audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Wachiwiri kwa mneneri wa police ku Kasungu Miracle Mkozi, wati mlangiziyu ndi Patricia Mtonga wazaka 33 ndi a mfumu a Mwimira azaka 42. | Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Kasungu Mirako Mkozi, wati mlangiziyu ndi Patirisha Mtonga wazaka sete-firi ndi a mfumu a Mwimira azaka fote-thu. | female | |
Malingana ndi mkozi, awiriwa adawanjata lachitatu, anthu ena atawatsina khutu kuti anthuwa ali ndi ziphaso za unzika zochuluka za alimi omwe akuyenera kupindula mndondomeko yazipangizo zotsika mtengozi. | Malingana ndi mkozi, awiriwa adawanjata lachitatu, anthu ena atawatsina khutu kuti anthuwa ali ndi ziphaso za unzika zochuluka za alimi omwe akuyenera kupindula mndondomeko yazipangizo zotsika mtengozi. | female | |
Iye wati awiriwa, akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa kukayankha mulandu wopezeka ndi ziphaso za unzika zomwe zikusemphana ndi gawo 89 loyendetsera ntchito yakalembera. | Iye wati awiriwa, akawonekera kubwalo lamilandu posachedwapa kukayankha mulandu wopezeka ndi ziphaso za unzika zomwe zikusemphana ndi gawo eyite nayini loyendetsera ntchito yakalembera. | female | |
Amfumu Mwimira omwe dzina lawo lenileni ndi Damiano Ntholo, ndi a m’mudzi wa mwimira mdera la mfumu Wimbe, pomwe a Mtonga ndi am’mudzi wa Chilima mdera la mfumu Magwazu m’boma la Kasungu. | Amfumu Mwimira omwe dzina lawo lenileni ndi Damiano Ntholo, ndi a m’mudzi wa mwimira mdera la mfumu Wimbe, pomwe a Mtonga ndi am’mudzi wa Chilima mdera la mfumu Magwazu m’boma la Kasungu. | female | |
M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pa zochitika zamdziko. Clement Makuwa, wapempha boma kuti liziyika chidwi chake pa zitukuko zomwe zingathandizire kuthana ndi mavuto omwe dzikolino likukumana nawo padakali pano. | M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pa zochitika zamdziko. Kilementi Makuwa, wapempha boma kuti liziyika chidwi chake pa zitukuko zomwe zingathandizire kuthana ndi mavuto omwe dzikolino likukumana nawo padakali pano. | female | |
Mawu ake akudza pomwe nduna ya maboma ang’ono umodzi ndi chikhalidwe walengeza kuti dzikolino lachinayi likhala likuchita chikondwerero chomwe chikutchedwa tsiku la umodzi mu mzinda wa Lilongwe. | Mawu ake akudza pomwe nduna ya maboma ang’ono umodzi ndi chikhalidwe walengeza kuti dzikolino lachinayi likhala likuchita chikondwerero chomwe chikutchedwa tsiku la umodzi mu mzinda wa Lilongwe. | female | |
Mwambo womwe ugwiritse ntchito ndalama zokwana wani handiredi miliyoni, kwacha za misonkho ya aMalawi. Pomwe wati ngakhale mwambowu uthandinzire kuyanjanitsa ndikuyika pamodzi mtundu wa a Malawi zomwe ndi nsanamira ya chitukuko, | Mwambo womwe ugwiritse ntchito ndalama zokwana 100,000,000, kwacha za misonkho ya aMalawi. Pomwe wati ngakhale mwambowu uthandinzire kuyanjanitsa ndikuyika pamodzi mtundu wa a Malawi zomwe ndi nsanamira ya chitukuko, | female | |
Makuwa wati komabe boma likanagwiritsa ntchito ndalamazi pa zitukuko zina, zomwe zikanathandizira kusintha dzikolino. | Makuwa wati komabe boma likanagwiritsa ntchito ndalamazi pa zitukuko zina, zomwe zikanathandizira kusintha dzikolino. | female | |
Iye wapereka chitsanzo zamavuto monga kupitirira kuvuti kwa anthu omwe anapsyinjidwa ndi Namondwe wa Freddy mchigawo chakummwera. | Iye wapereka chitsanzo zamavuto monga kupitirira kuvuti kwa anthu omwe anapsyinjidwa ndi Namondwe wa Furedi mchigawo chakummwera. | female | |
Komanso kuwonongeka kwa midadada ya yophunziriramo, zomwe zimasokoneza maphunziro maka mu nyengo yamvula yomwe yayambayi. | Komanso kuwonongeka kwa midadada ya yophunziriramo, zomwe zimasokoneza maphunziro maka mu nyengo yamvula yomwe yayambayi. | female | |
Bungwe lomwe limayang’anira ma khonsolo mdzikomuno, lati kuchedwa kusankha adindo a ma committee ya chitukuko cha m’madera a ADC komanso kumudzi a VDC kwadza kamba kamavuto azachuma. | Bungwe lomwe limayang’anira ma khonsolo mdzikomuno, lati kuchedwa kusankha adindo a ma komiti ya chitukuko cha m’madera a EDISI komanso kumudzi a VIDISI kwadza kamba kamavuto azachuma. | female | |
