audio
audioduration (s)
1.12
18.5
raw_text
stringlengths
1
297
normalized_text
stringlengths
1
267
gender
stringclasses
16 values
A Kamwendo atiwuza kuti ngati salandira yankho kuchokera ku boma pakutha pa sabata ziwiri, agwirizana ndi aphunzitsi a IPTE 13 mpaka 17
A Kamwendo atiwuza kuti ngati salandira yankho kuchokera ku boma pakutha pa sabata ziwiri, agwirizana ndi aphunzitsi a IPITE fetini mpaka seventini
Female
omwenso sanalembedwe ntchito, kukachita m'bindikiro ku nyumba ya mtsogoleri wa dzikoyu mu mzinda wa Lilongwe
omwenso sanalembedwe ntchito, kukachita m'bindikiro ku nyumba ya mtsogoleri wa dzikoyu mu mzinda wa Lilongwe
Female
Mfumu yayikulu Kaduya ya m'boma la Phalombe yapempha anthu, kampani komanso boma kuti apitilire kuthandiza, mu njira zosiyanasiyana, anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Freddy
Mfumu yayikulu Kaduya ya m'boma la Phalombe yapempha anthu, kampani komanso boma kuti apitilire kuthandiza, mu njira zosiyanasiyana, anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa fulede
Female
yemwe anaomba kum'mwera kwa dziko lino, miyezi pafupifupi isanu ndi iwiri yapitayo. A Kaduya ati anthu omwe anakhuzidwa ndi namondweyu akupitilira
yemwe anaomba kum'mwera kwa dziko lino, miyezi pafupifupi isanu ndi iwiri yapitayo. A Kaduya ati anthu omwe anakhuzidwa ndi namondweyu akupitilira
Female
kukumana ndi zokhoma mmagawo a chakudya, malo ogona ndi kukhala, zovala komanso thandizo la ana ku sukulu
kukumana ndi zokhoma mmagawo a chakudya, malo ogona ndi kukhala, zovala komanso thandizo la ana ku sukulu
Female
Iwo ayankhula izi lero ku likulu la gulu la chikhalidwe la Mulhakho Wa Alhomwe kwa Chonde m'boma la Mulanje komwe kuli mapemphero opemphelera anthu omwe anakhuzidwa ndi namondweyu
Iwo ayankhula izi lero ku likulu la gulu la chikhalidwe la Mulakho Wa Alomwe kwa Chonde m'boma la Mulanje komwe kuli mapemphero opemphelera anthu omwe anakhuzidwa ndi namondweyu
Female
Mapempherowa akuchitika, pambuyo pa mwambo wa pa chaka wa Mulhakho Wa Alhomwe wa chaka chino, omwe ufike pa chi indeinde, omwe ufike pa chi indeinde lamulungu likubwerali
Mapempherowa akuchitika, pambuyo pa mwambo wa pa chaka wa Mulakho Wa Alomwe wa chaka chino, omwe ufike pa chi indeinde, omwe ufike pa chi indeinde lamulungu likubwerali
Female
Pakadali pano, gulu la Mulhakho Wa Alhomwe-li lati likapereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu a m'maboma a Mulanje ndi Phalombe mawa lachisanu
Pakadali pano, gulu la Mulakho Wa Alomwe-li lati likapereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu a m'maboma a Mulanje ndi Phalombe mawa lachisanu
Female
Kampani yofulula mowa ya Castel lero yakhazikitsa kampeni ya dziko lonse yozindikilitsa anthu za kapewedwe ka ngozi za pa msewu, ndi cholinga chofuna kuchepesa ngozizi
Kampani yofulula mowa ya Casitelo lero yakhazikitsa kampeni ya dziko lonse yozindikilitsa anthu za kapewedwe ka ngozi za pa msewu, ndi cholinga chofuna kuchepesa ngozizi
Female
M'modzi mwa akuluakulu ku Castel, mayi Gloria Zimba ati anthu akatetezedwa ku ngozi, chitukuko cha dziko chimapita patsogolo
M'modzi mwa akuluakulu ku Casitelo, mayi Guloliya Zimba ati anthu akatetezedwa ku ngozi, chitukuko cha dziko chimapita patsogolo
Female
Ena mwa anthu omwe amayenda pa msewu ndi ka kasitomala athu, ndipo tikuyenera kuwateteza pomwe akuyenda pa msewupo. Tiwateteza powazindikilitsa njira zopewera ngozizi, atero mayi Zimba
Ena mwa anthu omwe amayenda pa msewu ndi ka kasitomala athu, ndipo tikuyenera kuwateteza pomwe akuyenda pa msewupo. Tiwateteza powazindikilitsa njira zopewera ngozizi, atero mayi Zimba
Female
Kampeniyi yomwe akuyitchula kuti 'Yendani Bwino pa msewu; Samalani Moyo,' yakhazikitsidwa ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre
Kampeniyi yomwe akuyitchula kuti 'Yendani Bwino pa msewu; Samalani Moyo,' yakhazikitsidwa ku Ndirande mu mzinda wa Bulantaya
Female
Ndipo m'mawu ake, a Madalitso Gunsaru omwe ndi mkulu wa nthambi yoona za pa msewu ya Director of Road Traffic and Safety Services (DRTSS) mchigawo cha kum'mwera
