audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
kuphatikizapo achinyamata, a malonda, omenyera maufulu aanthu, atolankhani komanso mafumu. Katundu wa ndalama zopitilira K20 Million | kuphatikizapo achinyamata, a malonda, omenyera maufulu aanthu, atolankhani komanso mafumu. Katundu wa ndalama zopitilira twente miliyoni kwcha | Female | |
waonongeka pa ngozi ya moto wa magetsi yomwe yakhudza nyumba yowulutsira mawu ya Mzati FM komanso Television ku Mulanje | waonongeka pa ngozi ya moto wa magetsi yomwe yakhudza nyumba yowulutsira mawu ya Mzati efuemu komanso Televizyoni ku Mulanje | Female | |
Ofalitsa nkhani za Mzati Media, Mercy Madzi wati akukayikira kuchuluka kwa moto wa magetsi a ESCOM ngati gwero la kupsa kwa katunduyu | Ofalitsa nkhani za Mzati Midiya, Mese Madzi wati akukayikira kuchuluka kwa moto wa magetsi a Esikomu ngati gwero la kupsa kwa katunduyu | Female | |
Pakadali pano, boma lati lizipereka kuonotsetsa kuti wailesiyi iyambirenso kuwulutsa mawu ndi zithunzi. Nduna ya zofalitsa nkhani, Moses Kunkuyu | Pakadali pano, boma lati lizipereka kuonotsetsa kuti wailesiyi iyambirenso kuwulutsa mawu ndi zithunzi. Nduna ya zofalitsa nkhani, Mozesi Kunkuyu | Female | |
yayendera nyumbayi lero komwe yati, ngoziyi yasokoneza chitukuko pa kapezedwe ka mauthenga pakati pa anthu | yayendera nyumbayi lero komwe yati, ngoziyi yasokoneza chitukuko pa kapezedwe ka mauthenga pakati pa anthu | Female | |
Makolo anjatidwa kaamba kolephera kusamalira ana awo. Apolisi ku Blantyre amanga makolo ena kaamba kolephera kupereka chisamaliro kwa ana awo | Makolo anjatidwa kaamba kolephera kusamalira ana awo. Apolisi ku Bulantaya amanga makolo ena kaamba kolephera kupereka chisamaliro kwa ana awo | Female | |
Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani ku polisi ya Blantyre, Ivy Mwalabu, makolowa omwe alipo atatu ndi a Akim Msinchalo, Patricia Zidana komanso a Fales Sumsa | Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani ku polisi ya Bulantaya, Aive Mwalabu, makolowa omwe alipo atatu ndi a Akimu Msinchalo, Patilisha Zidana komanso a Falesi Sumsa | Female | |
Kaamba kosowa chisamaliro cha makolo, anawa amayanda kuyendayenda mmisewu ya mu mzindawu,atero a Mwalabu. Pakadali pano, wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi ya Blantyre-yu | Kaamba kosowa chisamaliro cha makolo, anawa amayanda kuyendayenda mmisewu ya mu mzindawu,atero a Mwalabu. Pakadali pano, wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi ya Bulantaya-yu | Female | |
wati apolisi apitilira kufufuza makolo a ana ena kuti awagwire ndi kukayankha milandu. Kumayambiliro a mwezi uno, apolisi anagwira ana ena asanu ndi atatu | wati apolisi apitilira kufufuza makolo a ana ena kuti awagwire ndi kukayankha milandu. Kumayambiliro a mwezi uno, apolisi anagwira ana ena asanu ndi atatu | Female | |
omwe amangozungulira-zungulira mu mzinda wa Blantyre ndipo titawafunsa anatiwuza kuti anasiya kupita ku sukulu ndipo anatumizidwa ndi makolo awo kuti apite mmisewu | omwe amangozungulira-zungulira mu mzinda wa Blulantaya ndipo titawafunsa anatiwuza kuti anasiya kupita ku sukulu ndipo anatumizidwa ndi makolo awo kuti apite mmisewu | Female | |
azikafunafuna thandizo la maanja awo, afotokoza motero a Mwalabu. A Msinchalo, a Zidana komanso a Sumsa awatsegulira mlandu olekelera udindo opereka chakudya kwa ana | azikafunafuna thandizo la maanja awo, afotokoza motero a Mwalabu. A Msinchalo, a Zidana komanso a Sumsa awatsegulira mlandu olekelera udindo opereka chakudya kwa ana | Female | |
ndipo aonekera ku bwalo la milandu posachedwa. A Grivis Chirwa a ku Mzuzu apambana mphoto ya ndalama zokwana K1 million mu mpikisano wa Zanga Phee omwe banki ya First Capital (FCB) imachititsa | ndipo aonekera ku bwalo la milandu posachedwa. A Gilivinzi Chirwa a ku Mzuzu apambana mphoto ya ndalama zokwana wani miliyoni kwacha mu mpikisano wa Zanga Phee omwe banki ya fersiti kapito (efusibi) imachititsa | Female | |
Mpikisanowu, omwe cholinga chake chinali kupereka ngongole kwa ogwira ntchito m'boma okha, wakhalapo kwa miyezi itatu yapitayi | Mpikisanowu, omwe cholinga chake chinali kupereka ngongole kwa ogwira ntchito m'boma okha, wakhalapo kwa miyezi itatu yapitayi | Female | |
