audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Mc Mooly amachokera m’mudzi Makuni, m’boma la Rumphi pomwe Angela amachokera m’mudzi mwa Kainga, m’boma la Ntcheu | MMakimule amachokera m’mudzi Makuni, m’boma la Rumphi pomwe Anjela amachokera m’mudzi mwa Kainga, m’boma la Ntcheu | Female | |
Pomwe Amalawi akulira ndi vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto lomwe laimitsa ntchito zambiri makamaka zodalira mafutawo, anthu ena apezapo geni yotentha paululuwo | Pomwe Amalawi akulira ndi vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto lomwe laimitsa ntchito zambiri makamaka zodalira mafutawo, anthu ena apezapo geni yotentha paululuwo | Female | |
Mwachitsanzo, mavenda akugula mafutawo monga petulo akapezeka pa mtengo wa boma wa K1 700 pa lita n’kumagulitsa kwa Amalawi ozingwa pa mtengo wa K5 000 pa lita | Mwachitsanzo, mavenda akugula mafutawo monga petulo akapezeka pa mtengo wa boma wa wanisauzande seveni handede kwacha pa lita n’kumagulitsa kwa Amalawi ozingwa pa mtengo Faifi sauzande kwacha pa lita | Female | |
Koma akadaulo ati izi n’zomwe zalimbitsa kwambiri moyo wa anthu m’dziko muno poti kuti ayende akagwire ntchito kapena akapange bizinesi akuyenera kupereka kawiri | Koma akadaulo ati izi n’zomwe zalimbitsa kwambiri moyo wa anthu m’dziko muno poti kuti ayende akagwire ntchito kapena akapange bizinesi akuyenera kupereka kawiri | Female | |
mtengo womwe ankakwelera basi miyezi iwiri yapitayo mafutawo asadayambe kusowa. Kwa miyezi iwiri tsopano, Amalawi akugona mmalo mogulitsira mafuta ndi chiyembekezo kuti mwina mafutawo akhoza kubwera kuti aguleko pamtengo woyera | mtengo womwe ankakwelera basi miyezi iwiri yapitayo mafutawo asadayambe kusowa. Kwa miyezi iwiri tsopano, Amalawi akugona mmalo mogulitsira mafuta ndi chiyembekezo kuti mwina mafutawo akhoza kubwera kuti aguleko pamtengo woyera | Female | |
Kusowa kwa mafutawo n’komwe kwatsegula mgodi wa mavenda omwe akulolera kugona mmalo ogulitsira mafutawo kuti akafika agule n’kumagulitsa pamtengo wokwera wobera Amalawi | Kusowa kwa mafutawo n’komwe kwatsegula mgodi wa mavenda omwe akulolera kugona mmalo ogulitsira mafutawo kuti akafika agule n’kumagulitsa pamtengo wokwera wobera Amalawi | Female | |
Koma mkulu wa nthambi yoyang’anira za mphamvu zamagetsi ndi mafuta ya Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) a Henry Kachaje ati nthambiyo yaletsa kugula mafuta m’zigubu kapena magaloni | Koma mkulu wa nthambi yoyang’anira za mphamvu zamagetsi ndi mafuta ya Malawi Eneje legyuletale ofolite (Mera) a Henele Kachaje ati nthambiyo yaletsa kugula mafuta m’zigubu kapena magaloni | Female | |
chifukwa iyi ndi njira yomwe mavenda akugwiritsa ntchito. Timapereka chilolezo munthu akabwera kudzapempha kuti agule mafuta m’zigubu koma taona kuti mwayiwu walowa chibwana | chifukwa iyi ndi njira yomwe mavenda akugwiritsa ntchito. Timapereka chilolezo munthu akabwera kudzapempha kuti agule mafuta m’zigubu koma taona kuti mwayiwu walowa chibwana | Female | |
anthu akugula mafutawo kuti azikagulitsanso mobera anzawo, atero a Kachaje. Lachiwiri lapitali, apolisi adalanda zigubu, majenereta komanso mathanki a galimoto | anthu akugula mafutawo kuti azikagulitsanso mobera anzawo, atero a Kachaje. Lachiwiri lapitali, apolisi adalanda zigubu, majenereta komanso mathanki a galimoto | Female | |
ndi njinga zamoto zomwe mavenda amagwiritsa ntchito pogula feteleza ngati azingwa n’cholinga chokagulitsanso pamtengo wokwera | ndi njinga zamoto zomwe mavenda amagwiritsa ntchito pogula feteleza ngati azingwa n’cholinga chokagulitsanso pamtengo wokwera | Female | |
Mneneri wapolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu adatsimikiza kuti apolisi adalanda majenereta abodza 9, mathanki a galimoto ndi njinga zamoto 12 | Mneneri wapolisi ku Lilongwe a Hasiting’izi Chigalu adatsimikiza kuti apolisi adalanda majenereta abodza naini, mathanki a galimoto ndi njinga zamoto twelofu | Female | |