Ndipo m'mawu ake, a Madalitso Gunsaru omwe ndi mkulu wa nthambi yoona za pa msewu ya Dailekita ofu lodi thilafiki and sefete sevisezi (Diala tiesiesi) mchigawo cha kum'mwera
Female
anati kampeni yomwe kampani ya Castel yayambitsa ndi yofunika kwambiri polingalira kuti ngozi za pa msewu zimabwera pa zifukwa zosiyanasiyana ndipo anthu akuyenera kuzindikilitsidwa pa izi
anati kampeni yomwe kampani ya Casitelo yayambitsa ndi yofunika kwambiri polingalira kuti ngozi za pa msewu zimabwera pa zifukwa zosiyanasiyana ndipo anthu akuyenera kuzindikilitsidwa pa izi
Female
Ngozi zambiri zikumachitika chifukwa cha anthu amene akumayendetsa galimoto mothamanga kwambiri. Liwiro limakhala ndi zotsatira zake pa msewu
Ngozi zambiri zikumachitika chifukwa cha anthu amene akumayendetsa galimoto mothamanga kwambiri. Liwiro limakhala ndi zotsatira zake pa msewu
Female
China ndi kuyenda pa msewu munthu ataledzera kapena kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, atero a Gunsaru
China ndi kuyenda pa msewu munthu ataledzera kapena kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, atero a Gunsaru
Female
Malingana ndi malipoti, ngozi zopitilira 1000 zinachitika chaka chatha chokha zomwe adindo akuti ndi zodandawulitsa
Malingana ndi malipoti, ngozi zopitilira wani sauzande zinachitika chaka chatha chokha zomwe adindo akuti ndi zodandawulitsa
Female
Unduna wa maboma aang'ono, umodzi komanso chikhalidwe wati ugwiritsa ntchito tsiku lokumbukira mtendere la chaka chino kulimbikitsa kulolena pakati pa anthu
Unduna wa maboma aang'ono, umodzi komanso chikhalidwe wati ugwiritsa ntchito tsiku lokumbukira mtendere la chaka chino kulimbikitsa kulolena pakati pa anthu
Female
Mneneri mu undunawu, Anjoya Mwanza watiwuza kuti adindo mdziko muno agwirana kale manja ndi mayiko ena popeza njira zolimbikitsira kulolena-ku
Mneneri mu undunawu, Anjoya Mwanza watiwuza kuti adindo mdziko muno agwirana kale manja ndi mayiko ena popeza njira zolimbikitsira kulolena-ku
Female
Nthambi ya umodzi mu unduna wathu yagwirana kale manja ndi bungwe la United Nations pokonza mkumano wa masiku awiri okhuza mtendere, atero a Mwanza
Nthambi ya umodzi mu unduna wathu yagwirana kale manja ndi bungwe la yunaitedi neshonzi pokonza mkumano wa masiku awiri okhuza mtendere, atero a Mwanza
Female
Malingana ndi a Mwanza, tsikuli lomwe ndi pa 21 September, lithandizanso kukuza chitukuko cha dziko
Malingana ndi a Mwanza, tsikuli lomwe ndi pa twente wani sepitemba , lithandizanso kukuza chitukuko cha dziko
Female
Bungwe lotolera misonkho la MRA lati ndondomeko yolipira misonkho kudzera pa internet ya Msonkho online ikupindulira bungwe lawo, anthu komanso kampani zomwe zimalipira msonkho
Bungwe lotolera misonkho la emualae lati ndondomeko yolipira misonkho kudzera pa intaneti ya Msonkho onilaini ikupindulira bungwe lawo, anthu komanso kampani zomwe zimalipira msonkho
Female
Mwa zina, anthu sakuyenda maulendo atali-atali kuti akalipire msonkho ku ofesi za bungweli kapena ku bank
Mwa zina, anthu sakuyenda maulendo atali-atali kuti akalipire msonkho ku ofesi za bungweli kapena ku banki
Female
Izitu ndi malingana ndi m'modzi mwa akuluakulu ku MRA, a Wilma Chalulu omwe atinso msonkho wa 1%
Izitu ndi malingana ndi m'modzi mwa akuluakulu ku emualae, a Wilma Chalulu omwe atinso msonkho wa wani pelesenti
Female
omwe olemba anthu ntchito amalipira ku bungwe la TEVET wa TEVET Levy uyamba kulipilidwa pa internet kuyambira pa 1 October chaka chino
omwe olemba anthu ntchito amalipira ku bungwe la TEVETI wa TEVETI Leve uyamba kulipilidwa pa intaneti kuyambira pa wani okotoba chaka chino
Female
Mayi Chalulu anena izi ku Mangochi pomwe amayankhula pa msonkhano wa bungwe la anthu owerengera ndalama mdziko muno la ICAM
Mayi Chalulu anena izi ku Mangochi pomwe amayankhula pa msonkhano wa bungwe la anthu owerengera ndalama mdziko muno la aikamu
Female
Namwino wa pa chipatala cha Kasinje m'boma la Ntcheu, Moses Chimalizeni wafa atamwa poison. Malipoti akuti malemuyu wachita izi
Namwino wa pa chipatala cha Kasinje m'boma la Ntcheu, Mozesi Chimalizeni wafa atamwa poizoni. Malipoti akuti malemuyu wachita izi
