audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Anthu okwana 227 amwalira ndi cholera ku Blantyre kuchokera pomwe inabuka chaka chatha. Achinyamata omwe avala makaka a chipani cha MCP | Anthu okwana thu handiledi andi twente seveni amwalira ndi kolela ku Bulantaya kuchokera pomwe inabuka chaka chatha. Achinyamata omwe avala makaka a chipani cha emusipi | Female | |
amenya achinyamata a chipani cha UTM komanso kuwononga zikwangani zawo pa Chichiri mu mzinda wa Blantyre. Izi zachitika pomwe mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera | amenya achinyamata a chipani cha yutiemu komanso kuwononga zikwangani zawo pa Chichiri mu mzinda wa Bulantaya. Izi zachitika pomwe mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera | Female | |
akutsegulira chiwonetsero cha za malonda ku Trade Fair mu mzindawu. Achinyamata ovala za makaka a MCP-wa, ang'ambanso msalu za chipani cha UTM komanso kuchotsa mbendera za chipanichi pa malopa | akutsegulira chiwonetsero cha za malonda ku thiledi feya mu mzindawu. Achinyamata ovala za makaka a emusipi-wa, ang'ambanso msalu za chipani cha yutiemu komanso kuchotsa mbendera za chipanichi pa malopa | Female | |
Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera lero atsegulira chionetsero cha za malonda ku Trade Fair pa Chichiri mu mzinda wa Blantyre | Mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera lero atsegulira chionetsero cha za malonda ku thiledi feya pa Chichiri mu mzinda wa Bulantaya | Female | |
Mtsogoleriyu atseguliranso ofesi za tsopano za bungwe la Malawi Bureau of Standards asanachititse msonkhano wa chitukuko lero lomwe | Mtsogoleriyu atseguliranso ofesi za tsopano za bungwe la Malawi byulo ofu sitandadzi asanachititse msonkhano wa chitukuko lero lomwe | Female | |
Kalata yomwe wasainira ndi wachiwiri kwa Mlembi wa mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna, Janet Banda yati zochitikachitikazi ziyamba nthawi ya 8 koloko m’mawa | Kalata yomwe wasainira ndi wachiwiri kwa Mlembi wa mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna, Jeneti Banda yati zochitikachitikazi ziyamba nthawi ya eiti koloko m’mawa | Female | |
Ophunzira khumi a pa sukulu ya secondary ya Balaka Islamic Boys ali mchitokosi cha apolisi powaganizira kuti agwililira komanso kubera ndalama zokwana K7,500 | Ophunzira khumi a pa sukulu ya sekondale ya Balaka izilamiki boizi ali mchitokosi cha apolisi powaganizira kuti agwililira komanso kubera ndalama zokwana seveni sauzande faifi handiledi kwacha | Female | |
mayi wina wa zaka 27. Mayiyu, malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani ku Balaka-ko, Mphatso Munthali, anakumana ndi tsokali pomwe amachokera ku msika waukulu m'bomalo | mayi wina wa zaka twente seveni. Mayiyu, malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani ku Balaka-ko, Mphatso Munthali, anakumana ndi tsokali pomwe amachokera ku msika waukulu m'bomalo | Female | |
n'kulanjika ku msika wa Mthandizi. A Munthali ati ophunzirawa awatsegulira mlandu ogwililira komanso kuba ndipo aonekere ku bwalo la milandu posachedwapa | n'kulunjika ku msika wa Mthandizi. A Munthali ati ophunzirawa awatsegulira mlandu ogwililira komanso kuba ndipo aonekere ku bwalo la milandu posachedwapa | ||
Mwana wa zaka 8, Alifosina Watson wamwalira m'boma la Dowa galimoto la mtundu wa Toyota Probox litamuomba pomwe amaoloka msewu | Mwana wa zaka eiti, Alifosina Watisoni wamwalira m'boma la Dowa galimoto la mtundu wa Toyota Pulo bokosi litamuomba pomwe amaoloka msewu | Female | |
Ofalitsa nkhani za apolisi ku Dowa, Gladson M'bumpha wati izi zachitikira pa msika wa Maweru m'bomali | Ofalitsa nkhani za apolisi ku Dowa, Giladisoni M'bumpha wati izi zachitikira pa msika wa Maweru m'bomali | Female | |
Wa pa mpando wa chigawo cha kumwera kwa chipani cha AFORD, Joseph Pemba wati chiyembekezo chilipo kuti chipanichi motsogozedwa ndi a Enoch Chihana chilowa m'boma pa chisankho Cha ku 2025 | Wa pa mpando wa chigawo cha kumwera kwa chipani cha AFODI, Jozefe Pemba wati chiyembekezo chilipo kuti chipanichi motsogozedwa ndi a inoki Chihana chilowa m'boma pa chisankho Cha ku twente twente faifi | Female | |