komanso zigubu zoposa 20 pomwe apolisiwo amayendera mmalo ogulitsira mafuta. Tipitiriza ntchito imeneyi kuti mchitidwewu uthe chifukwa ukusokoneza zambiri | komanso zigubu zoposa tuwente pomwe apolisiwo amayendera mmalo ogulitsira mafuta. Tipitiriza ntchito imeneyi kuti mchitidwewu uthe chifukwa ukusokoneza zambiri | Female | |
ukupangitsa kuti mitengo ya basi ikwere moonjeza anthu n’kumalephera kuyenda, zimenezi n’zosokoneza dziko lonse atero a Chigalu | ukupangitsa kuti mitengo ya basi ikwere moonjeza anthu n’kumalephera kuyenda, zimenezi n’zosokoneza dziko lonse atero a Chigalu | Female | |
Mkulu wa bungwe la anthu ogula katundu la Consumers Association of Malawi Cama a John Kapito ati n’zomvetsa chisoni | Mkulu wa bungwe la anthu ogula katundu la Konzyumazi asosiyeshoni ofu malawi Kama a JonI Kapito ati n’zomvetsa chisoni | Female | |
kuti pomwe dziko la Malawi likufunika kutukula ntchito za mabizinesi kuti chuma chake chikwere, ntchitozo zikugwa pansi chifukwa chakusowa kwa mafuta. Timadandaula za magetsi koma tidayamba kuzolowera | kuti pomwe dziko la Malawi likufunika kutukula ntchito za mabizinesi kuti chuma chake chikwere, ntchitozo zikugwa pansi chifukwa chakusowa kwa mafuta. Timadandaula za magetsi koma tidayamba kuzolowera | Female | |
ndipo makampani adayamba kuzolowera kugwiritsa ntchito majenereta tsopano ndi apa mafuta wolizira majeneretawo akusowanso. N’kumati zinthu zikuyenda. atero a Kapito | ndipo makampani adayamba kuzolowera kugwiritsa ntchito majenereta tsopano ndi apa mafuta wolizira majeneretawo akusowanso. N’kumati zinthu zikuyenda. atero a Kapito | Female | |
Izi zidachititsa gulu la mabungwe omenyera anthu ufulu la Human Rights Defenders Coalition, HRDC kuchenjeza boma Lachiwiri kuti ngati silipangapo kanthu pavutoli, Malawi ayaka moto | Izi zidachititsa gulu la mabungwe omenyera anthu ufulu la Hyumani laitsi difendazi kowalishoni, Etchialadisi kuchenjeza boma Lachiwiri kuti ngati silipangapo kanthu pavutoli, Malawi ayaka moto | Female | |
Talipatsa bomalo masiku 21 kuti vuto la mafuta a galimoto lithe apo ayi timema Amalawi kuti kuyambira pa 7 December | Talipatsa bomalo masiku twentewani kuti vuto la mafuta a galimoto lithe apo ayi timema Amalawi kuti kuyambira pa seveni disemba | Female | |
kukhale zionetsero zamnanu, adatero wapampando wa HRDC a Gift Trapence. Iwo atinso mtsogoleri wa dziko lino | kukhale zionetsero zamnanu, adatero wapampando wa Etchialadisi a Gifiti Thilapensi. Iwo atinso mtsogoleri wa dziko lino | Female | |
a Lazarus Chakwera achotse mkulu wa nkhokwe za boma zosungirako mafuta agalimoto, Nocma a Hellen Buluma komanso aletse maulendo opanda phindu omwe akungoononga ndalama za boma | a Lazalasi Chakwera achotse mkulu wa nkhokwe za boma zosungirako mafuta agalimoto, Nokima a Heleni Buluma komanso aletse maulendo opanda phindu omwe akungoononga ndalama za boma | Female | |
Gulu la HRDC lidali patsogolo ponena kuti yemwe ankayendetsa chisankho a Jane Ansah atule pansi udindo chifukwa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino sichidayende bwino | Gulu la Etchialadisi lidali patsogolo ponena kuti yemwe ankayendetsa chisankho a Jeni Ansa atule pansi udindo chifukwa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino sichidayende bwino | Female | |
Pachisankhocho padagwiritsidwa ntchito zofutira zimene bwalo la milandu pa mapeto pa zonse lidagamula kuti sichidayende bwino ndipo pakhale chibwereza | Pachisankhocho padagwiritsidwa ntchito zofutira zimene bwalo la milandu pa mapeto pa zonse lidagamula kuti sichidayende bwino ndipo pakhale chibwereza | Female | |
Koma ngakhale nduna ya zofalitsa nkhani a Gospel Kazako omwenso ndi mneneri wa boma anena kuti a Chakwera apeza kale mayankho a vutolo ndi mavuto ena omwe ali m’dziko muno | Koma ngakhale nduna ya zofalitsa nkhani a Gosipelo Kazako omwenso ndi mneneri wa boma anena kuti a Chakwera apeza kale mayankho a vutolo ndi mavuto ena omwe ali m’dziko muno | Female | |
atinso vuto la mafutalo sichikonzero cha boma. Tonse tikudziwa gwero la kusowa kwa mafuta kuti ndi nkhondo ya azachuma omwe agwera dziko lonse | atinso vuto la mafutalo sichikonzero cha boma. Tonse tikudziwa gwero la kusowa kwa mafuta kuti ndi nkhondo ya azachuma omwe agwera dziko lonse | Female | |