Female
pambuyo pofunsidwa mafunso ndi apolisi pomuganizira kuti anagwililira komanso kupereka mimba kwa mwana wa zaka 15. Mneneri wa apolisi ku Ntcheu, Jacob Khembo
pambuyo pofunsidwa mafunso ndi apolisi pomuganizira kuti anagwililira komanso kupereka mimba kwa mwana wa zaka fifitini. Mneneri wa apolisi ku Ntcheu, Jakobo Khembo
Female
wati namwinoyu anapezeka atakomoka mphepete mwa msewu, ndipo wamwalilira ku chipatala chomwe anamutengera kuti akalandire thandizo la mankhwala
wati namwinoyu anapezeka atakomoka mphepete mwa msewu, ndipo wamwalilira ku chipatala chomwe anamutengera kuti akalandire thandizo la mankhwala
Female
Malemu Chimalizeni anali wa mdera la mfumu yayikulu Kwataine m'boma lomwelo la Ntcheu. Mu nkhani za masewelo Timu ya mpira wa miyendo ya mdziko muno, ya FCB Nyasa Big Bullets
Malemu Chimalizeni anali wa mdera la mfumu yayikulu Kwataine m'boma lomwelo la Ntcheu. Mu nkhani za masewelo Timu ya mpira wa miyendo ya mdziko muno, ya efusibi Nyasa Bigi Buletsi
Female
lero isewera ndi timu ya mdziko la DR Congo mu mpikisano wa CAF. Masewerowa omwe achitikire pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, ayamba nthawi ya 3 koloko masanawa
lero isewera ndi timu ya mdziko la Diala Kongo mu mpikisano wa kAFU. Masewerowa omwe achitikire pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, ayamba nthawi ya fili koloko masanawa
Female
Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma mnyumba ya malamulo Kondwani Nankhumwa walangiza apolisi kuti asiye mchitidwe omwe akuti ndi wozunza anthu omwe akuganizilidwa kuti apalumula milandu
Mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma mnyumba ya malamulo Kondwani Nankhumwa walangiza apolisi kuti asiye mchitidwe omwe akuti ndi wozunza anthu omwe akuganizilidwa kuti apalumula milandu
Female
Iwo ati anthuwa amakhala osalakwa kufikira bwalo la milandu litawapeza ndi mlandu ndi kuwapatsa chilango. A Nankhumwa omwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party-DPP
Iwo ati anthuwa amakhala osalakwa kufikira bwalo la milandu litawapeza ndi mlandu ndi kuwapatsa chilango. A Nankhumwa omwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Demokilatiki pulogilesivi pate -Dipipi
Female
mchigawo cha kum'mwera ayankhula izi atayendera omenyera ufulu wa anthu, a Bon Kalindo ku Mtakataka m'boma la Dedza omwe amangidwa lachisanu lapitali
mchigawo cha kum'mwera ayankhula izi atayendera omenyera ufulu wa anthu, a Boni Kalindo ku Mtakataka m'boma la Dedza omwe amangidwa lachisanu lapitali
Female
pa mlandu onyozera mfundo za belo la bwalo la milandu. A Nankhumwa ati ndi odabwa kuti mwa zina, apolisi akumatengera a Kalindo ku malo a kutali ndi komwe awamangira
pa mlandu onyozera mfundo za belo la bwalo la milandu. A Nankhumwa ati ndi odabwa kuti mwa zina, apolisi akumatengera a Kalindo ku malo a kutali ndi komwe awamangira
Female
Pali chiyembekezo kuti a Kalindo awonekera m'bwalo la milandu mawa lolemba. Bungwe lofalitsa mauthenga a za chitukuko la Initiative for Community Development Services (INCOS)
Pali chiyembekezo kuti a Kalindo awonekera m'bwalo la milandu mawa lolemba. Bungwe lofalitsa mauthenga a za chitukuko la inishetivi fo komyunite divelopumenti sevisezi (aieni sioesi)
Female
lalimbikitsa makolo komanso anthu oyang'anira ana kulola ana awo kulandira katemera oteteza ku nthenda ya polio pomwe gawo lina lopereka katemerayu likuyamba lero mdziko muno
lalimbikitsa makolo komanso anthu oyang'anira ana kulola ana awo kulandira katemera oteteza ku nthenda ya polio pomwe gawo lina lopereka katemerayu likuyamba lero mdziko muno
Female
Poyankhula ndi Ndirande FM, mkulu wa bungwe la INCOS, Kennedy Mwalwanda wati anthu asatengeke ndi nkhambakamwa zonse zokhuza katemerayu ponena kuti ndi otetezeka
Poyankhula ndi Ndirande efuemu, mkulu wa bungwe la aieni sioesi, Kenede Mwalwanda wati anthu asatengeke ndi nkhambakamwa zonse zokhuza katemerayu ponena kuti ndi otetezeka
Female