Mbali inayi, a Chris Thaulo omwe ndi wa pa mpando wa komiti yomwe imayendetsa zokonzekera za msonkhanowu wati anthu akuyenera kusintha kasankhidwe kawo ka adindo ku ndale | Mbali inayi, a khilisi Thaulo omwe ndi wa pa mpando wa komiti yomwe imayendetsa zokonzekera za msonkhanowu wati anthu akuyenera kusintha kasankhidwe kawo ka adindo ku ndale | Female | |
chifukwa atsogoleri omwe akhalapo alephera kuyendetsa dziko lino. Iwo awuza anthu kuti asazabwezeretsenso kusankha zipani zomwe zalamulirapo dziko lino | chifukwa atsogoleri omwe akhalapo alephera kuyendetsa dziko lino. Iwo awuza anthu kuti asazabwezeretsenso kusankha zipani zomwe zalamulirapo dziko lino | Female | |
koma mmalo mwake, ayese AFORD. Pakadali pano, A Davie Maluwa komanso a Philip Kamangira omwe amadziwika bwino ndi kumenyera ufulu wa anthu alengeza kuti alowa chipanichi | koma mmalo mwake, ayese Afodi. Pakadali pano, A Devi Maluwa komanso a filipi Kamangira omwe amadziwika bwino ndi kumenyera ufulu wa anthu alengeza kuti alowa chipanichi | Female | |
Mlembi wa chipani Cha a AFORD, Elias Wakuda Kamanga wabwerezanso kuti chipani chawo chidakali mu mgwirizano wa Tonse, ndipo chipitilira kulangizana ndi adindo pa momwe zinthu zikukhalira | Mlembi wa chipani Cha a Afodi, Eliyasi Wakuda Kamanga wabwerezanso kuti chipani chawo chidakali mu mgwirizano wa Tonse, ndipo chipitilira kulangizana ndi adindo pa momwe zinthu zikukhalira | Female | |
Chipani cha Alliance for Democracy (AFORD) lero chichititsa msonkhano wa ndale ku Ndirande mu mzdiko la wa Blantyre omwe mwa zina, ulunjike pa chikondwelero choti chipanichi chakwanitsa zaka 30 | Chipani cha alayansi fo demokilase (AFODI) lero chichititsa msonkhano wa ndale ku Ndirande mu mzdiko la wa Bulantaya omwe mwa zina, ulunjike pa chikondwelero choti chipanichi chakwanitsa zaka fete | Female | |
Poyankhula ndi Ndirande FM, wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za chipanichi, Saulos Thindwa wati msonkhanowu uyamba nthawi ya 1 koloko masana pa bwalo la za masewero la Nyambadwe | Poyankhula ndi Ndirande efuemu, wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za chipanichi, Saulosi Thindwa wati msonkhanowu uyamba nthawi ya wani koloko masana pa bwalo la za masewero la Nyambadwe | Female | |
komwe mlendo olemekezeka akhale mtsogoleri wake, Enoch Kamzingeni Chakufwa Chihana. A Thindwa ati anthu ayembekezere kumva mfundo zolimbikitsa ufulu wa democracy | komwe mlendo olemekezeka akhale mtsogoleri wake, Inoki Kamzingeni Chakufwa Chihana. A Thindwa ati anthu ayembekezere kumva mfundo zolimbikitsa ufulu wa demokilase | Female | |
Tikudziwa zokhumba za Ndirande ndipo takonza zinthu zosiyanasiyana zomwe ziwasangalatse, atero a Thindwa | Tikudziwa zokhumba za Ndirande ndipo takonza zinthu zosiyanasiyana zomwe ziwasangalatse, atero a Thindwa | Female | |
Kuchokera mchaka Cha 2020, chipani cha AFORD chakhala chili pa kalikiliki wochititsa misonkhano ya ndale mdziko muno, pomwe adindo ake akuti ndi njira yokonzanso ntchito za chipanichi, patsogolo pa chisankho Cha mu 2025 | Kuchokera mchaka Cha twente twente, chipani cha AFODI chakhala chili pa kalikiliki wochititsa misonkhano ya ndale mdziko muno, pomwe adindo ake akuti ndi njira yokonzanso ntchito za chipanichi, patsogolo pa chisankho Cha mu twente twente faifi | Female | |
Chipani cha Democratic Progressive-DPP lero chikuchititsa mwambo opeza ndalama zoyendetsera chipani. Mwambowu ukuchitikira ku Mount Soche Hotel mu mzinda wa Blantyre | Chipani cha Demokilatiki pulogilesivi-Dipipi lero chikuchititsa mwambo opeza ndalama zoyendetsera chipani. Mwambowu ukuchitikira ku maunti soche hotelo mu mzinda wa Bulantaya | Female | |
ndipo mlendo olemekezeka ndi mtsogolo wakale wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipanichi, Peter Mutharika Pakadali pano, anthu ochokera mmadera osiyanasiyana akusonkhana ku malowa | ndipo mlendo olemekezeka ndi mtsogolo wakale wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipanichi, Pita Mutharika Pakadali pano, anthu ochokera mmadera osiyanasiyana akusonkhana ku malowa | Female | |
Kampani yofulula mowa ya Castel Malawi lero yabzala mitengo ku nkhalango ya Mudi imene yili ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre ndi pempho loti anthu agwirane manja posamalira mitengoyi | Kampani yofulula mowa ya kasitelo Malawi lero yabzala mitengo ku nkhalango ya Mudi imene yili ku Ndirande mu mzinda wa Bulantaya ndi pempho loti anthu agwirane manja posamalira mitengoyi | Female | |
