audio
audioduration (s)
1.12
18.5
raw_text
stringlengths
1
297
normalized_text
stringlengths
1
267
gender
stringclasses
16 values
Chifukwa anali pamavuto kwambiri ndipo anakali pamavuto, pakuti chipatalachi sichinayambe kugwira ntchito. Koma akamaliza zonse, mavuto amakumana nawo, akhala mbiri yakale.
Chifukwa anali pamavuto kwambiri ndipo anakali pamavuto, pakuti chipatalachi sichinayambe kugwira ntchito. Koma akamaliza zonse, mavuto amakumana nawo, akhala mbiri yakale.
female
“Mwana akadwala, kapena munthu wamkula akadwala, timayesetsa kupeza njinga yamoto, yomwe amatilipiritsa 7,000 kwacha kupita ndi kubwera, kuti tikafike komwe kuli chipatala.
“Mwana akadwala, kapena munthu wamkula akadwala, timayesetsa kupeza njinga yamoto, yomwe amatilipiritsa seveni sauzandi kwacha kupita ndi kubwera, kuti tikafike komwe kuli chipatala.
female
Ndipo ndi mavuto ambiri, chifukwa anthu kunoko, timangokhala ndipo kuti tipeze ndalama ngati imeneyi, ndizovuta kwambiri.” Anatero a Felemu.
Ndipo ndi mavuto ambiri, chifukwa anthu kunoko, timangokhala ndipo kuti tipeze ndalama ngati imeneyi, ndizovuta kwambiri.” Anatero a Felemu.
female
Malingana ndi a Felemu, anthu akwa Felemu, chitukuko cha chipatala chimenechi, achilandira mosangalala kwambiri, chifukwa chipatala chomwe amapita, chili kutali kwambiri, pafupifupi ma Kilometer 15.
Malingana ndi a Felemu, anthu akwa Felemu, chitukuko cha chipatala chimenechi, achilandira mosangalala kwambiri, chifukwa chipatala chomwe amapita, chili kutali kwambiri, pafupifupi ma Kilomita fifitini.
female
Ndipo ambiri amakanika kupitako, ndiponso ambiri amamwalirira munjira. “Chaka chathachi tinataya ana awiri abanja limodzi, tilimunjira kupita nawo kuchipatala, chifukwa chamatenda a malungo.” Anatero a Felemu.
Ndipo ambiri amakanika kupitako, ndiponso ambiri amamwalirira munjira. “Chaka chathachi tinataya ana awiri abanja limodzi, tilimunjira kupita nawo kuchipatala, chifukwa chamatenda a malungo.” Anatero a Felemu.
female
Chipatala china chamangidwaso kwa mfumu Gonthu. Ndipo polankhula ndi Malawi 24, a Maxwell Nyumbu, omwe amayimira a group a aGonthi, anati chipatala achilandira kwa a Gonthi.
Chipatala china chamangidwanso kwa mfumu Gonthu. Ndipo polankhula ndi Malawi tuwente folo, a Makisiwelo Nyumbu, omwe amayimira a gurupu a Gonthi, anati chipatala achilandira kwa a Gonthi.
female
Ndipo ndi anthu wosangalala chifukwa mayendedwe opita ku chipatala mwa Magaleta ndiwovuta kwambiri. “Tili ndimitsinje imene imadzadza madzi nthawi ya dzinja.
Ndipo ndi anthu wosangalala chifukwa mayendedwe opita ku chipatala mwa Magaleta ndiwovuta kwambiri. “Tili ndimitsinje imene imadzadza madzi nthawi ya dzinja.
female
Imene amayi komanso ana, amatha kukomokera munjira. Kubwera kwa chipatala ichi, ndife wosangalala kunoko kwa Gonthi komanso kuthokoza kwambiri a unduna wazaumoyo komaso mtsogoleri wa dzikolino.
Imene amayi komanso ana, amatha kukomokera munjira. Kubwera kwa chipatala ichi, ndife wosangalala kunoko kwa Gonthi komanso kuthokoza kwambiri a unduna wazaumoyo komaso mtsogoleri wa dzikolino.
female
Kulingalira mozama kuti madera akumudzi kuti kukhale zipatala zing’onozing’ono, anatero a Nyumbu.” Mawu ake a Counselor Joseph Chiphaliwali, wadera la Ligowe komwe kwamangidwa zipatala ziwiri.
Kulingalira mozama kuti madera akumudzi kuti kukhale zipatala zing’onozing’ono, anatero a Nyumbu.” Mawu ake a Khansala Jozefe Chiphaliwali, wadera la Ligowe komwe kwamangidwa zipatala ziwiri.
female
Felemu ndi Gonthi, anayamikira boma kudzera ku unduna wa zawumoyo, pamodzi ndi bungwe la global fund, powabweretsera zipatala ziwiri mudera lawo, zomwe zithandize kwambiri anthu wokhala mderari.
Felemu ndi Gonthi, anayamikira boma kudzera ku unduna wa zawumoyo, pamodzi ndi bungwe la gulobo fandi, powabweretsera zipatala ziwiri mudera lawo, zomwe zithandize kwambiri anthu wokhala mderari.
female
Kunoko kuli mavuto kwambiri, mavuto wosaneneka. Anthu akuno amavutika kuti apite kuchipatala, kunoko anthu akadwala timapitanawo ku Chifunga komwe ndikutali.
Kunoko kuli mavuto kwambiri, mavuto wosaneneka. Anthu akuno amavutika kuti apite kuchipatala, kunoko anthu akadwala timapitanawo ku Chifunga komwe ndikutali.
female
Pena matenda akakula, timapitanawo ku Mwanza, koma nthawi zambiri ku Mwanza amatha kutibweza akatizindikira kuti tachokera kuno ku Neno.
Pena matenda akakula, timapitanawo ku Mwanza, koma nthawi zambiri ku Mwanza amatha kutibweza akatizindikira kuti tachokera kuno ku Neno.
female
Ndipo amatiwuza kuti tipite ku chipatala cha ku Neno, chomwe chili kutali kwambiri ndi kunoko. Anatero a Chiphaliwali. Omwe anayimira nduna yazawumoyo, a Matiyasi Joshua.
