audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
anayithetsa malipoti atamveka kuti panali zolakwika komanso zakatangale zambiri pomwe imaplekedwa ku Techno Brain. Pakadali pano, mneneri wa nthambi ya Immigration, Wellington Chiponde | anayithetsa malipoti atamveka kuti panali zolakwika komanso zakatangale zambiri pomwe imaplekedwa ku Tekino buleni. Pakadali pano, mneneri wa nthambi ya Imigileshoni, Weling’itoni Chiponde | Female | |
wauza nyumba ina yofalitsa nkhani kuti pali anthu opitilira 3,000 omwe akufuna ziphatsozi zomwe pa chingerezi zimadziwika kuti passport | wauza nyumba ina yofalitsa nkhani kuti pali anthu opitilira fili sauzande omwe akufuna ziphatsozi zomwe pa chingerezi zimadziwika kuti pasipoti | Female | |
Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera wasankha board ya tsopano yomwe ikuyembekezeleka kuyendetsa bungwe loona za mphanvu za magetsi, m’bwezera ndi zina, la MERA | Mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera wasankha bodi ya tsopano yomwe ikuyembekezeleka kuyendetsa bungwe loona za mphanvu za magetsi, m’bwezera ndi zina, la MERA | Female | |
A Chakwera asankha board-yi patapita sabata zingapo atachotsa board yomwe inalipo kutsatira kutumpha kwa zolakwitsa zomwe board-yo | A Chakwera asankha bodi-yi patapita sabata zingapo atachotsa bodi yomwe inalipo kutsatira kutumpha kwa zolakwitsa zomwe bodi-yo | Female | |
yomwe imatsogoleledwa ndi a Lenard Chikadya, inachita posankha mkulu wa bungweli, a Henry Kachaje | yomwe imatsogoleledwa ndi a Lennadi Chikadya, inachita posankha mkulu wa bungweli, a Henele Kachaje | Female | |
Malingana ndi kalata yomwe mlembi mu ofesi ya mtsogoleri mu unduna, Malingana ndi kalata yomwe mlembi mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna, Zangazanga Chikhosi watulutsa | Malingana ndi kalata yomwe mlembi mu ofesi ya mtsogoleri mu unduna, Malingana ndi kalata yomwe mlembi mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna, Zangazanga Chikhosi watulutsa | Female | |
wa pa mpando wa board ya tsopanoyi ndi a Reckford Kampanje omwe m’mbuyomu anakhalapo mkulu olondoloza chuma cha boma | wa pa mpando wa bodi ya tsopanoyi ndi a lekifodi Kampanje omwe m’mbuyomu anakhalapo mkulu olondoloza chuma cha boma | Female | |
Kalatayi yatinso a Innocencia Chirombo akhala wachiwiri kwa a Kampanje pamene a Charles Kambauwa ndi m’modzi mwa mamembala a boardyi | Kalatayi yatinso a Inosensha Chirombo akhala wachiwiri kwa a Kampanje pamene a Tchalosi Kambauwa ndi m’modzi mwa mamembala a bodiyi | Female | |
Boma lakwiyitsa zedi Phungu wa m’dera la pakati m’boma la Phalombe, kaamba kosatsekulira mofulumira chipatala chamakono chomwe chimamangidwa m’bomalo | Boma lakwiyitsa zedi Phungu wa m’dera la pakati m’boma la Phalombe, kaamba kosatsekulira mofulumira chipatala chamakono chomwe chimamangidwa m’bomalo | Female | |
Phunguyo, a George Million, wauza Nyumba ya Malamulo Lachisanu, kuti boma, kudzera ku Unduna Wa Za Umoyo, likuyenera kutsekulira chipatalachi, chimene chikuyembekezerela kuthandiza anthu ochuluka m’bomali | Phunguyo, a Joji Miliyoni, wauza Nyumba ya Malamulo Lachisanu, kuti boma, kudzera ku Unduna Wa Za Umoyo, likuyenera kutsekulira chipatalachi, chimene chikuyembekezerela kuthandiza anthu ochuluka m’bomali | Female | |
A Million amayakhula izi, kutsatira malipoti woti boma likukonza zodzasegulira chipatalachi mwezi wa October, ngakhale kuti ntchito yomanga chipatalachi inatha kale | A Miliyoni amayakhula izi, kutsatira malipoti woti boma likukonza zodzasegulira chipatalachi mwezi wa Okutoba, ngakhale kuti ntchito yomanga chipatalachi inatha kale | Female | |
Posachedwapa, Mneneri ku Unduna Wa Za Umoyo, Adrian Chikumbe, anawuza atolankhani kuti izi zili chomwechi kaamba koti boma silinagule zipangizo zina zofunikira pa chipatalachi | Posachedwapa, Mneneri ku Unduna Wa Za Umoyo, Adiliyani Chikumbe, anawuza atolankhani kuti izi zili chomwechi kaamba koti boma silinagule zipangizo zina zofunikira pa chipatalachi | Female | |
Mayi Maimuna Kassim a m’boma la Mangochi, ayamba kugwira ukayidi wazaka zisanu, Bwalo la Milandu litamupeza wolakwa pa mlandu olola mwamuna wake kugwililira mwana wake wazaka 14 | Mayi Maimuna Kasimu a m’boma la Mangochi, ayamba kugwira ukayidi wazaka zisanu, Bwalo la Milandu litamupeza wolakwa pa mlandu olola mwamuna wake kugwililira mwana wake wazaka fotini | Female | |