Mtsogoleri wa bungweri, Hardlord Mkandawire, wati lamulo losankha adindo atsopano m’ma komiti wa, linadza pakatikati pokhazikitsa ntchito zachitukuko zosiyana siyana. | Mtsogoleri wa bungweri, Hadilodi Mkandawire, wati lamulo losankha adindo atsopano m’ma komitiwa, linadza pakatikati pokhazikitsa ntchito zachitukuko zosiyana siyana. | female | |
Zomwe zachititsa kuti makhonsolo ochuluka, alephere kukhazikitsa makomitiwa, kamba koti anali atagwiritsa kale ntchito ndalama pa zitukuko zina. | Zomwe zachititsa kuti makhonsolo ochuluka, alephere kukhazikitsa makomitiwa, kamba koti anali atagwiritsa kale ntchito ndalama pa zitukuko zina. | female | |
Iye wapempha boma kuti liringalire zowonjezera ndalama zomwe makhonsolo amapatsidwa mundondomeko ya chuma chaboma, kuti azitha kugwira bwino ntchitozawo. | Iye wapempha boma kuti liringalire zowonjezera ndalama zomwe makhonsolo amapatsidwa mundondomeko ya chuma chaboma, kuti azitha kugwira bwino ntchitozawo. | female | |
Mabungwe ena monga lowona zochitira zinthu poyera la Centre for Social Accountability and Transparency. | Mabungwe ena monga lowona zochitira zinthu poyera la Senta fo Sosho Akauntabilite andi Thiransiparense, | female | |
Posachedwapa anadandawula ndikuchedwa kokhazikitsaso ma komitiwa, atathetsedwa ndi unduna wa maboma ang’ono umodzi ndi chikhalidwe. | Posachedwapa anadandawula ndikuchedwa kokhazikitsaso ma komitiwa, atathetsedwa ndi unduna wa maboma ang’ono umodzi ndi chikhalidwe. | female | |
Mneneri mu unduna wachinyamata komanso masewero Mc Millan Mwale, wati unduna tsopano, wamaliza zofunikira zonse zokhudza kukhazikitsa ndondomeko yatsopano yokhudza masewero. | Mneneri mu unduna wachinyamata komanso masewero Makimilani Mwale, wati unduna tsopano, wamaliza zofunikira zonse zokhudza kukhazikitsa ndondomeko yatsopano yokhudza masewero. | female | |
Mwale wanena izi, pomwe undunawo ukufuna kukhazikitsa ndondomeko yatsopano yokhudza achinyamata yomwe ayikhazikitsenso kubwalo lochitira misonkhano la Bingu, | Mwale wanena izi, pomwe undunawo ukufuna kukhazikitsa ndondomeko yatsopano yokhudza achinyamata yomwe ayikhazikitsenso kubwalo lochitira misonkhano la Bingu, | female | |
Komwe mtsogoleri wadzikolino Dr Lazarus Chakwera, akakhaleko. Iye wati ndondomeko yatsopanoyi yomwe ayikhazikitseyi. | Komwe mtsogoleri wadzikolino Dr Lazarus Chakwera, akakhaleko. Iye wati ndondomeko yatsopanoyi yomwe ayikhazikitseyi. | female | |
Ikhale ikugwirizana ndimomwe masewera akuyendera pakadali pano, komanso fundo zachitukuko za chaka cha 2063. Malingana ndi Mwale, izi zichitika pompano | Ikhale ikugwirizana ndimomwe masewera akuyendera pakadali pano, komanso fundo zachitukuko za chaka cha tuwente sikisite firi. Malingana ndi Mwale, izi zichitika pompano | female | |
Kamba koti chidwichawo pano chidalikale posintha mfundo mundondomeko zatsopano zoyendetsera nkhani za achinyamata. Bungwe la ma Lawyer akazi mdzikolino lati ndi lokhutira ndimomwe anthu omwe amachitiridwira nkhanza. | Kamba koti chidwichawo pano chidalikale posintha mfundo mundondomeko zatsopano zoyendetsera nkhani za achinyamata. Bungwe la ma Loya akazi mdzikolino lati ndi lokhutira ndimomwe anthu omwe amachitiridwira nkhanza. | female | |
Kamba koti ndi amayi kapena abambo, akugwiritsira ntchito lamya yapadera ya ulere, yomwe bungweri lidakhazikitsa. Mtsogoleri wabungweri Chisomo Nyemba, | Kamba koti ndi amayi kapena abambo, akugwiritsira ntchito lamya yapadera ya ulere, yomwe bungweri lidakhazikitsa. Mtsogoleri wabungweri Chisomo Nyemba, | female | |
Wati bungweri lidaganiza zokhazikitsa nambalayi, atazindikira kuti ambiri mwa anthuwa omwe amachokera m’madera akutali ndi likulu lawo mu mzinda wa Lilongwe, amakanika kuti apeze thandizo lawo. | Wati bungweri lidaganiza zokhazikitsa nambalayi, atazindikira kuti ambiri mwa anthuwa omwe amachokera m’madera akutali ndi likulu lawo mu mzinda wa Lilongwe, amakanika kuti apeze thandizo lawo. | female | |
Iye wati, chikhazikitsireni nambalayi, anthu ambiri omwe achitiridwa nkhanza, akutha kuwayimbira lamya ndikufotokoza zomwe akukumana nazo. | Iye wati, chikhazikitsireni nambalayi, anthu ambiri omwe achitiridwa nkhanza, akutha kuwayimbira lamya ndikufotokoza zomwe akukumana nazo. | female | |
