audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Malingana ndi m'neneri wa nthambi ya ndende m'dziko muno, a Chimwemwe Shaba, a Suluma anawagwira ndi ma simu kadi 99 omwe anawabitsa m'mafuta odzola pa 12 December chaka chatha | Malingana ndi m'neneri wa nthambi ya ndende m'dziko muno, a Chimwemwe Shawa, a Suluma anawagwira ndi ma simu kadi nainte naini omwe anawabitsa m'mafuta odzola pa thwelofu Disemba chaka chatha | Female | |
Bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate ku Mangochi lati mulandu wa a Bon Kalindo udzazengedwanso pa 9 February 2024 | Bwalo la milandu la Siniyo lezidenti majesitileti ku Mangochi lati mulandu wa a Boni Kalindo udzazengedwanso pa naini febuluwale twente twente folo | Female | |
Bwaloli lati patsikuli lidzagamula ngati a Kalindo ali ndi mlandu woti ayankhe kapena ayi pachisokonezo chomwe chinachitika m'boma la Mangochi kaamba kachionetsero chomwe anatsogolera a Kalindo | Bwaloli lati patsikuli lidzagamula ngati a Kalindo ali ndi mlandu woti ayankhe kapena ayi pachisokonezo chomwe chinachitika m'boma la Mangochi kaamba kachionetsero chomwe anatsogolera a Kalindo | Female | |
pa 30 November chaka chatha. Izi zadziwika mboni zonse zinayi zaboma zitamaliza kuperekera umboni wawo | pa fete novemba chaka chatha. Izi zadziwika mboni zonse zinayi zaboma zitamaliza kuperekera umboni wawo | Female | |
Pakadali pano, bwaloli likuyembekezera kulandira maumboni olembedwa kuchokera kumbali zonse ziwiri pa mlanduwu | Pakadali pano, bwaloli likuyembekezera kulandira maumboni olembedwa kuchokera kumbali zonse ziwiri pa mlanduwu | Female | |
Katswiri wa mayimbidwe Zeze Kingston yemwe ndi m'modzi wa asangalatsi omwe anasankhidwa ndi anthu pa mwambo wa MBC Entertainers of the Year wa chaka cha 2023 | Katswiri wa mayimbidwe Zeze King’isitoni yemwe ndi m'modzi wa asangalatsi omwe anasankhidwa ndi anthu pa mwambo wa Emubisi intatenazi ofu ve iye wa chaka cha twente twente fili | Female | |
walandira mphoto zake kuchokera ku Hifi-Electronics. Katswiriyu walandira zinkuza mawu microphone ziwiri komanso ma gitala awiri | walandira mphoto zake kuchokera ku Haifai-Elekithilonikisi. Katswiriyu walandira zinkuza mawu maikulofoni ziwiri komanso ma gitala awiri | Female | |
Katswiriyu anasankhidwa kukhala oyimba yemwe wachita bwino komanso nyimbo yake ya Kusangalala inasankhidwa kukhala nyimbo yomwe yasangalatsa anthu mchaka cha 2023 | Katswiriyu anasankhidwa kukhala oyimba yemwe wachita bwino komanso nyimbo yake ya Kusangalala inasankhidwa kukhala nyimbo yomwe yasangalatsa anthu mchaka cha twente twente fili | Female | |
Bungwe la Malawi Red Cross Society lapereka nyumba zatsopano zisanu ndi ziwiri kwa anthu omwe anapulumuka pa Namondwe Freddy m’boma la Phalombe | Bungwe la Malawi Redi khulosi sosayate lapereka nyumba zatsopano zisanu ndi ziwiri kwa anthu omwe anapulumuka pa Namondwe Fulede m’boma la Phalombe | Female | |
Nyumbazi zamangidwa ndi ndalama zokwana K50 miliyoni zomwe zinaperekedwa ndi bungwe la Big Win kutsatira pempho la bungwe la bungwe la Joyce Banda Foundation | Nyumbazi zamangidwa ndi ndalama zokwana fifite miliyoni kwacha zomwe zinaperekedwa ndi bungwe la Bigi Wini kutsatira pempho la bungwe la bungwe la Joisi Banda Faundeshoni | Female | |
A Edith Akridge omwe ndi mkulu oyendetsa ntchito za Joyce Banda Foundation wati ndalamazi zinaperekedwa kudzera ku bungweli | A Edifi Akiliji omwe ndi mkulu oyendetsa ntchito za Joisi Banda Faundeshoni wati ndalamazi zinaperekedwa kudzera ku bungweli | Female | |
Mfumu Malima yayamikira chitukukochi ndipo yalimbikitsa ena akufuna kwabwino kuchitanso chimodzimodzi | Mfumu Malima yayamikira chitukukochi ndipo yalimbikitsa ena akufuna kwabwino kuchitanso chimodzimodzi | Female | |
Chaka chatha, atsogoleri opuma a dziko lino Dr Bakili Muluzi komanso Dr Joyce Banda anapereka nyumba zokwana 45 ndipo nyumba zatsopanozi zonse zakwana 52 | Chaka chatha, atsogoleri opuma a dziko lino Dokota Bakili Muluzi komanso Dokota Joisi Banda anapereka nyumba zokwana fotefaifi ndipo nyumba zatsopanozi zonse zakwana fifitethu | Female | |