Ndipo amatiwuza kuti tipite ku chipatala cha ku Neno, chomwe chili kutali kwambiri ndi kunoko. Anatero a Chiphaliwali. Omwe anayimira nduna yazawumoyo, a Matiyasi Joshuwa.
female
Omwe ndi wamkulu woyang’ana zakasinthidwe ka ntchito ku undunaku, anati ndiwosangalala ndimmene ntchito yomanga zipatalazi ikuyendera, ndipo ali ndi chiyembekezo kuti pofika mwenzi wa June, anthu ayamba kulandira thandizo ku zipatalazi.
Omwe ndi wamkulu woyang’ana zakasinthidwe ka ntchito ku undunaku, anati ndiwosangalala ndimmene ntchito yomanga zipatalazi ikuyendera, ndipo ali ndi chiyembekezo kuti pofika mwenzi wa Juni, anthu ayamba kulandira thandizo ku zipatalazi.
female
M’mene tayenderamu, zikuwoneka kuti zinthu zikuyenda. Tikukhulupirira pomatha miyezi iwiri kapena itatu, zipatalazi zikhala zonse zatha.
M’mene tayenderamu, zikuwoneka kuti zinthu zikuyenda. Tikukhulupirira pomatha miyezi iwiri kapena itatu, zipatalazi zikhala zonse zatha.
female
Ogwira ntchito talemba kale, ndipo kungomaliza tikhala tikutumiza anthu akayambe ntchito,akayambe kugwira ntchito, mankhwalaso ayamba kufika. Anatero a Joshua.
Ogwira ntchito talemba kale, ndipo kungomaliza tikhala tikutumiza anthu akayambe ntchito,akayambe kugwira ntchito, mankhwalaso ayamba kufika. Anatero a Joshuwa.
female
Boma lachititsa maphunziro a phunzitsi awophunzira amene ali ndi ulumali. Unduna wazamaphunziro mogwirizana ndi bungwe la Malawi Communication Regulatory Authority, MACRA.
Boma lachititsa maphunziro a phunzitsi awophunzira amene ali ndi ulumali. Unduna wazamaphunziro mogwirizana ndi bungwe la Malawi kominikashoni Reguletare Othorite, MAKIRA.
female
Wakhazikitsa gawo lachiwiri la maphunziro kwa anthu amene amaphunzitsa chiyankhulo chamanja kwa anthu amene ali ndi ulumali. Maphunzirowa amene akuchitikira ku Mponera mu boma la Dowa,
Wakhazikitsa gawo lachiwiri la maphunziro kwa anthu amene amaphunzitsa chiyankhulo chamanja kwa anthu amene ali ndi ulumali. Maphunzirowa amene akuchitikira ku Mponera mu boma la Dowa,
female
Athandizira kupititsa patsogolo kaphunziridwe ka chiyankhulo cha manja kwa anthu amene ali ndi ulumali wonsava. Mu mawu ake wachiwiri wa mkulu amene akuyang’anira maphunziro,
Athandizira kupititsa patsogolo kaphunziridwe ka chiyankhulo cha manja kwa anthu amene ali ndi ulumali wonsava. Mu mawu ake wachiwiri wa mkulu amene akuyang’anira maphunziro,
female
A Lucy Magagula, Unduna wazamaphunziro wadzipereka kuthandiza aphunzitsiwa, kuti akhale ndi luso lokwanira lophunzitsa anthu awulumali mu chiyankhulo cha manja.
A Luse Magagula, "Unduna wazamaphunziro wadzipereka kuthandiza aphunzitsiwa, kuti akhale ndi luso lokwanira lophunzitsa anthu awulumali mu chiyankhulo cha manja.
female
Tachiyesa chamwayi kuti tibweretse maphunzirowa, chifukwa athandizira kwambiri ana amene ali msukulu za anthu amene ali ndi ulumali.” Anatero Magagula.
Tachiyesa chamwayi kuti tibweretse maphunzirowa, chifukwa athandizira kwambiri ana amene ali msukulu za anthu amene ali ndi ulumali.” Anatero Magagula.
female
Maphunziro akuchitika ndi thandizo lochokera ku bungwe la MACRA komanso Universal Service Fund USB. Maphunzirowa akuyembekezeka kutha masiku asanu.
Maphunziro akuchitika ndi thandizo lochokera ku bungwe la MAKIRA komanso Yuniveso Sevisi Fandi (YU ESI BI). Maphunzirowa akuyembekezeka kutha masiku asanu.
female
Ndipo Maphunzitsi wokwana makumi asanu ndi awiri 70 wochokera m’maboma khumi, asanu ndi anayi 19, ndiamene akutenga nawo mbali.
Ndipo Maphunzitsi wokwana makumi asanu ndi awiri (sevente) wochokera m’maboma khumi, asanu ndi anayi (nayintini), ndiamene akutenga nawo mbali.
female
Mkangano wamalire, anthu aku Mozambique, atchetchanso chimanga cha a Malawi ku Makanjira. Pomwe pali kale chopsezo cha njala yadzawoneni chakachino, a police komanso anthu a mdziko la Mozambique,
Mkangano wamalire, anthu aku Mozambiki, atchetchanso chimanga cha a Malawi ku Makanjira. Pomwe pali kale chopsezo cha njala yadzawoneni chakachino, a polisi komanso anthu a mdziko la Mozambiki,
female
Pa 17 January, 2024 komanso usiku wa loweruka lapitali, atchetchanso chimanga cha a Malawi pa mkangano wa malire apakati a dzikolino ndi lawolo ku Makanjira m’boma la Mangochi.
Pa seventini januware tuwente tuwente-folo komanso usiku wa loweruka lapitali, atchetchanso chimanga cha a Malawi pa mkangano wa malire apakati a dzikolino ndi lawolo ku Makanjira m’boma la Mangochi.
female
Tsambalino lapezakuti anthu a m’midzi yaku Mozambique yomwe yachita malire ndi dzikolino, akumaperekezedwa ndi a police mdzikolo usiku ndikuyamba kutchetcha chimanga cha nzika za dzikolino.