Amnzathu a unduna wa zaumoyo amatsindika za kufunika kokhala oteteza ku nthenda, ndipo izi ndi zotheka maka tikalandira katemera, atero a Mwalwanda
Amnzathu a unduna wa zaumoyo amatsindika za kufunika kokhala oteteza ku nthenda, ndipo izi ndi zotheka maka tikalandira katemera, atero a Mwalwanda
Female
Azaumoyo azipereka katemerayu kudzera mu njira za khomo ndi Khomo, mzipitala, ku sukulu komanso sikelo ndi malo ena omwe akhazikitsidwa
Azaumoyo azipereka katemerayu kudzera mu njira za khomo ndi Khomo, mzipitala, ku sukulu komanso sikelo ndi malo ena omwe akhazikitsidwa
Female
Atsogoleri komanso adindo ena ochokera m'boma la Blantyre alonjeza kuti ayamba kufalitsa mauthenga okhuza kusintha kaganizidwe pakati pa anthu awo, zomwe zili ndi kuthekera kotukula miyoyo yawo
Atsogoleri komanso adindo ena ochokera m'boma la Bulantaya alonjeza kuti ayamba kufalitsa mauthenga okhuza kusintha kaganizidwe pakati pa anthu awo, zomwe zili ndi kuthekera kotukula miyoyo yawo
Female
Atsogoleriwa ndi ochokera mmagawo a zipembezo, mafumu, magulu aachinyamata, nthambi ya maphunziro komanso wailesi za m'madera
Atsogoleriwa ndi ochokera mmagawo a zipembezo, mafumu, magulu aachinyamata, nthambi ya maphunziro komanso wailesi za m'madera
Female
omwe anakumana ndi cholinga chofuna kukambirana mavuto omwe akudza kaamba ka kunyalanyaza kwa anthu kutengawo nawo mbali pa zochitika zomwe zikuwakhuza
omwe anakumana ndi cholinga chofuna kukambirana mavuto omwe akudza kaamba ka kunyalanyaza kwa anthu kutengawo nawo mbali pa zochitika zomwe zikuwakhuza
Female
Poyankhula ndi atolankhani, M'busa Richard Luwamba wa mpingo wa Zambezi Evangelical anati ngati kunyalanyaza kotere kungapitilire
Poyankhula ndi atolankhani, M'busa Litchadi Luwamba wa mpingo wa Zambezi Evanjeliko anati ngati kunyalanyaza kotere kungapitilire
Female
umphawi, kuchita zinthu zobwelera m'mbuyo komanso kusachita bwino pa chuma kupitilira. Udindo wathu ndi kukakhala nawo anthu pansi ndi kuwafotokozera kufunikira kosintha kaganizidwe pakati pawo
umphawi, kuchita zinthu zobwelera m'mbuyo komanso kusachita bwino pa chuma kupitilira. Udindo wathu ndi kukakhala nawo anthu pansi ndi kuwafotokozera kufunikira kosintha kaganizidwe pakati pawo
Female
atero a Luwamba. Ndipo bwanamkubwa wa boma la Blantyre, Alex Mdooko anati ndi pakuyenera kupitilira kuyika chidwi pa ntchito zozindikilitsa anthu pa nkhanizi, ngakhale patakhala zosamwitsa
atero a Luwamba. Ndipo bwanamkubwa wa boma la Bulantaya, Aleisi Mdooko anati ndi pakuyenera kupitilira kuyika chidwi pa ntchito zozindikilitsa anthu pa nkhanizi, ngakhale patakhala zosamwitsa
Female
Msonkhanowu ndi ofunikira polingalira kuti cholinga chake ndi kufalitsa mauthenga osiyanasiyana omwe timakhala nawo okhuza m'mene dziko likuyendera, atero a Mdooko
Msonkhanowu ndi ofunikira polingalira kuti cholinga chake ndi kufalitsa mauthenga osiyanasiyana omwe timakhala nawo okhuza m'mene dziko likuyendera, atero a Mdooko
Female
Mkumanowu unachitika ndi komiti ya mauthenga ya Social Mobilization pansi pa kampeni ya Kulumikiza yomwe ikuchitika m'maboma a Lilongwe, Blantrye, Kasungu, Mulanje komanso Phalombe
Mkumanowu unachitika ndi komiti ya mauthenga ya sosho mobolaizeshoni pansi pa kampeni ya Kulumikiza yomwe ikuchitika m'maboma a Lilongwe, Bulantaya, Kasungu, Mulanje komanso Phalombe
Female
ndipo ikulandira thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la UNICEF. Ofesi ya umoyo m'boma la Blantyre lero ikukhazikitsa ntchito yopereka katemera oteteza ku nthenda ya polio
ndipo ikulandira thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la Yunisefu. Ofesi ya umoyo m'boma la Bulantaya lero ikukhazikitsa ntchito yopereka katemera oteteza ku nthenda ya poliyo
Female
mwambo omwe ukuchitikira mdera la Mfumu yayikulu Chigalu m'bomali. Ofesiyi ikukonza zofikira ana osadutsa zaka 15
mwambo omwe ukuchitikira mdera la Mfumu yayikulu Chigalu m'bomali. Ofesiyi ikukonza zofikira ana osadutsa zaka fifitini
Female
osakwana 578,176 pa ntchitoyi yomwe ifike kumapeto lachisanu sabata ino
osakwana faifi handiledi andi sevente faifi sauzande wani handiledi andi sevente sikisi pa ntchitoyi yomwe ifike kumapeto lachisanu sabata ino