amene ndi mwana omupeza wa bamboyu. M’modzi woyimilira boma pa milandu, a Maggie Chibulire | amene ndi mwana omupeza wa bamboyu. M’modzi woyimilira boma pa milandu, a Magi Chibulire | Female | |
anawuza bwalo la milandu kuti mayi Kassim anagwilizana ndi mwamuna wawo, amene akugwira ukayidi wazaka 21 pa mlandu ogwililirawu, kuti azigonana ndi mwanayu, ngati chizimba cholimbitsira banja lawo | anawuza bwalo la milandu kuti mayi Kasimu anagwilizana ndi mwamuna wawo, amene akugwira ukayidi wazaka twente wani pa mlandu ogwililirawu, kuti azigonana ndi mwanayu, ngati chizimba cholimbitsira banja lawo | Female | |
kuti azigonana ndi mwanayu ngati chizimba cholimbitsila banja lawo Mayi Kassim anawukana mlanduwu, koma mbali ya boma yinakwanitsa kutsimikizira bwalo la milandu, kuti mayiyu anapalamuladi mlanduwu | kuti azigonana ndi mwanayu ngati chizimba cholimbitsila banja lawo Mayi Kasimu anawukana mlanduwu, koma mbali ya boma yinakwanitsa kutsimikizira bwalo la milandu, kuti mayiyu anapalamuladi mlanduwu | Female | |
ndipo bwalo linamupeza wolakwa. Popereka chigamulo chake, oweruza mlandu, a Rodrick Michongwe, analamula mayiyu kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu, pofuna kupereka chenjenzo ndi phunziro kwa anthu a malingaliro ngati akewa | ndipo bwalo linamupeza wolakwa. Popereka chigamulo chake, oweruza mlandu, a Rodiliki Michongwe, analamula mayiyu kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu, pofuna kupereka chenjenzo ndi phunziro kwa anthu a malingaliro ngati akewa | Female | |
Nthambi Yowona za Kusintha kwa Nyengo -Department Of Climate Change And Metrological Services- yati Namondwe otchedwa Gombe akuyembekezereka kufika m’dziko muno lero, Lachisanu | Nthambi Yowona za Kusintha kwa Nyengo –Dipatimenti ofu kilaimeti chenji andi metilolojiko sevisezi - yati Namondwe otchedwa Gombe akuyembekezereka kufika m’dziko muno lero, Lachisanu | Female | |
Mneneri ku nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wati maboma ambiri a m’chigawo chakum’mwera ayembekezere mvula ya mphamvu, komanso ya mphepo yamkuntho, kutsatira Namondweyu | Mneneri ku nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wati maboma ambiri a m’chigawo chakum’mwera ayembekezere mvula ya mphamvu, komanso ya mphepo yamkuntho, kutsatira Namondweyu | Female | |
Nthambi Yowona za Kusintha kwa Nyengo -Department Of Climate Change And Metrological Services- yati Namondwe otchedwa Gombe akuyembekezereka kufika m’dziko muno lero, Lachisanu | Nthambi Yowona za Kusintha kwa Nyengo - Dipatimenti ofu kilaimeti chenji andi metilolojiko sevisezi - yati Namondwe otchedwa Gombe akuyembekezereka kufika m’dziko muno lero, Lachisanu | Female | |
Mneneri ku nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wati maboma ambiri a m’chigawo chakum’mwera ayembekezere mvula ya mphamvu, komanso ya mphepo yamkuntho, kutsatira Namondweyu | Mneneri ku nthambiyi, a Yobu Kachiwanda, wati maboma ambiri a m’chigawo chakum’mwera ayembekezere mvula ya mphamvu, komanso ya mphepo yamkuntho, kutsatira Namondweyu | Female | |
Malingana ndi a Kachiwanda, mvula ya mphamvuyi, ipangitsa kuti madzi asefukire, choncho akuchenjeza anthu onse omwe akukhala m’madera omwe amakonda kusefukira madzi, kuti asamukire ku mtunda | Malingana ndi a Kachiwanda, mvula ya mphamvuyi, ipangitsa kuti madzi asefukire, choncho akuchenjeza anthu onse omwe akukhala m’madera omwe amakonda kusefukira madzi, kuti asamukire ku mtunda | Female | |
Sing’anga wina mu mzinda wa Lilongwe amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu, atapezeka olakwa pa mlandu obera mayi wina, pomunamiza kuti amudzutsira mwamuna wake amene anamwalira | Sing’anga wina mu mzinda wa Lilongwe amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu, atapezeka olakwa pa mlandu obera mayi wina, pomunamiza kuti amudzutsira mwamuna wake amene anamwalira | Female | |
Bwalo la Lilongwe Magistrate, linamva kuti singa’angayu, Winstone Mvula, anapita pa sitolo pa mayiyu, pa pa 21 October chaka chatha n’kumunamiza kuti amuthandiza kudzutsa mwamuna wakeyu | Bwalo la Lilongwe Majisitileti, linamva kuti singa’angayu, Winisitoni Mvula, anapita pa sitolo pa mayiyu, pa pa twente wani okutoba chaka chatha n’kumunamiza kuti amuthandiza kudzutsa mwamuna wakeyu | Female | |