M'modzi mwa akuluakulu a ku kampaniyi, mayi Gloria Zimba ati kugwirana manjaku kuthandiza kuti mitengoyi ikule, ndipo izapindulira dziko lino mu njira zosiyanasiyana | M'modzi mwa akuluakulu a ku kampaniyi, mayi Guloliya Zimba ati kugwirana manjaku kuthandiza kuti mitengoyi ikule, ndipo izapindulira dziko lino mu njira zosiyanasiyana | Female | |
Ndipo mmawu ake, mfumu Matope ya ku Ndirande'ku yalonjeza kuti ipitilira kulimbikitsa anthu ake kutenga umwini posamalira khalango ya Mudi komwe kuli dziwe | Ndipo mmawu ake, mfumu Matope ya ku Ndirande'ku yalonjeza kuti ipitilira kulimbikitsa anthu ake kutenga umwini posamalira khalango ya Mudi komwe kuli dziwe | Female | |
limene bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Blantyre Water Board limapopako madzi ake. Mfumuyi yayamikiranso kampani ya Castel Malawi kaamba ka chidwi chake chobwezeretsa nkhalango ya Mudi mchimake | limene bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Bulantaya wota bodi limapopako madzi ake. Mfumuyi yayamikiranso kampani ya kasitelol Malawi kaamba ka chidwi chake chobwezeretsa nkhalango ya Mudi mchimake | Female | |
Castel Malawi yayika pa dera mitengo yopitilira 10 thousand yomwe izalidwe mmadera osiyanasiyana. Chigamulo chokakhala ku ndende kwa zaka 8 chomwe chinapelekedwa kwa Mussa John | Casitelo Malawi yayika pa dera mitengo yopitilira teni sauzande yomwe izalidwe mmadera osiyanasiyana. Chigamulo chokakhala ku ndende kwa zaka eiti chomwe chinapelekedwa kwa Musa Joni | Female | |
kutsatira kupezeka olakwa pa mlandu opezeka ndi chamba chachepetsedwa kufika pa zaka zitatu. Oweluza Vikochi Chima wachepetsa chilangochi atamva pempho la mbali yomwe ikuyimira Mussa | kutsatira kupezeka olakwa pa mlandu opezeka ndi chamba chachepetsedwa kufika pa zaka zitatu. Oweluza Vikochi Chima wachepetsa chilangochi atamva pempho la mbali yomwe ikuyimira Mussa | Female | |
kuti chilangochi ndi cha chikukulu. Anthu osiyanasiyana omwe asonkhana ku bwalo la milandu ku Blantyre aonetsa kusakhutira ndi chigamulochi | kuti chilangochi ndi cha chikukulu. Anthu osiyanasiyana omwe asonkhana ku bwalo la milandu ku Bulantaya aonetsa kusakhutira ndi chigamulochi | Female | |
Ngati akudzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa chipani cha UDF pa msonkhano wake waukulu | Ngati akudzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa chipani cha yudiefu pa msonkhano wake waukulu | Female | |
Ku Mzimba Apolisi amanga Bambo wa zaka 100, Stanley Gondwe kaamba kopezeka ndi ndowa ziwiri za chamba | Ku Mzimba Apolisi amanga Bambo wa zaka wani handiledi, Sitanile Gondwe kaamba kopezeka ndi ndowa ziwiri za chamba | Female | |
Ofalitsa nkhani za apolisi ku Mzimba'ko, Peter Botha wati a Gondwe amangidwa pambuyo pa chipikisheni chomwe apolisi anachita ku nyumba kwawo, anthu ena atawatsina khutu za nkhaniyi | Ofalitsa nkhani za apolisi ku Mzimba'ko, Pita Botha wati a Gondwe amangidwa pambuyo pa chipikisheni chomwe apolisi anachita ku nyumba kwawo, anthu ena atawatsina khutu za nkhaniyi | Female | |
A Police ku Ndirande akulengeza za malemu omwe sakuziwika kwawo ndipo thupi lawo likusungidwa ku nyumba ya chisoni ku gulupu Queens Elizabeth Central Hospital | A Polisi ku Ndirande akulengeza za malemu omwe sakuziwika kwawo ndipo thupi lawo likusungidwa ku nyumba ya chisoni ku gulupu kwinzi elizabefi sentilo hosipito | Female | |
Bambo wa omwe zaka zawo ndi pakati pa 30 ndi 40 anamwalira atagundidwa ndi galimoto yomwe siikuziwika pa 24 August 2022, nthawi ya 8 Koloko madzulo | Bambo wa omwe zaka zawo ndi pakati pa fete ndi fote anamwalira atagundidwa ndi galimoto yomwe siikuziwika pa twente folo ogasiti twente twente thu, nthawi ya eiti Koloko madzulo | Female | |
pafupi ndi Sukulu ya Pulaimale ya Spring field mmusewu wa Mlanga kwa Golio, mmzinda wa Ndirande. Iwowo anali odelapo ,a msinkhu wa pakati kati, ndipo anali ndi tsitsi | pafupi ndi Sukulu ya Pulaimale ya sipuling’I fuludi mmusewu wa Mlanga kwa Golio, mmzinda wa Ndirande. Iwowo anali odelapo, a msinkhu wa pakati kati, ndipo anali ndi tsitsi | Female | |
