audio
audioduration (s)
1.12
18.5
raw_text
stringlengths
1
297
normalized_text
stringlengths
1
267
gender
stringclasses
16 values
asapeze phindu lochuluka pa ulimiwawo. Ngakhale pali kudandawulaku, unduna wazawulimi, watsimikizira anthu mdzikomuno, kuti palibe yemwe amfe ndi njala, potengera kuti ayika ndondomeko zochuluka zothanirana ndi vutoli.
asapeze phindu lochuluka pa ulimiwawo. Ngakhale pali kudandawulaku, unduna wazawulimi, watsimikizira anthu mdzikomuno, kuti palibe yemwe amfe ndi njala, potengera kuti ayika ndondomeko zochuluka zothanirana ndi vutoli.
female
Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma mnyumba yamalamulo, Kondwani Nankhumwa, wadzudzula ndondomeko zomwe boma lati layika pofuna kuthandizira kuti a Malawi asavutike kwambiri.
Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma mnyumba yamalamulo, Kondwani Nankhumwa, wadzudzula ndondomeko zomwe boma lati layika pofuna kuthandizira kuti a Malawi asavutike kwambiri.
female
Ndikuchepetsedwa mphavu kwa ndalama yakwacha, ndi 47%, ponena kuti asiya zinazofunikira kwambiri.
Ndikuchepetsedwa mphavu kwa ndalama yakwacha, ndi fote folo peresenti, ponena kuti asiya zinazofunikira kwambiri.
female
Iye amayankhulapo pazomwe nduna yazachuma Simplex Chitchola Banda, yayankhula lero mnyumba yamalamulo pankhani yokhudza chuma cha dzikolino.
Iye amayankhulapo pazomwe nduna yazachuma Simpulekisi Chitchola Banda, yayankhula lero mnyumba yamalamulo pankhani yokhudza chuma cha dzikolino.
female
Nankhumwa akugwirizana ndimabungwe omenyera ufulu wa anthu mdzikomuno, kuti boma layiwala kuchepetsa mawulendo adzikolino, omwe ati afika kale 40, chiloweleni m’boma.
Nankhumwa akugwirizana ndimabungwe omenyera ufulu wa anthu mdzikomuno, kuti boma layiwala kuchepetsa mawulendo adzikolino, omwe ati afika kale fote, chiloweleni m’boma.
female
Zomwe ati zawononga ndalama zakunja mdzikomuno. Iye wati ngati boma likuti ndondomekozi zayikidwa pofuna kuthandiza a Malawi, likadakhazikitsa ndalama yakwacha isanatsike mphavu.
Zomwe ati zawononga ndalama zakunja mdzikomuno. Iye wati ngati boma likuti ndondomekozi zayikidwa pofuna kuthandiza a Malawi, likadakhazikitsa ndalama yakwacha isanatsike mphavu.
female
Phungu wanyumba yamalamulo m’dera lakumwera chakumawa mu mzinda wa Blantyre Samir Suleiman, wati Simplex Chitchola Banda, sakuyenera kukhala nduna yazachuma yadzikolino.
Phungu wanyumba yamalamulo m’dera lakumwera chakumawa mu mzinda wa Bulantaya Samiye Suleyimani, wati Simpulekisi Chitchola Banda, sakuyenera kukhala nduna yazachuma yadzikolino.
female
Suleiman wawuza nyumba yamalamulo kuti Chitchola Banda, anakhudzidwa ndi nkhani yosakadza chuma chomwe chimayenera kuthandiza atsikana ndi amayi achichepere, zaka zapitazo.
Suleyimani wawuza nyumba yamalamulo kuti Chitchola Banda, anakhudzidwa ndi nkhani yosakadza chuma chomwe chimayenera kuthandiza atsikana ndi amayi achichepere, zaka zapitazo.
female
Izi zinadzetsa mpungwepungwe mnyumba yamalamulo. Ndipo wachiwiri kwa sipikala wa nyumba yamalamulo Madalitso Kazombo, walamula kuti Suleiman, abweretse umboni wankhaniyi.
Izi zinadzetsa mpungwepungwe mnyumba yamalamulo. Ndipo wachiwiri kwa sipikala wa nyumba yamalamulo Madalitso Kazombo, walamula kuti Suleyimani, abweretse umboni wankhaniyi.
female
Chitchola Banda, wakana zakukhudzidwa kwake pankhaniyi. Ndipo wati izi ndindale chabe. Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Centre For Democracy and Economic Development Initiative CEDEDI.
Chitchola Banda, wakana zakukhudzidwa kwake pankhaniyi. Ndipo wati izi ndindale chabe. Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Senta fo Demokirase andi Ikonomiki Divelopumenti Inishiyativi (SIDEDI).
female
Lati mawulendo osatha omwe mtsogoleri wadzikolino, Dr Lazarus Chakwera akukhalanawo, ndiomwe achititsa kuti dzikolino, livutike pankhani yazachuma.
Lati mawulendo osatha omwe mtsogoleri wadzikolino, Dr Lazarus Chakwera akukhalanawo, ndiomwe achititsa kuti dzikolino, livutike pankhani yazachuma.
female
Mkulu wa Bungwe la CEDEDI, Sylvester Namiwa, wawuza Umunthu FM, kuti mawulendowa achititsa kuti ndalama zakunja zisowe mdzikomuno, powonjezera kuti ndalama zomwe boma limanena kuti lapeza pa ulondowa.
Mkulu wa Bungwe la SIDEDI, Silivesita Namiwa, wawuza Umunthu EFU EMU, kuti mawulendowa achititsa kuti ndalama zakunja zisowe mdzikomuno, powonjezera kuti ndalama zomwe boma limanena kuti lapeza pa ulondowa.
female
Sizithandiza nkomwe kupititsa patsogolo chuma chadzikolino. Iye pakadalipano, boma la Tonse lotsogozedwa ndi Dr Chakwera, lalephera kuthana ndi mavuto omwe dzikolino likukumana nawo.