Tsambalino lapezakuti anthu a m’midzi yaku Mozambiki yomwe yachita malire ndi dzikolino, akumaperekezedwa ndi a polisi mdzikolo usiku ndikuyamba kutchetcha chimanga cha nzika za dzikolino.
female
Ponena kuti malowo ali mdzikolawo, ndipo chakachino chokha, anthuwa apanga chipongwechi kawiri, zomwe zikuyika a Malawi mderari, pa chowopsezo cha njala.
Ponena kuti malowo ali mdzikolawo, ndipo chakachino chokha, anthuwa apanga chipongwechi kawiri, zomwe zikuyika a Malawi mderari, pa chowopsezo cha njala.
female
Malawi 24, yavetsedwanso kuti anthu a m’mudzi mwa Chala omwe uli mdziko la Mozambique, usiku wapa 17 January chakachino, anaperekezedwa ndi a police a mdzikolo,
Malawi tuwente-folo, yavetsedwanso kuti anthu a m’mudzi mwa Chala omwe uli mdziko la Mozambiki, usiku wapa seventini januware chakachino, anaperekezedwa ndi a polisi a mdzikolo,
female
Ndikuyamba kutchetcha minda yachimanga ingapo ya anthu a m’mudzi mwa Madi ku Makanjira komweko ponena kuti mindayo ili mdzikomwawo, ndipo a Malawi sakuyenera kumayitenga ngati yawo ndikumalimamo.
Ndikuyamba kutchetcha minda yachimanga ingapo ya anthu a m’mudzi mwa Madi ku Makanjira komweko ponena kuti mindayo ili mdzikomwawo, ndipo a Malawi sakuyenera kumayitenga ngati yawo ndikumalimamo.
female
Kupatula apo, anthuwo akuti usiku wa loweruka lapitali, pa 20 January, 2024, anaperekezedwanso ndi a police a mdzikolo,
Kupatula apo, anthuwo akuti usiku wa loweruka lapitali, pa tuwente Januware, januware tuwente tuwente-folo, anaperekezedwanso ndi a polisi a mdzikolo,
female
Ndukayambanso kutchetcha chimanga chomwe chili m’minda ya anthu a m’mudzi mwa Lukono kudera lomweri, nkhani yake ya malire omwewa. Aka sikoyamba kuti izi zichitike,
Ndukayambanso kutchetcha chimanga chomwe chili m’minda ya anthu a m’mudzi mwa Lukono kudera lomweri, nkhani yake ya malire omwewa. Aka sikoyamba kuti izi zichitike,
female
Kamba koti kangapo konse,kumapeto a chakachatha, anthuwa anatchetchaso minda ina ingapo ya a Malawi, ndipo tukamba pano akuti zafika poti akuluakulu a mudzi mwa Chala,
Kamba koti kangapo konse,kumapeto a chakachatha, anthuwa anatchetchaso minda ina ingapo ya a Malawi, ndipo tukamba pano akuti zafika poti akuluakulu a mudzi mwa Chala,
female
Awuza anthu awo kuti asamamweranenso madzi ndi anthu a midzi yaku Malawi yomwe ndikuphatikizapo Makunula, Mkopiti, Madi, Lukono, Ngwati, Bonasani ndi ina yambiri.
Awuza anthu awo kuti asamamweranenso madzi ndi anthu a midzi yaku Malawi yomwe ndikuphatikizapo Makunula, Mkopiti, Madi, Lukono, Ngwati, Bonasani ndi ina yambiri.
female
Loweruka pa 20 January 2024, atchetchanso chimanga mudzi wa Lukuno. Akumayenda ndi a police usiku kumatchetcha chimanga cha anthu aku Malawi.
Loweruka pa tuwente Januware, tuwente tuwente-folo, atchetchanso chimanga mudzi wa Lukuno. Akumayenda ndi a police usiku kumatchetcha chimanga cha anthu aku Malawi.
female
Tikunena pano, anthu aku Mozambique, awaletsa kuti asamabwere kumadzacheza ku Malawi, maka kumidzi yomwe akutchetcha chimanga cha anthuwo, kuti mwina anthu omwe akuwatchetchera chimangawo, kuti aziwawona akhoza kuwapanga chipongwe.
Tikunena pano, anthu aku Mozambiki, awaletsa kuti asamabwere kumadzacheza ku Malawi, maka kumidzi yomwe akutchetcha chimanga cha anthuwo, kuti mwina anthu omwe akuwatchetchera chimangawo, kuti aziwawona akhoza kuwapanga chipongwe.
female
Chiganizo chimenecho achipanga ndi mafumu, moti pano anthu akwa Chala ku Mozambique, sakubwera midzi yozungulira yomwe yakhudzidwa ndi kutchetcheredwa chimangayo, akumangobwera usiku kudzatchetcha chimanga nkumapita. Amayenda ndi a polisi awo.
Chiganizo chimenecho achipanga ndi mafumu, moti pano anthu akwa Chala ku Mozambiki, sakubwera midzi yozungulira yomwe yakhudzidwa ndi kutchetcheredwa chimangayo, akumangobwera usiku kudzatchetcha chimanga nkumapita. Amayenda ndi a polisi awo.
female
Watitsina khutu munthu wina. Munthuyu watiso kucha kwa lamulungu pa 22 January, 2024, apolisi mudziko la Mozambique, anathamangitsa anthu omwe anakhamukira kuminda yotchetchedwa.
Watitsina khutu munthu wina. Munthuyu watinso kucha kwa lamulungu pa tuwente thu Januware, tuwente tuwente-folo, apolisi mudziko la Mozambiki, anathamangitsa anthu omwe anakhamukira kuminda yotchetchedwa.
female
Pomwe amafuna kukadziwonera wokha malodzawo. Phungu wadandawulira boma kuthetsa mkangano wa malirewu, pomwe palikale chiwopsezo cha njala yadzawoneni chakachino.