ngati atamupatsa ndalama zokwanira K13.8 Million. Kaamba ka chikondi chimene anali nacho kwa mwamuna wake omwaliyo, mayiyo anapereka ndalamazo mosawilingula | ngati atamupatsa ndalama zokwanira fetini pointi eiti miliyoni. Kaamba ka chikondi chimene anali nacho kwa mwamuna wake omwaliyo, mayiyo anapereka ndalamazo mosawilingula | Female | |
Ndalamazo anakaziperekela ku manda kumene mwamunayo anamuyika, ndipo sing’angayo anauzanso mayiyo kuti abweretse zovala za malemuyo, kuti adzavale akawuka | Ndalamazo anakaziperekela ku manda kumene mwamunayo anamuyika, ndipo sing’angayo anauzanso mayiyo kuti abweretse zovala za malemuyo, kuti adzavale akawuka | Female | |
Bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Blantyre Water Board lero labzala mitengo ku malo ozungulira dziwe lomwe limapopako madzi la Mudi | Bungwe lopopa ndi kugulitsa madzi la Bulantaya wota bodi lero labzala mitengo ku malo ozungulira dziwe lomwe limapopako madzi la Mudi | Female | |
Mwambowu wachitika motsogozedwa ndi nduna yoona za madzi ndi za ukhondo, Abida Mia yomwenso yabzala mitengo ingapo | Mwambowu wachitika motsogozedwa ndi nduna yoona za madzi ndi za ukhondo, Abida Miya yomwenso yabzala mitengo ingapo | Female | |
yomwe malingana ndi bungwe la Blantyre water board ithandiza kuteteza nthaka kuti isakokoloke. Bungweli mothandizidwa ndi ena mwa ophunzira a sukulu za ku mzinda wa Blantyre | yomwe malingana ndi bungwe la Bulantaya wota bodi ithandiza kuteteza nthaka kuti isakokoloke. Bungweli mothandizidwa ndi ena mwa ophunzira a sukulu za ku mzinda wa Bulantaya | Female | |
anthu okhala ku Ndirande komanso nthumwi za ku bank ya FDH, labzala mitengo yopitilira 2000 ndipo bungweli lati likukonza zobzala mitengo yopitilira 65,000 mu nyengo ino yobzala mitengo ya chaka chino | anthu okhala ku Ndirande komanso nthumwi za ku bank ya efudietchi, labzala mitengo yopitilira thu sauzande ndipo bungweli lati likukonza zobzala mitengo yopitilira sikisite faifi sauzande mu nyengo ino yobzala mitengo ya chaka chino | Female | |
Dziko la Nigeria lalamula akonzi a mafirimu a kanema kuti asamayikemo m’mafirimu awo nkhani zokhudza matsenga obweretsa kapena kuchulukitsa ndalama | Dziko la Naijeliya lalamula akonzi a mafirimu a kanema kuti asamayikemo m’mafirimu awo nkhani zokhudza matsenga obweretsa kapena kuchulukitsa ndalama | Female | |
Nduna yowona Zofaritsa Nkhani ndi Chikhalidwe m’dzikolo, a Lai Mohammed, ndi amene alengeza izi, pamene zadziwika kuti m’chitidwe opha anthu | Nduna yowona Zofaritsa Nkhani ndi Chikhalidwe m’dzikolo, a Lai Mouhamadi, ndi amene alengeza izi, pamene zadziwika kuti m’chitidwe opha anthu | Female | |
pofuna kugwiritsa ntchito ziwalo za matupi awo kuti ena akhwimire, n’kupeza chuma, zachuluka m’dzikolo | pofuna kugwiritsa ntchito ziwalo za matupi awo kuti ena akhwimire, n’kupeza chuma, zachuluka m’dzikolo | Female | |
Iwo ati, ambiri amene akhala akugwidwa akuchita zotereze, akhala akunena mvamvemve kuti amachita zamatsenga zotero popeza amaonera m’mafirimu, komanso pa masamba a mchezo a Internet, kuti zimenezo zimatheka | Iwo ati, ambiri amene akhala akugwidwa akuchita zotereze, akhala akunena mvamvemve kuti amachita zamatsenga zotero popeza amaonera m’mafirimu, komanso pa masamba a mchezo a Intaneti, kuti zimenezo zimatheka | Female | |
Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre akusakasaka anthu amene akuwaganizira kuti ndi amene anaba galimoto ku nyumba kwa katswiri wina wa zamalamulo | Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Bulantaya akusakasaka anthu amene akuwaganizira kuti ndi amene anaba galimoto ku nyumba kwa katswiri wina wa zamalamulo | Female | |
odziwika bwino m’dziko muno, a Gift Makhwawa masiku apitawo. Ofaritsa nkhani za apolisi pa polisi ya Limbe, Patrick Mussa | odziwika bwino m’dziko muno, a Gifiti Makhwawa masiku apitawo. Ofaritsa nkhani za apolisi pa polisi ya Limbe, Patiliki Musa | Female | |
watsimikiza za kufunidwa kwa anthuwa, pomwe wati galimotoyi yimene inabedwa Lolemba ku nyumba kwa a Makhwawa ku Namiwawa, yapezeka kwa Kachere, mu mzinda omwewu | watsimikiza za kufunidwa kwa anthuwa, pomwe wati galimotoyi yimene inabedwa Lolemba ku nyumba kwa a Makhwawa ku Namiwawa, yapezeka kwa Kachere, mu mzinda omwewu | Female | |