Nambalayi yomwe ndi 3081, idakhazikitsidwa ndi bungweri ndicholinga chofuna kuthandiza amayi, omwe adakumanapo ndi nkhanza komanso omwe akukumana nazo m’maanja ang’onoang’ono. | Nambalayi yomwe ndi 3081, idakhazikitsidwa ndi bungweri ndicholinga chofuna kuthandiza amayi, omwe adakumanapo ndi nkhanza komanso omwe akukumana nazo m’maanja ang’onoang’ono. | female | |
Mkulu wanthambi ya unsodzi m’bomala Nkhotakota, Charles Mandala, wachenjeza ansodzi m’bomali kuti alemekeze lamulo pomwe nyanja ya Malawi ndi malo ena ochitira usodzi, | Mkulu wanthambi ya unsodzi m’bomala Nkhotakota, tChalosi Mandala, wachenjeza ansodzi m’bomali kuti alemekeze lamulo pomwe nyanja ya Malawi ndi malo ena ochitira usodzi, | female | |
Atsekedwa komaso apewe kugwiritsa ntchito maukonde osaloledwa munthawiyi. Mandala wanena izi pomwe nthambiyi yakhazikitsa ntchito yotseka Nyanja, | Atsekedwa komaso apewe kugwiritsa ntchito maukonde osaloledwa munthawiyi. Mandala wanena izi pomwe nthambiyi yakhazikitsa ntchito yotseka Nyanja, | female | |
Ndicholinga choti nsomba ziswane, yomwe ikuyembekezeka kuyamba pa 1 November, 2023. Iye wati kupatula kudziwitsa anthu za izi. | Ndicholinga choti nsomba ziswane, yomwe ikuyembekezeka kuyamba pa wani Novemba, tuwente tuwente-firi. Iye wati kupatula kudziwitsa anthu za izi, | female | |
Nthambiyi ikhalanso ikuyendera ntchitoyi panyanja, komanso m’misika yabomali, Kuyang’ana nsomba zomwe zikugulitsidwa munyengoyi. | Nthambiyi ikhalanso ikuyendera ntchitoyi panyanja, komanso m’misika yabomali, Kuyang’ana nsomba zomwe zikugulitsidwa munyengoyi. | female | |
Iye watsindika kuti lamulo lidzagwira ntchito pa aliyese yemwe aphwanye lamulo lokhudza usodzi munthawi yotseka nyanja. Apolice azofufuzafufuza, ochokera ku likulu la apolice mdzikomuno, | Iye watsindika kuti lamulo lidzagwira ntchito pa aliyese yemwe aphwanye lamulo lokhudza usodzi munthawi yotseka nyanja. Apolisi azofufuzafufuza, ochokera ku likulu la apolisi mdzikomuno, | female | |
Atumizidwa kuti akafufuze nkhani yomwe a police ena apapolisi ya Nkhunga m’boma la Nkhotakota, akuganiziridwa kuti anagulitsa chamba chomwe analanda kwamunthu wina ochita malonda ogulitsa chamba. | Atumizidwa kuti akafufuze nkhani yomwe a polisi ena apapolisi ya Nkhunga m’boma la Nkhotakota, akuganiziridwa kuti anagulitsa chamba chomwe analanda kwamunthu wina ochita malonda ogulitsa chamba. | female | |
Apolisiwa omwe analipo asanu ndi m’modzi (6), anapita kukalanda chambachi atatsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwino, | Apolisiwa omwe analipo asanu ndi m’modzi (sikisi), anapita kukalanda chambachi atatsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwino, | female | |
Komwe anakwanitsa kulanda ma kilogram pafupifupi 800 achambachi, mdera la Mulala m’bomali. Koma m’malo moti apititse chambachi ku polisiyi, | Komwe anakwanitsa kulanda ma kilogiramu pafupifupi eyiti handiredi achambachi, mdera la Mulala m’bomali. Koma m’malo moti apititse chambachi ku polisiyi, | female | |
Zikuganiziridwa kuti iwowo, anagulitsanso chambachi kwa munthu wina, wochita malonda a chamba, pomwe amatsindika kuti nkhaniyi ili ndi kuthekera kowononga mbiri ya nthambi yachitetezo ya polisi mdziko muno. | Zikuganiziridwa kuti iwowo, anagulitsanso chambachi kwa munthu wina, wochita malonda a chamba, pomwe amatsindika kuti nkhaniyi ili ndi kuthekera kowononga mbiri ya nthambi yachitetezo ya polisi mdziko muno. | female | |
Mneneri wa police mdzikomuno, Peter Kalaya, wati aliyese yemwe apezeke olakwa kafukufukuyu akatsirizidwa, apatsidwa chilango choyenera. | Mneneri wa polisi mdzikomuno, Pita Kalaya, wati aliyese yemwe apezeke olakwa kafukufukuyu akatsirizidwa, apatsidwa chilango choyenera. | female | |
Anthu omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a AIDS ka HIV, maka achinyamata omwe akugwira ntchito kwa amwenye m’boma la Kasungu. | Anthu omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka ETCHI AYI VI, maka achinyamata omwe akugwira ntchito kwa amwenye m’boma la Kasungu. | ||
Ati akuphwanyiridwa ufuluwawo wopeza thandizo lazaumoyo loyenerera, pomwe akukanizidwa kukatenga mankhwala munthawi yake. M’modzi mwa achinyamatawa yemwe sitimutchula dzina. | Ati akuphwanyiridwa ufuluwawo wopeza thandizo lazaumoyo loyenerera, pomwe akukanizidwa kukatenga mankhwala munthawi yake. M’modzi mwa achinyamatawa yemwe sitimutchula dzina. | female | |