Pomwe amafuna kukadziwonera wokha malodzawo. Phungu wadandawulira boma kuthetsa mkangano wa malirewu, pomwe palikale chiwopsezo cha njala yadzawoneni chakachino.
female
Apolice komaso anthu a Mdziko la Mozambique, pa 17 January, 2024, komanso usiku wa loweruka lapitali, atchetchanso chimanga cha a Malawi pa mkangano wamalire.
Apolisi komanso anthu a Mdziko la Mozambiki, pa seventini Januware, tuwente tuwente-folo,komanso usiku wa loweruka lapitali, atchetchanso chimanga cha a Malawi pa mkangano wamalire.
female
Apakati padzikolino ndi lawolo ku Makanjira m’boma la Mangochi. Poyankhula ndi tsamba lino zankhaniyi, phungu wadera lakumpoto kwa boma la Mangochi a Benedicto Chambo.
Apakati padzikolino ndi lawolo ku Makanjira m’boma la Mangochi. Poyankhula ndi tsamba lino zankhaniyi, phungu wadera lakumpoto kwa boma la Mangochi a Benedikito Chambo.
female
Ati, zinthu zafika pa mwana wakana phala ku Makanjira, ndipo wati chodandawulitsa kwambiri mchakuti, pomwe a Malawi akukuamana ndi mazangazime amenewa, boma la Malawi, silikuwonetsa chidwi chenicheni pankhaniyi.
Ati, zinthu zafika pa mwana wakana phala ku Makanjira, ndipo wati chodandawulitsa kwambiri mchakuti, pomwe a Malawi akukuamana ndi mazangazime amenewa, boma la Malawi, silikuwonetsa chidwi chenicheni pankhaniyi.
female
A Chambo atiwuza kuti kwazaka zingapo tsopano, iwo akhala akupita ku unduna wazamalo, unduna wa chitetezo cha mdziko, komanso unduna owona za ubale wadzikolino ndi maiko ena.
A Chambo atiwuza kuti kwazaka zingapo tsopano, iwo akhala akupita ku unduna wazamalo, unduna wa chitetezo cha mdziko, komanso unduna owona za ubale wadzikolino ndi maiko ena.
female
Kupempha kuti boma lilowererepo pankhaniyi msanga, koma ati pempho lawo linagwera pamwala mpaka pano pomwe mkangano wafika pa mpondachimera. Nkhaniyi ine ndikuyidziwa bwino ndipo ndikuyendanawo limodzi anthuwa.
Kupempha kuti boma lilowererepo pankhaniyi msanga, koma ati pempho lawo linagwera pamwala mpaka pano pomwe mkangano wafika pa mpondachimera. Nkhaniyi ine ndikuyidziwa bwino ndipo ndikuyendanawo limodzi anthuwa.
female
Zotchetchedwa minda ineyo ndikuziwona ndipo ndakhala ndikupita ndikulankhula nawo,ndayenda mwa adindo onse wofunikira m’boma monga kwa bwanankubwa wa boma la Mangochi, ku police nkulu wa police amene ndakumananawo.
Zotchetchedwa minda ineyo ndikuziwona ndipo ndakhala ndikupita ndikulankhula nawo, ndayenda mwa adindo onse wofunikira m’boma monga kwa bwanankubwa wa boma la Mangochi, ku polisi nkulu wa polisi amene ndakumananawo.
female
Unduna wazamalo, unduna wowona za ubale wadzikolino ndi maiko ena, onsewo ndawafikira, koma kuti abwere adzatipatse yankho, zikuvuta.
Unduna wazamalo, unduna wowona za ubale wadzikolino ndi maiko ena, onsewo ndawafikira, koma kuti abwere adzatipatse yankho, zikuvuta.
female
Anthu kuno, akufuna awuzidwe malire awo enieni, zomwe boma mpakapano silinena chilichose, silinena kuchokera chaka cha 2011.
Anthu kuno, akufuna awuzidwe malire awo enieni, zomwe boma mpakapano silinena chilichose, silinena kuchokera chaka cha tuwente ileveni.
female
Kutchetchedwa kwa chimanga ndi nkhaza chabe za anthu aku Mozambique, koma sindikukhulupirira kuti boma la Malawi litabwera ndikunena malire enieni, anthu a Malawi, angamalimbanebe ndi anthu aku Mozambique.
Kutchetchedwa kwa chimanga ndi nkhaza chabe za anthu aku Mozambique, koma sindikukhulupirira kuti boma la Malawi litabwera ndikunena malire enieni, anthu a Malawi, angamalimbanebe ndi anthu aku Mozambiki.
female
Chinanso chomwe chikuchitipweteka, mchakuti boarder sikuyenera kukhala pomwe ilipano, imayenera kukakhala kumalire kwenikweni a dzikolino ndi Mozambique osati pomwe inayikidwa pano. wadandawula Chambo.
Chinanso chomwe chikuchitipweteka, mchakuti boarder sikuyenera kukhala pomwe ilipano, imayenera kukakhala kumalire kwenikweni a dzikolino ndi Mozambiki osati pomwe inayikidwa pano. wadandawula Chambo.
female
Kusamvana pa nkhani ya malireyi, kunayamba zaka zapitazo pomwe boma la Malawi, linachita mgwirizano ndi boma la Mozambique pantchito yofuna kuwunikanso malire a maiko awiriwa omwe poyamba anagawidwa mchaka cha 1920.
Kusamvana pa nkhani ya malireyi, kunayamba zaka zapitazo pomwe boma la Malawi, linachita mgwirizano ndi boma la Mozambiki pantchito yofuna kuwunikanso malire a maiko awiriwa omwe poyamba anagawidwa mchaka cha nayintini tuwente.
female
Ndipo ntchito yowunikaso malirewa, inayambika mchaka cha 2012. A polisi ayamba kumanga omwe anatchingira msewu Chakwera ku Blantyre.
Ndipo ntchito yowunikaso malirewa, inayambika mchaka cha tuwente thulofu. A polisi ayamba kumanga omwe anatchingira msewu Chakwera ku Bulantaya.
female
Ma report osatsimikizika, akusonyezakuti a police mu mzinda wa Blantyre, amanga anthu awiri, powaganizira kuti analinawo mgulu la anamalira omwe anatchingira msewu m’dipiti wa galimoto za mtsogoleri wadzikolino.