Apolisiwa apempha anthu amene akudziwapo kanthu pa za anthu amene anaba galimotoyi, imene nambala yake ndi KA 1537 kuti akanene ku polisi | Apolisiwa apempha anthu amene akudziwapo kanthu pa za anthu amene anaba galimotoyi, imene nambala yake ndi keie fifitini feteseveni kuti akanene ku polisi | Female | |
Apolisi m’boma la Dedza amanga m’nyamata wina wa zaka 15, pomuganizira kuti wakhala akugwirilira, mpaka kupereka pathupi, kwa mlongo wake omupeza, wa zaka 13 zakubadwa | Apolisi m’boma la Dedza amanga m’nyamata wina wa zaka fifitini, pomuganizira kuti wakhala akugwirilira, mpaka kupereka pathupi, kwa mlongo wake omupeza, wa zaka fetini zakubadwa | Female | |
Wachiwiri kwa ofaritsa nkhani za polisi pa polisi ya Dedza, a Cassim Manda, atsimikiza za kumangidwa kwa mnyamatayo, koma iwo sanamutchule dzina lake, pofuna kumuteteza | Wachiwiri kwa ofaritsa nkhani za polisi pa polisi ya Dedza, a Kasimu Manda, atsimikiza za kumangidwa kwa mnyamatayo, koma iwo sanamutchule dzina lake, pofuna kumuteteza | Female | |
A Manda ati mayi a mtsikana ogwililiridwayu, anasiyana banja ndi mamuna wawo oyamba miyezi yingapo yapitayo, ndipo anakwatirana ndi bambo ake a m’nyamata oganizilidwayu | A Manda ati mayi a mtsikana ogwililiridwayu, anasiyana banja ndi mamuna wawo oyamba miyezi yingapo yapitayo, ndipo anakwatirana ndi bambo ake a m’nyamata oganizilidwayu | Female | |
Koma kaamba kochepa kwa nyumba imene banjali limakhamo, oganiziridwayu pamodzi ndi mtsikanayu, anawayika chipinda chimodzi choti adzigonapo | Koma kaamba kochepa kwa nyumba imene banjali limakhamo, oganiziridwayu pamodzi ndi mtsikanayu, anawayika chipinda chimodzi choti adzigonapo | Female | |
pamenepa anakhala ngati akakhala pumbwa ku chipwete, pomwe awiriwa anayamba ubwezi ogonana. Nthambi yowona za anthu olowa komanso kutuluka m’dziko muno lamanga nzika za zaku Ethiopia zokwana 93 | pamenepa anakhala ngati akakhala pumbwa ku chipwete, pomwe awiriwa anayamba ubwezi ogonana. Nthambi yowona za anthu olowa komanso kutuluka m’dziko muno lamanga nzika za zaku Efiyopiya zokwana nainte fili | Female | |
poziganizira kuti zinalowa m’dziko muno opanda kalata za chiloledzo. Mneneri ku nthambiyi m’chigawo chaku mpoto, a Francis Chitambuli, watsimikiza za nkhaniyi | poziganizira kuti zinalowa m’dziko muno opanda kalata za chiloledzo. Mneneri ku nthambiyi m’chigawo chaku mpoto, a Fulansisi Chitambuli, watsimikiza za nkhaniyi | Female | |
ponena kuti nzika zaku Ethiopia zo zamangidwa madzulo a lolemba m’boma Mzimba. Malingana ndi a Chitambuli, anthuwa anali mu galimoto ya mtundu wa Lorry | ponena kuti nzika zaku Efiyopiya zo zamangidwa madzulo a lolemba m’boma Mzimba. Malingana ndi a Chitambuli, anthuwa anali mu galimoto ya mtundu wa Lole | Female | |
ndipo amalunjika mu mzinda wa Mzuzu kuchokera m’boma la Karonga. Nthambiyi yamanganso dalayivala wa galimoto yo, Yona Kamanga | ndipo amalunjika mu mzinda wa Mzuzu kuchokera m’boma la Karonga. Nthambiyi yamanganso dalayivala wa galimoto yo, Yona Kamanga | Female | |
amene amutsegulira mlandu othandiza nzika za mayiko ena kulowa m’dziko muno opanda kalata za chiloledzo | amene amutsegulira mlandu othandiza nzika za mayiko ena kulowa m’dziko muno opanda kalata za chiloledzo | Female | |
M’modzi wa akatswiri pa nkhani za uchembere wabwino m’dziko muno, Mayi Dorothy Ngoma, wapempha nyumba zofaritsa komanso kusindikiza nkhan | M’modzi wa akatswiri pa nkhani za uchembere wabwino m’dziko muno, Mayi Dolofe Ngoma, wapempha nyumba zofaritsa komanso kusindikiza nkhan | Female | |
kuti zigwirane manja ndi boma pa ntchito yozindikilitsa anthu za ubereki komanso uchembere wabwino. Iwo apereka pempholi Lolemba mu mzinda wa Blantyre, pa mkumano umene anali nawo ndi atolankhani | kuti zigwirane manja ndi boma pa ntchito yozindikilitsa anthu za ubereki komanso uchembere wabwino. Iwo apereka pempholi Lolemba mu mzinda wa Bulantaya, pa mkumano umene anali nawo ndi atolankhani | Female | |
ochokera ku nyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani zosiyanasiya. Mayi Ngoma ati atolankhani ali ndi udindo waukulu, makamaka pozikikilitsa anthu za uchembere wabwino | ochokera ku nyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani zosiyanasiya. Mayi Ngoma ati atolankhani ali ndi udindo waukulu, makamaka pozikikilitsa anthu za uchembere wabwino | Female | |