Sizithandiza nkomwe kupititsa patsogolo chuma chadzikolino. Iye pakadalipano, boma la Tonse lotsogozedwa ndi Dokota Chakwera, lalephera kuthana ndi mavuto omwe dzikolino likukumana nawo.
female
Ponena kuti kutsitsa mphavu kwa ndalama yakwacha, sikunayambe kwathandizapo dzikolino. Koma boma lati sililola kuti a Malawi avutike, pomwe lili kalikiliki, wokonzanso chuma cha dzikolino.
Ponena kuti kutsitsa mphavu kwa ndalama yakwacha, sikunayambe kwathandizapo dzikolino. Koma boma lati sililola kuti a Malawi avutike, pomwe lili kalikiliki, wokonzanso chuma cha dzikolino.
female
Chiwerengero cha anthu padzikolonse lapansi tsopano chadutsa 8.000,000,000. pomwenso zikuwonetsa kuti mulingo wa anthu wokhalila moyo ukunka nukwera, ngakhale dzikolapansi layika njira zambiri zofuna kuchepetsa chiwerengerochi.
Chiwerengero cha anthu padzikolonse lapansi tsopano chadutsa eyiti biliyoni. pomwenso zikuwonetsa kuti mulingo wa anthu wokhalila moyo ukunka nukwera, ngakhale dzikolapansi layika njira zambiri zofuna kuchepetsa chiwerengerochi.
female
Izi zanenedwa ndi nthambi yowona za chiwerengero cha anthu padzikolonse lapansi, lomwe likululake lili mdziko la America.
Izi zanenedwa ndi nthambi yowona za chiwerengero cha anthu padzikolonse lapansi, lomwe likululake lili mdziko la Amerika.
female
Bungwe la mgwirizano wamayiko a padziko lapansi la United Nations, lati chiwerengerochi ndichomwe chidawerengedwa pofika pa 22 November chaka cha 2022.
Bungwe la mgwirizano wamayiko a padziko lapansi la Yunayitedi Neshonzi, lati chiwerengerochi ndichomwe chidawerengedwa pofika pa tuwente-thu Novembala chaka cha tuwente tuwente-thu.
female
Ndipo tsiku limeneli lidapatsidwa dzina loti Tsiku lokwana anthu 8.000,000,000. Bungweri lati chiwerengero chikhoza kukhala chocheperako.
Ndipo tsiku limeneli lidapatsidwa dzina loti Tsiku lokwana anthu eyiti biliyoni. Bungweri lati chiwerengero chikhoza kukhala chocheperako.
female
Kamba koti mayiko ena amapereka ndondomeko yachiwerengero chawo mochedwerapokomaso ena samapereka. Mlembi wamkulu wa bungwe la Minbus Owners Association of Malawi MOAM Cox-ley Kamange,
Kamba koti mayiko ena amapereka ndondomeko yachiwerengero chawo mochedwerapokomaso ena samapereka. Mlembi wamkulu wa bungwe la Minibasi Onazi Asosiyeshoni ofu Malawi MOAMU Kokisile Kamange,
female
Wapempha boma kuti lichilimike popititsa patsogolo ndondomeko yolowetsa mafuta agalimoto mdzikomuno, kuchokera m’mayiko akunja kudzera pa sitima zapamtunda njanji.
Wapempha boma kuti lichilimike popititsa patsogolo ndondomeko yolowetsa mafuta agalimoto mdzikomuno, kuchokera m’mayiko akunja kudzera pa sitima zapamtunda njanji.
female
Iye akuwona kuti, izi zitha kuthandizira kuti mtengo wobweretsera mafuta mdzikomuno, uzikhala otsika. Zomwe zingachititsenso kuti mafutawa azigulidwanso pa mitengo yabwino mdzikomuno.
Iye akuwona kuti, izi zitha kuthandizira kuti mtengo wobweretsera mafuta mdzikomuno, uzikhala otsika. Zomwe zingachititsenso kuti mafutawa azigulidwanso pa mitengo yabwino mdzikomuno.
female
Kutsatira madando oti mitengo yokwerera galimoto yakwera kamba kakutsika mphavu kwa ndalama yakwacha, Kamange wapemphanso eni ma minibus kuti asakwezere dala mopsola muyeso mitengoyi .
Kutsatira madando oti mitengo yokwerera galimoto yakwera kamba kakutsika mphavu kwa ndalama yakwacha, Kamange wapemphanso eni ma minibasi kuti asakwezere dala mopsola muyeso mitengoyi .
female
Pakadali pano boma silidayankhepo kanthu pankhaniyi. Mphenzi yapha bambo wina wazaka 27, Mavuto Kaputa, ku Lumbadzi mu mzinda wa Lilongwe.
Pakadali pano boma silidayankhepo kanthu pankhaniyi. Mphenzi yapha bambo wina wazaka tuwente-seveni, Mavuto Kaputa, ku Lumbadzi mu mzinda wa Lilongwe.
female
Malingana ndi mneneri wa police ya Lumbadzi Sargent Felix Kunyani, bamboyu anawombedwa ndi mpheziyi pa 9 mwenzi uno, m’mudzi mwa Kalipande dera la mfumu Chitukula mu mzindawu, pomwe amachokera kuntchito.
Malingana ndi mneneri wa polisi ya Lumbadzi Sajenti Felikisi Kunyani, bamboyu anawombedwa ndi mpheziyi pa nayini mwenzi uno, m’mudzi mwa Kalipande dera la mfumu Chitukula mu mzindawu, pomwe amachokera kuntchito.
female
Iye amagwira ntchito ngati mulonda pa company ya Central Poultry limited, ndipo panthawiyi nkuti ali pa njinga yake yakapalasa.