Poyankhula pa mwambo wa mayere otsiriza a mpikisanowu ku Blantyre, mkulu wa nthambi ya za malonda ku FCB, Twikale Chirwa wati pomwe mpikisano wa Zanga Phee unali mkati | Poyankhula pa mwambo wa mayere otsiriza a mpikisanowu ku Bulantaya, mkulu wa nthambi ya za malonda ku efusibi, Twikale Chirwa wati pomwe mpikisano wa Zanga Phee unali mkati | Female | |
ndalama zokwana K10 billion zaperekedwa kwa anthu ngati ngongole. Cholinga cha mpikisanowu chinali kuthandiza anthu kupeza ndalama zomwe angagwiritse ntchito pa zofunika pa moyo wawo | ndalama zokwana teni biliyoni kwacha zaperekedwa kwa anthu ngati ngongole. Cholinga cha mpikisanowu chinali kuthandiza anthu kupeza ndalama zomwe angagwiritse ntchito pa zofunika pa moyo wawo | Female | |
Munthu wina wafa, sitima ya pa mtunda itamugunda ku Machijiri. Apolisi sanabwere poyera kufotokoza zambiri za nkhaniyi koma anthu ena akuti mkuluyu anayika zomvera nyimbo m'makutu | Munthu wina wafa, sitima ya pa mtunda itamugunda ku Machijiri. Apolisi sanabwere poyera kufotokoza zambiri za nkhaniyi koma anthu ena akuti mkuluyu anayika zomvera nyimbo m'makutu | Female | |
zomwe zachititsa kuti sitimayi imugunde pa nthawi yomwe amayenda mu njanje, kaamba koti sanamve mkokomo wake, pomwe imabwera | zomwe zachititsa kuti sitimayi imugunde pa nthawi yomwe amayenda mu njanje, kaamba koti sanamve mkokomo wake, pomwe imabwera | Female | |
Banki ya First Capital-FCB yasankha mayi Agnes Jazza kukhala mkulu wa bankiyi | Banki ya fesiti kapiti-Efusibi yasankha mayi Aginesi Jaza kukhala mkulu wa bankiyi | Female | |
Wa pa mpando wa bankiyi, Terence Davidson wati mayi Jazza omwe ayamba kugwira ntchito pa 21 July chaka chino, ali ndi ukadawulo pa ntchitoyi potengera kutalika kwa nthawi yomwe iwo akhala ku bankiyi | Wa pa mpando wa bankiyi, Terensi Devisoni wati mayi Jaza omwe ayamba kugwira ntchito pa twente wani julayi chaka chino, ali ndi ukadawulo pa ntchitoyi potengera kutalika kwa nthawi yomwe iwo akhala ku bankiyi | Female | |
Kalata yomwe atulutsa a Davidson yati mayi Mayi Jazza akhala akugwira ntchito ndi banki ya First Capital kwa zaka 25 | Kalata yomwe atulutsa a Devisoni yati mayi Mayi Jaza akhala akugwira ntchito ndi banki ya Fesiti kapito kwa zaka twente faifi | Female | |
Iwo alowa mmalo mwa a Spiro George omwe nthawi yawo yokhala pa udindowu inatha. Mtsogoleri wa Football Association of Malawi Walter Nyamilandu Manda | Iwo alowa mmalo mwa a Sipilo joji omwe nthawi yawo yokhala pa udindowu inatha. Mtsogoleri wa futubo asosiyeshoni ofu Malawi wota Nyamilandu Manda | Female | |
wasankhidwa kukhala membala komiti yoyendesa masewero a mpira wamiyendo wa mu Africa ku bungwe la CAF | wasankhidwa kukhala membala komiti yoyendesa masewero a mpira wamiyendo wa mu Afilika ku bungwe la KAFU | Female | |
Pa chisankho chomwe chachitikira mu mzinda wa Abidjan mdziko la Ivory Coast, Anyamilandu apeza mavoti 35 pa mavoti 54 omwe nthumwi zinaponya kunsonkhano waukuluwu | Pa chisankho chomwe chachitikira mu mzinda wa Abijani mdziko la aivole kositi, Anyamilandu apeza mavoti fete faifi pa mavoti fifite folo omwe nthumwi zinaponya kunsonkhano waukuluwu | Female | |
Iwo amapikitsana ndi Mohamed Ali ochokera ku Molicious komanso a Mokhosi Mohapi aku Lesotho apeza mavoti 15 komanso 5 pa chisankhochi | Iwo amapikitsana ndi Muhamadi Ali ochokera ku Molishasi komanso a Mokhosi Mohapi aku Lesotho apeza mavoti fifitini komanso faifi pa chisankhochi | Female | |
Ecobank yati chitetezo chokhwima ndi gwero la tsogolo labwino pa malonda, pomwe anthu amachita zinthu zawo momasuka komanso mopanda mantha | Ekobanki yati chitetezo chokhwima ndi gwero la tsogolo labwino pa malonda, pomwe anthu amachita zinthu zawo momasuka komanso mopanda mantha | Female | |
Mkulu wa bankiyi, Fabiano Makolija ndi yemwe wanena izi pomwe amapereka thandizo la ndalama zokwana K5.1 million ku polisi ya Blantyre | Mkulu wa bankiyi, Fabiano Makolija ndi yemwe wanena izi pomwe amapereka thandizo la ndalama zokwana faifi pointi wani miliyoni ku polisi ya Bulantaya | Female | |