Pa tsikuli anavala buluku la bulauni ndi shirt yodelapo. A Ndirande Police Station akupempha, omwe mm'bale wawo akusowa ndipo ndi wamaonekedwe tanenawa kuti abwele azathe kuzamuzindikila m'bale wawoyu | Pa tsikuli anavala buluku la bulauni ndi shati yodelapo. A Ndirande Polisi siteshoni akupempha, omwe mm'bale wawo akusowa ndipo ndi wamaonekedwe tanenawa kuti abwele azathe kuzamuzindikila m'bale wawoyu | Female | |
Gulu loyimba nyimbo za uzimu la Chinsapo Sweet Melodies la mu mzinda wa Lilongwe lati lichititsa chiphwando cha nyimbo za uzimu mu mzindawu pa 25 September chaka chino | Gulu loyimba nyimbo za uzimu la Chinsapo switi melodezi la mu mzinda wa Lilongwe lati lichititsa chiphwando cha nyimbo za uzimu mu mzindawu pa twente faifi sepitemba chaka chino | Female | |
Chiphwandochi chichitika ngati imodzi mwa njira yokonzekera mwambo waukulu okhazikitsa chimbale cha nyimbo za gululi, omwe uchitikire mu mzinda omwewu | Chiphwandochi chichitika ngati imodzi mwa njira yokonzekera mwambo waukulu okhazikitsa chimbale cha nyimbo za gululi, omwe uchitikire mu mzinda omwewu | Female | |
Izi ndi malingana ndi wa pa mpando wa gululi, Angel Chamkomera yemwe wati pa chiphwando cha pa 25 September-chi padzakhala zinthu za pa mwamba zomwe zizathandizenso kutukula miyoyo ya anthu mu uzimu | Izi ndi malingana ndi wa pa mpando wa gululi, Anjelo Chamkomera yemwe wati pa chiphwando cha pa twente faifi-chi padzakhala zinthu za pa mwamba zomwe zizathandizenso kutukula miyoyo ya anthu mu uzimu | Female | |
Pa chiphwandochi pazakhala oyimba osiyanasiyana koma tizabweranso kuzawuza anthu zambiri pa izi, atero a Chakomera | Pa chiphwandochi pazakhala oyimba osiyanasiyana koma tizabweranso kuzawuza anthu zambiri pa izi, atero a Chakomera | Female | |
Iwo ati pakadali pano ulendo opita ku Zambia omwe gululi limayenera kukhala nawo posachedwapa, walephereka, ndipo ichi ndi chifukwa chinanso akonza chiphwandochi | Iwo ati pakadali pano ulendo opita ku Zambiya omwe gululi limayenera kukhala nawo posachedwapa, walephereka, ndipo ichi ndi chifukwa chinanso akonza chiphwandochi | Female | |
Pali chiyembekezo kuti mwambo wa Mulhakho wa Alhomwe wa chaka chino ubweretsa zinthu za pa mwamba zomwe mwa zina zithandizire kusintha pakati pa anthu | Pali chiyembekezo kuti mwambo wa Mulakho wa Alomwe wa chaka chino ubweretsa zinthu za pa mwamba zomwe mwa zina zithandizire kusintha pakati pa anthu | Female | |
Kusinthaku ndi monga kubweretsa umodzi pakati pa anthu a zikhalidwe zosiyana komanso kuthandiza anthu pa Mavuto osiyanasiyana omwe akukumana nawo pa miyoyo yawo | Kusinthaku ndi monga kubweretsa umodzi pakati pa anthu a zikhalidwe zosiyana komanso kuthandiza anthu pa Mavuto osiyanasiyana omwe akukumana nawo pa miyoyo yawo | Female | |
Izitu ndi malingana ndi mkulu Wofalitsa nkhani wa komiti yomwe ikukonza mwambowu chaka chino, Jubeki Monjeza | Izitu ndi malingana ndi mkulu Wofalitsa nkhani wa komiti yomwe ikukonza mwambowu chaka chino, Jubeki Monjeza | Female | |
yemwe wauza atolankhani kuti kufikira pano, zokonzekera zonse kuti mwambowu uchitike pa 9 October, zikuyenda bwino | yemwe wauza atolankhani kuti kufikira pano, zokonzekera zonse kuti mwambowu uchitike pa Naini Okutoba , zikuyenda bwino | Female | |
A Monjeza ati anthu komanso mabungwe osiyanasiyana akupitilira kupeleka thandizo lawo lomwe ligwiritsidwe ntchito pa mwambowu, koma apempha ena omwe ali ndi kuthekera kuti athenso kufika ndi thandizo lawo | A Monjeza ati anthu komanso mabungwe osiyanasiyana akupitilira kupeleka thandizo lawo lomwe ligwiritsidwe ntchito pa mwambowu, koma apempha ena omwe ali ndi kuthekera kuti athenso kufika ndi thandizo lawo | Female | |
A Monjeza ati Mulhakho wa Alhomwe wa chaka chino wayitanitsanso anthu a zikhalidwe zina monga a Chewa ndi a Yao komanso kuti akatswiri odziwa mankhwala a zisamba kuchokera ku Mozambique, adzakhalapo | Monjeza ati Mulahko wa Alomwe wa chaka chino wayitanitsanso anthu a zikhalidwe zina monga a Chewa ndi a Yao komanso kuti akatswiri odziwa mankhwala a zisamba kuchokera ku Mozambiki, adzakhalapo | Female | |