Female
Malingana ndi ndondomeko yomwe yayikidwa, azaumoyo azipereka katemerayu m'makomo mwa anthu, n'zipitala komanso malo okwelera sikelo ndi malo ena. Katemerayu ndi odonthetsera mkamwa
Malingana ndi ndondomeko yomwe yayikidwa, azaumoyo azipereka katemerayu m'makomo mwa anthu, n'zipitala komanso malo okwelera sikelo ndi malo ena. Katemerayu ndi odonthetsera mkamwa
Female
Ogwira ntchito mu madepoti a kampani ya AGORA ayamba kunyanyala ntchito ati pofuna kuti mabwana awo awakwezere malipiro
Ogwira ntchito mu madepoti a kampani ya AGORA ayamba kunyanyala ntchito ati pofuna kuti mabwana awo awakwezere malipiro
Female
Mwa zina, iwo ati ma manejala akulandira ndalama zosapitilira K100,000 pa mwezi ndipo alonda akulandira ndalama zokwana K50,000
Mwa zina, iwo ati ma manejala akulandira ndalama zosapitilira wani handiledi sauzande kwacha pa mwezi ndipo alonda akulandira ndalama zokwana fifite sauzande kwacha
Female
zomwe akuti ndi zochepa, polingalira kukwera kwa mitengo ya katundu ofunikira pa moyo. Pakadali pano, ena mwa ogwira ntchitowa asonkhana ku ofesi ya AGORA ku Limbe
zomwe akuti ndi zochepa, polingalira kukwera kwa mitengo ya katundu ofunikira pa moyo. Pakadali pano, ena mwa ogwira ntchitowa asonkhana ku ofesi ya AGORA ku Limbe
Female
mu mzinda wa Blantyre komwe akutula nkhawa zawo. Ife tikufuna kuti malipiro athu akwere chifukwa zinthu zofunikira zinakwera mitengo. Tikuvutika
mu mzinda wa Bulantaya komwe akutula nkhawa zawo. Ife tikufuna kuti malipiro athu akwere chifukwa zinthu zofunikira zinakwera mitengo. Tikuvutika
Female
watero m'modzi mwa ogwira ntchitowa. Pomwe atolankhani amafuna kulowa ku ofesi za AGORA kuti amve tsatanetsatane wa nkhaniyi kuchoka kwa adindo
watero m'modzi mwa ogwira ntchitowa. Pomwe atolankhani amafuna kulowa ku ofesi za AGORA kuti amve tsatanetsatane wa nkhaniyi kuchoka kwa adindo
Female
m'modzi mwa akuluakulu a za chitetezo anawaletsa ponena kuti sakuloledwa kutero. Titayimbira mkulu wolemba komanso kuchotsa anthu ntchito ku kampaniyi (Human Resource Manager), a Benard Phiri
m'modzi mwa akuluakulu a za chitetezo anawaletsa ponena kuti sakuloledwa kutero. Titayimbira mkulu wolemba komanso kuchotsa anthu ntchito ku kampaniyi (Hyumani lisosi maneja), a Benadi Phiri
Female
anatiwuza kuti sali ololedwa kuyankhula ndi atolankhani pa nkhaniyi. Gulu la chikhalidwe la Mulhakho Wa Alhomwe lati zokonzekera za mwambo wa chikondwelero wa chaka chino zikuyenda bwino
anatiwuza kuti sali ololedwa kuyankhula ndi atolankhani pa nkhaniyi. Gulu la chikhalidwe la Mulhakho Wa Alomwe lati zokonzekera za mwambo wa chikondwelero wa chaka chino zikuyenda bwino
Female
Mwambo wa chaka chino omwe uchitike pa mutu oti Chikhalidwe Chathu, Udindo wa Aliyense uzayamba pa 6 ndipo uzatha pa 8 October
Mwambo wa chaka chino omwe uchitike pa mutu oti Chikhalidwe Chathu, Udindo wa Aliyense uzayamba pa 6sikisi ndipo uzatha pa siti okutoba
Female
Wa mpando wa komiti yomwe ikukonza mwambowu, Muchanakwaye Mpuluka, wawuza atolankhani kulikulu la bungweli kwa Chonde m'boma la Mulanje
Wa mpando wa komiti yomwe ikukonza mwambowu, Muchanakwaye Mpuluka, wawuza atolankhani kulikulu la bungweli kwa Chonde m'boma la Mulanje
Female
kuti kwa sabata ya tunthu, kuzakhala mwambo wa mapemphero kupemphelera anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Freddy, chikondwelero chenicheni chisanafike, mwa zochitika zina
kuti kwa sabata ya tunthu, kuzakhala mwambo wa mapemphero kupemphelera anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Fulede, chikondwelero chenicheni chisanafike, mwa zochitika zina
Female
Ndipo trustee wa board ya Mulhakho Wa Alhomwe, Elvis Thodwi watiwuza kuti mwambowu ulunjikanso pa kuzindilikitsa zambiri za chikhalidwe cha mtundu wa Alhomwe
Ndipo thilasitii wa bodi ya Mulakho Wa Alomwe, Eovisi Thodwi watiwuza kuti mwambowu ulunjikanso pa kuzindilikitsa zambiri za chikhalidwe cha mtundu wa Alomwe
Female
Usiku wapitawu, moto olusa watentha katundu wa ndalama zankhaninkhani ku msika wawukulu wa Ndirande. Mbali yomwe yapsayi ndi pomwe anthu amakwelera minibus zolunjika ku Limbe