Wati kubweretsa poyera zamomwe mthupimwawo muliri, kwadzetsa mavuto osiyanasiyana, zomweso zikukolezera chiwerengero cha anthu womwe ali ndi kachilomboko, koma sakumwa mankhwala otalikitsa moyo m’bomali. | Wati kubweretsa poyera zamomwe mthupimwawo muliri, kwadzetsa mavuto osiyanasiyana, zomweso zikukolezera chiwerengero cha anthu womwe ali ndi kachilomboko, koma sakumwa mankhwala otalikitsa moyo m’bomali. | female | |
Izi ndizokhumudwitsa maka panthawi yomwe dzikolino, likuchirimika zedi pothana ndi kachilombo ka HIV. Pakadali pano anthu 4 pa 100 aliwonse, ndiwomwe ali ndi HIV ku Kasungu. | Izi ndizokhumudwitsa maka panthawi yomwe dzikolino, likuchirimika zedi pothana ndi kachilombo ka ETCHI AYI VI. Pakadali pano anthu folo pa wani handiredi aliwonse, ndiwomwe ali ndi ETCHI AYI VI ku Kasungu. | female | |
Wachinyamatayu, watiwuzanso kuti awuza nkhaniyi adindo a bomali, kuti awathandize. Mkhalapampando wa committee yoyang’anira kachilombo ka HIV pa khonsolo ya municipal ya kasungu Joseph Nthondo, | Wachinyamatayu, watiwuzanso kuti awuza nkhaniyi adindo a bomali, kuti awathandize. Mkhalapampando wa komiti yoyang’anira kachilombo ka ETCHI AYI VI pa khonsolo ya municipal ya kasungu Jozefe Nthondo, | female | |
Watsimikiza kuti wawuzidwa zankhaniyi, ndipo wati akukoza zokambirana ndi amwenyewa kuti awone momwe angathandizire anthu okhudzidwawa. | Watsimikiza kuti wawuzidwa zankhaniyi, ndipo wati akukoza zokambirana ndi amwenyewa kuti awone momwe angathandizire anthu okhudzidwawa. | female | |
Bungwe lomwe limalimbikitsa kuchitira zinthu poyera la Centre for Social Accountability and Transparency, ladandawula ndikuchedwa kwaboma posankhanso mamembala a m’makomiti a chitukuko cha mdera, | Bungwe lomwe limalimbikitsa kuchitira zinthu poyera la senta fo Centre for Sosho Akauntabilite andi Thiransiparense, ladandawula ndikuchedwa kwaboma posankhanso mamembala a m’makomiti a chitukuko cha mdera, | female | |
Komanso kumudzi a ADC ndi VDC mdzikomuno. Poyankhula ndi Umunthu FM, mkulu wabungwe la CSAT, Willy Kambwandira, | Komanso kumudzi a edisi ndi VIDISI mdzikomuno. Poyankhula ndi Umunthu EFU EMU, mkulu wabungwe la SI ESI ETI, WilE Kambwandira, | female | |
Wadzudzulaso kuthetsedwa kwa makomitiwa, komwe kunachitika ndi unduna womaboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe, ponena kuti ganizoli, lidachitika posafusa mbali zokhudzidwa. | Wadzudzulaso kuthetsedwa kwa makomitiwa, komwe kunachitika ndi unduna womaboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe, ponena kuti ganizoli, lidachitika posafusa mbali zokhudzidwa. | female | |
Iye wati bungwe la CSAT, lalandira uthenga woti, akuluakulu ena a boma maka m’makhonsolo, akusankha anthu awo, kuti akhale m’makomitiwa. | Iye wati bungwe la SI ESI ETI, lalandira uthenga woti, akuluakulu ena a boma maka m’makhonsolo, akusankha anthu awo, kuti akhale m’makomitiwa. | female | |
Zomwe wati zikudzetsa mafunso maka pankhani yochitira zinthu poyera, komanso ndondomeko za mphavu ku anthu. Pakadalipano, bungwe la CSAT, lapempha boma kuti lichitepo kanthu msanga, | Zomwe wati zikudzetsa mafunso maka pankhani yochitira zinthu poyera, komanso ndondomeko za mphavu ku anthu. Pakadalipano, bungwe la SI ESI ETI, lapempha boma kuti lichitepo kanthu msanga, | female | |
Maka pokhazikitsanso makomitiwa, m’makhonsolo onse a dzikolino. Lamulo lokhudza maboma ang’onowa la mchaka cha 1998, limati komiti ya ADC ndi VDC ndiwofunikira zedi. | Maka pokhazikitsanso makomitiwa, m’makhonsolo onse a dzikolino. Lamulo lokhudza maboma ang’onowa la mchaka cha nayintini nayinte-eyiti, limati komiti ya disi ndi VIDISI ndiwofunikira zedi. | ||
Maka pankhani yopititsa patsogolo chitukuko, ndipo kusokonekera kwa makomitiwa, kukudzetsa mafunso, maka pakuthekera kowononga chuma cha boma. | Maka pankhani yopititsa patsogolo chitukuko, ndipo kusokonekera kwa makomitiwa, kukudzetsa mafunso, maka pakuthekera kowononga chuma cha boma. | female | |
Mtsogoleri wa dzikolino Dr Lazarus Chakwera, wati mdzikomuno muli mtendere komanso bata, kamba kakudzipereka kwa atsirikari omwe adafa pankhondo yoyamba komanso yachiwiri yapadzikolonse lapansi. | Mtsogoleri wa dzikolino Dokota Lazarasi Chakwera, wati mdzikomuno muli mtendere komanso bata, kamba kakudzipereka kwa atsirikari omwe adafa pankhondo yoyamba komanso yachiwiri yapadzikolonse lapansi. | female | |