Pakadali pano, gululi likupitilira kuchita mikumano yomwe cholinga chake ndi kukonzekera mwambowu omwenso ubweretse katswiri oyimba nyimbo osiyanasiyana omwe azakhale akusangalatsa anthu | Pakadali pano, gululi likupitilira kuchita mikumano yomwe cholinga chake ndi kukonzekera mwambowu omwenso ubweretse katswiri oyimba nyimbo osiyanasiyana omwe azakhale akusangalatsa anthu | Female | |
Ophunzira pa sukulu ya uphunzitsi ya Blantyre Teachers Training College (BTTC) akuchita zionetsero zosonyeza kukwiya ndi chakudya chomwe akuti chikumakhala chosalongosoka | Ophunzira pa sukulu ya uphunzitsi ya Bulantaya thilening’i tichazi koleji (Bititisi) akuchita zionetsero zosonyeza kukwiya ndi chakudya chomwe akuti chikumakhala chosalongosoka | Female | |
Zionetserozi zayamba pomwe akuti kwa masiku angapo tsopano, akhala akulandira nsima yosapsa kuchokera ku malo ophikira chakudyachi | Zionetserozi zayamba pomwe akuti kwa masiku angapo tsopano, akhala akulandira nsima yosapsa kuchokera ku malo ophikira chakudyachi | Female | |
M'modzi mwa ophunzirawa watiwuza kuti izi zikuchititsa kuti azidwala matenda monga otsegula mmimba, zomwenso zikusokoneza pa nthawi ino pomwe akulemba mayeso | M'modzi mwa ophunzirawa watiwuza kuti izi zikuchititsa kuti azidwala matenda monga otsegula mmimba, zomwenso zikusokoneza pa nthawi ino pomwe akulemba mayeso | Female | |
Bungwe la chikhalidwe la Mulhakho Wa Alhomwe lati adindo sanayankhebe pa nkhawa zomwe anatula zoti anthu a mtunduwu akukumana ndi zokhoma zosiyanasiyana mdziko | Bungwe la chikhalidwe la Mulakho Wa Alomwe lati adindo sanayankhebe pa nkhawa zomwe anatula zoti anthu a mtunduwu akukumana ndi zokhoma zosiyanasiyana mdziko | Female | |
Wa pa mpando wa bungweli mchigawo cha ku mmwera, Blessings Makwinja ndi yemwe wanena izi poyankhula ndi Ndirande FM | Wa pa mpando wa bungweli mchigawo cha ku mmwera, Bulesing’izi Makwinja ndi yemwe wanena izi poyankhula ndi Ndirande efuemu | Female | |
pomwe wati zikungotsimikizira kuti boma silikuyika chidwi pothana ndi Mavuto omwe anthu ake akukumana nawo Bungweli linachititsa zionetsero sabata yatha mboma la Phalombe | pomwe wati zikungotsimikizira kuti boma silikuyika chidwi pothana ndi Mavuto omwe anthu ake akukumana nawo Bungweli linachititsa zionetsero sabata yatha mboma la Phalombe | Female | |
komwe mwa zina atsogoleri ake anapeleka kalata ya madandaulo omwe anagona pa nkhani ya tsankho pakasankhidwe ka adindo mboma ndi kumangidwa kwa anthu a mtunduwu | komwe mwa zina atsogoleri ake anapeleka kalata ya madandaulo omwe anagona pa nkhani ya tsankho pakasankhidwe ka adindo mboma ndi kumangidwa kwa anthu a mtunduwu | Female | |
Ndipo kutsatira kukhala chete kwa boma pa madandaulowa, a Makwinja ati bungwe la Mulhakho wa Alhomwe lipitilira kuchita zionetsero. Pakadali pano, bungweli lichitititsa zionetsero zina lachinayi sabata ino | Ndipo kutsatira kukhala chete kwa boma pa madandaulowa, a Makwinja ati bungwe la Mulakho wa Alomwe lipitilira kuchita zionetsero. Pakadali pano, bungweli lichitititsa zionetsero zina lachinayi sabata ino | Female | |
Bungwe loyang'anira anthu komanso kampani zochita bizinesi zing'onozing'ono m'dziko muno la National Association for Small and Medium Enterprise (NASME) layamikira kampani yofulula mowa ya Chibuku | Bungwe loyang'anira anthu komanso kampani zochita bizinesi zing'onozing'ono m'dziko muno la neshono ososiyeshoni ofu simo andi midiyamu intapulaizesi (NASIME) layamikira kampani yofulula mowa ya Chibuku | Female | |
ati kaamba kogwira ntchito yake mokomera alimi ang'onoang'ono komanso anthu a ku mudzi. Mkulu wa NASME, William Mwale ndi yemwe wayankhula izi pomwe bungweli limapeleka chikho ku kampaniyi | ati kaamba kogwira ntchito yake mokomera alimi ang'onoang'ono komanso anthu a ku mudzi. Mkulu wa NASIME, Wiliyamu Mwale ndi yemwe wayankhula izi pomwe bungweli limapeleka chikho ku kampaniyi | Female | |
pomwe akuti mwa zina, zikuthandiza anthu osowa kukhala odzidalira pa chuma. Malingana ndi a Mwale, kupatula kugula zokolola za alimi kuti azipangira mowa ndi za kumwa zina | pomwe akuti mwa zina, zikuthandiza anthu osowa kukhala odzidalira pa chuma. Malingana ndi a Mwale, kupatula kugula zokolola za alimi kuti azipangira mowa ndi za kumwa zina | Female | |
kampaniyi ikuchilimikanso pa ntchito za Chifundo ndipo ichi ndi chifukwa chinanso bungwe la NASME lapeleka chikhochi | kampaniyi ikuchilimikanso pa ntchito za Chifundo ndipo ichi ndi chifukwa chinanso bungwe la NASIME lapeleka chikhochi | Female | |
Bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Blantyre Water Board lati liri ndi chiyembekezo kuti liyamba kupulumutsa zina mwa ndalama zomwe limalipira ku bungwe logulitsa magetsi la ESCOM, popopa madzi ake | Bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Bulantaya wota bodi lati liri ndi chiyembekezo kuti liyamba kupulumutsa zina mwa ndalama zomwe limalipira ku bungwe logulitsa magetsi la Esikomu, popopa madzi ake | Female | |
pambuyo pa magetsi a mphanvu ya dzuwa omwe bungweli likufuna kuyika ku amodzi mwa malo opopa madziwa, a Walkers Ferry | pambuyo pa magetsi a mphanvu ya dzuwa omwe bungweli likufuna kuyika ku amodzi mwa malo opopa madziwa, a Wokazi Fele | Female | |
Mkulu wa Blantyre water board, Dr. Robert Hanjahanja ndi yemwe wayankhula izi pomwe bungweli limasayinira mgwirizano ndi kampani yomwe itsogolere pa ukadawulo wa ntchitoyi, ya TATA Consulting Engineers | Mkulu wa Bulantaya wota bodi , Dokota Lobati Hanjahanja ndi yemwe wayankhula izi pomwe bungweli limasayinira mgwirizano ndi kampani yomwe itsogolere pa ukadawulo wa ntchitoyi, ya TATA konzating’i injiniyazi | Female | |
Malingana ndi a Hanjahanja, kupatula kuti Blantyre Water Board iyamba kupulumutsa ndalama, palinso chiyembekezo kuti bungweli lizitha kupopa madzi nthawi iliyonse posadalira magetsi a ESCOM | Malingana ndi a Hanjahanja, kupatula kuti Bulantaya wota bodi iyamba kupulumutsa ndalama, palinso chiyembekezo kuti bungweli lizitha kupopa madzi nthawi iliyonse posadalira magetsi a Esikomu | Female | |
zomwe zizathandizenso kuti makasitomala ake kukhala ndi madzi nthawi zonse | zomwe zizathandizenso kuti makasitomala ake kukhala ndi madzi nthawi zonse | Female | |
Malingana ndi mgwirizano omwe Blantyre water board yasayinira ndi kampani ya TATA, zonse zokhuza ntchitoyi, yomwe izayambe kupeleka ma megawatts 30 a magetsi ku Blantyre water board | Malingana ndi mgwirizano omwe Bulantaya wota bodi yasayinira ndi kampani ya TATA, zonse zokhuza ntchitoyi, yomwe izayambe kupeleka ma megawatsi fete a magetsi ku Bulantaya wota bodi | Female | |
zikuyembekezereka kufika ku mapeto pakati pa miyezi 18 kapena zaka ziwiri kuchokera pano. Pamenepa, kampani ya Tata Consulting Engineers | zikuyembekezereka kufika ku mapeto pakati pa miyezi eitini kapena zaka ziwiri kuchokera pano. Pamenepa, kampani ya Tata Konzating’i injiniyazi | Female | |
kudzera mwa mkulu wake, Rajeev Menon yalonjeza kuti igwira ntchito yoyika magetsiwa mwa changu komanso modalilika | kudzera mwa mkulu wake, Rajivi Menoni yalonjeza kuti igwira ntchito yoyika magetsiwa mwa changu komanso modalilika | Female | |
Ndipo m’mawu ake, m’modzi mwa nthumwi kuchokera ku unduna wa za chuma, a Nations Msowoya omwe anali nawo pa mwambo osayinira mgwirizanowu ati boma lizipeleka kupeleka thandizo loyenelera logwirizana ndi ntchitoyi | Ndipo m’mawu ake, m’modzi mwa nthumwi kuchokera ku unduna wa za chuma, a Nashonzi Msowoya omwe anali nawo pa mwambo osayinira mgwirizanowu ati boma lizipeleka kupeleka thandizo loyenelera logwirizana ndi ntchitoyi | Female | |
Chipani chosutsa boma cha DPP chawuza boma kuti liyitanitse voti yomva maganizo a anthu referendum maka ngati ndi koyenera kuti bomali lipitilire kulamuliro dziko lino kapena ayi | Chipani chosutsa boma cha Dipipi chawuza boma kuti liyitanitse voti yomva maganizo a anthu lifelendamu maka ngati ndi koyenera kuti bomali lipitilire kulamuliro dziko lino kapena ayi | Female | |
Ena mwa akuluakulu a chipanichi anena izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe komwenso alosera kuti dziko lino lipitilira kusambira m'mavuto a za chuma ngati boma silisintha kachitidwe kake ka zinthu | Ena mwa akuluakulu a chipanichi anena izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe komwenso alosera kuti dziko lino lipitilira kusambira m'mavuto a za chuma ngati boma silisintha kachitidwe kake ka zinthu | Female | |
Ogwira ntchito ku bungwe la ADMARC ati kuyambira lolemba sabata ya mawa, kunyanyala ntchito pofuna kukakamiza unduna wa za ulimi kuti uchotse board yoyendetsa bungweli | Ogwira ntchito ku bungwe la Adimaki ati kuyambira lolemba sabata ya mawa, kunyanyala ntchito pofuna kukakamiza unduna wa za ulimi kuti uchotse bodi yoyendetsa bungweli | Female | |