Nyumba zonsezi zili m'boma la Phalombe. Apolisi ati alimbikitsa ntchito yothana ndi mbava zonse zomwe zikusowetsa anthu mtendere mmadera osiyanasiyana | Nyumba zonsezi zili m’boma la Phalombe. Apolisi ati alimbikitsa ntchito yothana ndi mbava zonse zomwe zikusowetsa anthu mtendere mmadera osiyanasiyana | Female | |
Apolisiwa anena izi pamene posachedwapa amanga Alex Tembo, wazaka 33, kwa Jenda ku Mzimba yemwe anathyola sitolo ndicholinga choti abe | Apolisiwa anena izi pamene posachedwapa amanga Alekisi Tembo, wazaka fetefili, kwa Jenda ku Mzimba yemwe anathyola sitolo ndicholinga choti abe | Female | |
Mneneri wapolisi kwa Jenda, a Macfarlen Mseteka, ati mbavayo inalowa msitolo ina kuti ibe ndipo mkulu yemwe amalondera sitoloyo anadabwa atamva phokoso mkati mwa sitoloyo | Mneneri wapolisi kwa Jenda, a Makifaleni Mseteka, ati mbavayo inalowa msitolo ina kuti ibe ndipo mkulu yemwe amalondera sitoloyo anadabwa atamva phokoso mkati mwa sitoloyo | Female | |
Kenako anaitana apolisi ndipo mbavayo itadziwa kuti apolisi afika pamalopo, inaganiza zothawa podzera pa denga pomwe inalowera | Kenako anaitana apolisi ndipo mbavayo itadziwa kuti apolisi afika pamalopo, inaganiza zothawa podzera pa denga pomwe inalowera | Female | |
Apolisiwo atamuwona, anaphulitsa utsi wokhetsa msozi ndipo anabwelera mkati mwasitolomo kenako apolisiwo anamugwira | Apolisiwo atamuwona, anaphulitsa utsi wokhetsa msozi ndipo anabwelera mkati mwasitolomo kenako apolisiwo anamugwira | Female | |
Atamufufuza, anamupeza ndi ndalama pafupifupi K630,000 zomwe anaba musitoloyo. Tembo amachokera mmudzi wa Thom Mfumu yaikulu Chisemphere m'boma la Kasungu | Atamufufuza, anamupeza ndi ndalama pafupifupi sikisi handede andi fete sauzande kwacha zomwe anaba musitoloyo. Tembo amachokera mmudzi wa Thomu Mfumu yaikulu Chisemphere m'boma la Kasungu | Female | |
Lamulo la za ngozi zadzidzidzi lanunkhira. Lamulo lounika za ngozi zogwa mwadzidzidzi latsala pang’ono kupsa | Lamulo la za ngozi zadzidzidzi lanunkhira. Lamulo lounika za ngozi zogwa mwadzidzidzi latsala pang’ono kupsa | Female | |
malingana ndi zomwe mkulu woyang’anira zopanga malamulo ku unduna wa za malamulo a Amam Mussa anena | malingana ndi zomwe mkulu woyang’anira zopanga malamulo ku unduna wa za malamulo a Amamu Musa anena | Female | |
Mwa zina, lamulo latsopanolo lidzakonza ndondomeko yokonzekera bwino ngozi za dzidzidzi mmalo mongokamba zoyenera kuchita ngozizo zikachitika | Mwa zina, lamulo latsopanolo lidzakonza ndondomeko yokonzekera bwino ngozi za dzidzidzi mmalo mongokamba zoyenera kuchita ngozizo zikachitika | Female | |
Katundu wambiri adakokoloka ndi namondwe wotchedwa Freddy. A Mussa amapereka tsatanetsatane wa momwe ntchito yophika lamulolo ikuyendera ku komiti yoona za za chilengedwe | Katundu wambiri adakokoloka ndi namondwe wotchedwa Fulede. A Musa amapereka tsatanetsatane wa momwe ntchito yophika lamulolo ikuyendera ku komiti yoona za za chilengedwe | Female | |
Tikupanga zotheka kuti Bilu ya lamulolo ipite ku Nyumba ya Malamulo mkumano omwe uli mkatiwu potsatira zomwe adalonjeza a Pulezidenti a Lazarus Chakwera kuti lamulolo litheka | Tikupanga zotheka kuti Bilu ya lamulolo ipite ku Nyumba ya Malamulo mkumano omwe uli mkatiwu potsatira zomwe adalonjeza a Pulezidenti a Lazalasi Chakwera kuti lamulolo litheka | Female | |
adatero a Mussa, Komitiyo komanso mabungwe achilimika kufuna lamulolo litakhazikitsidwa potsatira ngozi ya Namondwe wa Freddy yemwe adaononga m’maboma a m’chigawo cha kummwera | adatero a Musa, Komitiyo komanso mabungwe achilimika kufuna lamulolo litakhazikitsidwa potsatira ngozi ya Namondwe wa Fulede yemwe adaononga m’maboma a m’chigawo cha kummwera | Female | |