Komanso nkhondo zapachiweniweni, mayiko atalandira ufulu wodzilamurira. Chakwera wayankhula izi, lachisanu kunyumba yachifumu mu mzinda wa Lilongwe, | Komanso nkhondo zapachiweniweni, mayiko atalandira ufulu wodzilamurira. Chakwera wayankhula izi, lachisanu kunyumba yachifumu mu mzinda wa Lilongwe, | female | |
Pomwe amatsekulira sabata yokumbukira asirikariwa, yomwe cholinga chake ndi kupeza thandizo lomwe limathandiza asirikari omwe akanali moyo omwe anamenyanawo nkhondozi, komanso ena opuma. | Pomwe amatsekulira sabata yokumbukira asirikariwa, yomwe cholinga chake ndi kupeza thandizo lomwe limathandiza asirikari omwe akanali moyo omwe anamenyanawo nkhondozi, komanso ena opuma. | female | |
Iye wati mtendere ndi chitetezo zilipo, kamba kakugwira ntchito modzipereka komanso mosunga mwambo kwa nthambi yachitetezo ya asirikari. | Iye wati mtendere ndi chitetezo zilipo, kamba kakugwira ntchito modzipereka komanso mosunga mwambo kwa nthambi yachitetezo ya asirikari. | female | |
Wapampando wabungwe la asirikari omwe anamenyanawo nkhondo komanso opuma. General Henley Odillo, opuma, wayamikira boma kamba kathandizo lake kwa asirikariwa, mdzikomuno. | Wapampando wabungwe la asirikari omwe anamenyanawo nkhondo komanso opuma. Jenero Henele Odilo, opuma, wayamikira boma kamba kathandizo lake kwa asirikariwa, mdzikomuno. | female | |
General Odillo, wawonjezera kuti msabatayi, akufuna kutolera thandizo la ndalama zokwana 100,000,000 Kwacha, zomwe zithandize kukozaso nyumba za asirikariwa, m’boma la Zomba. | Jenero Odilo, wawonjezera kuti msabatayi, akufuna kutolera thandizo la ndalama zokwana wani handiredi miliyoni Kwacha, zomwe zithandize kukozaso nyumba za asirikariwa, m’boma la Zomba. | female | |
Pomwe gululina lokhudzidwa linachita ziwonetsero lachitatu, losonyeza kusagwirizana ndi ganizo loti Walter Nyamilandu Manda, ayimilenso ngati mtsogoreri wabungwe loyendetsa masewero wamiyendo mdzikomuno la FAM. | Pomwe gululina lokhudzidwa linachita ziwonetsero lachitatu, losonyeza kusagwirizana ndi ganizo loti Wota Nyamilandu Manda, ayimilenso ngati mtsogoreri wabungwe loyendetsa masewero wamiyendo mdzikomuno la FAMU. | female | |
Gululina lomwe likuyikira kumbuyo Nyamilandu, lalonjeza kumuthandizira. Gululi lomwe likudzitcha kuti Team Nyamilandu, lati Nyamilandu wathandizira kupititsa patsogolo masewero ampira wamiyendo mdzikomuno. | Gululina lomwe likuyikira kumbuyo Nyamilandu, lalonjeza kumuthandizira. Gululi lomwe likudzitcha kuti Timi Nyamilandu, lati Nyamilandu wathandizira kupititsa patsogolo masewero ampira wamiyendo mdzikomuno. | female | |
Komanso ali pawubale wabwino ndi bungwe loyang’anira mpira wamiyendo padzikolonse la FIFA, zomwe zikutsimikiza kuti akugwirabwino ntchito yake. | Komanso ali pawubale wabwino ndi bungwe loyang’anira mpira wamiyendo padzikolonse la FIFA, zomwe zikutsimikiza kuti akugwirabwino ntchito yake. | female | |
Kapanda wati gululi likuyenera kubweretsa poyera munthu yemwe adzapikisanenawo pa chisankho, osati kumangochita ziwonwtsero. Kuwonjezera kuti Nyamilandu ndiwoyenera kupitiriza udindowu. | Kapanda wati gululi likuyenera kubweretsa poyera munthu yemwe adzapikisanenawo pa chisankho, osati kumangochita ziwonwtsero. Kuwonjezera kuti Nyamilandu ndiwoyenera kupitiriza udindowu. | female | |
Walter Nyamilandu Manda, wakhala ali pa udindo wa mtsogoleri wa bungwe la FAM kuchokera mchaka cha 2004, ndipo bungwe la FAM, likuyembekezereka kuchititsa zisankho pa 16 December chaka chino. | Wota Nyamilandu Manda, wakhala ali pa udindo wa mtsogoleri wa bungwe la FAMU kuchokera mchaka cha tuwente ziro folo, ndipo bungwe la FAMU, likuyembekezereka kuchititsa zisankho pa sikisitini Disemba chaka chino. | female | |
Adindo azawulimi m’boma la Kasungu, ati akhala ndi mkomano wa akuluakulu akhonsolo la bomali lachinayi, | Adindo azawulimi m’boma la Kasungu, ati akhala ndi mkomano wa akuluakulu akhonsolo la bomali lachinayi, | female | |
Pofuna kudziwitsana zamomwe ndondomeko yazipangizo zawulimi zotsika mtengo ya AIP, yakozedwera m’bomali. | Pofuna kudziwitsana zamomwe ndondomeko yazipangizo zawulimi zotsika mtengo ya eayipi, yakozedwera m’bomali. | female | |