yomwe ithandize pa ntchito yoyika ma camera a CCTV mu mzindawu yomwe ndi ya ndalama zokwana K18 million | yomwe ithandize pa ntchito yoyika ma kamela a sisitivi mu mzindawu yomwe ndi ya ndalama zokwana eitini miliyoni Kwacha | Female | |
Malingana ndi a Makolija, anthu komanso kampani kuphatikizapo banki zimafuna chitetezo chokhwima | Malingana ndi a Makolija, anthu komanso kampani kuphatikizapo banki zimafuna chitetezo chokhwima | Female | |
ndipo ichi ndi chifukwa chake aganiza zopereka thandizoli pofuna kuthandizira ntchito yokhwimitsa chitetezo | ndipo ichi ndi chifukwa chake aganiza zopereka thandizoli pofuna kuthandizira ntchito yokhwimitsa chitetezo | Female | |
Ndipo mmawu ake, mkulu wa apolisi mchigawo cha kum'mwera cha ku madzulo, Richard Luhanga wati ndi okondwa Kuti bankiyi yapereka thandizoli pa ntchito yomwe cholinga chake ndi kuthana ndi umbava ndi umbanda | Ndipo mmawu ake, mkulu wa apolisi mchigawo cha kum'mwera cha ku madzulo, Litchadi Luhanga wati ndi okondwa Kuti bankiyi yapereka thandizoli pa ntchito yomwe cholinga chake ndi kuthana ndi umbava ndi umbanda | Female | |
Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera wakhululukira akayidi okwana 2,298 kuchokera mndende zosiyanasiyana za dziko lino | Mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera wakhululukira akayidi okwana thu sauzande thu handede andi nainte eiti kuchokera mndende zosiyanasiyana za dziko lino | Female | |
ngati mbali imodzi ya chikondwelero choti dziko lino lakwanitsa zaka 59 liri pa ufulu ozilamulira. Malingana ndi kalata yomwe wasayinira ndi mlembi wa unduna wa za chitetezo cha m'dziko, Oliver Kumbambe | ngati mbali imodzi ya chikondwelero choti dziko lino lakwanitsa zaka fifite naini liri pa ufulu ozilamulira. Malingana ndi kalata yomwe wasayinira ndi mlembi wa unduna wa za chitetezo cha m'dziko, Oliva Kumbambe | Female | |
anthu okhululukilidwawa ndi omwe agwira theka la zilango zomwe analandira, okalamba komanso omwe akudwala ndipo kuti akwanilitsa mfundo zomwe munthu ayenera kukhululukilidwira monga kuonetsa khalidwe labwino | anthu okhululukilidwawa ndi omwe agwira theka la zilango zomwe analandira, okalamba komanso omwe akudwala ndipo kuti akwanilitsa mfundo zomwe munthu ayenera kukhululukilidwira monga kuonetsa khalidwe labwino | Female | |
Pakadali pano, bungwe la Centre for Human Rights Education Advice and Assistance kudzera mwa mkulu wake, Victor Mhango layamikira boma pa izi | Pakadali pano, bungwe la senta fo hyumani laitsi edyukeshoni adivaizi andi asisitansi kudzera mwa mkulu wake, Vikita Mhango layamikira boma pa izi | Female | |
ponena kuti zithandize kuchepesa chiwerengero cha akayidi mndendezi, chomwe pano ndi chokwera zedi. Chipani cha AFORD lero chikuchititsa msonkhano wa ndale kwa Bvumbwe m'boma la Thyolo | ponena kuti zithandize kuchepesa chiwerengero cha akayidi mndendezi, chomwe pano ndi chokwera zedi. Chipani cha AFODI lero chikuchititsa msonkhano wa ndale kwa Bvumbwe m'boma la Thyolo | Female | |
komwe atsogoleri ake akuti akudandawula limodzi ndi aMalawi pa zokhoma komanso zosamwitsa zomwe anthu akukumana nazo | komwe atsogoleri ake akuti akudandawula limodzi ndi aMalawi pa zokhoma komanso zosamwitsa zomwe anthu akukumana nazo | Female | |
Mwa zina, anthu ena omwe asonkhana pa msonkhawu pa bwalo la Chisawani atiwuza kuti ndalama zikuwavuta kupeza, ntchito zikusowa komanso chakudya ndi chovuta, zomwe zikukolezera umphawi wa zaoneni pakati pawo | Mwa zina, anthu ena omwe asonkhana pa msonkhawu pa bwalo la Chisawani atiwuza kuti ndalama zikuwavuta kupeza, ntchito zikusowa komanso chakudya ndi chovuta, zomwe zikukolezera umphawi wa zaoneni pakati pawo | Female | |
Ndipo pothilirapo ndemanga pa izi, mlembi wa zofalitsa nkhani mchipanichi, Annie Maluwa wati zomwe akukamba anthuwa ndi zomveka pomwe tsopano dziko lino liri pa moto wa chigumu | Ndipo pothilirapo ndemanga pa izi, mlembi wa zofalitsa nkhani mchipanichi, Ani Maluwa wati zomwe akukamba anthuwa ndi zomveka pomwe tsopano dziko lino liri pa moto wa chigumu | Female | |