Malipotit osatsimikizika, akusonyezakuti a polisi mu mzinda wa Bulantaya, amanga anthu awiri, powaganizira kuti analinawo mgulu la anamalira omwe anatchingira msewu m’dipiti wa galimoto za mtsogoleri wadzikolino.
female
a Lazarus Chakwera pa mphambano ya HHI ku Blantyre, koma wofalitsa nkhani za police mdzikomuno, wati atitsimikizirabe ngati mphekeserazi zili zoona.
a Lazarasi Chakwera pa mphambano ya ETCHI ETCHI AYI ku Bulantaya, koma wofalitsa nkhani za polisi mdzikomuno, wati atitsimikizirabe ngati mphekeserazi zili zoona.
female
Lachisanu lapitali kunali chifirimbiti pa mphambano ya HHI mu mzinda wa Blantyre, pomwe anamalira ena omwe ananyamula thupi la munthu wina lomwe amakaliyika m’manda a HHI mu mzindawu.
Lachisanu lapitali kunali chifirimbiti pa mphambano ya ETCHI ETCHI AYI mu mzinda wa Blantyre, pomwe anamalira ena omwe ananyamula thupi la munthu wina lomwe amakaliyika m’manda a ETCHI ETCHI AYI mu mzindawu.
female
Anayimitsa mwachipongwe mdipiti wa galimoto zoperekeza mtsogoleri wadzikolino a Chakwera. Panthawiyi a Chakwera anali akuchokera kunyumba yachifumu ya Sanjika, ndipo amathamangira kubwalo la ndege la Chileka.
Anayimitsa mwachipongwe mdipiti wa galimoto zoperekeza mtsogoleri wadzikolino a Chakwera. Panthawiyi a Chakwera anali akuchokera kunyumba yachifumu ya Sanjika, ndipo amathamangira kubwalo la ndege la Chileka.
female
Komwe amafuna kukakwera ndege, pa ulendo wawo wopita mdziko la Democratic Republic of Congo, komwe akuti ayitanidwa mwadzidzidzi ndi mtsogoleri wadzikolo.
Komwe amafuna kukakwera ndege, pa ulendo wawo wopita mdziko la Demokiratiki Repabuliki ofu kongo, komwe akuti ayitanidwa mwadzidzidzi ndi mtsogoleri wadzikolo.
female
Anamalirawa, anayimitsa mdipiyiwu ndikuyamba kuyimba nyimbo zachipongwe, amvekere mbuye timenyereni nkhondo kulimbana ndi satana , ali ndi zida zoopsa.
Anamalirawa, anayimitsa mdipiyiwu ndikuyamba kuyimba nyimbo zachipongwe, amvekere mbuye timenyereni nkhondo kulimbana ndi satana , ali ndi zida zoopsa.
female
Kenaka nkukayamba kuyimbakuti, wayimabe! wayimabe! wayimabe! Kwinaku atawunjikana pakati pa msewu wamagalasi.
Kenaka nkukayamba kuyimbakuti, wayimabe! wayimabe! wayimabe! Kwinaku atawunjikana pakati pa msewu wamagalasi.
female
Kuchititsa kakasi mzika yoyambayi, yomwe sikadachitira mwina, koma kudikirakaye kwa mphindi zingapo. Lero lachiwiri pa 23 January 2024.
Kuchititsa kakasi mzika yoyambayi, yomwe sikadachitira mwina, koma kudikirakaye kwa mphindi zingapo. Lero lachiwiri pa tuwente firi Januware tuwente tuwente-folo.
female
Anthu m’masamba a mchezo akugawana report lomwe likusonyeza kuti a police mu mzinda wa Blantyre, amanga a Pearson Chimimba azaka 48, ochokera m’mudzi mwa Magola mfumu yayikulu Njolomole m’boma la Ntcheu.
Anthu m’masamba a mchezo akugawana lipoti lomwe likusonyeza kuti a polisi mu mzinda wa Bulantaya, amanga a Piuyasoni Chimimba azaka fote-eyiti, ochokera m’mudzi mwa Magola mfumu yayikulu Njolomole m’boma la Ntcheu.
female
Komanso a Hector Ndawala azaka 38, ochokera m’mudzi mwa Katundu mfumu yayikulu Chimaliro ku Thyolo. Malingana ndi report la apolice lomwe tsamba lino lawona,
Komanso a Hekia Ndawala azaka sete eyiti, ochokera m’mudzi mwa Katundu mfumu yayikulu Chimaliro ku Thyolo. Malingana ndi lipoti la apolisi lomwe tsamba lino lawona,
female
A Chimimba akuganiziridwa kuti ankayendetsa galimoto ya mtundu wa Nissan Diseal nambala yake ZA5906, yomwe akuti inatchinga msewu, pamphambano ya HHI mu mzinda wa Blantyre.
A Chimimba akuganiziridwa kuti ankayendetsa galimoto ya mtundu wa Nisani Dizelo nambala yake Zedi e fayifi nayini ziro sikisi yomwe akuti inatchinga msewu pamphambano ya ETCHI ETCHI AYI mu mzinda wa Bulantaya.
female
Panthawi yomwe a Chakwera ankafuna kudutsa. Mbali inayi repert la apolisili lomwe lilkusonyeza kuti wodandawula ake anali a assistant superintendent Mervise Matenganya omwe ndi officer pa Blantyre police.
Panthawi yomwe a Chakwera ankafuna kudutsa. Mbali inayi lipoti la apolisili lomwe lilkusonyeza kuti wodandawula ake anali a asisitanti supurintendenti Mevisi Matenganya omwe ndi ofesala pa Bulantaya polisi.
female
Likusonyeza kuti bambo Ndawala akuganiziridwa kuti ndi m’modzi mwa anthu omwe anayambitsa kuponya miyala pamalowa. Report li lomwe pakadali pano sitingatsimikize kuti lili lowona kapena ayi.