Wachiwiri kwa mkulu woyang’anira za ngozi zogwa mwadzidzidzi a Fyaupie Mwafongo ati lamulo lomwe likugwira ntchito pano ndilopelewera muzina chifukwa limangokamba zoyenera kutsatidwa ngozi ikagwa | Wachiwiri kwa mkulu woyang’anira za ngozi zogwa mwadzidzidzi a Fyaupi Mwafongo ati lamulo lomwe likugwira ntchito pano ndilopelewera muzina chifukwa limangokamba zoyenera kutsatidwa ngozi ikagwa | Female | |
Tikufuna lamulo lomwe lizifotokoza ndondomeko yoyenera kutsata popewa ngozizo zisadagwe nkomwe. Timaononga ndalama zochuluka ngozi zikagwa | Tikufuna lamulo lomwe lizifotokoza ndondomeko yoyenera kutsata popewa ngozizo zisadagwe nkomwe. Timaononga ndalama zochuluka ngozi zikagwa | Female | |
koma titha kuchepetsa ndalamazo popewa ngozizo zisadagwe, atero a Mwafongo. Iwo ati lamulo latsopanolo lizidzapereka mphamvu ku boma zoti litha kuthamangitsa anthu m’madera | koma titha kuchepetsa ndalamazo popewa ngozizo zisadagwe, atero a Mwafongo. Iwo ati lamulo latsopanolo lizidzapereka mphamvu ku boma zoti litha kuthamangitsa anthu m’madera | Female | |
momwe likuona kuti mutha kugwa ngozi ndipo likhoza kupereka chilango kwa anthu ozengereza. M’madera ambiri a m’dziko muno anthu adamanga m’mapiri ndi m’mitsinje | momwe likuona kuti mutha kugwa ngozi ndipo likhoza kupereka chilango kwa anthu ozengereza. M’madera ambiri a m’dziko muno anthu adamanga m’mapiri ndi m’mitsinje | Female | |
koma a Mwafongo ati kumakhala kovuta kuwasuntha m’malomo chifukwa palibe lamulo lomwe limatsindika za komwe anthu angamange n’kukhazikika. Mchitidwe umenewu wameta mapiri | koma a Mwafongo ati kumakhala kovuta kuwasuntha m’malomo chifukwa palibe lamulo lomwe limatsindika za komwe anthu angamange n’kukhazikika. Mchitidwe umenewu wameta mapiri | Female | |
nchifukwa chake madzi ankati aphulike akumabwera ndi mphamvu nkumaononga choncho lamulo lomwe likubwera lidzidzaunikira zonsezi, atero a Mwafongo | nchifukwa chake madzi ankati aphulike akumabwera ndi mphamvu nkumaononga choncho lamulo lomwe likubwera lidzidzaunikira zonsezi, atero a Mwafongo | Female | |
Woyendetsa mapulogalamu ku bungwe lomangira anthu nyumba la Habitat for Humanity a Lucy Mwale ati mchitidwe wolekelera anthu kumanga mmalo osayenera ukuwonjezera umphawi wa nyumba | Woyendetsa mapulogalamu ku bungwe lomangira anthu nyumba la Habitati fo Hyumanite a Luse Mwale ati mchitidwe wolekelera anthu kumanga mmalo osayenera ukuwonjezera umphawi wa nyumba | Female | |
Iwo ati anthu 75 mwa anthu 100 aliwonse amakhala mnyumba zosalongosoka ndipo izi zimayika miyoyo ndi katundu wawo pachiwopsezo | Iwo ati anthu sevente faifi mwa anthu wani handede aliwonse amakhala mnyumba zosalongosoka ndipo izi zimayika miyoyo ndi katundu wawo pachiwopsezo | Female | |
Panopa timayenera kuti tizimanga nyumba 25 000 chaka chilichonse kwa zaka 10 kuti mavuto anyumba achepe ndiye mukawona sintchito yamasewera ayi | Panopa timayenera kuti tizimanga nyumba twentefaifi sauzande chaka chilichonse kwa zaka teni kuti mavuto anyumba achepe ndiye mukawona sintchito yamasewera ayi | Female | |
chifukwa pakufunika ndalama zambiri, atero a Mwale. Wapampando wa mgwirizano wamabungwe owona zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a Julias Ng’oma | chifukwa pakufunika ndalama zambiri, atero a Mwale. Wapampando wa mgwirizano wamabungwe owona zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a Juliyasi Ng’oma | Female | |
ati Bilu yomwe ikubwerayi ikadabwera kalekale, ngozi zina zomwe zagwa mdziko muno pakatipa sizikadawononga ngati momwe zidachitira Lamulolo linkayenera kukhala litapsa mchaka cha 2017 | ati Bilu yomwe ikubwerayi ikadabwera kalekale, ngozi zina zomwe zagwa mdziko muno pakatipa sizikadawononga ngati momwe zidachitira Lamulolo linkayenera kukhala litapsa mchaka cha twente seventini | Female | |
ndipo bwenzi latithandiza kupewa ngozi zina zomwe zidatigwera. Lamulolo likuyembekeza kudzasintha momwe timachitira zinthu zina zokhudza chilengedwe, atero a Ng’oma | ndipo bwenzi latithandiza kupewa ngozi zina zomwe zidatigwera. Lamulolo likuyembekeza kudzasintha momwe timachitira zinthu zina zokhudza chilengedwe, atero a Ng’oma | Female | |