pofuna kuchepetsa chiwelengero cha amayi amene akumamwalira pa nthawi imene akubereka. Amayi pafupifupi asanu ndi m'modzi akumwalira patsiku kaamba ka mavuto awubereki m’dziko muno | pofuna kuchepetsa chiwelengero cha amayi amene akumamwalira pa nthawi imene akubereka. Amayi pafupifupi asanu ndi m'modzi akumwalira patsiku kaamba ka mavuto awubereki m’dziko muno | Female | |
Malingana ndi bungwe la za Umoyo pa dziko la pansi la World Health Organisation ,dziko la Malawi liri pa nambala 13 pa m'ndandanda wa mayiko osawukisitsa ku Africa | Malingana ndi bungwe la za Umoyo pa dziko la pansi la waodi hefe oganaizeshoni , dziko la Malawi liri pa nambala fetini pa m'ndandanda wa mayiko osawukisitsa ku Afilika | Female | |
pa chiwerengero cha a mayi amene amamwalira kaamba ka mavuto okhudzana ndi uchembere. Ngati njira yimodzi yolimbana ndi kusitha kwa nyengo | pa chiwerengero cha a mayi amene amamwalira kaamba ka mavuto okhudzana ndi uchembere. Ngati njira yimodzi yolimbana ndi kusitha kwa nyengo | Female | |
achinyamata ena okhudzidwa, amene ali pansi pa utumiki wa Charismatic Redeemed, ku Ndirande, mu mzinda wa Blantyre, akhazikitsa ntchito yodzala mitengo mu Phiri la Ndirande | achinyamata ena okhudzidwa, amene ali pansi pa utumiki wa kalizimatiki lidimudi, ku Ndirande, mu mzinda wa Bulantaya akhazikitsa ntchito yodzala mitengo mu Phiri la Ndirande | Female | |
Amene akutsogolera achinyamata okhuzidwawa, a Brave Chatama, awuza wayilesi ya Ndirande FM, kuti pakadali pano adzala kale mitengo yokwana 700, | Amene akutsogolera achinyamata okhuzidwawa, a Bulevu Chatama, awuza wayilesi ya Ndirande efuemu, kuti pakadali pano adzala kale mitengo yokwana seveni handede | Female | |
ndipo akuyembekezeka kudzala yoposera 500 thousand chaka chino. Bungwe la Alakatuli la Poetry Association of Malawi (PAM) mchigawo cha ku mmwera mogwirizana ndi bungwe lowelengetsera ndalama la KB Accounting Services Limited | ndipo akuyembekezeka kudzala yoposera faifi handiledi sauzande chaka chino. Bungwe la Alakatuli la poetile asosiyeshoni ofu Malawi (PAMU) mchigawo cha ku mmwera mogwirizana ndi bungwe lowelengetsera ndalama la Keibi akaunting’i sevisezi limited | Female | |
lero abzala mitengo pa sukulu ya Mpata ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre. Bungwe komanso kampaniyi abzala mitengo yopitilira 200 pa sukuluyi | lero abzala mitengo pa sukulu ya Mpata ku Machinjiri mu mzinda wa Bulantaya. Bungwe komanso kampaniyi abzala mitengo yopitilira thu handiledi pa sukuluyi | Female | |
yomwe akuti ithandize, yomwe akuti ithandize pa ntchito yobwezeletsa Chilengedwe. Ndipo mmawu ake, mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi, Dorothy Maotcha anati kupatula kuthandiza pa ntchito yobwezeretsa Chilengedwe | yomwe akuti ithandize, yomwe akuti ithandize pa ntchito yobwezeletsa Chilengedwe. Ndipo mmawu ake, mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi, Dolofe Maotcha anati kupatula kuthandiza pa ntchito yobwezeretsa Chilengedwe | Female | |
mitengoyi ikazakula izathandiza kupeleka nthunzi kwa ophunzira, mwa zina. Mbali inayi, mkulu wa kampani ya KB Accounting Services, Joseph KB Kadzakumanja | mitengoyi ikazakula izathandiza kupeleka nthunzi kwa ophunzira, mwa zina. Mbali inayi, mkulu wa kampani ya Keibi akauntimg’i sevisezi, Jozefe Keibi Kadzakumanja | Female | |
wati kampani yawo ndi yokhuzika kwambiri ndi Mavuto omwe adza kaamba ka kuonongeka kwa Chilengedwe ndipo ichi ndi chifukwa chake anaganiza zogwirana manja ndi bungwe la PAM kuti abwezeletse ina mwa mitengo | wati kampani yawo ndi yokhuzika kwambiri ndi Mavuto omwe adza kaamba ka kuonongeka kwa Chilengedwe ndipo ichi ndi chifukwa chake anaganiza zogwirana manja ndi bungwe la PAMU kuti abwezeletse ina mwa mitengo | Female | |
Pakadali pano, ophunzira pa sukulupa alonjeza kusamalira mitengo yomwe yabzalidwayi. Apolisi ku Thyolo amanga mnyamata wa zaka 22, Madalitso Wyson | Pakadali pano, ophunzira pa sukulupa alonjeza kusamalira mitengo yomwe yabzalidwayi. Apolisi ku Thyolo amanga mnyamata wa zaka Twente thu, Madalitso Wayisoni | Female | |
pomuganizira kuti amafuna kugulitsa mwana wa zaka 11 kwa sing'anga wina mbomalo. Mneneri wa apolisi ku Thyolo, Tione Amos watsimikiza za nkhaniyi | pomuganizira kuti amafuna kugulitsa mwana wa zaka leveni kwa sing'anga wina mbomalo. Mneneri wa apolisi ku Thyolo, Tione Amosi watsimikiza za nkhaniyi | Female | |