Likusonyeza kuti bambo Ndawala akuganiziridwa kuti ndi m’modzi mwa anthu omwe anayambitsa kuponya miyala pamalowa. Lipotili lomwe pakadali pano sitingatsimikize kuti lili lowona kapena ayi.
female
Likusonyezanso kuti apolice alanda galimoto yomwe ankayendetsa bambo chimimba, ndipo akuti kafukufuku anakali nkati kusakasaka anthu ena omwe akukhudzidwa ndichipongwe chomwe mtsogoleri wadzikolinoyu anachitilidwa patsikuli.
Likusonyezanso kuti apolisi alanda galimoto yomwe ankayendetsa bambo chimimba, ndipo akuti kafukufuku anakali nkati kusakasaka anthu ena omwe akukhudzidwa ndichipongwe chomwe mtsogoleri wadzikolinoyu anachitilidwa patsikuli.
female
Koma titayimbira phone wofalitsa nkhani za police m’dzikomuno a Peter Kalata, kuti atsimikizire za nkhaniyi, atiwuza kuti nawonso adziwa za nkhaniyi kudzera pamasamba a mchezo
Koma titayimbira foni wofalitsa nkhani za polisi m’dzikomuno a Pita Kalata, kuti atsimikizire za nkhaniyi, atiwuza kuti nawonso adziwa za nkhaniyi kudzera pamasamba a mchezo
female
Ndipo apempha kuti tiwapatse kaye nthawi kuti afufuze ngati izi zilidi chomwecho, kapena ayi. Anthu mdera la Gundani m town ya Kasungu, anakhamukira kunyumba yamayi wina.
Ndipo apempha kuti tiwapatse kaye nthawi kuti afufuze ngati izi zilidi chomwecho, kapena ayi. Anthu mdera la Gundani mtawuni ya Kasungu, anakhamukira kunyumba yamayi wina.
female
Yemwe akumuganizira kuti watentha manja a mwana yemwe amakhalanaye, kamba koti wadya mbatatesi osapempha. Mwanayu akuti anamukanikiza pa chiwaya chopanda kanthu, chomwe anachitenthetsa pamoto.
Yemwe akumuganizira kuti watentha manja a mwana yemwe amakhalanaye, kamba koti wadya mbatatesi osapempha. Mwanayu akuti anamukanikiza pa chiwaya chopanda kanthu, chomwe anachitenthetsa pamoto.
femae
A group a Gundani a mderali omwe anathamangira pamalopo, ati mwanayu, watuluka matuza m’manja ndipo aliso ndi matuza mthupi omwe akuti mayiyu anamukwapula.
Agurupu a Gundani a mderali omwe anathamangira pamalopo, ati mwanayu, watuluka matuza m’manja ndipo aliso ndi matuza mthupi omwe akuti mayiyu anamukwapula.
female
Anthu wokhala mozungulira ndi nyumba yamayiyu, ndiwo anakanena kwa mfumuyi, atapeza mwanayo akulira, apolisi anathamangira kumaloko, ndipo atenga mayiyo pomuteteza kwa anthu wolusa.
Anthu wokhala mozungulira ndi nyumba yamayiyu, ndiwo anakanena kwa mfumuyi, atapeza mwanayo akulira, apolisi anathamangira kumaloko, ndipo atenga mayiyo pomuteteza kwa anthu wolusa.
female
Bungwe lomenyera ndi kulimbikitsa ufulu wa anthu okalamba mdziko lino la MANEPO, lati ganizo lofuna kutengera ku nyumba ya malamulo bill yoti malamulo a mdziko lino asamavomereze aliyense wopsola zaka 80,
Bungwe lomenyera ndi kulimbikitsa ufulu wa anthu okalamba mdziko lino la MANEPO, lati ganizo lofuna kutengera ku nyumba ya malamulo bilu yoti malamulo a mdziko lino asamavomereze aliyense wopsola zaka eyite,
Kupikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wadzikolino, mtsogoleri wadziko ndi lolakwika komanso lili ndikuthekera kokonzera nkhaza kwa anthu otere mdzikomuno.
Kupikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wadzikolino, mtsogoleri wadziko ndi lolakwika komanso lili ndikuthekera kokonzera nkhaza kwa anthu otere mdzikomuno.
female
Mkulu wa MANEPO a Andrew Kavala ati ganizoli ndi lotsutsana ndi ulamuliro wa democracy komanso ndilobwezeretsa m’mbuyo chitukuko chadziko, kamba koti ena samatenganawo gawo pazinthu zofunika.
Mkulu wa MANEPO a Anduru Kavala ati ganizoli ndi lotsutsana ndi ulamuliro wa demokirase komanso ndilobwezeretsa m’mbuyo chitukuko chadziko, kamba koti ena samatenganawo gawo pazinthu zofunika.
female
Iwo ati palibe umboni wokuti muthu wopsyola zaka 80, sangayendetse bwino dziko, kapena kutumikira mu ntchito zopititsa chitukuko cha dziko.
Iwo ati palibe umboni wokuti muthu wopsyola zaka 80, sangayendetse bwino dziko, kapena kutumikira mu ntchito zopititsa chitukuko cha dziko.
female
A Kavala ati akutsatira zomwe anthu akukambirana m’masamba amchezo, ndipo akupempha nyumba yamalamulo, kuti isachite zinthu zomwe zithandizire kuphwanya ufulu wa anthu wokalamba mdziko muno.
A Kavala ati akutsatira zomwe anthu akukambirana m’masamba amchezo, ndipo akupempha nyumba yamalamulo, kuti isachite zinthu zomwe zithandizire kuphwanya ufulu wa anthu wokalamba mdziko muno.
female
Bwalo lalikulu la milandu la High Court lapereka masiku 21, kuti mbali zonse zokhudzidwa pa mlandu wakuphedwa kwa mwana wakhungu la chi albino wazaka zitatu Talandira Chirwa m’boma la Kasungu.
Bwalo lalikulu la milandu la Hayi khoti lapereka masiku tuwente-wani, kuti mbali zonse zokhudzidwa pa mlandu wakuphedwa kwa mwana wakhungu la chi alibino wazaka zitatu Talandira Chirwa m’boma la Kasungu.
female
Zipereke zikalata zawo zomaliza pa mulanduwu. Justice Bruno Kalemba, wati bwaloli lidzapereka chigamulo pa mulanduwo pambuyo pamasiku 14, akalandira zikalata za mulanduwu kuchoka kumbali zomnse.