Koma iwo ati chipani chawo, chili ndi mayankho pa izi ndipo chifotokozere bwino nthawi yokopa anthu pa ulendo wa ku chisankho cha mu 2025 iyambikire | Koma iwo ati chipani chawo, chili ndi mayankho pa izi ndipo chifotokozere bwino nthawi yokopa anthu pa ulendo wa ku chisankho cha mu twente twente faifi iyambikire | Female | |
Pakadali pano, mtsogoleri wa chipani cha AFORD, Enoch Chihana akuyankhula kwa anthu omwe asonkhana pa bwaloli pomwe akuti utsogoleri wa chipani chawo uzayika chidwi chokweza ufulu wa democracy | Pakadali pano, mtsogoleri wa chipani cha Afodi, Enoki Chihana akuyankhula kwa anthu omwe asonkhana pa bwaloli pomwe akuti utsogoleri wa chipani chawo uzayika chidwi chokweza ufulu wa demokilase | Female | |
Iwo atinso utsogoleri wawo uzakonza ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo pomwe uzagawe ndondomekoyi pawiri, imodzi mwa Iwo, kukhala yokomera anthu okalamba ndi a maulumali osiyanasiyana | Iwo atinso utsogoleri wawo uzakonza ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo pomwe uzagawe ndondomekoyi pawiri, imodzi mwa Iwo, kukhala yokomera anthu okalamba ndi a maulumali osiyanasiyana | Female | |
Gulu la anthu ochita malonda ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre lapereka masiku asanu ndi awiri ku nkhosolo ya mzindawu kuti ikhale itayamba kumanga msika wamakono | Gulu la anthu ochita malonda ku Machinjiri mu mzinda wa Bulantaya lapereka masiku asanu ndi awiri ku nkhosolo ya mzindawu kuti ikhale itayamba kumanga msika wamakono | Female | |
pa malo wochitira malonda a Mthawila m'derali. Gululi lanena izi pa mbuyo pa zionetsero zokwiya zomwe lachita m'mawa wa lachinayi. Ofaritsa nkhani za gululi, Chikumbutso Phiri | pa malo wochitira malonda a Mthawila m'derali. Gululi lanena izi pa mbuyo pa zionetsero zokwiya zomwe lachita m'mawa wa lachinayi. Ofaritsa nkhani za gululi, Chikumbutso Phiri | Female | |
wati nkhosolo ya mzindawu inalonjeza zomanga msika pa malopa m'chaka cha 2017, koma kufikira pano palibe chomwe chikuchitika | wati nkhosolo ya mzindawu inalonjeza zomanga msika pa malopa m'chaka cha twente seventini, koma kufikira pano palibe chomwe chikuchitika | Female | |
Pamenepa, a Phiri ati ngati nkhosolo'yi isankhe kusayankha pempho lawo, iwo sachitira mwina koma kukapanga m'bidikiro ku nyumba ya chi mfumu (state house) pofuna kupeza thandizo | Pamenepa, a Phiri ati ngati nkhosolo'yi isankhe kusayankha pempho lawo, iwo sachitira mwina koma kukapanga m'bidikiro ku nyumba ya chi mfumu (siteti hausi) pofuna kupeza thandizo | Female | |
Komatu ngakhale nthumwi ya ku khonsoloyi yalandira kalata ya madandawulo pa izi yomwe anthuwa anatenga, mneneri wake, Deborah Luka watiwuza kuti sakudziwa kalikonse za izi | Komatu ngakhale nthumwi ya ku khonsoloyi yalandira kalata ya madandawulo pa izi yomwe anthuwa anatenga, mneneri wake, Debora Luka watiwuza kuti sakudziwa kalikonse za izi | Female | |
Anthuwa sanafike kuno, koma ndidikireni ndifufuze, ndikuwuzani, atero mayi Luka. Chipani cha Malawi Congress-MCP | Anthuwa sanafike kuno, koma ndidikireni ndifufuze, ndikuwuzani, atero mayi Luka. Chipani cha Malawi kongilesi-Emusipi | Female | |
chati chayamba kuchita mikumano ndi atsogoleri ake a mmadera komanso mzigawo, yomwe cholinga chake ndikulimbitsa ngodya za chipanichi patsogolo pa zisankho za mchaka cha 2025, komanso zisankho zina | chati chayamba kuchita mikumano ndi atsogoleri ake a mmadera komanso mzigawo, yomwe cholinga chake ndikulimbitsa ngodya za chipanichi patsogolo pa zisankho za mchaka cha twente twente faifi, komanso zisankho zina | Female | |
Chipanichi dzulo chinakumana ndi atsogoleri ake ochokera mmadera aaphungu komanso makhansala, mwa ena, a chigawo cha ku m'mwera | Chipanichi dzulo chinakumana ndi atsogoleri ake ochokera mmadera aaphungu komanso makhansala, mwa ena, a chigawo cha ku m'mwera | Female | |
Poyankhula pa mkumanowu, mlembi wa MCP, Eisenhower Mkaka anati akufuna chipani chawo chikhale cha mphanvu mmaderawa | Poyankhula pa mkumanowu, mlembi wa emusipi, isenihova Mkaka anati akufuna chipani chawo chikhale cha mphanvu mmaderawa | Female | |