komabe apulezidenti a Chakwera adatambasula kale njira zomwe akonza kuti vutoli ndi mavuto ena athe, adatero a Kazako | komabe apulezidenti a Chakwera adatambasula kale njira zomwe akonza kuti vutoli ndi mavuto ena athe, adatero a Kazako | Female | |
Katswiri pa nkhani za ulimi a Ronald Chilumpha wapempha alimi kuti asamale bwino mbatata zomwe akolora pomwe pali chiopsezo kuti njala itha kugwa m’dziko muno | Katswiri pa nkhani za ulimi a Ronadi Chilumpha wapempha alimi kuti asamale bwino mbatata zomwe akolora pomwe pali chiopsezo kuti njala itha kugwa m’dziko muno | Female | |
A Chilumpha ati alimi atha kuchita izi popala makaka a mbatata zomwe ndi zochuluka zedi m’madera ena a dziko lino kuti adzathe kugwiritsa ntchito mtsogolo | A Chilumpha ati alimi atha kuchita izi popala makaka a mbatata zomwe ndi zochuluka zedi m’madera ena a dziko lino kuti adzathe kugwiritsa ntchito mtsogolo | Female | |
Iwo aonjezeranso kuti kuchuluka kwa mbatatazi kupereke phunziro kwa adindo kuti pakhale ndondomeko zabwino zokonzera katundu osiyanasiyana kuchokera ku mbewu ngati izi | Iwo aonjezeranso kuti kuchuluka kwa mbatatazi kupereke phunziro kwa adindo kuti pakhale ndondomeko zabwino zokonzera katundu osiyanasiyana kuchokera ku mbewu ngati izi | Female | |
ufa wa mbatata ndi zina zomwe zingathe kugulitsidwa ngakhale m’maiko a kunja. Tisiyileni wathuyo pangani zanu | ufa wa mbatata ndi zina zomwe zingathe kugulitsidwa ngakhale m’maiko a kunja. Tisiyileni wathuyo pangani zanu | Female | |
BBC yakwiyitsa anthu a ku Africa pa nkhani ya malemu TB Joshua. Patadutsa zaka ziwiri ndi miyezi ingapo chimwalilireni mneneri TB Joshua ku Nigeria, wayilesi ya British Broadcasting Corporation (BBC) | Bibisi yakwiyitsa anthu a ku Afilika pa nkhani ya malemu TiBi Joshuwa. Patadutsa zaka ziwiri ndi miyezi ingapo chimwalilireni mneneri TiBi Joshuwa ku Naijeliya, wayilesi ya Bulitishi bulodikasiting’I kopaleshoni (Bibisi) | Female | |
yabweletsa poyera zotsatira za kafukufuku yemwe inapanga pa zoipa zomwe a Joshua amapanga monga kugwililira amayi ndi atsikana ndi kuwakakamiza kuchotsa mimba komanso kupanga zabodza | yabweletsa poyera zotsatira za kafukufuku yemwe inapanga pa zoipa zomwe a Joshuwa amapanga monga kugwililira amayi ndi atsikana ndi kuwakakamiza kuchotsa mimba komanso kupanga zabodza | Female | |
Koma nkhaniyi yakwiyitsa anthu ochuluka m’mayiko a mu Africa omwe akuti BBC imadana ndi anthu a ku Africa ndipo ena ati BBC ikugwilitsidwa ntchito ndi satana | Koma nkhaniyi yakwiyitsa anthu ochuluka m’mayiko a mu Afilika omwe akuti Bibisi imadana ndi anthu a ku Afilika ndipo ena ati Bibisi ikugwilitsidwa ntchito ndi satana | Female | |
Wayilesi ya BBC lero Lolemba pa 8 January, 2023 itulutsa gawo loyamba la kafukufuku yemwe ikuti yamuchita kwa zaka ziwiri pa momwe mneneri Temitope Balogun Joshua | Wayilesi ya Bibisi lero Lolemba pa eiti Januwale Twentetwente fili itulutsa gawo loyamba la kafukufuku yemwe ikuti yamuchita kwa zaka ziwiri pa momwe mneneri Temitope Balogani Joshuwa | Female | |
yemwe mwachidule amadziwika kuti TB Joshua amazunzira anthu aku mpingo wake wa Synagogue Church Of All Nations SCOAN | yemwe mwachidule amadziwika kuti Tibi Joshuwa amazunzira anthu aku mpingo wake wa Sunagoge Tchetchi ofu oneshonzi Sikowani | Female | |
Mbali ina ya kafukufukuyu, wayilesi ya BBC yati yapeza kuti malemu TB Joshua omwe anamwalira pa 5 June chaka cha 2021 | Mbali ina ya kafukufukuyu, wayilesi ya Bibisi yati yapeza kuti malemu Tibi Joshuwa omwe anamwalira pa faifi Juni chaka cha twente twente wani | Female | |
ankachitira nkhaza, kukhala pa maubwezi okakamiza ndi amayi amu mpingo wake ochokera maiko ena, ochokera maiko monga monga England, South Africa, Namibia ndi Nigeria | ankachitira nkhaza, kukhala pa maubwezi okakamiza ndi amayi amu mpingo wake ochokera maiko ena, ochokera maiko monga monga Engilandi, Saufi afilika, Namibiya ndi Naijeliya | Female | |