Yemwe amayang’anira ntchitoyi, m’boma la Kasungu Jonathan Baloyi, wauza Umunthu FM, kuti ndondomeko yogula zipangizozi, idzayamba ukatha mkomanowu. | Yemwe amayang’anira ntchitoyi, m’boma la Kasungu Jonafani Baloyi, wauza Umunthu EFU EMU, kuti ndondomeko yogula zipangizozi, idzayamba ukatha mkomanowu. | female | |
Monga mwandondomeko zake, powonjezera kuti mayina alimi omwe apindulenawo, atumizidwa ku mafumu, ukachitika mkomanowu. | Monga mwandondomeko zake, powonjezera kuti mayina alimi omwe apindulenawo, atumizidwa ku mafumu, ukachitika mkomanowu. | female | |
Lolemba sabata lino, anthu okhala mtown ya Kasungu, anasonkhana pa Depot ya bungwe la Small Holder Farmers Fertilizer Revolving Fund of Malawi kuti agule feteleza otsika mtengowu, | Lolemba sabata lino, anthu okhala mtown ya Kasungu, anasonkhana pa Depoti ya bungwe la Simoo Hoda Famazi Fetilayiza Revoving'i Fandi ofu Malawi kuti agule feteleza otsika mtengowu, | female | |
Koma ntchitoyi, inayimitsidwa ndi akuluakulu a khonsoloyi ponena kuti adindo oyenera sanamalizitse madongosolo onse okonzekera ntchitoyi. | Koma ntchitoyi, inayimitsidwa ndi akuluakulu a khonsoloyi ponena kuti adindo oyenera sanamalizitse madongosolo onse okonzekera ntchitoyi. | female | |
Mtsogoleri wadzikolino Dr. Lazarus Chakwera, anakhazikitsa ntchito yogula zipangizo zotsika mtengo ya AIP ya chakachino,pa 20, mwenzi uno m’boma la Kasungu, | Mtsogoleri wadzikolino Dr. Lazarasi Chakwera, anakhazikitsa ntchito yogula zipangizo zotsika mtengo ya eayipi ya chakachino, pa tuwente, mwenzi uno m’boma la Kasungu, | female | |
komwe analamula kuti ikhale itatsirizidwa pasanathe masiku khumi ndi anayi, ndipo anthu okwana 1.5,000,000 ndiwomwe apindule nawo. | komwe analamula kuti ikhale itatsirizidwa pasanathe masiku khumi ndi anayi, ndipo anthu okwana wani pointi fayifi miliyoni ndiwomwe apindule nawo. | female | |
Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo, yati boma la Nkhotakota, liyembekezera kulandira mvula ya mulingo wabwino, mnyengo yavula ya 2023 mpaka 2024. | Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo, yati boma la Nkhotakota, liyembekezera kulandira mvula ya mulingo wabwino, mnyengo yavula ya tuwente tuwente-firi mpaka tuwentetuwente-folo. | female | |
Mkulu woyang’anira kulosera kwanyengo kunthambiyi, James Pagoma, wanena izi pamkomano womwe nthambiyi inachititsa ndi akuluakulu apakhonsolo yabomali ya boma la Nkhotakota pomwe amawafotokozera momwe mvula igwere m’bomali. | Mkulu woyang’anira kulosera kwanyengo kunthambiyi, Jemusi Pagoma, wanena izi pamkomano womwe nthambiyi inachititsa ndi akuluakulu apakhonsolo yabomali ya boma la Nkhotakota pomwe amawafotokozera momwe mvula igwere m’bomali. | female | |
Chigona wati boma la Nkhotakota liyembekezera kulandira mvula kuyamba sabata lotsiriza la mwenzi wa November kapena sabata lachiwiri lamwenzi wa December chakachino. | Chigona wati boma la Nkhotakota liyembekezera kulandira mvula kuyamba sabata lotsiriza la mwenzi wa Novembala kapena sabata lachiwiri lamwenzi wa Disembala chakachino. | female | |
Malingana ndi kawuniwuni wanthambiyi, mvula ikuyembekezeka kugwa kwa miyezi isanu m’bomali yomwe ndi November, December, January, February, pomwe mwenzi wa March, idzagwa yopsyola muyezo. | Malingana ndi kawuniwuni wanthambiyi, mvula ikuyembekezeka kugwa kwa miyezi isanu m’bomali yomwe ndi Novemba, Disemba, Januwale, Feburuware, pomwe mwenzi wa Malichi, idzagwa yopsyola muyezo. | female | |
Koma nyengo yang’amba ikuyembekezereka mwenzi wa February chaka cha 2024. Nthambi yowona za misewu ya Roads Authority. | Koma nyengo yang’amba ikuyembekezereka mwenzi wa Feburuware chaka cha tuwente tuwente-folo. Nthambi yowona za misewu ya Rodzi Oforite. | female | |
Yati ili ndi chikhulupiriro kuti ntchito yokhoza msewu wa M5 kuchoka pa Kaphatenga m’boma la Salima mpaka ku Benga m’boma la Nkhotakota, itsirizidwa pofika kumapeto kwa chaka chamawa. | Yati ili ndi chikhulupiriro kuti ntchito yokhoza msewu wa EMU fayifi kuchoka pa Kaphatenga m’boma la Salima mpaka ku Benga m’boma la Nkhotakota, itsirizidwa pofika kumapeto kwa chaka chamawa. | female | |
Izi zanenedwa lero pomwe akuluakulu kunthambiyi, anachititsa mkomano ndi anthu adera la Bzyobzyo, m’boma la Nkhotakota. | Izi zanenedwa lero pomwe akuluakulu kunthambiyi, anachititsa mkomano ndi anthu adera la Bzyobzyo, m’boma la Nkhotakota. | female | |
