audio audioduration (s) 1.12 18.5 | raw_text stringlengths 1 297 | normalized_text stringlengths 1 267 | gender stringclasses 16
values |
|---|---|---|---|
Ndipo kumbali yawo, Apostle Harry Nthara a Mpingo wa Divine Word Ministry anali wodabwa kuti ndi chifukwa chani lamuloli lakhala lisakutsatilidwa kuchokera mchaka cha 1992 | Ndipo kumbali yawo, Aposito Hale Nthara a Mpingo wa Divaini waodi minisitile anali wodabwa kuti ndi chifukwa chani lamuloli lakhala lisakutsatilidwa kuchokera mchaka cha naintini nainte thu | Female | |
ponena kuti ngati liri lamulo labwino, silimayenera kutayidwa chotere. Pamenepa, iwo anati likuyenera kuchotsedwa m'malamulowa kapena lisinthidwe lizimveka mwa njira ina osati kunyonga | ponena kuti ngati liri lamulo labwino, silimayenera kutayidwa chotere. Pamenepa, iwo anati likuyenera kuchotsedwa m'malamulowa kapena lisinthidwe lizimveka mwa njira ina osati kunyonga | Female | |
Ndipo ena mwa anthu omwe anayimba phone m'program-yi anati ndi koyenera kuti lamuloli lithetsedwe chifukwa silikufunikiranso mu ulamuliro wa democracy | Ndipo ena mwa anthu omwe anayimba foni mpulogilamuyo anati ndi koyenera kuti lamuloli lithetsedwe chifukwa silikufunikiranso mu ulamuliro wa demokilase | Female | |
Nayo komiti ya za malamulo ya ku nyumba ya malamulo, posachedwapa, yachititsa misonkhano yomva maganizo a anthu pa nkhaniyi ndipo zotsatira zake azipeleka mnyumbayi pofuna kuti aphungu azikambirane | Nayo komiti ya za malamulo ya ku nyumba ya malamulo, posachedwapa, yachititsa misonkhano yomva maganizo a anthu pa nkhaniyi ndipo zotsatira zake azipeleka mnyumbayi pofuna kuti aphungu azikambirane | Female | |
Mkulu wa banki yaikulu m'dziko muno ya Reserve, Dr. Wilson Banda wati bankiyi ili ndi chikhulupuliro kuti mavuto ena a za chuma omwe akhuza dziko lino achepa | Mkulu wa banki yaikulu m'dziko muno yalizevu , Dokota Wilisoni Banda wati bankiyi ili ndi chikhulupuliro kuti mavuto ena a za chuma omwe akhuza dziko lino achepa | Female | |
kutsatira kugwetsedwa mphanvu kwa ndalama ya kwacha. Iwo ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani omwe akuchititsa mu mzinda wa Blantyre | kutsatira kugwetsedwa mphanvu kwa ndalama ya kwacha. Iwo ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani omwe akuchititsa mu mzinda wa Bulantaya | Female | |
komwe atchulako nkhondo ya pakati pa Ukraine ndi Russia, mvula ya namondwe wa Ana komanso mliri wa COVID-19 ngati zina mwa zinthu zomwe zakolezera kuti dziko lino lisambire m'mavuto a chuma | komwe atchulako nkhondo ya pakati pa Uyukileni ndi Rasha, mvula ya namondwe wa Ana komanso mliri wa Kovidi – naintini ngati zina mwa zinthu zomwe zakolezera kuti dziko lino lisambire m'mavuto a chuma | Female | |
Komatu a Banda asutsa malipoti oti dziko lino lalangizidwa ndi boma la za chuma pa dziko lonse la International Monetary Fund (IMF) kuti ligwetse mphanvu ya ndalamayi | Komatu a Banda asutsa malipoti oti dziko lino lalangizidwa ndi boma la za chuma pa dziko lonse la intaneshono monetale fandi (aiemuefu) kuti ligwetse mphanvu ya ndalamayi | Female | |
Ife timakhala kuno ndipo timawona momwe chuma chikuyendera. Sitingadalire IMF kuti itiwuze kuti tisitse mphanvu ya kwacha. Zikanachitikabe, atero a za Banda | Ife timakhala kuno ndipo timawona momwe chuma chikuyendera. Sitingadalire aiemuefu kuti itiwuze kuti tisitse mphanvu ya kwacha. Zikanachitikabe, atero a za Banda | Female | |
Mkulu wina wochita malonda ku msika wa Makata ku Ndirande mu mzinda wa Blantyre ali mu ululu owopsa anyamata ena okwiya atamukwilira wa moyo m’dzenje lina lomwe bamboyu amakumba ngati chimbuzi | Mkulu wina wochita malonda ku msika wa Makata ku Ndirande mu mzinda wa Bulantaya ali mu ululu owopsa anyamata ena okwiya atamukwilira wa moyo m’dzenje lina lomwe bamboyu amakumba ngati chimbuzi | Female | |