Wogwira ntchitowa kudzera mwa owayimilira, a John Hassan komanso a Memory Kanyenda ati akufuna undunawu uchotse board-yi chifukwa ikulowelera kwambiri ntchito za bungweli | Wogwira ntchitowa kudzera mwa owayimilira, a Joni Hasani komanso a Memole Kanyenda ati akufuna undunawu uchotse bodi-yi chifukwa ikulowelera kwambiri ntchito za bungweli | Female | |
Mwa zina, iwo atchulapo ziganizo zomwe board-yi ikupanga zomwe akuti sizikuwakomera. Iwo akuti m'miyezi 19 yomwe board yi yakhalapo | Mwa zina, iwo atchulapo ziganizo zomwe bodi-yi ikupanga zomwe akuti sizikuwakomera. Iwo akuti m'miyezi naintini yomwe bodi yi yakhalapo | Female | |
bungwe la ADMARC lasintha adindo mu ofesi ya wa mkulu kanayi konse zikukhuza ntchito za bungweli | bungwe la Adimaki lasintha adindo mu ofesi ya wa mkulu kanayi konse zikukhuza ntchito za bungweli | Female | |
Amuna awiri, a Lorman Khola komanso a George Mkwinda awalamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi chimodzi | Amuna awiri, a Lomani Khola komanso a Joji Mkwinda awalamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi chimodzi | Female | |
aliyense atapezeka wolakwa pa mlandu wopezeka ndi fodya wamkulu wa chamba koma popanda chilolezo | aliyense atapezeka wolakwa pa mlandu wopezeka ndi fodya wamkulu wa chamba koma popanda chilolezo | Female | |
Bwalolo linamva kuti amunawa anapezeka ndi matumba a chamba okwana 57 mgalimoto mwawo ndipo onse pamodzi amalemera makilogalamu 1,221 | Bwalolo linamva kuti amunawa anapezeka ndi matumba a chamba okwana fifite seveni mgalimoto mwawo ndipo onse pamodzi amalemera makilogalamu wani sauzande thu handiledi andi twente wani | Female | |
Powonekera m'bwalo la milandu la Chief Resident Magistrate ku Lilongwe, a Khola ndi a Mkwinda anavomera mlandu omwe mbali ya boma inawatsegulira | Powonekera m'bwalo la milandu la Tchifi lezidenti majesitileti ku Lilongwe, a Khola ndi a Mkwinda anavomera mlandu omwe mbali ya boma inawatsegulira | Female | |
zomwe zinachititsa oweluza Madalitso Chimwaza kuwalamula kukakhala ku ndende kwa zaka 6 | zomwe zinachititsa oweluza Madalitso Chimwaza kuwalamula kukakhala ku ndende kwa zaka sikisi | Female | |
Malingana ndi bwalolo, awiriwa analakwira gawo 19 ndime ya 1 ya malamulo oyendetsera nkhani za mankhwala owopsa | Malingana ndi bwalolo, awiriwa analakwira gawo naintini ndime ya wani ya malamulo oyendetsera nkhani za mankhwala owopsa | Female | |
Gawo lachitatu lopeleka katemera woteteza ku nthenda ya polio akuti liyamba mwezi wa June. Izi ndi malingana ndi mkulu wa alangizi a zaumoyo ku ofesi ya za umoyo mu mboma la Blantyre, a Penjani Chunda | Gawo lachitatu lopeleka katemera woteteza ku nthenda ya poliyo akuti liyamba mwezi wa Juni. Izi ndi malingana ndi mkulu wa alangizi a zaumoyo ku ofesi ya za umoyo mu mboma la Bulantaya, a Penjani Chunda | Female | |
omwe ati gawo lachiwiri la ntchitoyi linayenda mbomali komanso dziko lonse. Malingana ndi a Chunda, dziko lino linafikira anthu opyola ndi 2% pa mlingo wa anthu omwe linakonza kuti lifikire ndi katemerayu | omwe ati gawo lachiwiri la ntchitoyi linayenda mbomali komanso dziko lonse. Malingana ndi a Chunda, dziko lino linafikira anthu opyola ndi thu pelesenti pa mlingo wa anthu omwe linakonza kuti lifikire ndi katemerayu | Female | |
Pamenepa, mkulu wa alangizi a zaumoyo ku Blantyre yu wati gawo lachitatu lopeleka katemera lisanayambe, adindo akhala kaye pansi kuwunikirana za momwe angayendesere gawoli | Pamenepa, mkulu wa alangizi a zaumoyo ku Bulantaya yu wati gawo lachitatu lopeleka katemera lisanayambe, adindo akhala kaye pansi kuwunikirana za momwe angayendesere gawoli | Female | |
Ofesi ya za umoyo ku Blantyre inapeza anthu asanu ndi anayi (9) omwe imawakayikira kuti ali ndi nthenda ya polio | Ofesi ya za umoyo ku Bulantaya inapeza anthu asanu ndi anayi (naini) omwe imawakayikira kuti ali ndi nthenda ya poliyo | Female | |
koma a zaumoyo apeza kuti asanu mwa iwo alibe nthendayi ndipo zotsatira za anthu awiri sizinatuluke | koma a zaumoyo apeza kuti asanu mwa iwo alibe nthendayi ndipo zotsatira za anthu awiri sizinatuluke | Female | |