pomwe wati izi zachitika lachisanu sabata yatha pomwe oganizilidwayu anapita ku sukulu ya Chingazi komwe mwanayu amaphunzira | pomwe wati izi zachitika lachisanu sabata yatha pomwe oganizilidwayu anapita ku sukulu ya Chingazi komwe mwanayu amaphunzira | Female | |
ndi kukamutenga popanda kudziwitsa Makolo ake. Amos watiuza kuti atachoka naye ku sukulu-ko, Wyson anatengera mwanayu kwa bwenzi lake komwe anakagona | ndi kukamutenga popanda kudziwitsa Makolo ake. Amosi watiuza kuti atachoka naye ku sukulu-ko, Wayisoni anatengera mwanayu kwa bwenzi lake komwe anakagona | Female | |
asanapitilire ku Ntambanyama mmawa wa tsiku lotsatiralo komwe anakakumana ndi singangayu. Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi ku Thyolo, singangayu anadziwitsa anthu a mmudzi za izi | asanapitilire ku Ntambanyama mmawa wa tsiku lotsatiralo komwe anakakumana ndi singangayu. Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi ku Thyolo, singangayu anadziwitsa anthu a mmudzi za izi | Female | |
omwe sanachedwe koma kugwira oganizilidwayu ndi kukamutula ku polisi. Madalitso Wyson yemwe ndi wa mmudzi mwa Chawoneka mfumu yaikulu Khwethemule mboma lomweli la Thyolo | omwe sanachedwe koma kugwira oganizilidwayu ndi kukamutula ku polisi. Madalitso Wayisoni yemwe ndi wa mmudzi mwa Chawoneka mfumu yaikulu Khwethemule mboma lomweli la Thyolo | Female | |
akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu ozembetsa munthu. M'madera ambiri mu mzinda wa Blantyre kuli mvula yochuluka yomwe yayamba kugwa usiku wapitawu | akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu ozembetsa munthu. M'madera ambiri mu mzinda wa Bulantaya kuli mvula yochuluka yomwe yayamba kugwa usiku wapitawu | Female | |
Kodi kwanuko nyengo ili motani Malipoti akuti nyumba zambiri zagwa m'madera ena a dziko lino kaamba ka mvulayi, tipatseni chinthuzithunzi cha momwe ziliri kwanuko | Kodi kwanuko nyengo ili motani Malipoti akuti nyumba zambiri zagwa m'madera ena a dziko lino kaamba ka mvulayi, tipatseni chinthuzithunzi cha momwe ziliri kwanuko | Female | |
Kampani ya ntchito za lamya ya TNM yati yadzipereka pofuna kutukula miyoyo ya ophunzira m’sukulu za ukachenjede m’dziko muno pa maphunziro awo, pa nthawi yomwe kampaniyi yachilimikanso kutukula ntchito zake | Kampani ya ntchito za lamya ya Tieniemu yati yadzipereka pofuna kutukula miyoyo ya ophunzira m’sukulu za ukachenjede m’dziko muno pa maphunziro awo, pa nthawi yomwe kampaniyi yachilimikanso kutukula ntchito zake | Female | |
Izi ndi malingana ndi mkulu wa zofaritsa nkhani ku TNM, Limbani Nsapato yemwe wati, pakadali pano, kampaniyi yayambapo ntchito yopeza akazembe m’sukuluzi | Izi ndi malingana ndi mkulu wa zofaritsa nkhani ku Tieniemu, Limbani Nsapato yemwe wati, pakadali pano, kampaniyi yayambapo ntchito yopeza akazembe m’sukuluzi | Female | |
amene adzithandiza kutukula, komanso kudziwitsa ena zambiri zokhuza kampaniyi. Malingana ndi a Nsapato, kupatula kukhaka akazembe, ophunzirawa azipezanso phindu lina | amene adzithandiza kutukula, komanso kudziwitsa ena zambiri zokhuza kampaniyi. Malingana ndi a Nsapato, kupatula kukhaka akazembe, ophunzirawa azipezanso phindu lina | Female | |
lomwe lidziwathandiza pa moyo wawo wa maphunziro. Posachedwapa, kampaniyi inali ku sukulu ya ukachenjede ya MUBAS, ku nthambi ya Continuing Education Centre komwe imazindikiritsa ophunzira ku sukuluyi | lomwe lidziwathandiza pa moyo wawo wa maphunziro. Posachedwapa, kampaniyi inali ku sukulu ya ukachenjede ya MUBASI, ku nthambi ya kontinyuwing’i ejukeshoni senta komwe imazindikiritsa ophunzira ku sukuluyi | Female | |
zambiri za momwe angakhalire akazembe. Phungu wa dera la kum’mwera, chaku m’mawa, kwa boma la Lilongwe, Steven Malondera | zambiri za momwe angakhalire akazembe. Phungu wa dera la kum’mwera, chaku m’mawa, kwa boma la Lilongwe, Sitiveni Malondera | Female | |
wapepesa kwa a Malawi kaamba kopempha Nyumba ya Malamulo, kuti igulire aphungu a Nyumbayo, zovala zozitetezela ku Mvula – Raincoat, pa chingerezi | wapepesa kwa a Malawi kaamba kopempha Nyumba ya Malamulo, kuti igulire aphungu a Nyumbayo, zovala zozitetezela ku Mvula – lenikhoti, pa chingerezi | Female | |