Iye amagwira ntchito ngati mulonda pa kampani ya Senturo Potire limitedi, ndipo panthawiyi nkuti ali pa njinga yake yakapalasa.
female
Zotsatira za kuchipatala chaching’ono cha Lumbadzi, zawonetsa kuti Kaputa wafa kamba ka nyesi ya mphezi. Kaputa anali wam’mudzi mwa kunsensa mdera la mfumu Chitukula ku Lumbadzi mu mzinda wa Lilongwe.
Zotsatira za kuchipatala chaching’ono cha Lumbadzi, zawonetsa kuti Kaputa wafa kamba ka nyesi ya mphezi. Kaputa anali wam’mudzi mwa kunsensa mdera la mfumu Chitukula ku Lumbadzi mu mzinda wa Lilongwe.
female
Bungwe la Feed the Children, lati ndilokhudzidwa ndi vuto la kunyentchera lomwe lakhudza kwambiri ana komanso amayi oyembekezera, m’boma la Nkhotakota.
Bungwe la Fidi dhe Chudireni, lati ndilokhudzidwa ndi vuto la kunyentchera lomwe lakhudza kwambiri ana komanso amayi oyembekezera, m’boma la Nkhotakota.
female
Mkulu wowona ntchito zosiyanasiyana ku bungweri Chimwemwe Nyasulu, wanena izi pomwe amafotokozera committee yayikulu ya chitukuko ya m’bomali, zokhudza ntchito yapadera yotchedwa akule ndi thanzi.
Mkulu wowona ntchito zosiyanasiyana ku bungweri Chimwemwe Nyasulu, wanena izi pomwe amafotokozera komiti yayikulu ya chitukuko ya m’bomali, zokhudza ntchito yapadera yotchedwa akule ndi thanzi.
female
Yomwe ikhazikitsidwe m’madera amfumu Kafuzira komanso Kanyenda. Iye wati ngati vuto lonyentchera silingathetsedwe, zitha kupangitsa kuti amayi abereke ana omwe angadzakhalenso ndi vuto pophunzira zinthu.
Yomwe ikhazikitsidwe m’madera amfumu Kafuzira komanso Kanyenda. Iye wati ngati vuto lonyentchera silingathetsedwe, zitha kupangitsa kuti amayi abereke ana omwe angadzakhalenso ndi vuto pophunzira zinthu.
female
Bungwe la Feed the Children, likugwira ntchitoyi, yomwe ikufuna kulimbana ndi vuto lonyentchera, pakati pa ana komanso amayi oyembekezera, ndi thandizo landalama kuchokera ku bungwe lachitukuko la mdziko la United States of America.
Bungwe la Fidi dhe Chudireni, likugwira ntchitoyi, yomwe ikufuna kulimbana ndi vuto lonyentchera, pakati pa ana komanso amayi oyembekezera, ndi thandizo landalama kuchokera ku bungwe lachitukuko la mdziko la Yunayitedi Sitetsi ofu Amerika.
female
Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority MERA, Lakweza mitengo yamagetsi ndi mafuta agalimoto mdzikomuno. Izi ndi malingana ndi mkhalapampando wa board ya mbungweri, Reckford Kampanje.
Bungwe la Malawi Eneje Reguletare Oforite (MERA), lakweza mitengo yamagetsi ndi mafuta agalimoto mdzikomuno. Izi ndi malingana ndi mkhalapampando wa bodi ya mbungweri, Rekifodi Kampanje.
female
Zadza kamba kakutsika mphavu kwa ndalama ya kwacha. Pano magetsi afika pa K173.70t kuchoka pa K123.26t pa kilowatt.
Zadza kamba kakutsika mphavu kwa ndalama ya kwacha. Pano magetsi afika pa wani handiredi andi sevente firi kwacha sevente tambala kuchoka pa wani handiredi andi tuwente-firi kwacha tuwente-sikisi tambala pa kilowati.
female
Kumbali ina, Mafuta a Petrol tsopano ali pa K2530.00, pa litre, kuchoka pa K1746.00.
Kumbali ina, Mafuta a Peturo tsopano ali pa thu sauzandi fayifi handiredi and sete kwacha, pa lita, kuchoka pa wani sauzandi seveni handiredi andi fote-sikisi.
female
Zomwe zikuyimira kukwera kwa pafupifupi 45kwacha pa 100 kwacha iliyonse. Diseal tsopano, azigulitsidwa pa mtengo wa 2734 kwacha.
Zomwe zikuyimira kukwera kwa pafupifupi fote-fayifi kwacha pa wani handiredi kwacha iliyonse. Dizilo tsopano, azigulitsidwa pa mtengo wa thu sauzandi seveni handiredi and sete folo kwacha.
female
Kuchoka pa 1920 kwacha pa litre, kukwera pafupifupi 42 kwacha pa 100 kwacha iliyonse.
Kuchoka pa wani sauzandi nayini handiredi andi tuwente kwacha pa lita, kukwera pafupifupi fote-thu kwacha pa handiredi kwacha iliyonse.
female
Apolice ku Nkhotakota, amanga anthu asanu, kamba kowaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya Saidi Nkhumba yapalasa.
Apolisi ku Nkhotakota, amanga anthu asanu, kamba kowaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya Saidi Nkhumba yapalasa.
female
Wazaka 22, yemwe anafa pa 6, mwenzi uno, m’mudzi wa Katongola, m’boma la Nkhotakota.
Wazaka tuwente-thu, yemwe anafa pa sikisi, mwenzi uno, m’mudzi wa Katongola, m’boma la Nkhotakota.
female
Mneneri wa police ya Nkhotakota Paul Malimwe, wati mwa omangidwawa, atatu ndi amuna pomwe awiri ndi akazi.