Nkhaniyi ikuti bamboyu amakumba chimbuzi pa Malo ake omwe ali pafupi ndi msikawu, zomwe anyamata ena oyang'anira msikawu sanakondwere nazo | Nkhaniyi ikuti bamboyu amakumba chimbuzi pa Malo ake omwe ali pafupi ndi msikawu, zomwe anyamata ena oyang'anira msikawu sanakondwere nazo | Female | |
ndipo amamuwuza kuti asiye chifukwa ziwasokonezera bizinesi yawo ya zimbudzi. Komatu ngakhale anali atamukuntha makofi, mkuluyu sanamve malangizo a anthuwa ndipo anapitilira ndi ntchito yake | ndipo amamuwuza kuti asiye chifukwa ziwasokonezera bizinesi yawo ya zimbudzi. Komatu ngakhale anali atamukuntha makofi, mkuluyu sanamve malangizo a anthuwa ndipo anapitilira ndi ntchito yake | Female | |
zomwe zinakolezera mkwiyo mwa anyamatawa. Apa ndi pomwe anabweranso koma mwa mkokomo ndipo anangofikira kukankhira bamboyu mdzenje | zomwe zinakolezera mkwiyo mwa anyamatawa. Apa ndi pomwe anabweranso koma mwa mkokomo ndipo anangofikira kukankhira bamboyu mdzenje | Female | |
ndi kuyamba kumukwilira, ndi miyala, njerwa komanso dothi ngati momwe zimakhalira ku manda. Pomwetu izi zimachitika ndi kuti anyamatawa akuwuza anthu ozungulira | ndi kuyamba kumukwilira, ndi miyala, njerwa komanso dothi ngati momwe zimakhalira ku manda. Pomwetu izi zimachitika ndi kuti anyamatawa akuwuza anthu ozungulira | Female | |
kuti pasapezeke olesesa ponena kuti yemwe atero aona zakuda. Patapita nthawi, ndi pomwe anthu ena olimba mtima anachilimika ndi kupulumutsa m’dalayu ndipo | kuti pasapezeke olesesa ponena kuti yemwe atero aona zakuda. Patapita nthawi, ndi pomwe anthu ena olimba mtima anachilimika ndi kupulumutsa m’dalayu ndipo | Female | |
malingana ndi malipoti, akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Queens. Pakadali pano, akulu-akulu apolisi ku Ndirande sanayankhulepo kanthu pa nkhaniyi | malingana ndi malipoti, akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha kwinzi. Pakadali pano, akulu-akulu apolisi ku Ndirande sanayankhulepo kanthu pa nkhaniyi | Female | |
Katswiri pa nkhani za chuma, a Dr. Betchani Tchereni, wati anthu ayembekezere kukwera mtengo kwa katundu osiyanasiyana m’dziko muno kutsatira kuchepetsedwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha | Katswiri pa nkhani za chuma, a Dokota Betchani Tchereni, wati anthu ayembekezere kukwera mtengo kwa katundu osiyanasiyana m’dziko muno kutsatira kuchepetsedwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha | Female | |
Dr. Tchereni anena izi pomwe Banki Yaikulu m’dziko Ya Reserve yachepetsa mphamvu ya ndalama ya kwacha ndi 25 kwacha pa 100 kwacha iliyonse kuyambira lero Lachisanu | Dokota Tchereni anena izi pomwe Banki Yaikulu m’dziko Ya lizevu yachepetsa mphamvu ya ndalama ya kwacha ndi twente faifi kwacha pa wani handiledi kwacha iliyonse kuyambira lero Lachisanu | Female | |
M’mawu awo, a Tchereni, ati dziko la Malawi limadalira kwambiri kuitanitsa katundu osiyanasiyana kuchokera kunja kwa dziko lino | M’mawu awo, a Tchereni, ati dziko la Malawi limadalira kwambiri kuitanitsa katundu osiyanasiyana kuchokera kunja kwa dziko lino | Female | |
chomcho pali kuthekera kwakukulu kuti katundu yo akwera mtengo kaamba kuchepa mphamvu kwa kwacha | chomcho pali kuthekera kwakukulu kuti katundu yo akwera mtengo kaamba kuchepa mphamvu kwa kwacha | Female | |