Pomwe mlandu wa mmwenye wina wochita malonda, Zunneth Sattar yemwe akumuganizira kuti amachita katangale ndi boma la Malawi, ukupitilira mdziko la United Kingdom (UK) | Pomwe mlandu wa mmwenye wina wochita malonda, Zunefi Sata yemwe akumuganizira kuti amachita katangale ndi boma la Malawi, ukupitilira mdziko la Yunaitedi king’idomu (Yukei) | Female | |
wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima wati sangayankhulepo kanthu pa nkhaniyi pomwe malipoti ena akuwonetsa kuti akukhuzidwa pa mlanduwu | wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulosi Chilima wati sangayankhulepo kanthu pa nkhaniyi pomwe malipoti ena akuwonetsa kuti akukhuzidwa pa mlanduwu | Female | |
Kalata zolumbira zokhuza mlanduwo zikuwonetsa kuti kupatula a Chilima, a Sattar amachitanso za katangale mothandizana ndi anthu ena, monga mkulu wakale wa ACB, Reyneck Matemba | Kalata zolumbira zokhuza mlanduwo zikuwonetsa kuti kupatula a Chilima, a Sata amachitanso za katangale mothandizana ndi anthu ena, monga mkulu wakale wa Esibi, Reineki Matemba | Female | |
mkulu wa apolisi mdziko muno, Dr. George Kainja, lawyer George Kaluba ndi ena. Koma poyankhula ndi atolankhani lachisanu ku khonsolo ya Mbelwa, a Chilima ati nkhaniyi ndi yokhuza malamulo | mkulu wa apolisi mdziko muno, Dokota Joji Kainja, loya Joji Kalwa ndi ena. Koma poyankhula ndi atolankhani lachisanu ku khonsolo ya Mbelwa, a Chilima ati nkhaniyi ndi yokhuza malamulo | Female | |
ndipo malamulowo akuyenera atsatidwe. Dziko la UK kudzera ku nthambi yake ya National Crimes Agency | ndipo malamulowo akuyenera atsatidwe. Dziko la yukei kudzera ku nthambi yake ya neshono kilaimuzi ejense | Female | |
linamanga a Sattar pa 5 October chaka chatha pambuyo pa kafukufuku wake yemwe inachita wokhuza nkhani za katangalezi | linamanga a Sata pa faifi okutoba chaka chatha pambuyo pa kafukufuku wake yemwe inachita wokhuza nkhani za katangalezi | Female | |
Mwa zina, mkuluyu akumuganizira kuti amapeza makontilakiti a boma mosasata ndondomeko komanso kuti amagulitsa dziko lino katundu wina pa mitengo yokwera zedi | Mwa zina, mkuluyu akumuganizira kuti amapeza makontilakiti a boma mosasata ndondomeko komanso kuti amagulitsa dziko lino katundu wina pa mitengo yokwera zedi | Female | |
Mtsuso pa nkhani yoti chilango chonyonga chichotsedwe mmalamulo a dziko lino ukupitilira pomwe magulu osiyanasiyana okhuzidwa ndi nkhaniyi akupitilira kupeleka maganizo osiyana | Mtsuso pa nkhani yoti chilango chonyonga chichotsedwe mmalamulo a dziko lino ukupitilira pomwe magulu osiyanasiyana okhuzidwa ndi nkhaniyi akupitilira kupeleka maganizo osiyana | Female | |
Maguluwa ndi monga mabungwe omenyera maufulu a anthu, akatswiri a za malamulo komanso atsogoleri a mipingo | Maguluwa ndi monga mabungwe omenyera maufulu a anthu, akatswiri a za malamulo komanso atsogoleri a mipingo | Female | |
Maguluwa omwe mayankhula mprogram ya Mutipo Chani ya pa Ndirande F M, anakhazikika pa mfundo zoti lamuloli likuphwanya ufulu wa anthu komanso kuti kulichotsa likusutsa ndi mfundo zina za chipembezo | Maguluwa omwe mayankhula mpulohilamu ya Mutipo Chani ya pa Ndirande efuemu, anakhazikika pa mfundo zoti lamuloli likuphwanya ufulu wa anthu komanso kuti kulichotsa likusutsa ndi mfundo zina za chipembezo | Female | |
Bambo Alexious Kamangira omwe ndi lawyer komanso omenyera ufulu wa anthu anati ndi koyenera kuti lamuloli lichotsedwe chifukwa likuphwanya ufulu wokhala ndi moyo | Bambo Alekishasi Kamangira omwe ndi loya komanso omenyera ufulu wa anthu anati ndi koyenera kuti lamuloli lichotsedwe chifukwa likuphwanya ufulu wokhala ndi moyo | Female | |
koma mfundo yawo inasutsidwa ndi Sheik Shaibu a bungwe la Islamic Commission for Freedom and Freedom omwe anati lamuloli likachotsedwa lidzetsa chisawawa mdziko | koma mfundo yawo inasutsidwa ndi Shekhi Shaibu a bungwe la Izilamiki komishoni fo fulidomu andi fulidomu omwe anati lamuloli likachotsedwa lidzetsa chisawawa mdziko | Female | |
Pamenepa, Sheik Shaibu anati lisiyidwe momwe liliri powonjezera kuti ngakhale Mulungu mbayibulo saletsa chilango chonyonga | Pamenepa, Shekhi Shaibu anati lisiyidwe momwe liliri powonjezera kuti ngakhale Mulungu mbayibulo saletsa chilango chonyonga | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.