Zipereke zikalata zawo zomaliza pa mulanduwu. Jasitisi Buruno Kalemba, wati bwaloli lidzapereka chigamulo pa mulanduwo pambuyo pamasiku fotini, akalandira zikalata za mulanduwu kuchoka kumbali zomnse.
female
Woyimira boma pamulanduwu, Senior State Advocate Festace Sakanda, wati ndiwokhutira ndi momwe mulanduwu wayendera, ponena kuti anali mwa anthu asanu ndi m’modzi (6) omwe akuyankha mulanduwu.
Woyimira boma pamulanduwu, Siniyo Siteti Adivoketi Fesitasi Sakanda, wati ndiwokhutira ndi momwe mulanduwu wayendera, ponena kuti anali mwa anthu asanu ndi m’modzi (sikisi) omwe akuyankha mulanduwu.
female
Anapezeka kale wolakwa atavomera mulanduwu ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti awiri ena wotsalawa, bwalo liwapezaso wolakwa, potsatira umboni womwe waperekedwa.
Anapezeka kale wolakwa atavomera mulanduwu ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti awiri ena wotsalawa, bwalo liwapezaso wolakwa, potsatira umboni womwe waperekedwa.
female
Talandira Chirwa adaphedwa pa 30 November 2022, m’mudzi mwa Mawawa mdera la mfumu Chulu pomwe anthuwa adathyola nyumba yomwe amagonamo ndi agogo ake, ndikumubaya pakhosi, kenako ndikumudula nkuno ndikuthawa nawo
Talandira Chirwa adaphedwa pa sete Novemba tuwente tuwente-thu, m’mudzi mwa Mawawa mdera la mfumu Chulu pomwe anthuwa adathyola nyumba yomwe amagonamo ndi agogo ake, ndikumubaya pakhosi, kenako ndikumudula nkuno ndikuthawa nawo
female
Mawu ake mtsogoleri wabungwe la anthu akhungu la chi albino la ALBAM, Young Muhamba, wati ndiwokhutira ndi momwe milandu ya anthu wochitira nkhaza anthu akhungu la chi albino ikuyendera.
Mawu ake mtsogoleri wabungwe la anthu akhungu la chi alibino la APAMu, Yang'i Muhamba, wati ndiwokhutira ndi momwe milandu ya anthu wochitira nkhaza anthu akhungu la chi alibino ikuyendera.
female
Ena mwa woganiziridwawo ndi bambo ake womupeza Mostain Mumba, agogo ake akazo Joyce Nkhoma ndi Jeremiah Nkhoma, Keneth Zimba komaso Charles Chipeta.Ena mwa woganiziridwawo ndi bambo ake womupeza Mostain Mumba, agogo ake akazo Joyce Nkhoma ndi Jeremiah Nkhoma, Keneth Zimba komaso Charles Chipeta.
Ena mwa woganiziridwawo ndi bambo ake womupeza Mositeni Mumba, agogo ake akazo Joyisi Nkhoma ndi Jeremayh Nkhoma, Kenefi Zimba komanso Tchalosi Chipeta.
female
Nduna yofalitsa uthenga Moses Kunkuyu, yati boma lili ndi lingaliro lokhala ndi nthambi yapadera pansi pa unduna wowona zantchito yomwe iyike ndondomeko zomwe zingathandizire ma khonsolo mdzikomuno.
Nduna yofalitsa uthenga Mozesi Kunkuyu, yati boma lili ndi lingaliro lokhala ndi nthambi yapadera pansi pa unduna wowona zantchito yomwe iyike ndondomeko zomwe zingathandizire ma khonsolo mdzikomuno.
female
Kupeza anthu omwe azipita maiko akunja, kukagwira ntchito zosiyanasiyana. Kunkuyu wati boma pamodzi ndi dziko la Israel.
Kupeza anthu omwe azipita maiko akunja, kukagwira ntchito zosiyanasiyana. Kunkuyu wati boma pamodzi ndi dziko la Izirayelo.
female
Ali mkati mowunikira komaso kumalizitsa mapepala amgwirizano wokhudza kupeza anthu okagwira ntchito mdzikoli, kuti boma liziyendetsa ntchitoyi m’malo mwa ma agent.
Ali mkati mowunikira komaso kumalizitsa mapepala amgwirizano wokhudza kupeza anthu okagwira ntchito mdzikoli, kuti boma liziyendetsa ntchitoyi m’malo mwa ma ejenti.
female
Iye wati, njira yomwe ikugwiritsiridwa ntchito pakadalipano, yopezera anthu okagwira ntchito m’mayiko akunja, siyomwe boma likufuna kutsatira.
Iye wati, njira yomwe ikugwiritsiridwa ntchito pakadalipano, yopezera anthu okagwira ntchito m’mayiko akunja, siyomwe boma likufuna kutsatira.
female
Izi zadziwika, pamwambo wokumbukira kuti wireless ya m’mudzi ya Nkhotakota, yakwanitsa zaka 20, chikhazikitsireni mchaka cha 2003.
Izi zadziwika, pamwambo wokumbukira kuti wayilesi ya m’mudzi ya Nkhotakota, yakwanitsa zaka tuwente, chikhazikitsireni mchaka cha tuwente ziro firi.
female
Koma kumbali yake, mkhalapampando wa board ya wireless ya Nkhotakota a Milward Kamanga, wati zaka 20, zowulutsa ndi kufalitsa mawu, zakhala za kasakaniza, pomwe akumana ndi zabwino ndi zobetchera.
Koma kumbali yake, mkhalapampando wa bodi ya wayilesi ya Nkhotakota a Miliwadi Kamanga, wati zaka tuwent zowulutsa ndi kufalitsa mawu, zakhala za kasakaniza, pomwe akumana ndi zabwino ndi zobetchera.
female
Ndipo wapempha boma kuti lithandize kupereka ntchito zomwe zingathandizire kutukula wayilesiyi. Unduna wazawumoyo, wapempha mabungwe omwe siaboma ndi adindo osiyanasiyana kuti ayikepo chidwi.