Mneneri wa polisi ya Nkhotakota Poo Malimwe, wati mwa omangidwawa, atatu ndi amuna pomwe awiri ndi akazi.
female
Anthuwa omwe ndi Chikumbutso Chithumba, Mike Chithumba, Samson Biziwick, Bindala Malandi ndi Eveless Essau.
Anthuwa omwe ndi Chikumbutso Chithumba, Mayiki Chithumba, Samusoni Biziwiki, Bindala Malandi ndi Evelesi Esawu
female
Amaganizira kuti Nkhumbayapalasa, anaba lamya mnyumba ya m’modzi mwa woganiziridwawa. Iwo anamtengera kunyumba kwawo, komwe anakamumanga ndikuyamba kumumenya mpaka kukomoka ndi kumusiya pamalo pomwe amamumenyera.
Amaganizira kuti Nkhumbayapalasa, anaba lamya mnyumba ya m’modzi mwa woganiziridwawa. Iwo anamtengera kunyumba kwawo, komwe anakamumanga ndikuyamba kumumenya mpaka kukomoka ndi kumusiya pamalo pomwe amamumenyera.
female
Atapeza mphamvu,anakwanitsa kufika kunyumba kwawo, komwe anamutengera ku chipatala cha Mwansambo, koma anafa ali mnjira. Ndipo zotsatira za chipatalazi,
Atapeza mphamvu,anakwanitsa kufika kunyumba kwawo, komwe anamutengera ku chipatala cha Mwansambo, koma anafa ali mnjira. Ndipo zotsatira za chipatalazi,
female
Zinawonetsa kuti imfayi. inadza kamba ka kumenyedwa komaso mabala owotchedwa ndi moto. Izi zitachitika, oganiziridwawa, anathawa, koma amangidwa atabwerera m’mudzimwawo pa 8, mwenzi uno.
Zinawonetsa kuti imfayi. inadza kamba ka kumenyedwa komaso mabala owotchedwa ndi moto. Izi zitachitika, oganiziridwawa, anathawa, koma amangidwa atabwerera m’mudzimwawo pa eyiti, mwenzi uno.
female
Ndipo akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa, kukayankha mulandu wakupha munthu. Banja lina lamangidwa m’boma la Nkhotakota poliganizira kuti limafuna kugulitsa pakati, mimba.
Ndipo akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa, kukayankha mulandu wakupha munthu. Banja lina lamangidwa m’boma la Nkhotakota poliganizira kuti limafuna kugulitsa pakati, mimba.
female
Mneneri wapolice ku Nkhotakota Paul Malimwe, wati awiriwa ndi Frank Malaki wazaka 23 komanso mkaziwake Enita Joseph, wazaka 20. Malingana ndi Malimwe.
Mneneri wapolisi ku Nkhotakota Poo Malimwe, wati awiriwa ndi Furanki Malaki wazaka tuwente-firi komanso mkaziwake Enita Jozefe, wazaka tuwente. Malingana ndi Malimwe.
female
Awiriwa omwe ali pa banja ndipo ali ndi ana awiri komanso mkaziyu ndi woyembekezera, pa 7 mwenziwuno, anapita kwa munthu wina wochita malonda kukamutsatsa kuti awagule mimba ya mkaziyo.
Awiriwa omwe ali pa banja ndipo ali ndi ana awiri komanso mkaziyu ndi woyembekezera, pa seveni mwenziwuno, anapita kwa munthu wina wochita malonda kukamutsatsa kuti awagule mimba ya mkaziyo.
female
Pa ndalama zokwana 200.000 kwacha, ati pofuna kubweza ndalama kugulu la banki mkhonde. Iye wati wamalondayu anachita tsemwe atava izi, koma banjali limakakamira kuti likhoza kuchotsa pakatipa.
Pa ndalama zokwana thu handiredi kwacha, ati pofuna kubweza ndalama kugulu la banki mkhonde. Iye wati wamalondayu anachita tsemwe atava izi, koma banjali limakakamira kuti likhoza kuchotsa pakatipa.
female
Ngati angavomere kupereka ndalamayo. Kenaka anakaneneza za nkhaniyi pa police ya Mkayika, koma apolicewa anagwirizana ndi munthu wina kuti aliwuze banjali.
Ngati angavomere kupereka ndalamayo. Kenaka anakaneneza za nkhaniyi pa polisi ya Mkayika, koma apolisiwa anagwirizana ndi munthu wina kuti aliwuze banjali.
female
Kuti lidzatenge ndalama kwa agent wa Airtel money pamalo ochitira malonda a Mkayika, ndipo apolice amanga banjali litafika pamalowa.
Kuti lidzatenge ndalama kwa ajenti wa eyatelo mane pamalo ochitira malonda a Mkayika, ndipo apolisi amanga banjali litafika pamalowa.
female
Malaki ndi wamudzi mwa Masinja, pomwe Joseph ndi wapamudzi mwa Simavu, Midzi yomwe ili mdera la mfumu Mwadzama m’bomali.
Malaki ndi wamudzi mwa Masinja, pomwe Jozefe ndi wapamudzi mwa Simavu, Midzi yomwe ili mdera la mfumu Mwadzama m’bomali.
female
Mwana wazaka 14, wafa dzulo pangozi yapamsewu, m’mudzi wa Chiozi pafupi ndi mulathowa Lupsozi mu msewu wa Nkhotakota-Salima.
Mwana wazaka fotini, wafa dzulo pangozi yapamsewu, m’mudzi wa Chiozi pafupi ndi mulathowa Lupsozi mu msewu wa Nkhotakota-Salima.
female
Wachiwiri kwa mneneri wa police ya Nkhotakota, Chisomo Chuma, wati mwanayu ndi Yasman Amans wa m’mudzi mwa Chiozi, mdera la mfumu Mwadzama m’boma la Nkhotakota.
Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Nkhotakota, Chisomo Chuma, wati mwanayu ndi Yasimani Amanzi wa m’mudzi mwa Chiozi, mdera la mfumu Mwadzama m’boma la Nkhotakota.
female
Chuma wati mwanayu, amayendetsa njinga yakapalasa ndipo amafuna kudutsa galimoto ina yomwe sikudziwika. Koma ali mkati motero,
Chuma wati mwanayu, amayendetsa njinga yakapalasa ndipo amafuna kudutsa galimoto ina yomwe sikudziwika. Koma ali mkati motero,
female
Anawombana ndi galimoto ina yomwe inanyamula matumba a sugar, yomwe imapita ku Salima. Kamba ka kuwombanaku, mwanayo anavulala kwambiri m’mutu ndipo anafera pamalo angoziyo.
Anawombana ndi galimoto ina yomwe inanyamula matumba a shuga, yomwe imapita ku Salima. Kamba ka kuwombanaku, mwanayo anavulala kwambiri m’mutu ndipo anafera pamalo angoziyo.
female
Zotsatira zakuchipatala cha Alinafe, zawonetsa kuti imfayi yadza kamba kotaya magazi ochuluka. Boma la Malawi mogwirizana ndi bungwe lomwe limayang’anira chisamaliao cha anthu othawa kwawo,
Zotsatira zakuchipatala cha Alinafe, zawonetsa kuti imfayi yadza kamba kotaya magazi ochuluka. Boma la Malawi mogwirizana ndi bungwe lomwe limayang’anira chisamaliao cha anthu othawa kwawo,
female
Lati likuchilimika kufuna kuwonwtsetsa kuti ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo, kuchoka ku msasa wa Dzaleka m’boma la Dowa kupita m’boma la Chitipa, iyambe kuchitika.
Lati likuchilimika kufuna kuwonwtsetsa kuti ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo, kuchoka ku msasa wa Dzaleka m’boma la Dowa kupita m’boma la Chitipa, iyambe kuchitika.
female
Poyankhula ku likulu la ma Office a boma lachitatu mu mzinda wa Lilongwe, pa mkomano ndi akuluakulu wochokera ku bungwe la UNHCR, nduna yowona zachitetezo mdzikomuno Dr. Kenneth Zikhale Ng’oma,
Poyankhula ku likulu la ma Ofesi a boma lachitatu mu mzinda wa Lilongwe, pa mkomano ndi akuluakulu wochokera ku bungwe la YU ENI ECHI SI ARA, nduna yowona zachitetezo mdzikomuno Dokota Kenefi Zikhale Ng’oma,
female
Yati boma layika ndondomeko zomwe zithandizire ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo. Dr, Ng’oma wati undunawu uliso ndi malingaliro ochita kafukufuku wachiwerengero chenicheni cha anthu wothawa kwawo,
Yati boma layika ndondomeko zomwe zithandizire ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo. Dokota, Ng’oma wati undunawu uliso ndi malingaliro ochita kafukufuku wachiwerengero chenicheni cha anthu wothawa kwawo,
female
Omwe akukhala ku msasa wa Dzaleka. Kumayambiliro achakachino, boma kudzera ku unduna wowona zachitetezo cha mdzikolino, linapeza malo ku Kayirizi mdera la mfumu Mwenewenya m’boma la Chitipa.
Omwe akukhala ku msasa wa Dzaleka. Kumayambiliro achakachino, boma kudzera ku unduna wowona zachitetezo cha mdzikolino, linapeza malo ku Kayirizi mdera la mfumu Mwenewenya m’boma la Chitipa.
female
Komwe asamutsireko msasa wa anthu othawa kwawo. Pakadali pano bungwe la UNHCR, kudzera kwa wachiwiri wamkulu wabungweri mchigwa cha Africa Angel Jossal,
Komwe asamutsireko msasa wa anthu othawa kwawo. Pakadali pano bungwe la YU ENI ECHI SI ARA, kudzera kwa wachiwiri wamkulu wabungweri mchigwa cha Afrika Anjelo Joso,
female
Walonjeza kupitiriza kupereka thandinzo loyenerera lokhudza ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo. Anthu pafupifupi 500, omwe ali pansi pa ndondomeko yaboma ya mthandizi,
Walonjeza kupitiriza kupereka thandinzo loyenerera lokhudza ntchito yosamutsa anthu othawa kwawo. Anthu pafupifupi fayifi handiredi, omwe ali pansi pa ndondomeko yaboma ya mthandizi,
female
Ku Nsenjere, mdera la mfumu Kanyenda m’boma la Nkhotakota, akwanitsa kusunga ndi kusamala mbande za mitengo zopitirira 12,000, zomwe zidzalidwe mnyengo yadzunja ikudzayi.
Ku Nsenjere, mdera la mfumu Kanyenda m’boma la Nkhotakota, akwanitsa kusunga ndi kusamala mbande za mitengo zopitirira thuwelofu sauzandi, zomwe zidzalidwe mnyengo yadzunja ikudzayi.
female
Mlangizi wazamalimidwe kuderari, Ledfan Chilongo, wati mbandezi ndizomwe zinapulumuka pomwe zina zinawonongeka kamba kokhalitsa nthawi yayitali pamalo osungira mbandezi.
Mlangizi wazamalimidwe kuderari, Ledifani Chilongo, wati mbandezi ndizomwe zinapulumuka pomwe zina zinawonongeka kamba kokhalitsa nthawi yayitali pamalo osungira mbandezi.
female
Iye wapempha anthu ena a mderari,kuti nawo abzale mitengo, pofuna kuthana ndi kuwonongeka kwa nthaka. Nawomi Kanyenda mkhalapampando wa dera la madzalidwe la Nsenjere wa m’mudzi wa Maloma m’bomali.