Ndipo mbali inayi, wa pa mpando wake ku chigawo cha ku m'mwera, Peter Simbi anati chipani chawo chikudziwa kufunika kolimbikitsa anthu | Ndipo mbali inayi, wa pa mpando wake ku chigawo cha ku m'mwera, Pita Simbi anati chipani chawo chikudziwa kufunika kolimbikitsa anthu | Female | |
kuti akhale odzuka, potengera kuti chakhala kunja kwa boma kwa zaka 26. Pakadali pano, katswiri pa nkhani za ndale, Enerst Thindwa wayamikira MCP pa izi | kuti akhale odzuka, potengera kuti chakhala kunja kwa boma kwa zaka twente sikisi. Pakadali pano, katswiri pa nkhani za ndale, EnesitiThindwa wayamikira emusipi pa izi | Female | |
ndipo wati zipani zina zitengerepo phunziro, osati kuchita ndale za mzigawo kapena kusankhana mitundu. Tikudziwa chomwe chimavuta ku zipani zinazi ndi kuchita zinthu motengera mitundu komanso zigawo | ndipo wati zipani zina zitengerepo phunziro, osati kuchita ndale za mzigawo kapena kusankhana mitundu. Tikudziwa chomwe chimavuta ku zipani zinazi ndi kuchita zinthu motengera mitundu komanso zigawo | Female | |
zomwe pamapeto pake zimazabala mavuto monga pa nthawi ya misonkhano yayikulu pa yemwe ayenera kuvota posankha adindo ndi zina | zomwe pamapeto pake zimazabala mavuto monga pa nthawi ya misonkhano yayikulu pa yemwe ayenera kuvota posankha adindo ndi zina | Female | |
yapereka ndalama zokwana K15 million ku chipatala chothandiza ana a ulumuli osiyanasiyana wa mafupa cha Beit Cure International mu mzinda wa Blantyre | yapereka ndalama zokwana fifitini miliyoni kwacha ku chipatala chothandiza ana a ulumuli osiyanasiyana wa mafupa cha beti kyuwa intaneshono mu mzinda wa Bulantaya | Female | |
Thandizoli likudza patsogolo pa mgonero ofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito za chipatalachi omwe chikufuna kuchititsa pa 4 August chaka chino | Thandizoli likudza patsogolo pa mgonero ofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito za chipatalachi omwe chikufuna kuchititsa pa folo Ogasiti chaka chino | Female | |
Poyankhula pomwe amapeleka thandizoli dzulo, mkulu wa nthambi ya za malonda komanso kufalitsa mauthenga ku FCB, a Twikale Chirwa | Poyankhula pomwe amapeleka thandizoli dzulo, mkulu wa nthambi ya za malonda komanso kufalitsa mauthenga ku efusibi, a Twikale Chirwa | Female | |
anati banki yawo imakhulupilira kuti chipatala cha Beit Cure chimagwira ntchito zake ndi masomphenya otukula anthu pa chuma poonetsetsa kuti mibadwo izikula ya nthanzi ndinso ya mphanvu | anati banki yawo imakhulupilira kuti chipatala cha Beti kyuwa chimagwira ntchito zake ndi masomphenya otukula anthu pa chuma poonetsetsa kuti mibadwo izikula ya nthanzi ndinso ya mphanvu | Female | |
Ichitu akuti ndi chifukwa chake iwo aganiza zothandizapo pa mgonerowu. Mmawu ake, mkulu wa chipatala cha Beit Cure, Elly Chemey | Ichitu akuti ndi chifukwa chake iwo aganiza zothandizapo pa mgonerowu. Mmawu ake, mkulu wa chipatala cha beti kyuwa, Eli Chime | Female | |
anati thandizo lomwe chipatalachi chalandira kuchokera ku FCB, ladza mu nthawi yake ndipo lithandiza kuti afikire ana ochuluka ndi ntchito zawo | anati thandizo lomwe chipatalachi chalandira kuchokera ku Efusibi, ladza mu nthawi yake ndipo lithandiza kuti afikire ana ochuluka ndi ntchito zawo | Female | |
Chipatalachi chimafunika ndalama pafupifupi K1.5 million kuti chithandize mwana m'modzi ndi thandizo loyenelera | Chipatalachi chimafunika ndalama pafupifupi wani pointi faifi miliyoni kwacha kuti chithandize mwana m'modzi ndi thandizo loyenelera | Female | |
Anthu 17 afa pa ngozi ya galimoto yomwe yachitika mu msewu wa Chitipa-Karonga. Izi, malingana ndi malipoti zachitika pa malo a Tenede | Anthu seventini afa pa ngozi ya galimoto yomwe yachitika mu msewu wa Chitipa-Karonga. Izi, malingana ndi malipoti zachitika pa malo a Tenede | Female | |
pomwe dalaivala wa galimotoyi yomwe ndi mtundu wa lorry, Moses Mkandawire analephera kuongolera bwino pa gulaye lina. Anthuwa ndi ena omwe pamodzi analipo 80, akuti ndi otsatira timu ina ya mpira | pomwe dalaivala wa galimotoyi yomwe ndi mtundu wa lore, Mozesi Mkandawire analephera kuongolera bwino pa gulaye lina. Anthuwa ndi ena omwe pamodzi analipo eite, akuti ndi otsatira timu ina ya mpira | Female | |
Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha Afro Pop, Wikise watulutsa nyimbo ya tsopano yomwe mutu wake akuti Male | Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha afulo popu, Wikise watulutsa nyimbo ya tsopano yomwe mutu wake akuti Male | Female | |
Mu nyimboyi, Wikise yemwe dzina lake lenileni ndi Frank Chawinga akusimba za ubwino wa mkazi wina yemwe wagwa naye mchikondi koma anasiyidwapo ndi mwamuna wina ex-lover | Mu nyimboyi, Wikise yemwe dzina lake lenileni ndi Fulanki Chawinga akusimba za ubwino wa mkazi wina yemwe wagwa naye mchikondi koma anasiyidwapo ndi mwamuna wina ekisi-lava | Female | |
Nyimboyi, yomwe yayamba kale kuseweredwa mu wailesi zosiyanasiyana mdziko muno komanso yatenga kale chikoka cha anthu pa masamba a mchezo, Wikise wayimba limodzi ndi Don Kalonga | Nyimboyi, yomwe yayamba kale kuseweredwa mu wailesi zosiyanasiyana mdziko muno komanso yatenga kale chikoka cha anthu pa masamba a mchezo, Wikise wayimba limodzi ndi Doni Kalonga | Female | |
Posachedwapa, oyimbayu anatulutsanso nyimbo ina yomwe mutu wake amati Mwana wa Agama, Mwana wa zaka 4, Vincent Mphaso wafa, agalu olusa atamuluma pa mudzi pa Mwera | Posachedwapa, oyimbayu anatulutsanso nyimbo ina yomwe mutu wake amati Mwana wa Agama, Mwana wa zaka folo, Vinisenti Mphaso wafa, agalu olusa atamuluma pa mudzi pa Mwera | Female | |
ku Chitipi m'boma la Lilongwe. Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi ku Lilongwe-ko, Foster Benjamin watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti izi zachitika pomwe Vincent ndi mchimwene wake wina | ku Chitipi m'boma la Lilongwe. Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi ku Lilongwe-ko, Fosita Benjamini watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti izi zachitika pomwe Vinisenti ndi mchimwene wake wina | Female | |
amatsatira mayi awo ku malo awo ogwira ntchito komwe amaweterako agaluwa. Mayiyu, Chifundo Mphaso, yemwe samadziwa kuti ana akewa anali pambuyo pake | amatsatira mayi awo ku malo awo ogwira ntchito komwe amaweterako agaluwa. Mayiyu, Chifundo Mphaso, yemwe samadziwa kuti ana akewa anali pambuyo pake | Female | |
anatsegulira agaluwa ndipo zotsatira zake inali ngoziyi, atero a Benjamin. Agalu olusawa avulazanso mayiyu komanso mkulu wake wa Vincent | anatsegulira agaluwa ndipo zotsatira zake inali ngoziyi, atero a Benjamini. Agalu olusawa avulazanso mayiyu komanso mkulu wake wa Vinisenti | Female | |
Amayi komanso atsikana oyembekezera pafupifupi 4 thousand omwe anachotsa pa thupi mosasata ndondomeko za chipatala, akuti analandira thandizo la chipatala mzipitala zosiyanasiyana m'boma la Blantyre chaka chatha | Amayi komanso atsikana oyembekezera pafupifupi folo sauzande omwe anachotsa pa thupi mosasata ndondomeko za chipatala, akuti analandira thandizo la chipatala mzipitala zosiyanasiyana m'boma la Bulantaya chaka chatha | Female | |
Izi zawululika ku Chileka m'bomali, komwe bungwe la Ipas mogwirizan ndi bungwe la Young Voices of Malawi likuchita zokambirana ndi adindo komanso anthu ena okhuzidwa pa nkhani za ubereki ndi uchembere wabwino | Izi zawululika ku Chileka m'bomali, komwe bungwe la aipasi mogwirizan ndi bungwe la yang’I voisezi ofu Malawi likuchita zokambirana ndi adindo komanso anthu ena okhuzidwa pa nkhani za ubereki ndi uchembere wabwino | Female | |
Kuonjezera apo, mabungwewa likuzindikilitsanso anthu za bill ya tsopano yokhuza lamulo lochotsa mimba pakati pa amayi ndi atsikana | Kuonjezera apo, mabungwewa likuzindikilitsanso anthu za billu ya tsopano yokhuza lamulo lochotsa mimba pakati pa amayi ndi atsikana | Female | |
Malingana ndi malipoti omwe atumphuka, atsikana a zaka za pakati pa 20 kufika 24 pafupifupi 900 komanso ena a zaka za pakati pa 25 kufika 29 | Malingana ndi malipoti omwe atumphuka, atsikana a zaka za pakati pa twente kufika twente folo pafupifupi naini handiledi komanso ena a zaka za pakati pa twente faifi kufika twentenaini | Female | |
pafupifupi 800 ndi omwe alandira thandizoli, kutsatira kuchotsa mimba. Amuna atatu, Enock Chirwa, Ishmael Akim komanso Vinkula Kavwenje | pafupifupi eiti handiledi ndi omwe alandira thandizoli, kutsatira kuchotsa mimba. Amuna atatu, inoki Chirwa, Ishumaeli Akimu komanso Vinkula Kavwenje | Female | |