Wachiwiri kwa wapampando wa komiti yowona za zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a George Katunga Miliyoni adati Nyumba ya Malamulo ikungodikira biluyo kuti akayipange kukhala lamulo | Wachiwiri kwa wapampando wa komiti yowona za zachilengedwe ndikusintha kwa nyengo a Joji Katunga Miliyoni adati Nyumba ya Malamulo ikungodikira biluyo kuti akayipange kukhala lamulo | Female | |
Panopa dziko lonse lili nchiyembekezo chachikulu mu Bilu imeneyi ndiye tikungodikira kuti itipeze kunyumba ya Malamuloyo atikayipange kukhala lamulo, atero a Miliyoni | Panopa dziko lonse lili nchiyembekezo chachikulu mu Bilu imeneyi ndiye tikungodikira kuti itipeze kunyumba ya Malamuloyo atikayipange kukhala lamulo, atero a Miliyoni | Female | |
Iwo ati omwe akupanga lamulolo akuyenera kuchita machawi kuti aphungu akamadzatseka mkumano wa bajeti ya 2023/2024, biluyo idzakhala itadutsa ku Nyumbayo | Iwo ati omwe akupanga lamulolo akuyenera kuchita machawi kuti aphungu akamadzatseka mkumano wa bajeti ya twente twente fili/ twente twente folo, biluyo idzakhala itadutsa ku Nyumbayo | Female | |
Nyuzipepala zikuluzikulu za ku Mangalande Lachisanu zidadzala ndi nkhani ya bambo wina wa ku Malawi amene akumuganizira kuti adabaya ndi kupha mkazi wake ku Northampton | Nyuzipepala zikuluzikulu za ku Mangalande Lachisanu zidadzala ndi nkhani ya bambo wina wa ku Malawi amene akumuganizira kuti adabaya ndi kupha mkazi wake ku Nofihamputoni | Female | |
Nkhani yoti Phillip Dafter, wa zaka 32, adabaya mkazi wake Diana wa zaka 36 ka 17 atasemphana m’banja, idayala nthenje m’nyuzipepala zazikulu ku UK | Nkhani yoti filipi dafuta, wa zaka fetethu, adabaya mkazi wake Dayana wa zaka fetesikisi ka seventini atasemphana m’banja, idayala nthenje m’nyuzipepala zazikulu ku yukeyi | Female | |
monga The Sun, Daily Mail ndi The Telegraph. Dafter akumuganizira kuti adapha mkazi wakeyo mu October chaka chatha. Mlanduwo ukuzengedwa kubwalo la Northampton Crown Court | monga ve sani, Deile melo ndi Ve telegilafu. Dafuta akumuganizira kuti adapha mkazi wakeyo mu Okotoba chaka chatha. Mlanduwo ukuzengedwa kubwalo la Nofihamputoni kilawoni khoti | Female | |
momwe zidamveka kuti awiriwo adakumana ku UK komweko ndipo adayamba kukhalira limodzi monga banja Nyuzipepa ya The Sun | momwe zidamveka kuti awiriwo adakumana ku Yukeyi komweko ndipo adayamba kukhalira limodzi monga banja Nyuzipepa ya Ve sani | Female | |
idati wozenga milandu a Gordon Aspen adati ngakhale zinkaoneka kunjaku kuti banjalo lili pa mtambasale, zinthu sizimayenda. Palibe amene amazindikira kuti zinthu zidasololobana | idati wozenga milandu a Godoni asipeni adati ngakhale zinkaoneka kunjaku kuti banjalo lili pa mtambasale, zinthu sizimayenda. Palibe amene amazindikira kuti zinthu zidasololobana | Female | |
Koma pakati pa awiriwo zinthu sizimayenda, iwo adauza bwalo. Malinga ndi Daily Mail, awiriwo adakangana pa nkhani zokhudza msonkho wa galimoto yawo | Koma pakati pa awiriwo zinthu sizimayenda, iwo adauza bwalo. Malinga ndi Deile melo , awiriwo adakangana pa nkhani zokhudza msonkho wa galimoto yawo | Female | |
komanso kuti Phillip amatumizirana mauthenga a Chikondi ndi mkazi wina yemwe anali ku Malawi kuno. Makamera a CCTV adatola kanema wa iye akukagula mipeni ya kukitchini m’sitolo ina | komanso kuti Filipi amatumizirana mauthenga a Chikondi ndi mkazi wina yemwe anali ku Malawi kuno. Makamera a sisitivi adatola kanema wa iye akukagula mipeni ya kukitchini m’sitolo ina | Female | |
Adabwerera kunyumba ndipo atalasa mkaziyo ka 17, iye adamwa mowa wa whisky n’kudzibaya pamimba. Apa adapita kukakwera sitima ulendo wa ku Euston kumene adagwidwa | Adabwerera kunyumba ndipo atalasa mkaziyo ka seventini, iye adamwa mowa wa wisike n’kudzibaya pamimba. Apa adapita kukakwera sitima ulendo wa ku yusitoni kumene adagwidwa | Female | |