Usiku wapitawu, moto olusa watentha katundu wa ndalama zankhaninkhani ku msika wawukulu wa Ndirande. Mbali yomwe yapsayi ndi pomwe anthu amakwelera minibasi zolunjika ku Limbe
Female
pafupi ndi msewu olowera Ku sukulu ya secondary Namalimwe. Motowu unayamba thawi 20 past 7 ndipo wayaka kwa ka nthawi ngakhale anthu amayesesa kuwuzimitsa, koma sizimabala zipatso
pafupi ndi msewu olowera Ku sukulu ya sekondale Namalimwe. Motowu unayamba thawi twente pasiti seveni ndipo wayaka kwa ka nthawi ngakhale anthu amayesesa kuwuzimitsa, koma sizimabala zipatso
Female
Pomwe nkhawa inakula kuti motowu utha kukhuza mbali ya chipatala cha Ndirande chomwe chili pafupi ndi pomwe unayambira kuyaka ndi pomwe anthu ozimitsa moto amafika ndi galimoto zawo ndipo anathandizira kwambiri kuti ugonje

Komabe, pomwe ozimitsa motowa amafika, anthu ena anali okwiya ponena kuti achedwa ndipo anayamba kuwagenda miyala zomwe sizinakondweletse anthu ena omwe analeletsa izi
Komabe, pomwe ozimitsa motowa amafika, anthu ena anali okwiya ponena kuti achedwa ndipo anayamba kuwagenda miyala zomwe sizinakondweletse anthu ena omwe analeletsa izi
Female
Pakadali pano, wa pa mpando wa msika wa Ndirande, Chancy Widon wati izi ndi zokhumudwitsa ponena kuti zibwezeretsa ntchito za malonda mu msikawu
Pakadali pano, wa pa mpando wa msika wa Ndirande, Tchanse Widoni wati izi ndi zokhumudwitsa ponena kuti zibwezeretsa ntchito za malonda mu msikawu
Female
Sitinakwanitse kuyankhula ndi anthu omwe shopu zawo zapsa kaamba koti anali otangwanika zedi, koma mmaonekedwe ake, amaoneka okhumudwa komanso a chisoni
Sitinakwanitse kuyankhula ndi anthu omwe shopu zawo zapsa kaamba koti anali otangwanika zedi, koma mmaonekedwe ake, amaoneka okhumudwa komanso a chisoni
Female
Katundu yemwe wapsa ndi monga zoyimba, mipando ya sofa, ma bed komanso ma tebulo. Tidakatsatirabe mwachidwi pofuna kudziwa chomwe chinachititsa kuti motowu ubuke
Katundu yemwe wapsa ndi monga zoyimba, mipando ya sofa, ma bedi komanso ma tebulo. Tidakatsatirabe mwachidwi pofuna kudziwa chomwe chinachititsa kuti motowu ubuke
Female
Apolisi ku Blantyre amanga anthu okwana 25 powaganizira kuti apalamula milandu yosiyanasiyana
Apolisi ku Bulantaya amanga anthu okwana twente faifi powaganizira kuti apalamula milandu yosiyanasiyana
Female
Mwa zina, anthuwa amangidwa pa milandu monga kupezeka ndi fodya wamkulu wa chamba, kusunga mafuta a galimoto mzigubu, kusunga katundu obedwa komanso kugula zitsulo popanda chilolezo
Mwa zina, anthuwa amangidwa pa milandu monga kupezeka ndi fodya wamkulu wa chamba, kusunga mafuta a galimoto mzigubu, kusunga katundu obedwa komanso kugula zitsulo popanda chilolezo
Female
Wachiwiri wa ofalitsa nkhani ku polisi ya Blantyre, Ivy Mwalabu watiwuza kuti anthuwa awonekera ku bwalo la milandu posachedwapa, pomwe ntchito yothana ndi mchitidwe wa umbava ndi umbanda ikupitilira
Wachiwiri wa ofalitsa nkhani ku polisi ya Bulantaya, aive Mwalabu watiwuza kuti anthuwa awonekera ku bwalo la milandu posachedwapa, pomwe ntchito yothana ndi mchitidwe wa umbava ndi umbanda ikupitilira
Female
Bungwe la anthu ochita malonda ang'onoang'ono la Small Scale Business Operators Association of Malawi lachenjeza kuti lichititsa zionetsero ngati boma silibwezeretsa ku msasa wa Dzaleka
Bungwe la anthu ochita malonda ang'onoang'ono la simo sikelo bizinezi opaletazi asosiyeshoni ofu Malawi lachenjeza kuti lichititsa zionetsero ngati boma silibwezeretsa ku msasa wa Dzaleka
Female
anthu othawa kwawo omwe sali ku msasawu, m'malo mwake akukhala m'madera ndi mizinda wa dziko lino lino
anthu othawa kwawo omwe sali ku msasawu, m'malo mwake akukhala m'madera ndi mizinda wa dziko lino lino
Female
Chenjezoli likudza pomwe posachedwapa, boma linakangalika kusamusa anthuwa kukawasiya ku Dzaleka, koma malingana ndi bungweli izi sizinaphule kanthu pomwe tsopano ambiri mwa iwo anathawako
Chenjezoli likudza pomwe posachedwapa, boma linakangalika kusamusa anthuwa kukawasiya ku Dzaleka, koma malingana ndi bungweli izi sizinaphule kanthu pomwe tsopano ambiri mwa iwo anathawako