Ndalama ya Kwacha yachepetsedwa mphamvu pomwe akuluakulu oyimira bungwe lowona za chuma pa dziko lonse la International Monetary Fund (IMF) ali m’dziko muno kuzachita zokambirana ndi boma zokhudza mavuto azachuma | Ndalama ya Kwacha yachepetsedwa mphamvu pomwe akuluakulu oyimira bungwe lowona za chuma pa dziko lonse la intaneshono m0onetale fandi (aimuefu) ali m’dziko muno kuzachita zokambirana ndi boma zokhudza mavuto azachuma | Female | |
omwe dziko lino likukumana nawo. Pali malipoti oti woyimba wodziwika bwino pa chamba cha Hip Hop, Martse wamwalira | omwe dziko lino likukumana nawo. Pali malipoti oti woyimba wodziwika bwino pa chamba cha Hipopu Matse wamwalira | Female | |
Martse yemwe dzina lake lenileni linali Martin Nkhata wamwalira mphindi zochepa zapitazo pa chipatala cha Queen Elizabeth Central | Matse yemwe dzina lake lenileni linali Matini Nkhata wamwalira mphindi zochepa zapitazo pa chipatala cha kwinzi elizabefi sentilo | Female | |
kutsatira kupsa ndi moto omwe unabuka mnyumba yomwe anagona ku Mangochi, masiku angapo apitawo | kutsatira kupsa ndi moto omwe unabuka mnyumba yomwe anagona ku Mangochi, masiku angapo apitawo | Female | |
Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Peter Mutharika wati ndi zotheka kuti dziko lino lituluke mmavuto a za chuma omwe likukumana nawo, koma pokhapokha adindo atakhazikitsa njira zolozeka zothanirana ndi mavutowa | Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Pita Mutharika wati ndi zotheka kuti dziko lino lituluke mmavuto a za chuma omwe likukumana nawo, koma pokhapokha adindo atakhazikitsa njira zolozeka zothanirana ndi mavutowa | Female | |
A Mutharika ayankhula izi dzulo lachisanu pomwe amachita zokambirana ndi bungwe la zipembezo la Public Affairs Committee (PAC) pa zinthu zina zokhuza utsogoleri | A Mutharika ayankhula izi dzulo lachisanu pomwe amachita zokambirana ndi bungwe la zipembezo la pabuliki afeyazi komiti (PAKI) pa zinthu zina zokhuza utsogoleri | Female | |
Malingana ndi a Mutharika, pomwe DPP imatenganso boma mchaka cha 2014, inapeza chuma chisakuyenda bwino koma inakwanitsa kuchibwezeletsa mmiyezi isanu ndi umodzi yokha | Malingana ndi a Mutharika, pomwe Dipipi imatenganso boma mchaka cha twente fotini, inapeza chuma chisakuyenda bwino koma inakwanitsa kuchibwezeletsa mmiyezi isanu ndi umodzi yokha | Female | |
Kupatula nkhani za chuma, mtsogoleri wa chipani cha DPP-yu pamodzi ndi bungwe la PAC anakambirananso zambiri zokhuza umodzi pa ndale | Kupatula nkhani za chuma, mtsogoleri wa chipani cha Dipipi-yu pamodzi ndi bungwe la PAKI anakambirananso zambiri zokhuza umodzi pa ndale | Female | |
Pamenepa, wa pa mpando wa bungwe la PAC, Monsignor Patrick Thawale anakumbutsa a Mutharika pa za udindo omwe chipani chomwe amatsogolera cha DPP chili nawo pa ulamuliro wa democracy | Pamenepa, wa pa mpando wa bungwe la PAKI, Monsinyo Patiliki Thawale anakumbutsa a Mutharika pa za udindo omwe chipani chomwe amatsogolera cha Dipipi chili nawo pa ulamuliro wa demokilase | Female | |
Apolisi ku Mulanje atsekera mchitokosi amuna anayi powaganizira kuti amapanga upo ofuna kuchita umbanda ndi umbava | Apolisi ku Mulanje atsekera mchitokosi amuna anayi powaganizira kuti amapanga upo ofuna kuchita umbanda ndi umbava | Female | |
Ofalitsa nkhani za apolisi mbomali, Gresham Ngwira wati amunawa omwe ndi a Manuel Monja, Enock Sailesi komanso Reymond Ngulube a ku Malawi ndi a Innocent Benjamin a ku Mozambique | Ofalitsa nkhani za apolisi mbomali, Gileshamu Ngwira wati amunawa omwe ndi a Manuwelo Monja, Inoki Sailesi komanso Reyimondi Ngulube a ku Malawi ndi a Inosenti Benjamini a ku Mozambiki | Female | |
anagwidwa pa malo ena otchedwa Minimini pomwe amadutsa mu msewu wa Limbe-Mloza. Malingana ndi a Ngwira, anthu ena a mmudzi ndi omwe anagwira anthuwa | anagwidwa pa malo ena otchedwa Minimini pomwe amadutsa mu msewu wa Limbe-Mloza. Malingana ndi a Ngwira, anthu ena a mmudzi ndi omwe anagwira anthuwa | Female | |