idatero nyuzipepalayo. Iyo idapitiriza kunena kuti asanakwere sitimayo adauza wogulitsa matikiti kuti: Ndine munthu woipitsitsa | idatero nyuzipepalayo. Iyo idapitiriza kunena kuti asanakwere sitimayo adauza wogulitsa matikiti kuti: Ndine munthu woipitsitsa | Female | |
Ndipo ali m’sitimayo adatumiza uthenga pagulu lina la WhatsApp pomwe adati, Boys and D. Ndikupita kundende, ndapha Diana Dafter lero | Ndipo ali m’sitimayo adatumiza uthenga pagulu lina la Watsapu pomwe adati, Boizi andi Di. Ndikupita kundende, ndapha Dayana Dafuta lero | Female | |
Phillip, yemwe adali msilikali wa nkhondo wa dziko la Britain asadapume n’kukhala woyendetsa basi. Iye adamenyapo nkhondo ku Afghanstan kumene ena amadwala matenda a kuganiza akabwerako | Filipi, yemwe adali msilikali wa nkhondo wa dziko la Buliteni asadapume n’kukhala woyendetsa basi. Iye adamenyapo nkhondo ku Afuganisitani kumene ena amadwala matenda a kuganiza akabwerako | Female | |
Iye akukana kuti adapha munthu mwadala, koma zidachitika mwa ngozi. Umboni wa a nyumba zoyandikira komanso komwe Phillip adakagula mipeni udaonetsa kuti patsiku Lachisanu limene izi zidachitika | Iye akukana kuti adapha munthu mwadala, koma zidachitika mwa ngozi. Umboni wa a nyumba zoyandikira komanso komwe Filipi adakagula mipeni udaonetsa kuti patsiku Lachisanu limene izi zidachitika | Female | |
Phillip amaoneka wachimwemwe momwe amakhalira nthawi zonse. Mu umboni wina umene udaperekedwa, Phillip adauza kadaulo wa za matenda a kaganizidwe | Filipi amaoneka wachimwemwe momwe amakhalira nthawi zonse. Mu umboni wina umene udaperekedwa, Filipi adauza kadaulo wa za matenda a kaganizidwe | Female | |
kuti ankadziwa kuti adapha mkazi wake koma adati adachita izi chifukwa Diana amamukhambitsa. Kuphako kudachitika pomwe ndidazingidwa | kuti ankadziwa kuti adapha mkazi wake koma adati adachita izi chifukwa Dayana amamukhambitsa. Kuphako kudachitika pomwe ndidazingidwa | Female | |
ndi kusagwira kwa mutu. Zidzandizunza moyo wanga onse, iye adauza dotoloyo. Ndipo apolisi atamumanga, iye adakana kawiri kuti sangayankhe mafunso ndipo iwo adamutsegulira mlandu wopha munthu | ndi kusagwira kwa mutu. Zidzandizunza moyo wanga onse, iye adauza dotoloyo. Ndipo apolisi atamumanga, iye adakana kawiri kuti sangayankhe mafunso ndipo iwo adamutsegulira mlandu wopha munthu | Female | |
Womuimira pamlanduwo, David Nathan, wati Phillip sankadiwa zimene zimachitika chifukwa mutu siumagwira choncho sadalakwe | Womuimira pamlanduwo, Devidi Nafani, wati Filipi sankadiwa zimene zimachitika chifukwa mutu siumagwira choncho sadalakwe | Female | |
Malipotiwo adati ngakhale Diana adabaidwa ka 17 kuphatikizapo m’zala kusonyeza kuti amadziteteza | Malipotiwo adati ngakhale Dayana adabaidwa ka seventini kuphatikizapo m’zala kusonyeza kuti amadziteteza | Female | |
chipatala cha Leicester Royal Family chidapeza kuti kubaya kumene kudatenga moyo wake kudali kwa pamtima | chipatala cha lesita loyo famile chidapeza kuti kubaya kumene kudatenga moyo wake kudali kwa pamtima | Female | |
Nthawi yomwe mlanduwo udafika apa, Phillip adali akulira ndi kupuputa misozi yake ndi kansalu. Mlanduwo ukupitirira | Nthawi yomwe mlanduwo udafika apa, filipi adali akulira ndi kupuputa misozi yake ndi kansalu. Mlanduwo ukupitirira | Female | |
Amayi oyendayenda sakumwera madzi chitsime chimodzi m’boma la Ntchisi polimbirana migodi. Nkhaniyi ikuti pali gulu la amayi achichepere ogulitsa matupi awo m’malo azisangalalo m’bomalo | Amayi oyendayenda sakumwera madzi chitsime chimodzi m’boma la Ntchisi polimbirana migodi. Nkhaniyi ikuti pali gulu la amayi achichepere ogulitsa matupi awo m’malo azisangalalo m’bomalo | Female | |
lomwe likumathamangitsa ndi kunyoza amayi okulirapo misinkhu kuti awalekere migodi yawo | lomwe likumathamangitsa ndi kunyoza amayi okulirapo misinkhu kuti awalekere migodi yawo | Female | |