Iye wapempha anthu ena a mderari,kuti nawo abzale mitengo, pofuna kuthana ndi kuwonongeka kwa nthaka. Nawomi Kanyenda mkhalapampando wa dera la madzalidwe la Nsenjere wa m’mudzi wa Maloma m’bomali.
female
Iye wapempha anthu ena a mderari,kuti nawo abzale mitengo, pofuna kuthana ndi kuwonongeka kwa nthaka. Nawomi Kanyenda mkhalapampando wa dera la madzalidwe la Nsenjere wa m’mudzi wa Maloma m’bomali.
Iye wapempha anthu ena a mderari,kuti nawo abzale mitengo, pofuna kuthana ndi kuwonongeka kwa nthaka. Nawomi Kanyenda mkhalapampando wa dera la madzalidwe la Nsenjere wa m’mudzi wa Maloma m’bomali.
female
Wati mbandezi zikadzalidwa, zidzathandizira kubwenzeretsa nthaka mchimake, komanso kupeza ndalama akagulitsa nkhuni zochokera ku mitengoyi.
Wati mbandezi zikadzalidwa, zidzathandizira kubwenzeretsa nthaka mchimake, komanso kupeza ndalama akagulitsa nkhuni zochokera ku mitengoyi.
female
Komabe iye wapempha boma kuti liwonjenzere ndalama zomwe amalandira pa mwenzi kuchokera ku mthandizi zomwe ndi 28,000 Kwacha. Ponema kuti ndalamayi sikukwanira kugula zofunikira kugula zofunikira monga Feteleza,
Komabe iye wapempha boma kuti liwonjenzere ndalama zomwe amalandira pa mwenzi kuchokera ku mthandizi zomwe ndi tuwente eyiti sauzandi Kwacha. Ponema kuti ndalamayi sikukwanira kugula zofunikira kugula zofunikira monga Feteleza,
female
Kamba koti mamembala a gululi, sali pa mndandanda wolandira nawo fetereza wotsika mtengo. Mitengo yomwe ikuyembekezeredwa kudzalidwayi ndi Nsangu, Njerenjere, Tangatanga, Msambamfumu komanso Chithowe.
Kamba koti mamembala a gululi, sali pa mndandanda wolandira nawo fetereza wotsika mtengo. Mitengo yomwe ikuyembekezeredwa kudzalidwayi ndi Nsangu, Njerenjere, Tangatanga, Msambamfumu komanso Chithowe.
female
Pansi pa ndondomeko yaboma yobwenzeretsa chilengedwe ya Climate smart enhance public works, mchingerezi, Anduna Jean Sendeza, ayamikira alezi omwe akuphunzitsa ana msukulu za mkombaphala.
Pansi pa ndondomeko yaboma yobwenzeretsa chilengedwe ya kilayimeti simati Inhensi pabuliki wekisi, mchingerezi. Anduna Jini Sendeza, ayamikira alezi omwe akuphunzitsa ana msukulu za mkombaphala,
female
Kamba ka chidwi chomwe alinacho ngakhale akukomana ndi mavuto ochuluka. Sendeza wapempha mafumu kuti awonetsetse kuti m’mudzi mwawo muli sukulu ya mkombaphala, pofuna kuwonetsa kuti ana akupeza maphunziro kuyamba akadali achichepere.
Kamba ka chidwi chomwe alinacho ngakhale akukomana ndi mavuto ochuluka. Sendeza wapempha mafumu kuti awonetsetse kuti m’mudzi mwawo muli sukulu ya mkombaphala, pofuna kuwonetsa kuti ana akupeza maphunziro kuyamba akadali achichepere.
female
Mwambowu wachitika pa mutu woti, Kutengulira tsogolo lowala, kupititsa patsogolo ntchito za m’merampoyamba , sukulu ya m’merampoyamba mudzi uliwonse.
Mwambowu wachitika pa mutu woti, Kutengulira tsogolo lowala, kupititsa patsogolo ntchito za m’merampoyamba , sukulu ya m’merampoyamba mudzi uliwonse.
female
Charles Chimzukuzuku, mkhalapampando wa khonsolo ya boma la Nkhotakota, wati anthu m’bomali, akudandawula ndikuchepa kwa chiwerengero cha maanja omwe apindula nawo mundondomeko yazipangizo za ulimi.
Tchalosi Chimzukuzuku, mkhalapampando wa khonsolo ya boma la Nkhotakota, wati anthu m’bomali, akudandawula ndikuchepa kwa chiwerengero cha maanja omwe apindula nawo mundondomeko yazipangizo za ulimi.
female
Zotsika mtengo ya AIP. Iye wati midzi ina munthu m’modzi yekha ndi yemwe wapindula nawo, pomwe m’midzi ina palibe ndi munthu m’modzi yemwe.
Zotsika mtengo ya EAYIIPI. Iye wati midzi ina munthu m’modzi yekha ndi yemwe wapindula nawo, pomwe m’midzi ina palibe ndi munthu m’modzi yemwe.
female
Apa iye wapempha boma kuti liwonetsetse kuti ma program ena omwe akonzedwa kuti afikire anthu omwe sanapindulenawo ndi AIP, Afikire anthu ochuluka.
Apa iye wapempha boma kuti liwonetsetse kuti ma purogiramu ena omwe akonzedwa kuti afikire anthu omwe sanapindulenawo ndi EAYIIPI, Afikire anthu ochuluka.
female
Bambo wina wazaka 69 Levison Lington, lero wapezeka atafa atadzimangirira mnyumba yake, mdera la Khombemadzi, M’boma la Dowa.
Bambo wina wazaka sikisite-nayini Levisoni Ling'itoni, lero wapezeka atafa atadzimangirira mnyumba yake, mdera la Khombemadzi, M’boma la Dowa.
female
Malingana ndi mneneri wa police ya Dowa Alice Sitima, mkazi wa Lington Sawutsamanja Jonasi, adawasiya bambowa panyumba pomwe amapita kuchigayo.