Ndipo wapempha boma kuti lithandize kupereka ntchito zomwe zingathandizire kutukula wayilesiyi. Unduna wazawumoyo, wapempha mabungwe omwe siaboma ndi adindo osiyanasiyana kuti ayikepo chidwi.
female
Pankhani yolimbana ndi nthenda ya Cancer, popeza njira zomwe zingathandizire kuthana ndi vutoli kwa mtheradi. Mawu ake akudza kutsatira tsiku lokumbukira tsiku lothetsa nthenda ya Cancer.
Pankhani yolimbana ndi nthenda ya Khansa, popeza njira zomwe zingathandizire kuthana ndi vutoli kwa mtheradi. Mawu ake akudza kutsatira tsiku lokumbukira tsiku lothetsa nthenda ya Khansa.
female
Lomwe limakumbulidwa pa 4 February, chaka chilichonse, ndipo mutu wake wa chakachino ndiwoti, kufunikira kogwira ntchito limodzi, pofuna kuthetsa nthenda ya Cancer.
Lomwe limakumbulidwa pa folo Feburuware, chaka chilichonse, ndipo mutu wake wa chakachino ndiwoti, kufunikira kogwira ntchito limodzi, pofuna kuthetsa nthenda ya Khansa.
female
Malingana ndi mlembi mu unduna wazawumoyo Dr. Samson Mndolo, pafupifupi chiwerengero cha anthu okwana 19,000,000, Amapezeka ndi nthendayi pa dzikolonse lapansi.
Malingana ndi mlembi mu unduna wazawumoyo Dokota. Samusoni Mndolo, pafupifupi chiwerengero cha anthu okwana nayintini miliyoni, Amapezeka ndi nthendayi pa dzikolonse lapansi.
female
Ndipafupifupi anthu 20,000,000, amamwalira ndi nthendayi, chakachilichonse, ndipo imfa zambiri, zimachitika mayiko osawuka.
Ndipafupifupi anthu tuwente miliyoni, amamwalira ndi nthendayi, chakachilichonse, ndipo imfa zambiri, zimachitika mayiko osawuka.
female
Dr, Mndolo, ati vuto la Cancer mdzikomuno, limathandizira kudzetsa imfa za anthu 50 pa 100 iliyonse, kutsatira matenda osapatsirana.
Dokota, Mndolo, ati vuto la Khansa mdzikomuno, limathandizira kudzetsa imfa za anthu fifite pa wani handiredi iliyonse, kutsatira matenda osapatsirana.
female
Ndipo mitundu ya Cancer yomwe imapha anthu, ndimonga Cancer yakhomo lachiberekero, koposa sacomer ndi Cancer ya m’mawere mwazina. Iye wawonjezera kuti boma likuchita zothekera kufuna kuthana ndi nthendayi.
Ndipo mitundu ya khansa yomwe imapha anthu, ndimonga khansa yakhomo lachiberekero, koposa sakoma ndi khansa ya m’mawere mwazina. Iye wawonjezera kuti boma likuchita zothekera kufuna kuthana ndi nthendayi.
female
Ndipo ili ndi ndondomeko, zomwe zikutsatidwa, kuti nthendayi ithe. Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo chapakati, Uladi Mussa,
Ndipo ili ndi ndondomeko, zomwe zikutsatidwa, kuti nthendayi ithe. Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DIPIPI mchigawo chapakati, Uladi Musa,
female
Lero walandiridwa mchipani cha MCP, pa msonkhano wa chitukuko, omwe mtsogoleri wadzikolino Dr Lazarus Chakwera akuchititsa m’boma la Salima.
Lero walandiridwa mchipani cha EMUSIPI, pa msonkhano wa chitukuko, omwe mtsogoleri wadzikolino DOKOTA Lazarasi Chakwera akuchititsa m’boma la Salima.
female
Poyankhula pa msonkhanowu, Mussa wati wathandizira chipani cha MCP, mosatopa, iye anati, ena mukungoyankhula kuti a Mussa ndi woyendayenda, koma ndikuwuzeni, munthu umayenda pa chifukwa.
Poyankhula pa msonkhanowu, Musa wati wathandizira chipani cha EMUSIPI, mosatopa, iye anati, ena mukungoyankhula kuti a Musa ndi woyendayenda, koma ndikuwuzeni, munthu umayenda pa chifukwa.
female
Ndinakhala kundende ine zaka zitatu sinatuluke chipani cha DPP, ngakhale kuti a Chakwera ndiomwe ananditulutsa kundende, kenako muzindiwuza kuti ndiyime mchipani miyezi 9, ndisanachite chilichonse, ndidikire ine ndiri ndi mimba?
Ndinakhala kundende ine zaka zitatu sinatuluke chipani cha DIPIPI, ngakhale kuti a Chakwera ndiomwe ananditulutsa kundende, kenako muzindiwuza kuti ndiyime mchipani miyezi nayini, ndisanachite chilichonse, ndidikire ine ndiri ndi mimba?
female
Anafunsa choncho a Mussa. Iye wamema anthu kuti alowe chipani cha MCP, chomwe malingana ndi Mussa ndi chakolo onse mdzikomuno.
Anafunsa choncho a Musa. Iye wamema anthu kuti alowe chipani cha EMUSIPI, chomwe malingana ndi Musa ndi chakolo onse mdzikomuno.
female
Mussa analandulidwa kukhala mndende kwazaka zisanu, kamba kopereka ziphaso za uzika komanso zoyendera kwa zika zamayiko ena, koma anatulutsidwa atakhululukiridwa munyengo ya Pasaka, chaka chatha atakhalako zaka zitatu.
Musa analandulidwa kukhala mndende kwazaka zisanu, kamba kopereka ziphaso za uzika komanso zoyendera kwa zika zamayiko ena, koma anatulutsidwa atakhululukiridwa munyengo ya Pasaka, chaka chatha atakhalako zaka zitatu.
female