Wapampando wa amayi oyenendayenda m’bomalo a Legester Chimkanda anatsimikiza kuti mikanganoyi yomwe ndi ya pa kanthawi yafika povuta m’bomalo | Wapampando wa amayi oyenendayenda m’bomalo a Lejesita Chimkanda anatsimikiza kuti mikanganoyi yomwe ndi ya pa kanthawi yafika povuta m’bomalo | Female | |
Iwo anati chifukwa cha kutopa ndi mtudzu, ndewu ya mnanu inabuka Lamulungu yomwe inasiya amayi 5 atabaidwa ndi mabotolo | Iwo anati chifukwa cha kutopa ndi mtudzu, ndewu ya mnanu inabuka Lamulungu yomwe inasiya amayi faifi atabaidwa ndi mabotolo | Female | |
katundu kuonongedwa pomwe amayi ena awiri omwe ndi achichepere komanso apachibale ali m’manja mwa apolisi | katundu kuonongedwa pomwe amayi ena awiri omwe ndi achichepere komanso apachibale ali m’manja mwa apolisi | Female | |
Gwero la nkhaniyi ndi yoti amayi achicheperewa akumanyoza anzawo achikulire akapeza mphongo, kwinaku akuiseka mphongo ija kuti yatenga mayi wachikulire kusiya achichepere | Gwero la nkhaniyi ndi yoti amayi achicheperewa akumanyoza anzawo achikulire akapeza mphongo, kwinaku akuiseka mphongo ija kuti yatenga mayi wachikulire kusiya achichepere | Female | |
anatero a Chimkanda. Iwo anati pali chiopsezo kuti ngati nkhanizi siziunikilidwa bwino, ena akhoza kutayapo miyoyo | anatero a Chimkanda. Iwo anati pali chiopsezo kuti ngati nkhanizi siziunikilidwa bwino, ena akhoza kutayapo miyoyo | Female | |
Ndipo pakadalipano, apolisi m’bomalo alowererapo pokhazika pansi mbali ziwirizo. mneneri wa polisi m’boma la Ntchisi a Yohane Tasowana | Ndipo pakadalipano, apolisi m’bomalo alowererapo pokhazika pansi mbali ziwirizo. mneneri wa polisi m’boma la Ntchisi a Yohane Tasowana | Female | |
anatsimikiza kuti anatsekera a Anastanzia Banda a zaka 22 komanso Janet Banda a zaka 19 powaganizira kuti anabaya anzawo ena asanu ndi mabotolo a mowa | anatsimikiza kuti anatsekera a Anasitanziya Banda a zaka twente thu komanso Jeneti Banda a zaka naintini powaganizira kuti anabaya anzawo ena asanu ndi mabotolo a mowa | Female | |
Iwo anati magulu awiriwa akhala akumenyana chifukwa cholimbirana amuna kwa miyezi ingapo tsopano. Milandu ya magulu awiriwa yakhala ikutipeza ku polisi kuno ndithu, anatero a Tasowana | Iwo anati magulu awiriwa akhala akumenyana chifukwa cholimbirana amuna kwa miyezi ingapo tsopano. Milandu ya magulu awiriwa yakhala ikutipeza ku polisi kuno ndithu, anatero a Tasowana | Female | |
A Tasowana anati amayi apachibalewo, anapeza mphongo zomwe anagwirizana nazo ndipo ali paulendo wopita ku malo ogona alendo | A Tasowana anati amayi apachibalewo, anapeza mphongo zomwe anagwirizana nazo ndipo ali paulendo wopita ku malo ogona alendo | Female | |
anakumana ndi amayi ena 5 omwe anawakaniza amayi awiriwo kutengana ndi mphongozo. Izi sizidakomere amayi a pa chibalewo ndipo ndewu yoopsa inabuka pamalopo, anatero a Tasowana | anakumana ndi amayi ena faifi omwe anawakaniza amayi awiriwo kutengana ndi mphongozo. Izi sizidakomere amayi a pa chibalewo ndipo ndewu yoopsa inabuka pamalopo, anatero a Tasowana | Female | |
Iwo anati amayi apachibalewo anabaya amnzawo asanuwo ndi mabotolo ndi kuvulaza atatu mwa iwo kwambiri | Iwo anati amayi apachibalewo anabaya amnzawo asanuwo ndi mabotolo ndi kuvulaza atatu mwa iwo kwambiri | Female | |
A Tasowana anati amayi a pachibalewo omwe amachokera m’mudzi mwa Maunde, Mfumu Tambala, m’boma la Dedza, awatsekulira mulandu yovulaza anthu | A Tasowana anati amayi a pachibalewo omwe amachokera m’mudzi mwa Maunde, Mfumu Tambala, m’boma la Dedza, awatsekulira mulandu yovulaza anthu | Female | |
Iwo anati amayi ovulazidwawo anathamangira nawo kuchipatala cha Ntchisi komwe anakalandira thandizo la mankhwala | Iwo anati amayi ovulazidwawo anathamangira nawo kuchipatala cha Ntchisi komwe anakalandira thandizo la mankhwala | Female | |
Mkulu wa bungwe lolimbana ndi katangale ndi ziphuphu a Martha Chizuma akadali ndi ulendo wautali woteteza ntchito yawo yothana ndi anthu omwe akukhudzidwa ndi nkhani zakatangale komanso ziphuphu m’dziko muno | Mkulu wa bungwe lolimbana ndi katangale ndi ziphuphu a Mafa Chizuma akadali ndi ulendo wautali woteteza ntchito yawo yothana ndi anthu omwe akukhudzidwa ndi nkhani zakatangale komanso ziphuphu m’dziko muno | Female | |