A Malondera anapereka pempholi Lachitatu, ponena kuti aphunguwa akumanyowa ndi mvula yimene yakhala ikugwa mu mzinda wa Lilongwe | A Malondera anapereka pempholi Lachitatu, ponena kuti aphunguwa akumanyowa ndi mvula yimene yakhala ikugwa mu mzinda wa Lilongwe | Female | |
makamaka akatsika galimoto zawo, panja pa Nyumba ya Malamulo, akamakalowa mu Nyumbayo. Atapereka pempholi, mtsogoleri wa Nyumbayi, a Richard Chimwendo Banda | makamaka akatsika galimoto zawo, panja pa Nyumba ya Malamulo, akamakalowa mu Nyumbayo. Atapereka pempholi, mtsogoleri wa Nyumbayi, a Ritchadi Chimwendo Banda | Female | |
anati pempholi limafunika kuwunikidwa bwino ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo wa. Koma nkhaniyi inakwiyitsa a Malawi ambiri pa masamba a mchezo a pa Internet | anati pempholi limafunika kuwunikidwa bwino ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo wa. Koma nkhaniyi inakwiyitsa a Malawi ambiri pa masamba a mchezo a pa Intaneti | Female | |
pomwe ambiri mwa iwo anadzudzula phunguyu pa pempholi, ponena kuti aphunguwa amalandila kale ndalama zochuluka, ndipo sangalephere kugula Raincoat mwa iwo okha | pomwe ambiri mwa iwo anadzudzula phunguyu pa pempholi, ponena kuti aphunguwa amalandila kale ndalama zochuluka, ndipo sangalephere kugula lenikhoti mwa iwo okha | Female | |
Mkwiyo wa a Malawiwu wapangitsa, Malondera , kupepesa kudzera pa tsamba lako la mchezo la Facebook, pomwe wati anthu sanamve bwino pa za pempho lakeli | Mkwiyo wa a Malawiwu wapangitsa, Malondera , kupepesa kudzera pa tsamba lako la mchezo la Fesibuku, pomwe wati anthu sanamve bwino pa za pempho lakeli | Female | |
Apolisi ku Thyolo akufunafuna mbava zina, zimene akuziganizira kuti zapha mlonda, amene amapereka chitetezo pa nyumba ya mpondamatiki wina, m’bomali | Apolisi ku Thyolo akufunafuna mbava zina, zimene akuziganizira kuti zapha mlonda, amene amapereka chitetezo pa nyumba ya mpondamatiki wina, m’bomali | Female | |
Ofaritsa nkhani za apolisi ku Thyolo ko, Amos Tione, watsimikiza za nkhaniyi, ndipo anafotokoza kuti malemuwa, a Mateyu Mchikocho, aphedwa usiku wapitawu | Ofaritsa nkhani za apolisi ku Thyolo ko, Amosi Tione, watsimikiza za nkhaniyi, ndipo anafotokoza kuti malemuwa, a Mateyu Mchikocho, aphedwa usiku wapitawu | Female | |
Malingana ndi Tione, mbavazi zinamangalira a Mchikocho, ndi kuwayika ka nsalu m’kamwa, asanawaphe ndi kuba ma Feremu amazenela, pa malopa | Malingana ndi Tione, mbavazi zinamangalira a Mchikocho, ndi kuwayika ka nsalu m’kamwa, asanawaphe ndi kuba ma Feremu amazenela, pa malopa | Female | |
Yemwe anakhalapo mfumu ya mzinda wa Mzuzu, Egbert Chibambo wamwalira. Malipoti akuti a Chiwambo amwalira usiku wapitawu pa chipatala cha Mumbwe, mu mzindawu | Yemwe anakhalapo mfumu ya mzinda wa Mzuzu, igibeti Chiwambo wamwalira. Malipoti akuti a Chiwambo amwalira usiku wapitawu pa chipatala cha Mumbwe, mu mzindawu | Female | |
Wachibale wa a Chibambo, Kamuzu Chibambo watsikimiza za imfayi koma wati zambiri zake azilengezabe Kupatula kukhala Mfumu ya Mzinda wa Mzuzu | Wachibale wa a Chiwambo, Kamuzu Chiwambo watsikimiza za imfayi koma wati zambiri zake azilengezabe Kupatula kukhala Mfumu ya Mzinda wa Mzuzu | Female | |
malemuwo anakhalaponso pa ma udindo akuluakulu ambiri m’chipani cha Alliance for Democracy [Aford], kupatulapo kuthandiziranso kumenyera ufulu wa demokalase m’dziko lino | malemuwo anakhalaponso pa ma udindo akuluakulu ambiri m’chipani cha alayansi fo demokilase [Afodi], kupatulapo kuthandiziranso kumenyera ufulu wa demokalase m’dziko lino | Female | |
Mtsikana wa zaka 24, Christian Masina , amene amapanga malonda ogulitsa thupi lake ku Chigwiri mu mzinda wa Lilongwe | Mtsikana wa zaka twente folo, khilisitina Masina , amene amapanga malonda ogulitsa thupi lake ku Chigwiri mu mzinda wa Lilongwe | Female | |
amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi zitatu, atapezeka wolakwa pa mlandu ogwilira ana awiri, aamuna | amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi zitatu, atapezeka wolakwa pa mlandu ogwilira ana awiri, aamuna | Female | |
Bwalo la Lilongwe Senior Magistrate, kudzera mwa amene amayimila boma pa mlanduwu, a Richard Kandeya, linamva kuti Masina anapalamula mlanduwu pa 27 June 2021 | Bwalo la Lilongwe siniyo majesitileti, kudzera mwa amene amayimila boma pa mlanduwu, a Litchadi Kandeya, linamva kuti Masina anapalamula mlanduwu pa twente seneni Juni twente twente wani | Female | |
