m'chemwali wake | Female | |
Padakali pano kafukufuku ali mkati ndipo akapezeka adzaimbidwa mlandu okupha omwe umatsutsana ndi gawo 209 la malamulo a dziko lino | Padakali pano kafukufuku ali mkati ndipo akapezeka adzaimbidwa mlandu okupha omwe umatsutsana ndi gawo thu zilonaini la malamulo a dziko lino | Female | |
Apolisi ati sikoyenera kuti pakakhala kusamvana kulikonse anthu adzitengera malamulo mmanja mwawo kapena kuchita zaupandu mu njira Ina iliyonse kaamba koti ochita zotere adzapatsidwa chilango | Apolisi ati sikoyenera kuti pakakhala kusamvana kulikonse anthu adzitengera malamulo mmanja mwawo kapena kuchita zaupandu mu njira Ina iliyonse kaamba koti ochita zotere adzapatsidwa chilango | Female | |
Bwalo la milandu ku Zomba lagamula kuti bambo wina Tamani Suluma akagwire ukaidi kwa miyezi isanu ndi umodzi atapezeka olakwa pa mulandu olowetsa masimu kadi kundende ya Zomba | Bwalo la milandu ku Zomba lagamula kuti bambo wina Tamani Suluma akagwire ukaidi kwa miyezi isanu ndi umodzi atapezeka olakwa pa mulandu olowetsa masimu kadi kundende ya Zomba | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.