ali mchitokosi cha apolisi ku Blantyre, powaganizira kuti anapezeka ndi ndalama za pepala, koma za chinyengo. Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi mchigawo cha ku m'mwera cha ku madzulo kwa dziko lino | ali mchitokosi cha apolisi ku Bulantaya, powaganizira kuti anapezeka ndi ndalama za pepala, koma za chinyengo. Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi mchigawo cha ku m'mwera cha ku madzulo kwa dziko lino | Female | |
Beatrice Mikuwa watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti amunawa, amafuna kutumiza ndalamazi, zomwe ndi ma 5 thousand kwacha okwana K40,000, pa agent wina ku Chitawira | Bitilisi Mikuwa watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti amunawa, amafuna kutumiza ndalamazi, zomwe ndi ma faifi sauzande kwacha okwana fote sauzande kwacha, pa ajenti wina ku Chitawira | Female | |
Malingana ndi Mikuwa, agent-yu anadziwitsa apolisi za nkhaniyi omwe sanachedwe koma kunjata oganizilidwawa | Malingana ndi Mikuwa, ajenti-yu anadziwitsa apolisi za nkhaniyi omwe sanachedwe koma kunjata oganizilidwawa | Female | |
Timu ya mpira wa miyendo koma osewera ake kukhala akazi ya Mtopwa yati isewera nawo mu mpikisano wa chikho cha COSAFA Women Club Championship | Timu ya mpira wa miyendo koma osewera ake kukhala akazi ya Mtopwa yati isewera nawo mu mpikisano wa chikho cha KOSAFA wimeni kilabu tchampiyonishipi | Female | |
omwe uchitikire mdziko la South Africa m'mwezi wa August Chaka chino. Mpikisanowu uzayamba pa 10 ndipo uzatha pa 28 August | omwe uchitikire mdziko la Saufi afilika m'mwezi wa ogasitit Chaka chino. Mpikisanowu uzayamba pa teni ndipo uzatha pa twente eiti Ogasiti | Female | |
ndipo monga mwa nthawi zonse, ukhudzanso matimu omwe achita bwino mu mipikisano ya maiko awo. Timu ya Mtopwa inakhala akatswiri a chikho cha mpira wa miyendo osewera ake amayi Cha FAM Women National Championship | ndipo monga mwa nthawi zonse, ukhudzanso matimu omwe achita bwino mu mipikisano ya maiko awo. Timu ya Mtopwa inakhala akatswiri a chikho cha mpira wa miyendo osewera ake amayi Cha FAMU wimeni neshono tchampiyonishipi | Female | |
Mwini wake wa timuyi, Isaac Jomo Osman, watiwuza kuti akuyamba dongosolo lofikira anthu komanso kampani zosiyanasiyana ndi kuzipempha thandizo la ndalama ndi Zina, zomwe atsikana ake akagwiritse ntchito ku mpikisanowu | Mwini wake wa timuyi, aizeki Jomo Osimani, watiwuza kuti akuyamba dongosolo lofikira anthu komanso kampani zosiyanasiyana ndi kuzipempha thandizo la ndalama ndi Zina, zomwe atsikana ake akagwiritse ntchito ku mpikisanowu | Female | |
Boma silikubwelera mmbuyo ndi ganizo lake lobwezeretsa ku msasa wa Dzaleka anthu othawa kwawo omwe amakhala kunja kwa msasawu. Kodi zimenezi inu mukuziona bwanji | Boma silikubwelera mmbuyo ndi ganizo lake lobwezeretsa ku msasa wa Dzaleka anthu othawa kwawo omwe amakhala kunja kwa msasawu. Kodi zimenezi inu mukuziona bwanji | Female | |
Mverani Ndirande FM nthawi ya 5 kololoko pomwenso mukhalenso ndi danga loyankhula pa nkhaniyi. Anjatidwa kaamba kopezeka ndi nyama ya ngaka | Mverani Ndirande efuemu nthawi ya faifi kololoko pomwenso mukhalenso ndi danga loyankhula pa nkhaniyi. Anjatidwa kaamba kopezeka ndi nyama ya ngaka | Female | |
Amuna awiri ali mchitilokosi cha polisi kaamba kopezeka akutsatsa malonda a ngaka ya moyo ku Limbe munzinda wa Blantyre. Wofalitsa nkhani za polisi ya Limbe Aubrey Singanyama | Amuna awiri ali mchitilokosi cha polisi kaamba kopezeka akutsatsa malonda a ngaka ya moyo ku Limbe munzinda wa Bulantaya. Wofalitsa nkhani za polisi ya Limbe Obule Singanyama | Female | |
wati awiriwa ndi Frank Ng’ambi a zaka 48 zakubadwa a mmudzi wa Ngoleka mfumu yaikulu Likoswe ku Chiradzulu | wati awiriwa ndi Fulanki Ng’ambi a zaka fote eiti zakubadwa a mmudzi wa Ngoleka mfumu yaikulu Likoswe ku Chiradzulu | Female | |
ndi a Lazarus Bakuwa a zaka 73 ochokera mudzi wa Nachamba mfumu yaikulu Machinjiri m'boma la Blantyre | ndi a Lazalasi Bakuwa a zaka sevente fili ochokera mudzi wa Nachamba mfumu yaikulu Machinjiri m'boma la Bulantaya | Female | |