Malingana ndi zomwe yalemba BBC pa tsamba lake la pa intaneti, Joshua anayamba kugwililira ambiri mwa amayiwa ali ndi zaka zosakwana 18 | Malingana ndi zomwe yalemba Bibisi pa tsamba lake la pa intaneti, Joshuwa anayamba kugwililira ambiri mwa amayiwa ali ndi zaka zosakwana 18 | Female | |
ndipo ena amawachita nkhazazi mpaka kwa zaka zisanu. Amayiwa awuza BBC kuti ena mwa iwo amawakakamiza kuchotsa mimba zomwe Joshua ankawapatsa | ndipo ena amawachita nkhazazi mpaka kwa zaka zisanu. Amayiwa awuza Bibisi kuti ena mwa iwo amawakakamiza kuchotsa mimba zomwe Joshuwa ankawapatsa | Female | |
Ena omwe ankagwira ntchito ndi Joshua awuza BBC kuti munthu wa Mulungu-yu ankapanga zozizwitsa zonama ponena kuti ankachita kugwirizana ndi anthu nseli | Ena omwe ankagwira ntchito ndi Joshuwa awuza Bibisi kuti munthu wa Mulungu-yu ankapanga zozizwitsa zonama ponena kuti ankachita kugwirizana ndi anthu nseli | Female | |
BBC yati zotsatilazi, zomwe zitulutsidwe m’magawo atatu, zibweretsa mboni zosiyanasiyana omwe ambiri mwa iwo ndi ogwira ntchito akale, adindo akale komaso mamembala akale | Bibisi yati zotsatilazi, zomwe zitulutsidwe m’magawo atatu, zibweretsa mboni zosiyanasiyana omwe ambiri mwa iwo ndi ogwira ntchito akale, adindo akale komaso mamembala akale | Female | |
a mpingo wa SCOAN omwe malemu Joshua ankatsogolera omwe pano akutsogolera ndi mkazi wawo Evelyn | a mpingo wa Sikowani omwe malemu Joshuwa ankatsogolera omwe pano akutsogolera ndi mkazi wawo Evelini | Female | |
Iyo yati anthuwa abweretsanso pa mbalambanda momwe malemuwa komaso akuluakulu ena mu mpingowu ankachitira zosaweruzika ndi azimayi komaso momwe mneneri Joshua ankachitila zozwizwitsa | Iyo yati anthuwa abweretsanso pa mbalambanda momwe malemuwa komaso akuluakulu ena mu mpingowu ankachitira zosaweruzika ndi azimayi komaso momwe mneneri Joshuwa ankachitila zozwizwitsa | Female | |
Nkhaniyi siyinisangalatse anthu ochuluka omwe ambiri mwa iwo ndi ochokera mmaiko amu Africa ndipo akudzudzula BBC kamba ka nkhani | Nkhaniyi siyinisangalatse anthu ochuluka omwe ambiri mwa iwo ndi ochokera mmaiko amu Afilika ndipo akudzudzula Bibisi kamba ka nkhani | Female | |
omwe ambiri akuti uku ndikungofuna kuyipitsa mbiri ya bwino yomwe malemu TB Joshua anasiya asanamwalire mu 2021 | omwe ambiri akuti uku ndikungofuna kuyipitsa mbiri ya bwino yomwe malemu Tibi Joshuwa anasiya asanamwalire mu twente twente wani | Female | |
Malingana ndi ena mwa mauthenga omwe tsamba lino lapeza pa masamba anchezo osiyanasiyana kuchokera Lamulungu pa 7 January, 2024 | Malingana ndi ena mwa mauthenga omwe tsamba lino lapeza pa masamba anchezo osiyanasiyana kuchokera Lamulungu pa seveni Januwale Twente twente folo | Female | |
pomwe BBC inalengeza zoti itulutsa potsatira za kafukufukuzo, anthu ochuluka ati BBC yawonetseratu kuti imadana komaso simafuna kuyamikira anthu amayiko amu Africa | pomwe Bibisi inalengeza zoti itulutsa potsatira za kafukufukuzo, anthu ochuluka ati Bibisi yawonetseratu kuti imadana komaso simafuna kuyamikira anthu amayiko amu Afilika | Female | |
Inu anthu akumadzulo, lekani kuyang’anira pansi anthu amu Africa. Sitilinso ochepa mphamvu kuti tingakhale pansi pautsamunda wanu odzala ndi mabodza. Kudzikuza kwanu kunatiika pansi paukapolo | Inu anthu akumadzulo, lekani kuyang’anira pansi anthu amu Afilika. Sitilinso ochepa mphamvu kuti tingakhale pansi pautsamunda wanu odzala ndi mabodza. Kudzikuza kwanu kunatiika pansi paukapolo | Female | |
Malingaliro anu oyipa kwa Africa ndiomwe ayambitsa kafukufuku osavetsetsekayu. Ndi chifukwa chiyani koma, wadabwa munthu wina pa fesibuku mu uthenga omwe anaulemba nchingerezi | Malingaliro anu oyipa kwa Afilika ndiomwe ayambitsa kafukufuku osavetsetsekayu. Ndi chifukwa chiyani koma, wadabwa munthu wina pa fesibuku mu uthenga omwe anaulemba nchingerezi | Female | |
Munthu winaso yemwe anaikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la BBC pomwe wayilesiyi inalengeza kuti iwulutsa za zotsatira za kafukufuku wakeyu | Munthu winaso yemwe anaikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la Bibisi pomwe wayilesiyi inalengeza kuti iwulutsa za zotsatira za kafukufuku wakeyu | Female | |