Pomwe mwazina, alangiza anthu kuti sakuyenera kugwiritsa ntchito mwanjira inailiyonse, malo amalire a msewu, kamba koti zitha kusokoneza ntchitoyi. | Pomwe mwazina, alangiza anthu kuti sakuyenera kugwiritsa ntchito mwanjira inailiyonse, malo amalire a msewu, kamba koti zitha kusokoneza ntchitoyi. | female | |
Mneneri wathambiyi Portia Kajanga, wati poyamba company yomwe ikugwira ntchitoyi ya China Railway, imagwira ntchito yopeza anthu othandizira ntchitoyi komanso zipangizo zina. | Mneneri wathambiyi Posha Kajanga, wati poyamba company yomwe ikugwira ntchitoyi ya Chayina Reluwayi, imagwira ntchito yopeza anthu othandizira ntchitoyi komanso zipangizo zina. | female | |
Malingana ndi Kajanga, nthambiyi, yatsiriza ntchito yopereka chipuputa misozi kwa ena mwa eni malo, omwe pagwiridwe ntchitoyi koma ena okwana pafupifupi 600, | Malingana ndi Kajanga, nthambiyi, yatsiriza ntchito yopereka chipuputa misozi kwa ena mwa eni malo, omwe pagwiridwe ntchitoyi koma ena okwana pafupifupi sikisi handiredi, | female | |
Akuyembekezereka kulandira ndalama zawo posachedwapa. Ntchito yokozanso msewu omwe ndiwotalikira ma kilometer 60, inayamba chakachatha. | Akuyembekezereka kulandira ndalama zawo posachedwapa. Ntchito yokozanso msewu omwe ndiwotalikira ma kilomita sikisite, inayamba chakachatha. | female | |
Ndipo ndalama zokwana 3.7,000,000,000, Kwacha, mzomwe zigwiritsidwe ntchito. Mtsogoleri wadzikolino Dr. Lazarus Chakwera, | Ndipo ndalama zokwana firi pointi seveni biliyoni Kwacha, mzomwe zigwiritsidwe ntchito. Mtsogoleri wadzikolino Dokota Lazarasi Chakwera, | female | |
lero kumasanaku akhale akutsegulira ntchito yogula zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya AIP ya chakachino. | lero kumasanaku akhale akutsegulira ntchito yogula zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya eayipi ya chakachino. | female | |
Izi zikuyembekezereka kuchitika pa bwalo lazamasewero la school ya Primary ya Kavidebwere mdera la mfumu Kaluluma, m’boma la Kasungu. | Izi zikuyembekezereka kuchitika pa bwalo lazamasewero la sukulu ya Purayimare ya Kavidebwere mdera la mfumu Kaluluma, m’boma la Kasungu. | female | |
Kum’mawaku, Dr. Chakwera, anakachitira umboni pantchito yokolola mbeu ya Tirigu, pansi pa company ya PAI XUS mdera la mfumu Chakhadza, m’boma la Dowa. | Kum’mawaku, Dokota Chakwera, anakachitira umboni pantchito yokolola mbeu ya Tirigu, pansi pa kampani ya Paisasi mdera la mfumu Chakhadza, m’boma la Dowa. | female | |
Malingana ndi unduna wazaulimi, alimi pafupifupi 1.5,000,000 ndiwomwe akuyembekezeleka kupindula nawo mndondomekoyi, chakachino. | Malingana ndi unduna wazaulimi, alimi pafupifupi wani pointi fayifi miliyoni ndiwomwe akuyembekezeleka kupindula nawo mndondomekoyi, chakachino. | female | |
Ndipo alimi azigula thumba lolemera ma kilogram 50 la feteleza, pa mtengo wa 15,000 Kwacha. Azanyengo aja kani amanenadi zoona eti? | Ndipo alimi azigula thumba lolemera ma kilogiramu fifite la feteleza, pa mtengo wa fifitini sauzandi Kwacha. Azanyengo aja kani amanenadi zoona eti? | female | |
Awa ndimawu omwe alimkamwamkamwa pakati pa nzika zokhala m’boma la Kasungu pomwe mvula yodza ndi mabingu komanso ziphaliwali, ikugwa m’bomali. | Awa ndimawu omwe alimkamwamkamwa pakati pa nzika zokhala m’boma la Kasungu pomwe mvula yodza ndi mabingu komanso ziphaliwali, ikugwa m’bomali. | female | |
Izi ndikutsatira uthenga omwe nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo idatulutsa podziwitsa a Malawi kuti kuyambira lachiwiri sabata ino, | Izi ndikutsatira uthenga omwe nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwanyengo idatulutsa podziwitsa a Malawi kuti kuyambira lachiwiri sabata ino, | female | |
Madera ena amchigawo chapakati komanso kummwera, kugwa mvula yamabingu. Nthambiyi, inachenjeza kuti nthawi zambiri mvula yamabingu imadza ndi mphenzi. | Madera ena amchigawo chapakati komanso kummwera, kugwa mvula yamabingu. Nthambiyi, inachenjeza kuti nthawi zambiri mvula yamabingu imadza ndi mphenzi. | female | |