Malingana ndi mneneri wa polisi ya Dowa Alice Sitima, mkazi wa Ling'itoni Sawutsamanja Jonasi, adawasiya bambowa panyumba pomwe amapita kuchigayo.
female
Koma atabwerera adapeza thupi lamamuna wakeyo yemwe panthawiyo anali atafa, lili pakhonde la nyumba yawo, pomwe anadzimangilira koma chingwe chomwe anagwiritsa ntchito chitaduka kamba ka kulemera kwathupi la mamuna wakeyo.
Koma atabwerera adapeza thupi lamamuna wakeyo yemwe panthawiyo anali atafa, lili pakhonde la nyumba yawo, pomwe anadzimangilira koma chingwe chomwe anagwiritsa ntchito chitaduka kamba ka kulemera kwathupi la mamuna wakeyo.
female
Kudzera pa uthenga womwe wasiya, Lington adatenga ngongole ku magulu atatu a banki mkhonde, ndipo wakhala akuwuzidwa kuti abweze ndalamazi, koma amalephera.
Kudzera pa uthenga womwe wasiya, Ling'itoni adatenga ngongole ku magulu atatu a banki mkhonde, ndipo wakhala akuwuzidwa kuti abweze ndalamazi, koma amalephera.
female
Atawuzidwaso kuti abweze ndalamazi mwenzi wa September chakachino, Lington, adalonjeza kuti abweza ndalamazi kumapeto a mwenzi wa October chakachino, koma sanakwanitse kutero.
Atawuzidwaso kuti abweze ndalamazi mwenzi wa Seputembala chakachino, Ling'itoni, adalonjeza kuti abweza ndalamazi kumapeto a mwenzi wa Okutobala chakachino, koma sanakwanitse kutero.
Kenako iye waganiza zodzipha. Ndipo zotsatira zakuchipatala zawonetsa kuti imfayi yadza kamba kobanika kutsatira kudzimangilira. Malingana ndi Sitima.
Kenako iye waganiza zodzipha. Ndipo zotsatira zakuchipatala zawonetsa kuti imfayi yadza kamba kobanika kutsatira kudzimangilira. Malingana ndi Sitima.
female
Gavanala wa banki yayikulu mdzikomuno ya Reserve. Dr. Wilson Banda, Wati a Malawi ochuluka alibe mtima wosunga ndalama zomwe amapeza, zomwe ati zimakhudza chuma chomwe dzikolino lilinacho.
Gavanala wa banki yayikulu mdzikomuno ya Rizevu, Dokota Wilisoni Banda, Wati a Malawi ochuluka alibe mtima wosunga ndalama zomwe amapeza, zomwe ati zimakhudza chuma chomwe dzikolino lilinacho.
female
Dr. Banda wati, pakadalipano, a Malawi 9 pa 100 aliwonse ndiwomwe amasunga ndalama zawo, kuyerekeza ndi maiko ena amu Africa, Zomwe zikuonetsa kuti chiwerengerochi ndi chochepa.
Dokota Banda wati, pakadalipano, a Malawi nayini pa wani handiredi aliwonse ndiwomwe amasunga ndalama zawo, kuyerekeza ndi maiko ena amu Afrika, Zomwe zikuonetsa kuti chiwerengerochi ndi chochepa.
female
Iye walankhula iz mu mzinda wa Lilongwe, pamwambo yokhazikitsa sabata yolimbikitsa anthu kuti azisunga ndalama zomwe amapeza, omwe unachitikira ku Bingu International Conference Centre BICC.
Iye walankhula iz mu mzinda wa Lilongwe, pamwambo yokhazikitsa sabata yolimbikitsa anthu kuti azisunga ndalama zomwe amapeza, omwe unachitikira ku Bingu Intanashono komferensi Senta (BI AYI SISI).
female
Pomwe amavomereza kuti a Malawi amapeza ndalama zochepa mu ntchito zosiyanasiyana zomwe amagwira. Dr. Banda wati, ichi chizikhala chilimbikitso choti azisunga ndalamazi.
Pomwe amavomereza kuti a Malawi amapeza ndalama zochepa mu ntchito zosiyanasiyana zomwe amagwira. Dokota Banda wati, ichi chizikhala chilimbikitso choti azisunga ndalamazi.
female
Ndicholinga choti mtsogolomu, adzakhale ndi ndalama zochuluka. Pakadalipano mkulu wa company ya Malawi Stock Exchange, John Kamanga, wati msabatayi akhala akufalitsa uthenga wozindikilitsa anthu.
Ndicholinga choti mtsogolomu, adzakhale ndi ndalama zochuluka. Pakadalipano mkulu wa kampani ya Malawi Sitoko Ekisichanji, Joni Kamanga, wati msabatayi akhala akufalitsa uthenga wozindikilitsa anthu.
female
Za ubwino wosunga ndalama m’misika komanso msukulu zosiyanasiyana mdzikomuno. Ku Nkhotakota, a police akusunga mchitokosi Charles Domoya wazaka 46.
Za ubwino wosunga ndalama m’misika komanso msukulu zosiyanasiyana mdzikomuno. Ku Nkhotakota, a polisi akusunga mchitokosi Tchalosi Domoya wazaka fote-sikisi.
female
Yemwe ndi dalayivala wa galimoto ya mtundu wa truck, kamba kopezeka ndi fodya wachamba, mopanda chilolezo. Malingana ndi mneneri wa police ya Nkhotakota, Paul Malimwe.