A Singanyama ati lachitatu madzulo, apolisi anatsinidwa khutu kuti awiriwa akutsatsa malonda a ngaka pa Dalton court | A Singanyama ati lachitatu madzulo, apolisi anatsinidwa khutu kuti awiriwa akutsatsa malonda a ngaka pa Datoni koti | Female | |
Apolisi a zofufuzafufuza atamva za nkhaniyi anayamba kafukufuku ndipo anakwanitsa kumanga awiriwa omwe awatsekulira mlandu opezeka ndi nyama yotetezedwa, atero a Singanyama | Apolisi a zofufuzafufuza atamva za nkhaniyi anayamba kafukufuku ndipo anakwanitsa kumanga awiriwa omwe awatsekulira mlandu opezeka ndi nyama yotetezedwa, atero a Singanyama | Female | |
Pakadali pano nyamayi ayitumiza kwa owona za nkhalango ndi nyama zakutchire kuti ayisunge ndi kuyisamalira | Pakadali pano nyamayi ayitumiza kwa owona za nkhalango ndi nyama zakutchire kuti ayisunge ndi kuyisamalira | Female | |
Bungwe lalikulu loyendesa masewero ampira mziko muno la Football Association of Malawi FAM lachitisa mayere a matimu 32 ampikisano wa FDH | Bungwe lalikulu loyendesa masewero ampira mziko muno la futubo asosiyeshoni ofu malawi lachitisa mayere a matimu fetethu ampikisano wa efudietchi | Female | |
Mpikisanowu uyamba pa 17 June chaka chino ndipo ndimeyi ikuyembekezereka kuthaso mwezi omwewo wa June ndipo Draw yonse ili motere | Mpikisanowu uyamba pa seventini Juni chaka chino ndipo ndimeyi ikuyembekezereka kuthaso mwezi omwewo wa Juni ndipo Dilo yonse ili motere | Female | |
Yemwe azapambane mpikisanowu azalandira ndalama zokwana K30 Million Malawi Kwacha. Mayere a mpikisano wa masewero a mpira wa miyendo osewera pa mchenga a Beach Soccer | Yemwe azapambane mpikisanowu azalandira ndalama zokwana fete miliyoni Malawi Kwacha. Mayere a mpikisano wa masewero a mpira wa miyendo osewera pa mchenga a Bitchi soka | Female | |
achitika lero, ndi pempho loti anthu agwirane manja pofuna kuti masewerowa atukuke. Mayerewa achitikira mu mzinda wa Blantyre ndipo matimu asanu ndi imodzi ndi omwe atenge nawo mbali | achitika lero, ndi pempho loti anthu agwirane manja pofuna kuti masewerowa atukuke. Mayerewa achitikira mu mzinda wa Bulantaya ndipo matimu asanu ndi imodzi ndi omwe atenge nawo mbali | Female | |
Poyankhula pa mwambo wa mayerewa, mmodzi mwa akuluakulu ku kampani yomwe ikuthandiza mpikisanowu ya HTD Limited, Jawad Imed | Poyankhula pa mwambo wa mayerewa, mmodzi mwa akuluakulu ku kampani yomwe ikuthandiza mpikisanowu ya etchitidi limitedi, Jawadi Imedi | Female | |
anati ndi zokondweletsa kuti kampani yawo yakhala yoyamba kuyika ndalama zokwana K20 million kuti zitukule masewero otere | anati ndi zokondweletsa kuti kampani yawo yakhala yoyamba kuyika ndalama zokwana twente miliyoni kuti zitukule masewero otere | Female | |
Ndipo mmawu ake, wa pa mpando bungwe la National Beach Soccer, Gift Chimbalanga anathokoza kampani ya HTD Limited | Ndipo mmawu ake, wa pa mpando bungwe la neshono bitchi soka, Gifiti Chimbalanga anathokoza kampani ya Etchitidi limitedi | Female | |
kaamba ka thandizo lake koma wapepesa okonda masewerowa kuti achitika mochedwerako kaamba ka mavuto a za nyengo Masewerowa chaka chino achitika pa 3 ndi pa 4 June m'boma la Salima | kaamba ka thandizo lake koma wapepesa okonda masewerowa kuti achitika mochedwerako kaamba ka mavuto a za nyengo Masewerowa chaka chino achitika pa fili ndi pa folo Juni m'boma la Salima | Female | |
Mayi wa zaka 38 zakubadwa, Mercy Majawa amulipilitsa chindapusa cha ndalama zokwana K200 thousand atapezeka olakwa pa mlandu ogawa kanema olawula wa mayi mnzake pa masamba a mchezo | Mayi wa zaka fete eiti zakubadwa, Mese Majawa amulipilitsa chindapusa cha ndalama zokwana thu handiledi sauzande kwacha atapezeka olakwa pa mlandu ogawa kanema olawula wa mayi mnzake pa masamba a mchezo | Female | |
Bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate ku Limbe ndi lomwe lapeza olakwa komanso kupereka chilangochi kwa mayiyu | Bwalo la milandu la siniyo lezidenti majesitileti ku Limbe ndi lomwe lapeza olakwa komanso kupereka chilangochi kwa mayiyu | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.