Komanso mphepo yamkuntho, choncho kupewa ngozi, anthu akhale pamalo otetezeka panthawi yomwe mvula ikugwa. Pakadalipano mvulayi yomwe yayamba chakumasanaku, ikugwabe ku Kasungu | Komanso mphepo yamkuntho, choncho kupewa ngozi, anthu akhale pamalo otetezeka panthawi yomwe mvula ikugwa. Pakadalipano mvulayi yomwe yayamba chakumasanaku, ikugwabe ku Kasungu | female | |
Komanso mu mzinda wa Lilongwe, pomwe m’boma la Nkhotakota, kunja kwangotsekana mowonetsa kuti ikhala ikudontha nthawi ina iliyonse. | Komanso mu mzinda wa Lilongwe, pomwe m’boma la Nkhotakota, kunja kwangotsekana mowonetsa kuti ikhala ikudontha nthawi ina iliyonse. | female | |
Anthu awiri afa atamira panyanja ya Malawi pa doko la Dupa m’boma la Nkhotakota. Mneneri wa apolice m’bomali Paul Malimwe, | Anthu awiri afa atamira panyanja ya Malawi pa doko la Dupa m’boma la Nkhotakota. Mneneri wa apolisi m’bomali Poo Malimwe, | female | |
Wati awiriwa ndi a Joseph Phiri a mdera la mfumu Mfumamapiri ndi a Eliya Gama a mdera la mfumu Malanda, onse ochokera m’boma la Nkhata-Bay. | Wati awiriwa ndi a Jozefe Phiri a mdera la mfumu Mfumamapiri ndi a Eliya Gama a mdera la mfumu Malanda, onse ochokera m’boma la Nkhata-Bay. | female | |
Malingana ndi Malimwe, awiriwa anali mgulu la asodzi okwana asanu ndi anayi (9), omwe amakasodza panyanja ya Malawi lachiwiri sabata lino. | Malingana ndi Malimwe, awiriwa anali mgulu la asodzi okwana asanu ndi anayi (nayini), omwe amakasodza panyanja ya Malawi lachiwiri sabata lino. | female | |
Koma pomwe amabwerera lachitatu sabata ino, anakumana ndi mphepo yamwera ndipo bwato lawo linamira. Ena mwa asodziwa anakwanitsa kusambira kufika pa mtunda, | Koma pomwe amabwerera lachitatu sabata ino, anakumana ndi mphepo yamwera ndipo bwato lawo linamira. Ena mwa asodziwa anakwanitsa kusambira kufika pa mtunda, | female | |
Koma awiriwa anamira ndipo matupi awo awapeza ndi anthu akufuna kwabwino. Zotsatira zakuchipatala chachikulu cha m’boma la Nkhota kota, zawonetsa kuti anthuwa afa kamba kobanika. | Koma awiriwa anamira ndipo matupi awo awapeza ndi anthu akufuna kwabwino. Zotsatira zakuchipatala chachikulu cha m’boma la Nkhota kota, zawonetsa kuti anthuwa afa kamba kobanika. | female | |
Malimwe wawonjenzera kuti m’modzi mwa asodziwa John Phiri, wa m’mudzi wa Kapita mdera la mfumu mphonde m’boma la Nkhotakota, akulandira thandizo lamankhwala pa chipatala cha Nkhotakota. | Malimwe wawonjenzera kuti m’modzi mwa asodziwa Joni Phiri, wa m’mudzi wa Kapita mdera la mfumu mphonde m’boma la Nkhotakota, akulandira thandizo lamankhwala pa chipatala cha Nkhotakota. | female | |
Mneneri mu unduna wa achinyamata komaso masewero McMillan Mwale, wati undunawu upanga chiganizo chotseka bwalo lamasewero la mpira wa miyendo la Bingu, | Mneneri mu unduna wa achinyamata komaso masewero Makimilani Mwale, wati undunawu upanga chiganizo chotseka bwalo lamasewero la mpira wa miyendo la Bingu, | female | |
Ukamaliza kulandira ma Report kuchokera kwa adindo omwe amayang’anira bwalori. Iye wati pakadalipano, adindowa akusonkhanitsa ma report komanso chomwe chichitike. | Ukamaliza kulandira malipoti kuchokera kwa adindo omwe amayang’anira bwalori. Iye wati pakadalipano, adindowa akusonkhanitsa malipoti komanso chomwe chichitike. | female | |
Kutsatira ndikuwonongeka kwa katundu komwe kudachitika pabwalori ndi anthu ena pamasewero apakati pa Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderes. | Kutsatira ndikuwonongeka kwa katundu komwe kudachitika pabwalori ndi anthu ena pamasewero apakati pa Siliva Sitirayikazi ndi Mayite Mukuru Wandarazi. | female | |
Mwale wati kapinga wapabwalori sadakhudzidwe ndi chipwirikiticho, koma mipando yokwanira 239 yakummwera kwabwalori ndiyo yawonongeka. | Mwale wati kapinga wapabwalori sadakhudzidwe ndi chipwirikiticho, koma mipando yokwanira thu handiredi andi sete-nayini yakummwera kwabwalori ndiyo yawonongeka. | female | |
Lolemba undunawu udatulutsa kalata yomwe idadzudzula chipolowe chomwe chidachitika pabwalori, ndipo udapempha mabungwe owona zamasewero a Malawi National Council of Sports and Football Association of Malawi FAM, | Lolemba undunawu udatulutsa kalata yomwe idadzudzula chipolowe chomwe chidachitika pabwalori, ndipo udapempha mabungwe owona zamasewero a Malawi Nashono Khanso ofu Sipotsi andi Futubo Asosiyeshoni ofu Malawi FAMU, | female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.