Female
Mlembi wa bungweli, Tennyson Mulimbula wati pali za katangale zochuluka zomwe zachitika pakatipa mokhuzana ndi ntchitoyi
Mlembi wa bungweli, Tenesoni Mulimbula wati pali za katangale zochuluka zomwe zachitika pakatipa mokhuzana ndi ntchitoyi
Female
ndipo ndi chifukwa chake zina mwa mzika za mayiko ena zothawa kwawozi, zili kunja kwa msasa. Anthuwa amachita nawo ntchito za malonda zosiyanasiyana mdziko muno
ndipo ndi chifukwa chake zina mwa mzika za mayiko ena zothawa kwawozi, zili kunja kwa msasa. Anthuwa amachita nawo ntchito za malonda zosiyanasiyana mdziko muno
Female
zomwe bungwe Small Scale Business Operators limati uku ndi kuphwanya ufulu wa eni nthaka. Pamenepa, bungweli lapereka masiku khumi ndi asanu
zomwe bungwe simo sikelo bizinezi opaletazi limati uku ndi kuphwanya ufulu wa eni nthaka. Pamenepa, bungweli lapereka masiku khumi ndi asanu
Female
kuti nkhawa zawo pa nkhaniyi zikhale zayankhidwa, kulephera kutero, lichititsa zionetsero. Komatu poyankhapo pa izi, mneneri mu unduna wa chitetezo cha mdziko, a Patrick Botha
kuti nkhawa zawo pa nkhaniyi zikhale zayankhidwa, kulephera kutero, lichititsa zionetsero. Komatu poyankhapo pa izi, mneneri mu unduna wa chitetezo cha mdziko, a Patiliki Botha
Female
ati boma silikulekelera mzika iliyonse yothawa kwawo kuti izikhala kunja kwa msasa wa Dzaleka ndipo ikapezeka yotero, boma ligwiritsa ntchito lamulo
ati boma silikulekelera mzika iliyonse yothawa kwawo kuti izikhala kunja kwa msasa wa Dzaleka ndipo ikapezeka yotero, boma ligwiritsa ntchito lamulo
Female
Pali zinthu ziwiri zimene zingachitike chifukwa zitanthawuza kuti sanabwelere kufuna chitetezo. Anthuwa amenewa agwidwa ndipo athamangitsidwa mdziko muno
Pali zinthu ziwiri zimene zingachitike chifukwa zitanthawuza kuti sanabwelere kufuna chitetezo. Anthuwa amenewa agwidwa ndipo athamangitsidwa mdziko muno
Female
Ngati akufuna kuti azichitika malonda momasuka, apite ku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka akapeze ziphatso zoyenelera, atero a Botha
Ngati akufuna kuti azichitika malonda momasuka, apite ku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka akapeze ziphatso zoyenelera, atero a Botha
Female
Mfumu Kumthembwe ya ku Blantyre yapempha mbali zokhuzidwa pa nkhani za umoyo kuti zimvetse bwino bill yokhuza kuonjezera mphanvu za lamulo lolola amayi kapena atsikana kuchotsa pakati
Mfumu Kumthembwe ya ku Bulantaya yapempha mbali zokhuzidwa pa nkhani za umoyo kuti zimvetse bwino bilu yokhuza kuonjezera mphanvu za lamulo lolola amayi kapena atsikana kuchotsa pakati
Female
Termination of Pregnancy Bill, zisanapange chiganizo kapena kuthilirapo ndemanga. Bill-yi yomwe yakhala nthawi yayitali isanapite ku nyumba ya malamulo kuti aphungu akayikambirane
temineshoni ofu puleginanse bilu, zisanapange chiganizo kapena kuthilirapo ndemanga. Bilu-yi yomwe yakhala nthawi yayitali isanapite ku nyumba ya malamulo kuti aphungu akayikambirane
Female
yakhala ikukumana ndi msutso kuchokera m'magawo osiyanasiyana pomwe ena amati, ikufuna kudzetsa chisawawa pa kachotsedwe ka mimba pomwe mayi kapena mtsikana ali oyembekezera
yakhala ikukumana ndi msutso kuchokera m'magawo osiyanasiyana pomwe ena amati, ikufuna kudzetsa chisawawa pa kachotsedwe ka mimba pomwe mayi kapena mtsikana ali oyembekezera
Female
Komatu Mfumu Kunthembwe yati kumvetsetsa kwake pa bill-yi ndi koti ikufuna kupulumutsa miyoyo komanso kuthana ndi mchitidwe ochotsa mimba mosayenera omwe ukuchulukira pakadali pano
omatu Mfumu Kunthembwe yati kumvetsetsa kwake pa billu-yi ndi koti ikufuna kupulumutsa miyoyo komanso kuthana ndi mchitidwe ochotsa mimba mosayenera omwe ukuchulukira pakadali pano
Female
Kumvetsetsa kwa ine, bill iyi ikufuna iteteze miyoyo komanso izipereka danga la upangiri kwa anthu ena ofuna kuchotsa mimba kuti asatero, azaumoyo akamva mbali yawo, atero a Kunthembwe
Kumvetsetsa kwa ine, billu iyi ikufuna iteteze miyoyo komanso izipereka danga la upangiri kwa anthu ena ofuna kuchotsa mimba kuti asatero, azaumoyo akamva mbali yawo, atero a Kunthembwe