wauza wailesiyi kuti iyambe yapanga kafukufuku onga uyu pa anthu akhungu lachizungu. Pitani mukafufuze kaye za banja lachifumu. Mu Africa tili bwino kuno chonde tisiyeni, wateloso kwina pa fesibuku | wauza wailesiyi kuti iyambe yapanga kafukufuku onga uyu pa anthu akhungu lachizungu. Pitani mukafufuze kaye za banja lachifumu. Mu Afilika tili bwino kuno chonde tisiyeni, wateloso kwina pa fesibuku | Female | |
pamene winaso wati, chonde kambani zambiri zokhudza mayiko 52 aku America Polembapo pa tsamba lake la mchezo, oyimba wa ku Malawi wa nyimbo za uzimu Shammah Vocals | pamene winaso wati, chonde kambani zambiri zokhudza mayiko fifite thu aku Amelika Polembapo pa tsamba lake la mchezo, oyimba wa ku Malawi wa nyimbo za uzimu Shama Vokozi | Female | |
anati zomwe ikuchita BBC zikuoneka kuti ikugwilitsidwa ntchito ndi satana chifukwa Joshua anali munthu wabwino | anati zomwe ikuchita Bibisi zikuoneka kuti ikugwilitsidwa ntchito ndi satana chifukwa Joshuwa anali munthu wabwino | Female | |
Ndi zodabwitsa kuti anthu asankha kuona zoipa zomwe zalembedwa pa masamba a mchezo kusiya zabwino zomwe akuziona pa galaundi Anthu ambiri anamaliza maphunziro awo chifukwa cha Joshua | Ndi zodabwitsa kuti anthu asankha kuona zoipa zomwe zalembedwa pa masamba a mchezo kusiya zabwino zomwe akuziona pa galaundi Anthu ambiri anamaliza maphunziro awo chifukwa cha Joshuwa | Female | |
ena ali ndi nyumba kamba ka iyeyo ndipo ambiri anawapatsa chakudya iye ali moyo. BBC sinalembeko zimenezi | ena ali ndi nyumba kamba ka iyeyo ndipo ambiri anawapatsa chakudya iye ali moyo. Bibisi sinalembeko zimenezi | Female | |
koma lero yabwera ndikumati Joshua anali oipa. Iyi ndi ntchito ya satana mdyerekezi,” watero Shammah Vocals | koma lero yabwera ndikumati Joshuwa anali oipa. Iyi ndi ntchito ya satana mdyerekezi, watelo shama vokozi | Female | |
Mkumano wa makhansala ku zomba walepheleka chifukwa cha chisokonezo | Mkumano wa makhansala ku zomba walepheleka chifukwa cha chisokonezo | Female | |
Mkumano wa nambala 19 wama Khansala komanso wa Phungu yekhayo wamu mzinda wa Zomba omwe pachingerezi umatchedwa Full Council walephereka chifukwa chachisokonedzo chomwe chidabuka munyumbayi | Mkumano wa nambala naintini wama Khansala komanso wa Phungu yekhayo wamu mzinda wa Zomba omwe pachingerezi umatchedwa fu khanso walephereka chifukwa chachisokonedzo chomwe chidabuka munyumbayi | Female | |
Makhansala achipani cha DPP komanso Phungu wachipani cha DPP Bester Awali adafunsa Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde | Makhansala achipani cha Dipipi komanso Phungu wachipani cha Dipipi Besita Awali adafunsa Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Devi Maunde | Female | |
kuti ndichifikwa chiyani adalepheretsa mkumano womwe umayenera kuchitika Lachisanu pa 2 February Poyankhulapo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde adakumbutsa nyumbayi | Khansala Devi Maunde kuti ndichifikwa chiyani adalepheretsa mkumano womwe umayenera kuchitika Lachisanu pa thu febuluwale Poyankhulapo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba adakumbutsa nyumbayi | Female | |
kuti zomwe akunena makhansalawo ndizotsamveka chifukwa nkhaniyi adayikambirana kale pa gulupu yawo lapa Whatsapp lomwe makhansala ochuluka adamvomereza kuti mkumanowo uchitike Lolemba pa 5 February | kuti zomwe akunena makhansalawo ndizotsamveka chifukwa nkhaniyi adayikambirana kale pa gulupu yawo lapa Watsapu lomwe makhansala ochuluka adamvomereza kuti mkumanowo uchitike Lolemba pa faifi febuluwale | Female | |
Ndipo chifukwa chakusamvana komanso kulodzana dzala komwe kudabuka pakati pawo, Mfumuyi idalamula kuti mkumanowo ulephereke mpaka mtsogolo muno | Ndipo chifukwa chakusamvana komanso kulodzana dzala komwe kudabuka pakati pawo, Mfumuyi idalamula kuti mkumanowo ulephereke mpaka mtsogolo muno | Female | |
Pamenepa Khansala Davie Maunde wadzudzula makhansala komanso phunguyu chifukwa choyambitsa chisokonezo zomwe zapangitsa kuti zokambiranazi zilephereke | Pamenepa Khansala Devi Maunde wadzudzula makhansala komanso phunguyu chifukwa choyambitsa chisokonezo zomwe zapangitsa kuti zokambiranazi zilephereke | Female | |