Lachitatu lapitali, a Chizuma adalandira kalata kuchokera ku ofesi ya Pulezidenti ndi nduna yosainidwa ndi mlembi wa ofesiyi a Colleen Zamba yowaimitsa ntchito mpaka milandu yomwe akuyankha ithe | Lachitatu lapitali, a Chizuma adalandira kalata kuchokera ku ofesi ya Pulezidenti ndi nduna yosainidwa ndi mlembi wa ofesiyi a Kolini Zamba yowaimitsa ntchito mpaka milandu yomwe akuyankha ithe | Female | |
Izi zikuchitika pomwe m’manja mwa a Chizuma muli mafailo ochuluka okhudza zakatangale ndipo iwo adanenapo m’mbuyomo | Izi zikuchitika pomwe m’manja mwa a Chizuma muli mafailo ochuluka okhudza zakatangale ndipo iwo adanenapo m’mbuyomo | Female | |
kuti pa mndandanda womwe alinawo, palinso maina ena a nduna ndi akuluakulu m’boma. Pa tsiku lokumbukira kuthana ndi katangale ndi ziphuphu chaka chatha | kuti pa mndandanda womwe alinawo, palinso maina ena a nduna ndi akuluakulu m’boma. Pa tsiku lokumbukira kuthana ndi katangale ndi ziphuphu chaka chatha | Female | |
a Chizuma adagwedeza dziko atanenetsa pamaso pa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi nduna zaboma kuti sakuopa kanthu ndipo athana ndi aliyense amene ali m’mafailo awo | a Chizuma adagwedeza dziko atanenetsa pamaso pa mtsogoleri wa dziko lino a Lazalasi Chakwera ndi nduna zaboma kuti sakuopa kanthu ndipo athana ndi aliyense amene ali m’mafailo awo | Female | |
Ntchito yanga n’kuthana ndi katangale ndi ziphuphu ndiye sindiopa kuti munthu ndiotchuka bwanji, ali ndi ndalama zochuluka bwanji kapena kuti ndi wandale | Ntchito yanga n’kuthana ndi katangale ndi ziphuphu ndiye sindiopa kuti munthu ndiotchuka bwanji, ali ndi ndalama zochuluka bwanji kapena kuti ndi wandale | Female | |
Ngati mphepo yandipeza kuti adapangapo katangale, akwekwesedwa, iwo adatero. Owaimilira pa milandu a Martha Kaukonde adatsimikiza zoti a Chizuma adalandira kalata yowaimitsa ntchito | Ngati mphepo yandipeza kuti adapangapo katangale, akwekwesedwa, iwo adatero. Owaimilira pa milandu a Mafa Kaukonde adatsimikiza zoti a Chizuma adalandira kalata yowaimitsa ntchito | Female | |
Koma adati n’zodabwitsa chifukwa adawaimitsa ntchito chifukwa cha mlandu womwe sadapelekere umboni. N’zoona awaimitsa | Koma adati n’zodabwitsa chifukwa adawaimitsa ntchito chifukwa cha mlandu womwe sadapelekere umboni. N’zoona awaimitsa | Female | |
koma n’zodabwitsa chifukwa mlandu omwe akunenawo sitidakalowe m’khoti tidzalowa pa 8 February 2023 adatero a Kaukonde | koma n’zodabwitsa chifukwa mlandu omwe akunenawo sitidakalowe m’khoti tidzalowa pa aiti febuluwale twente twente fili adatero a Kaukonde | Female | |
Polankhulapo, wapampando wa komiti yoona zamalamulo ku Nyumba ya Malamulo a Peter Dimba adati kuimitsidwa kwa a Chizuma ndinkhani yomvetsa chisoni | Polankhulapo, wapampando wa komiti yoona zamalamulo ku Nyumba ya Malamulo a Pita Dimba adati kuimitsidwa kwa a Chizuma ndinkhani yomvetsa chisoni | Female | |
ndipo yoonekeratu kuti atcheredwa. Ndife odabwa komanso okhudzidwa kuti akuluakulu athu akuyesetsa kufuna kukankhira dzikoli kuphedi | ndipo yoonekeratu kuti atcheredwa. Ndife odabwa komanso okhudzidwa kuti akuluakulu athu akuyesetsa kufuna kukankhira dzikoli kuphedi | Female | |
Zikutidabwitsa kwambiri komabe izizi zidawonekera patali pomwe, adatero a Dimba. Ndipo mkulu wa bungwe la Centre For Democracy and Economic Development Initiative, Cdedi | Zikutidabwitsa kwambiri komabe izizi zidawonekera patali pomwe, adatero a Dimba. Ndipo mkulu wa bungwe la Senta fo demokalase andi ikonomiki divelopumenti inishetivi, Sidedi | Female | |
a Silvestre Namiwa ati akuona kuti chachuluka pankhaniyi n’kufuna kutetezana pakati pa akuluakulu omwe akudziwana kuti adapanga zakatangale | a Silivesita Namiwa ati akuona kuti chachuluka pankhaniyi n’kufuna kutetezana pakati pa akuluakulu omwe akudziwana kuti adapanga zakatangale | Female | |