Yemwe ndi dalayivala wa galimoto ya mtundu wa thiraki, kamba kopezeka ndi fodya wachamba, mopanda chilolezo. Malingana ndi mneneri wa polisi ya Nkhotakota, Poo Malimwe.
female
Domoya wamangidwa m’mawa walero pa school ya primary ya Loko, m’bomali. Iye wati apolice anatsinidwa khutu kuti mu galimoto lomwe dalayivalayu amanyamula sugar,
Domoya wamangidwa m’mawa walero pa sukulu ya pulayimale ya Loko, m’bomali. Iye wati apolisi anatsinidwa khutu kuti mu galimoto lomwe dalayivalayu amanyamula shuga,
female
Anaphatikizamo matumba a fodya wachamba okwana anayi. Kenako apolice anayimitsa galimotoli ndipo analamula dalayivalayu kuti atengere galimotoli ku police ya Nkhotakota kuti akafufuze bwino.
Anaphatikizamo matumba a fodya wachamba okwana anayi. Kenako apolisi anayimitsa galimotoli ndipo analamula dalayivalayu kuti atengere galimotoli ku polisi ya Nkhotakota kuti akafufuze bwino.
female
Atafufuza apeza fodya wachamba wolemera ma kilogram 215, kenako amanga dalayivalayu, atalephera kuwonetsa zikalata zoyenerera kupezeka ndi chambachi.
Atafufuza apeza fodya wachamba wolemera ma kilogiramu thu handiredi andi fifitini, kenako amanga dalayivalayu, atalephera kuwonetsa zikalata zoyenerera kupezeka ndi chambachi.
female
Malimwe wati Domoya yemwe ndi wam’mudzi wa Chathunya mdera la mfumu Msamala m’boma la Balaka, akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa, kukayankha mulandu wopezeka ndi chamba wopanda chilolenzo.
Malimwe wati Domoya yemwe ndi wam’mudzi wa Chathunya mdera la mfumu Msamala m’boma la Balaka, akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa, kukayankha mulandu wopezeka ndi chamba wopanda chilolenzo.
female
Bambo wina wazaka 56, Chimwala Chimwele, wamfa atadzimangilira mnyumba mwake m’mudzi wa Zuze ku Lumbadzi, mu mzinda wa Lilongwe.
Bambo wina wazaka fifite-sikisi, Chimwala Chimwele, wamfa atadzimangilira mnyumba mwake m’mudzi wa Zuze ku Lumbadzi, mu mzinda wa Lilongwe.
female
Mneneri wa police ya Lumbadzi Felix Kwinyani, wati bamboyu yemwe amakhala ndi banja lake, dzulo anatsazika kuti watsala ndi masiku wochepa kukhala padzikolapansipano, koma sadanene chifukwa chomwe amanenera izi.
Mneneri wa polisi ya Lumbadzi Felikisi Kwinyani, wati bamboyu yemwe amakhala ndi banja lake, dzulo anatsazika kuti watsala ndi masiku wochepa kukhala padzikolapansipano, koma sadanene chifukwa chomwe amanenera izi.
female
Iye wati kenako lero abale abamboyo anampeza atadzimangirira ndipo anakaneneza za izi kupolice ya Lumbadzi.
Iye wati kenako lero abale abamboyo anampeza atadzimangirira ndipo anakaneneza za izi kupolice ya Lumbadzi.
female
Malingana ndi kwinyani, zotsatira kuchipatala cha Lumbadzi, zawonetsa kuti bamboyu wafa kamba ka kubanika kutsatira kudzimangilira.
Malingana ndi kwinyani, zotsatira kuchipatala cha Lumbadzi, zawonetsa kuti bamboyu wafa kamba ka kubanika kutsatira kudzimangilira.
female
Chimwele adali wa m’mudzi wa Zuze mdera la mfumu Chitukula mumzinda wa Lilongwe. Nduna yazamalo Deusi Gumba.
Chimwele adali wa m’mudzi wa Zuze mdera la mfumu Chitukula mumzinda wa Lilongwe. Nduna yazamalo Deusi Gumba.
female
Yomwe yayimira nduna yofalitsa nkhani pamwambo wokhazikitsa makina akanema a Clear clear ku Kasungu, yati kanemayo athandizira anthu kupeza uthenga wamsangulutso, maphunziro komanso chitukuko mosavuta.
Yomwe yayimira nduna yofalitsa nkhani pamwambo wokhazikitsa makina akanema a kiliye kiliye ku Kasungu, yati kanemayo athandizira anthu kupeza uthenga wamsangulutso, maphunziro komanso chitukuko mosavuta.
female
Gumba wati ndi ulamuliro wa Dr Lazarus Chakwera, boma la Kasungu latukuka pankhani ya zomangamanga pomwe watchula kumangidwa kwa nyumba za police.
Gumba wati ndi ulamuliro wa Dokota Lazarasi Chakwera, boma la Kasungu latukuka pankhani ya zomangamanga pomwe watchula kumangidwa kwa nyumba za polisi.
female
Komanso asilikari ankhondo. Ndunayi ikutsegulira kanema wa clear clear ku Kasungu.
Komanso asilikari ankhondo. Ndunayi ikutsegulira kanema wa kiliye kiliye ku Kasungu.
female
Apolice ku Kasungu, anjata mlangizi wazawulimi komanso mfumu ina, powaganizira kuti apezeka ndi ziphaso za unzika zokwana 89.
Apolisi ku Kasungu, anjata mlangizi wazawulimi komanso mfumu ina, powaganizira kuti apezeka ndi ziphaso za unzika zokwana eyite nayini.
female
Zomwe zimafunika kugwiritsidwa ntchito pogula zipangizo za ulimi zotsika mtengo, Mlangiziyu amagwira ntchito mchigawo cha Chilipa, pansi pa office yazawulimi ya Chamama m’bomali.
Zomwe zimafunika kugwiritsidwa ntchito pogula zipangizo za ulimi zotsika mtengo, Mlangiziyu amagwira ntchito mchigawo cha Chilipa, pansi pa ofesi yazawulimi ya Chamama m’bomali.
female