Pa tsikulu, Masina, amene anali ataledzera ananyengelera ndi kugonana ndi ana Awiriwa, a zaka 4 ndi 16, amene ndi ana a mnzake, amene amapanga naye malonda ogulitsa thupi ku Chigwirizanoko | Pa tsikulu, Masina, amene anali ataledzera ananyengelera ndi kugonana ndi ana Awiriwa, a zaka folo ndi sikisitini, amene ndi ana a mnzake, amene amapanga naye malonda ogulitsa thupi ku Chigwirizanoko | Female | |
Pali malipoti oti katangale wakula kwambiri ku nyumba ya chimfumu pamene ogwira ntchito ku nyumbayi akumalandira ziphuphu ku kampani komanso anthu omwe akufuna kulandira makontilakiti a boma, mwa zina | Pali malipoti oti katangale wakula kwambiri ku nyumba ya chimfumu pamene ogwira ntchito ku nyumbayi akumalandira ziphuphu ku kampani komanso anthu omwe akufuna kulandira makontilakiti a boma, mwa zina | Female | |
Izi malingana ndi kalata yomwe Ndirande FM yaona yimene mkulu oyang’anira ogwira ntchito ku nyumbayi, a Prince Kapondamgaga alembera a ntchitowa yomwe yadzudzula kolimba za mchitidwewu | Izi malingana ndi kalata yomwe Ndirande efuemu yaona yimene mkulu oyang’anira ogwira ntchito ku nyumbayi, a Pulinsi Kapondamgaga alembera a ntchitowa yomwe yadzudzula kolimba za mchitidwewu | Female | |
Malingana ndi a Kapondamgaga, anthu omwe akukhuzidwa ndi mchitidwewu akuyenera kulekeratu komanso akonze pomwe akuona kuti analakwira lamulo | Malingana ndi a Kapondamgaga, anthu omwe akukhuzidwa ndi mchitidwewu akuyenera kulekeratu komanso akonze pomwe akuona kuti analakwira lamulo | Female | |
Kalatayi yatchulapo kugwilitsa ntchito dzina la ku nyumba kwa mtsogoleri wa dziko lino-state house-potenga zinthu kwa anthu koma zosapindulira nyumbayi | Kalatayi yatchulapo kugwilitsa ntchito dzina la ku nyumba kwa mtsogoleri wa dziko lino, siteti hausi potenga zinthu kwa anthu koma zosapindulira nyumbayi | Female | |
komanso kulandira ndalama mu dzina la mtsogoleriyu, Lazarus Chakwera zomwe mapeto ake zikumapindulira anthu a ziphuphuwa | komanso kulandira ndalama mu dzina la mtsogoleriyu, Lazalasi Chakwera zomwe mapeto ake zikumapindulira anthu a ziphuphuwa | Female | |
Pakadali pano, bungwe lomenyera ufulu wa anthu la HRDC lati nyumba ya bomayi yawasiya anthu m’malere maka potengera kuti sinabweletse poyera mayina a anthu omwe akukhuzidwa ndi mchitidwewu | Pakadali pano, bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Etchialadisi lati nyumba ya bomayi yawasiya anthu m’malere maka potengera kuti sinabweletse poyera mayina a anthu omwe akukhuzidwa ndi mchitidwewu | Female | |
HRDC yati kuchita za chinyengo mwa njira iliyonse ndi mlandu ndipo ikuyembekezera kuti anthu oterewa anenezedwa ku bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu | Etchialadisi yati kuchita za chinyengo mwa njira iliyonse ndi mlandu ndipo ikuyembekezera kuti anthu oterewa anenezedwa ku bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu | Female | |
la ACB kuti lamulo ligwire ntchito yake. Ngakhale mbali zosiyanasiyana zakhala zikupempha mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera kuti asankhe mndandanda wa nduna zochepa mu cabinet yake | la Esibi kuti lamulo ligwire ntchito yake. Ngakhale mbali zosiyanasiyana zakhala zikupempha mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera kuti asankhe mndandanda wa nduna zochepa mu kabineti yake | Female | |
mtsogoleriyu wasankha nduna komanso wachiwiri kwa nduna za boma zokwana 29. Izi ndi zosiyana ndi pempho lomwe mbalizi zomwe ndi kuphatikizapo bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula la CAMA | mtsogoleriyu wasankha nduna komanso wachiwiri kwa nduna za boma zokwana twente naini. Izi ndi zosiyana ndi pempho lomwe mbalizi zomwe ndi kuphatikizapo bungwe lomenyera ufulu wa anthu ogula la KAMA | Female | |
lomwe limafuna kuti mtsogoleriyu asankhe nduna zosapitilira Khumi ndi zisanu, (15). Malingana ndi mndandanda wa nduna zomwe a Chakwera atulutsa | lomwe limafuna kuti mtsogoleriyu asankhe nduna zosapitilira Khumi ndi zisanu, (fifitini). Malingana ndi mndandanda wa nduna zomwe a Chakwera atulutsa | Female | |
anthu ena achotsedwa pa unduna ndi kuikapo a tsopano pamene ena asinthidwa maunduna awo ndipo ena abwereza maundunawa | anthu ena achotsedwa pa unduna ndi kuikapo a tsopano pamene ena asinthidwa maunduna awo ndipo ena abwereza maundunawa | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.