Phungu wa Zomba Malosa wagona ku ma ofesi a Works Training Center kufuna chimanga. Phungu wa mdera la Zomba Malosa Grace Kwelepeta wagona kuma ofesi a Zomba Training Center | Phungu wa Zomba Malosa wagona ku ma ofesi a wekisi thilening’I senta kufuna chimanga. Phungu wa mdera la Zomba Malosa Gilesi Kwelepeta wagona kuma ofesi a Zomba Thilening’I senta | Female | |
kufuna kukakamiza galimoto yayikulu yomwe yanyamula chimanga chogawira anthu mwaulele omwe akuvutika ndi njala kuti ipite mdera lake | kufuna kukakamiza galimoto yayikulu yomwe yanyamula chimanga chogawira anthu mwaulele omwe akuvutika ndi njala kuti ipite mdera lake | Female | |
Kwelepeta wauza Malawi24 kuti chiyambireni Boma kugawira anthu chimanga mu mwezi wa October chaka chatha anthu a mdera lake alandira kamodzi kokha ndipo wati ndidzokhumudwitsa | Kwelepeta wauza Malawi twente folo kuti chiyambireni Boma kugawira anthu chimanga mu mwezi wa Okotoba chaka chatha anthu a mdera lake alandira kamodzi kokha ndipo wati ndidzokhumudwitsa | Female | |
popeza madera ena aphungu alandira kambiri mbiri. Iye wati mdera lake la Zomba Malosa anthu akugona ndi njala | popeza madera ena aphungu alandira kambiri mbiri. Iye wati mdera lake la Zomba Malosa anthu akugona ndi njala | Female | |
chifukwa chosowa chakudya ndipo wati ali ndi nkhawa popedza ntchito yogawa chimanga chawulere yomwe Boma lidakhadzikitsa itha mwezi wamawa wa February | chifukwa chosowa chakudya ndipo wati ali ndi nkhawa popedza ntchito yogawa chimanga chawulere yomwe Boma lidakhadzikitsa itha mwezi wamawa wa Febuluwale | Female | |
zomwe zikusonyedza kuti anthu amdera lake apitilirabe kuvutika ndi njala komanso sapindura ndi ntchitoyi. Atafunsidwa ngati Bwanamkubwa wa boma la Zomba akudziwa zankhaniyi | zomwe zikusonyedza kuti anthu amdera lake apitilirabe kuvutika ndi njala komanso sapindura ndi ntchitoyi. Atafunsidwa ngati Bwanamkubwa wa boma la Zomba akudziwa zankhaniyi | Female | |
Kwelepeta adati wakhala akupita ku Office ya Bwanamkubwayu kukapereka madandaulo amomwe chimanga chikagawidwira koma sizikuthandidza kanthu | Kwelepeta adati wakhala akupita ku Ofesi ya Bwanamkubwayu kukapereka madandaulo amomwe chimanga chikagawidwira koma sizikuthandidza kanthu | Female | |
Mdera langa anthu amagonera mango chifukwa chosowa chimanga koma tsopano poti mango atha ayamba kugona osadya moti ana ambiri sakupita kusukulu chifukwa chosowa chokudya | Mdera langa anthu amagonera mango chifukwa chosowa chimanga koma tsopano poti mango atha ayamba kugona osadya moti ana ambiri sakupita kusukulu chifukwa chosowa chokudya | Female | |
ndiye ndipemphe Boma kuti atithandidze ndi chimanga, adayankhula motero Grace Kwelepeta | ndiye ndipemphe Boma kuti atithandidze ndi chimanga, adayankhula motero Gilesi Kwelepeta | Female | |
Pamenepa Phunguyu wapempha mabungwe, makampani komanso anthu akufuna kwabwino kuti athandidze anthu amdera la Zomba Malosa ndi chokudya popedza mdera lake lidakhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy | Pamenepa Phunguyu wapempha mabungwe, makampani komanso anthu akufuna kwabwino kuti athandidze anthu amdera la Zomba Malosa ndi chokudya popedza mdera lake lidakhudzidwa ndi Namondwe wa Fulede | Female | |
Boma lidakhazikitsa ntchito yogawa chimanga chaulere kwa anthu omwe alibe chokudya mwezi wa October chaka chatha ndipo ntchitoyi ikuyembekedzereka kutha mwezi wa February chaka chino | Boma lidakhazikitsa ntchito yogawa chimanga chaulere kwa anthu omwe alibe chokudya mwezi wa Okotoba chaka chatha ndipo ntchitoyi ikuyembekedzereka kutha mwezi wa Febuluwale chaka chino | Female | |
Ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi, abambo awiri ali m’manja mwa apolisi kamba kakupha bambo wina yemwe akuti anamugwira akufuna kugwililira mayi yemwe anali nyumba yake usiku | Ku Monkibe m’boma la Mangochi, abambo awiri ali m’manja mwa apolisi kamba kakupha bambo wina yemwe akuti anamugwira akufuna kugwililira mayi yemwe anali nyumba yake usiku | Female | |
Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Monkey Bay, Sergeant Alice Sichali omwe azindikira abambo awiriwa ngati a Oscar Lungwa a zaka 34 | Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Monkibe, Sajentiergeant Alisi Sichali omwe azindikira abambo awiriwa ngati a Osika Lungwa a zaka fetefolo | Female | |
komaso a Uladi Frank a zaka 25 omwe akuganizilidwa kupha a Ishmael Makiyi azaka 32 | komaso a Uladi Fulanki a zaka twente faifi omwe akuganizilidwa kupha a Ishumaeli Makiyi azaka fete thu | Female | |
Malingana ndi a Sichali, usiku wa Lachinayi sabata imene ikungothayi pa 11 January, 2024 oganizilidwa awiri, anakumanizana ndi a Mikiyi pa malo ena otchedwa Lake Service Beach | Malingana ndi a Sichali, usiku wa Lachinayi sabata imene ikungothayi pa leveni Januwale Twente twente folo oganizilidwa awiri, anakumanizana ndi a Mikiyi pa malo ena otchedwa Leki sevisi bitchi | Female | |
omwe ali mphepete mwa nyanja ya Malawi ku Monkey Bay komweko. Pa nthawiyi, a Makiyi akuti anali atalowa munchisakasa momwe ankafuna kugwililira mayi wina yemwe pa nthawiyi anali akugona | omwe ali mphepete mwa nyanja ya Malawi ku Monkibe komweko. Pa nthawiyi, a Makiyi akuti anali atalowa munchisakasa momwe ankafuna kugwililira mayi wina yemwe pa nthawiyi anali akugona | Female | |
A Lungwa komaso a Frank anafika pa chisakasachi atava kufuwula kopempha thandizo kwa mayiyo ndipo awiriwa atafika anapezadi a Makiyi ali jijili jijili | A Lungwa komaso a Fulanki anafika pa chisakasachi atava kufuwula kopempha thandizo kwa mayiyo ndipo awiriwa atafika anapezadi a Makiyi ali jijili jijili | Female | |
ndipo kenaka anayamba kuwamenya. Awiriwi anavulaza bambo Makiyi ndi zibonyongo mpaka mkuluyu anali thapsya, zomwe zinachititsa kakasi oganizilidwa awiriwa | ndipo kenaka anayamba kuwamenya. Awiriwi anavulaza bambo Makiyi ndi zibonyongo mpaka mkuluyu anali thapsya, zomwe zinachititsa kakasi oganizilidwa awiriwa | Female | |
ndipo posakhalitsa ananyamula bambo oganizilidwa kufuna kugwililirayo ndikukamuponya pa tchire lina ali chikomokele | ndipo posakhalitsa ananyamula bambo oganizilidwa kufuna kugwililirayo ndikukamuponya pa tchire lina ali chikomokele | Female | |
Nkhaniyi inakasiyidwa m’manja mwa a polisi kuderako omwe anathamangira kumaloko ndikukatenga bambo Makiyi kupita nawo ku chipatala chaching’omo komweko ndipo kenaka anatumizidwa ku chipatala chachikulu cha Mangochi | Nkhaniyi inakasiyidwa m’manja mwa a polisi kuderako omwe anathamangira kumaloko ndikukatenga bambo Makiyi kupita nawo ku chipatala chaching’omo komweko ndipo kenaka anatumizidwa ku chipatala chachikulu cha Mangochi | Female | |
Apolisi ati bambo Makiyi analengezedwa kuti amwalira atangofika nawo pa chipatala cha Mangochi zomwe zinapangitsa kuti apolisi ayambe kusakasaka anthu omwe achita chipomgwechi | Apolisi ati bambo Makiyi analengezedwa kuti amwalira atangofika nawo pa chipatala cha Mangochi zomwe zinapangitsa kuti apolisi ayambe kusakasaka anthu omwe achita chipomgwechi | Female | |
ndipo pamapeto pake a Lungwa ndi a Frank anamangidwa. Awiriwa omwe amachokera kudera la mfumu yaikulu Nankumba | ndipo pamapeto pake a Lungwa ndi a Frulanki anamangidwa. Awiriwa omwe amachokera kudera la mfumu yaikulu Nankumba | Female | |
akuyembekezeka kukaonekera ku khothi posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakupha munthu. Ofuna kuyimira pa mpando wa khansala wamanga nyumba ya mlangizi ku Nkhata Bay | akuyembekezeka kukaonekera ku khothi posachedwapa kuti akayankhe mlandu wakupha munthu. Ofuna kuyimira pa mpando wa khansala wamanga nyumba ya mlangizi ku Nkhatabe | Female | |
Mfumu Chawola ya dera la Kangoi yomwe ili pansi pa Mfumu ya yikulu Timbiri M’boma la Nkhata Bay yati iyo limodzi ndi anthu awo ndiwokondwa kuti tsopano ntchito za umoyo | Mfumu Chawola ya dera la Kangoi yomwe ili pansi pa Mfumu ya yikulu Timbiri M’boma la Nkhatabe yati iyo limodzi ndi anthu awo ndiwokondwa kuti tsopano ntchito za umoyo | Female | |