A Namiwa ati pazomwe zachitikazo, boma la a Chakwera liyenera kubwera poyera kuwuza Amalawi ngati sakufuna bungwe lolimbana ndi katangale pa ulamuliro wawo m’malo mongophimba Amalawi m’maso | A Namiwa ati pazomwe zachitikazo, boma la a Chakwera liyenera kubwera poyera kuwuza Amalawi ngati sakufuna bungwe lolimbana ndi katangale pa ulamuliro wawo m’malo mongophimba Amalawi m’maso | Female | |
N’chifukwa chiyani nkhani iyiyi imangobwerabwera, Kapena akungofuna kutetezana. Angotiuza ngati sakufuna bungwe la ACB pa ulamuliro wawo,adatero a Namiwa | N’chifukwa chiyani nkhani iyiyi imangobwerabwera, Kapena akungofuna kutetezana. Angotiuza ngati sakufuna bungwe la Esibi pa ulamuliro wawo,adatero a Namiwa | Female | |
Kadaulo wa zamalamulo a Garton Kamchedzera adauza The Nation kuti a Chakwera akudzikolakola okha chifukwa adalonjeza pagulu kuti a Chizuma akhalabe mkulu wa ACB | Kadaulo wa zamalamulo a Gatoni Kamchedzera adauza Ve neshoni kuti a Chakwera akudzikolakola okha chifukwa adalonjeza pagulu kuti a Chizuma akhalabe mkulu wa Esibi | Female | |
Mc Mooly Makuni Gondwe yemwe amagwira ntchito kundende ya dziko lino ndi mkazi wake Angela Chikho yemwe ndi msilikari anakulira limodzi pa ubwana wawo | Makimule Makuni Gondwe yemwe amagwira ntchito kundende ya dziko lino ndi mkazi wake Anjela Chikho yemwe ndi msilikari anakulira limodzi pa ubwana wawo | Female | |
Takulira limodzi ndipo tinkacheza tili ana achichepere, koma sitinasiyane m’chaka cha 2012, anatero Mc Mooly | Takulira limodzi ndipo tinkacheza tili ana achichepere, koma sitinasiyane m’chaka cha twente thwelofu , anatero Makimule | Female | |
Takulira limodzi ndipo tinkacheza tili ana achichepere, koma sitinasiyane m’chaka cha 2012, anatero Mc Mooly | Takulira limodzi ndipo tinkacheza tili ana achichepere, koma sitinasiyane m’chaka cha twente thwelofu, anatero Makimule | Female | |
Koma awiriwo anadzakumananso m’chaka cha 2019 kumapemphero ochezera usiku onse pampingo wa CCAP wa Livingstonia ku Kanengo, mumzinda wa Lilongwe komwe patadutsa kanyengo, ubwenzi wawo unayamba | Koma awiriwo anadzakumananso m’chaka cha twente naintini kumapemphero ochezera usiku onse pampingo wa sisiepi wa Living’isitoniya ku Kanengo, mumzinda wa Lilongwe komwe patadutsa kanyengo, ubwenzi wawo unayamba | Female | |
Patadutsa zaka ziwiri ali pa ubwenzi, awiriwo anadalitsa ukwati wawo pa 3 September pampingo wa Livingstonia Kanengo CCAP | Patadutsa zaka ziwiri ali pa ubwenzi, awiriwo anadalitsa ukwati wawo pa fili sepitemba pampingo wa Living’isitoniya Kanengo sisiepi | Female | |
ndipo madyerero anachitikira kuholo ya sukulu ya sekondale ya Kabwabwa ku Area 25, mzinda wa Lilongwe | ndipo madyerero anachitikira kuholo ya sukulu ya sekondale ya Kabwabwa ku El;iya twente faifi , mzinda wa Lilongwe | Female | |
Komatu awiriwo sanayende moyera ayi chifukwa ubwenzi wawo unali woyenderana chifukwa Mc Mooly amakhala mumzinda wa Lilongwe pomwe Angela amagwira ntchito yake ku Moyale, mumzinda wa Mzuzu panthawiyo | Komatu awiriwo sanayende moyera ayi chifukwa ubwenzi wawo unali woyenderana chifukwa Makimule amakhala mumzinda wa Lilongwe pomwe Angela amagwira ntchito yake ku Moyale, mumzinda wa Mzuzu panthawiyo | Female | |
Mc Mooly anadandaula kuti kunali kovuta kukumana pafupipafupi pa yomwe anali pa ubwenzi | Makimule anadandaula kuti kunali kovuta kukumana pafupipafupi pa yomwe anali pa ubwenzi | Female | |
Kupatula apo awiriwo anati zokhoma zina zomwe anakumana nazo pa ulendo wawo wabanja zinali zolankhula za anthu | Kupatula apo awiriwo anati zokhoma zina zomwe anakumana nazo pa ulendo wawo wabanja zinali zolankhula za anthu | Female | |
Chachikulu timayamika Mulungu kuti zinatheka palibe chomwe chimalepheretsa ngati matenda kapena maliro, iwo anatero | Chachikulu timayamika Mulungu kuti zinatheka palibe chomwe chimalepheretsa ngati matenda kapena maliro, iwo anatero | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.