Female
Mfumuyi imayankhula pa mkumano omwe bungwe la Coalition for the Prevention of Unsafe Abortion linachititsa mdera lake, omwe cholinga chake chachikulu chinali kuzindikilitsa anthu zambiri za lamuloli
Mfumuyi imayankhula pa mkumano omwe bungwe la kowalishoni fo ve pulivenshoni ofu anisefu aboshoni linachititsa mdera lake, omwe cholinga chake chachikulu chinali kuzindikilitsa anthu zambiri za lamuloli
Female
Mkumanowu unatheka ndi thandizo lochokera ku bungwe la Solidarity for African Women's Rights (SOAWR). Ndipo pothilirapo ndemanga, anthu omwe anasonkhana pa mkumanowu
Mkumanowu unatheka ndi thandizo lochokera ku bungwe la dolidalite fo afulikani wimenzi laitsi (SOWA). Ndipo pothilirapo ndemanga, anthu omwe anasonkhana pa mkumanowu
Female
omwe ndi kuphatikizapo a zipembezo, amayi komanso abambo, anati amvetsa za bill-yi ponena kuti poyamba anali ndi uthenga olakwika
omwe ndi kuphatikizapo a zipembezo, amayi komanso abambo, anati amvetsa za billu-yi ponena kuti poyamba anali ndi uthenga olakwika
Female
Malipoti ena amati boma likugwiritsa ntchito ndalama za nkhaninkhani kuthandiza amayi ndi atsikana omwe achotsa mimba popanda thandizo la chipatala
Malipoti ena amati boma likugwiritsa ntchito ndalama za nkhaninkhani kuthandiza amayi ndi atsikana omwe achotsa mimba popanda thandizo la chipatala
Female
Mfumu Somanje Makata ya ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre yati, tsopano anthu ambiri ayamba kuzindikira za kufunika kotenga mbali mu kafukufuku osiyanasiyana
Mfumu Somanje Makata ya ku Ndirande mu mzinda wa Bulantaya yati, tsopano anthu ambiri ayamba kuzindikira za kufunika kotenga mbali mu kafukufuku osiyanasiyana
Female
okhuza umoyo maka pa nthenda ya HIV and AIDS. Iwo ayankhula izi lero mu mzinda wa Blantyre pambuyo pa mkumano omwe bungwe lomwe limagwira ntchito ngati n'khalapakati wa anthu
okhuza umoyo maka pa nthenda ya etchiaivi andi edzi. Iwo ayankhula izi lero mu mzinda wa Bulantaya pambuyo pa mkumano omwe bungwe lomwe limagwira ntchito ngati n'khalapakati wa anthu
Female
ofufuza-fufuza ndi anthu a mdera la Community Advisory Board-CAB, linachititsa ndi atolankhani, omwe cholinga chake chinali kuthandiza kumvetsetsa pa ntchito zake
ofufuza-fufuza ndi anthu a mdera la komyunite adivaizale bodi-siebi, linachititsa ndi atolankhani, omwe cholinga chake chinali kuthandiza kumvetsetsa pa ntchito zake
Female
Malingana ndi a Somanje Makata, omwe ndi membala oimira mafumu ku bungwe la CAB, kuyika chidwi pa ntchito yozindikiritsa anthu pa kufunika kwa ntchito za kafukufukuyu
Malingana ndi a Somanje Makata, omwe ndi membala oimira mafumu ku bungwe la siebi, kuyika chidwi pa ntchito yozindikiritsa anthu pa kufunika kwa ntchito za kafukufukuyu
Female
ndi komwe kwathandiza kuti anthuwa azikhalanso ndi chidwi chotenga nawo mbali popereka maganizo ndi zina, pomwe akuchitika
ndi komwe kwathandiza kuti anthuwa azikhalanso ndi chidwi chotenga nawo mbali popereka maganizo ndi zina, pomwe akuchitika
Female
Ndipo m'mawu ake, wa pa mpando wa bungwe la CAB, David Odali wati ntchito zawo ngati bungwe zathandizira kwambiri kupeza njira za makono zoletsera kufala kwa HIV, mwa zina
Ndipo m'mawu ake, wa pa mpando wa bungwe la siebi, Devidi Odali wati ntchito zawo ngati bungwe zathandizira kwambiri kupeza njira za makono zoletsera kufala kwa Etchiaivi, mwa zina
Female
Taona kusintha kwambiri pa chidwi cha anthu pa kafukufuku yemwe a John Hopkins amachita mdziko muno. Anthu ambiri tsopano akumatenga nawo mbali pa kafukufuku ndipo zimenezi zimatisangalatsa zedi
Taona kusintha kwambiri pa chidwi cha anthu pa kafukufuku yemwe a Joni Hopukinzi amachita mdziko muno. Anthu ambiri tsopano akumatenga nawo mbali pa kafukufuku ndipo zimenezi zimatisangalatsa zedi
Female
atero a Odali. Bungwe la CAB lomwe liri pansi pa project ya John Hopkins lili ndi mamembala ochokera ku m'magawo osiyanasiyana
atero a Odali. Bungwe la siebi lomwe liri pansi pa pulojekiti ya Joni Hopukinzus lili ndi mamembala ochokera ku m'magawo osiyanasiyana
Female