pa chipatala chaching’ono cha Kangoi ziyamba kuyenda bwino. Mfumuyi yanena izi pomwe Bambo Lloyd Ndhlozi omwe akufuna kuzapikisana pa mpando wa ukhansala ku wadi ya Mwambazi | pa chipatala chaching’ono cha Kangoi ziyamba kuyenda bwino. Mfumuyi yanena izi pomwe Bambo Loyidi Zyozi omwe akufuna kuzapikisana pa mpando wa ukhansala ku wadi ya Mwambazi | Female | |
amanga nyumba ya mlangizi wa zaumoyo pa Chipatalachi, chomwe chakhala zaka zambiri popanda mlangizi waza umoyo | amanga nyumba ya mlangizi wa zaumoyo pa Chipatalachi, chomwe chakhala zaka zambiri popanda mlangizi waza umoyo | Female | |
Ndine wokondwa kwambiri kuti tsopano tikhala ndi mulangizi waza umoyo pa kiliniki yathu, yomwe yakhala nthawi yayitali popanda mulangizi komanso kamba ka vuto lakusoweka kwanyumba yokhalamo | Ndine wokondwa kwambiri kuti tsopano tikhala ndi mulangizi waza umoyo pa kiliniki yathu, yomwe yakhala nthawi yayitali popanda mulangizi komanso kamba ka vuto lakusoweka kwanyumba yokhalamo | Female | |
koma pano ndi nyumba yomwe a shado khansala bambo Lloyd Ndhlozi atimangira vuto lakusowa kwa mulangizi waza umoyo kudera langa ili likhala mbiri yakale, adatero a Mfumu Chiwola | koma pano ndi nyumba yomwe a shado khansala bambo Loyidi Zyozi atimangira vuto lakusowa kwa mulangizi waza umoyo kudera langa ili likhala mbiri yakale, adatero a Mfumu Chiwola | Female | |
adatero a Mfumu Chiwola Bambo James Chioni Chimphoyo omwe ndi wapampando wa komiti ya Chipatalachi awuza Malawi24 | adatero a Mfumu Chiwola Bambo Jemusi Chioni Chimphoyo omwe ndi wapampando wa komiti ya Chipatalachi awuza Malawi twente folo | Female | |
kuti kumangidwa kwa nyumbayi pa chipatalachi kwathetsa mavuto omwe mlangizi amakumana nawo maka kumayenda mtunda wawutali kuchokera ku Chikwina | kuti kumangidwa kwa nyumbayi pa chipatalachi kwathetsa mavuto omwe mlangizi amakumana nawo maka kumayenda mtunda wawutali kuchokera ku Chikwina | Female | |
ndipo nthawi zina amafika mochedwa kamba kamayendedwe. Tithokoze ofesi ya za umoyo ya Nkhata Bay yomwe ya titumizira mulangizi waza umoyo | ndipo nthawi zina amafika mochedwa kamba kamayendedwe. Tithokoze ofesi ya za umoyo ya Nkhatabe yomwe ya titumizira mulangizi waza umoyo | Female | |
Amai a dera lathu amayenda mtunda wautali kukafuna thandizo koma pano anthu azithandizikira pafupi” Anatero a Chimphoyo | Amai a dera lathu amayenda mtunda wautali kukafuna thandizo koma pano anthu azithandizikira pafupi” Anatero a Chimphoyo | Female | |
M’mau awo bambo, Lloyd Ndhlozi ati anthu okhala mdera la Mwambazi mwambazi wadi akukumana ndi mavuto ambiri | M’mau awo bambo, Loyidi Zyozi ati anthu okhala mdera la Mwambazi mwambazi wadi akukumana ndi mavuto ambiri | Female | |
koma ati anaganiza kuti akonze kaye vuto lakusowa kwa mlangizi wa zaumoyo kudera la Kangoi pomanga nyumba yokhalamo mlangiziyo | koma ati anaganiza kuti akonze kaye vuto lakusowa kwa mlangizi wa zaumoyo kudera la Kangoi pomanga nyumba yokhalamo mlangiziyo | Female | |
Angakhale kuti derali kuli mavuto osiyana siyana koma ndinaona kuti ndiyambe kaye ndathetsa vuto la kusoweka kwa mlangizi wa za umoyo | Angakhale kuti derali kuli mavuto osiyana siyana koma ndinaona kuti ndiyambe kaye ndathetsa vuto la kusoweka kwa mlangizi wa za umoyo | Female | |
pomanga nyumba pa Chipatala Chaching’ono cha Kangoi. Ndine wokondwa kuti ntchitoyi yayenda bwino ndipo pano tikuyika malata, posachedwapa nyumbayi mlangiziyi alowamo, anatero a Ndhlozi | pomanga nyumba pa Chipatala Chaching’ono cha Kangoi. Ndine wokondwa kuti ntchitoyi yayenda bwino ndipo pano tikuyika malata, posachedwapa nyumbayi mlangiziyi alowamo, anatero a Zyozi | Female | |
Iwo alimbikisanso anthu akuderali kuti apitilize kutengapo gawo pa nkhani za chitukuko zomwe zikubwera kuderali | Iwo alimbikisanso anthu akuderali kuti apitilize kutengapo gawo pa nkhani za chitukuko zomwe zikubwera kuderali | Female | |
Ndhlozi ati kusiyana kwa zipani zomwe akutsatira kuderali kusawagawanitse pankhani yotengapo mbali pa chitukuko | Ndhlozi ati kusiyana kwa zipani zomwe akutsatira kuderali kusawagawanitse pankhani yotengapo mbali pa chitukuko | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.