atadabwa ndi machitidwe awo ndipo anapezeka ndi chikwanje ndi zina . Atatengeledwa ku polisi, ndi pomwe amunawa amawulula kuti amafuna akabere mzika ina ya ku India yomwe ikuchita ntchito za malonda mdziko la Mozambique | atadabwa ndi machitidwe awo ndipo anapezeka ndi chikwanje ndi zina. Atatengeledwa ku polisi, ndi pomwe amunawa amawulula kuti amafuna akabere mzika ina ya ku Indiya yomwe ikuchita ntchito za malonda mdziko la Mozambiki | Female | |
Bwalo la milandu la First Grade Magistrate ku Chikwawa lagamula amuna awiri kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana K200,000 aliyense | Bwalo la milandu la fesiti giledi majesitileti ku Chikwawa lagamula amuna awiri kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana thu handiledi sauzande aliyense | Female | |
kaamba kopezeka olakwa pa mlandu opezeka ndi mafuta a galimoto a petulo popanda chilolezo. Malingana ndi mbali ya boma, amunawa, Yonasi Seveliano komanso Tembo Malizani | kaamba kopezeka olakwa pa mlandu opezeka ndi mafuta a galimoto a petulo popanda chilolezo. Malingana ndi mbali ya boma, amunawa, Yonasi Seveliyano komanso Tembo Malizani | Female | |
anapezeka ma-litre 267 a mafutawa mgalimoto zawo koma popanda chilolezo chochokera ku bungwe la mphanvu za magetsi ndi m'bwezera la MERA choti atha kutero | anapezeka ma-lita thu handiledi sikisite seveni a mafutawa mgalimoto zawo koma popanda chilolezo chochokera ku bungwe la mphanvu za magetsi ndi m'bwezera la MERA choti atha kutero | Female | |
Pamenepa, bwalolo lalamula amunawa kupeleka chindapusa cha ndalamazi ponena kuti ngati alephere kutero, akakhale ku ndende kwa miyezi khumi ndi iwiri | Pamenepa, bwalolo lalamula amunawa kupeleka chindapusa cha ndalamazi ponena kuti ngati alephere kutero, akakhale ku ndende kwa miyezi khumi ndi iwiri | Female | |
Pakadali pano, mafutawa alandidwa ndipo abwezeledwa ku boma la Malawi. Adindo ku Nthambi ya ndende za dziko lino | Pakadali pano, mafutawa alandidwa ndipo abwezeledwa ku boma la Malawi. Adindo ku Nthambi ya ndende za dziko lino | Female | |
asiyana zoyankhula pa malipoti oti mkayidi wina ku ndende ya Zomba wapezeka ndi lamya za m'manja ziwiri m'mimba mwake | asiyana zoyankhula pa malipoti oti mkayidi wina ku ndende ya Zomba wapezeka ndi lamya za m'manja ziwiri m'mimba mwake | Female | |
Pomwe mneneri ku nthambiyi, Chimwemwe Shaba watsimikizira nyumba Zina zofalitsa nkhani za nkhaniyi, wa pa mpando wa Nthambiyi, Justice Ken Manda | Pomwe mneneri ku nthambiyi, Chimwemwe Shawa watsimikizira nyumba Zina zofalitsa nkhani za nkhaniyi, wa pa mpando wa Nthambiyi, Jusitisi Keni Manda | Female | |
wati izi zachitika m'dziko la India osati ku Malawi. Pomwe amatsimikiza za nkhaniyi maola angapo apitawo, a Shaba anakana kuyankhula zambiri zokhuza izi | wati izi zachitika m'dziko la Indiya osati ku Malawi. Pomwe amatsimikiza za nkhaniyi maola angapo apitawo, a Shawa anakana kuyankhula zambiri zokhuza izi | Female | |
Komatu mphindi zochepa zapitazo, a Manda awuza komiti ya ku nyumba ya malamulo yowona za malamu kuti ngakhale nkhaniyi sinachitikire ku Malawi | Komatu mphindi zochepa zapitazo, a Manda awuza komiti ya ku nyumba ya malamulo yowona za malamu kuti ngakhale nkhaniyi sinachitikire ku Malawi | Female | |
akayidi ena ndende za dziko lino amakhala ndi lamyazi pomwe ali mndende. Mapemphero a Eidul fitr pa dziko lonse la pansi achitika lero lolemba | akayidi ena ndende za dziko lino amakhala ndi lamyazi pomwe ali mndende. Mapemphero a idi ufiti pa dziko lonse la pansi achitika lero lolemba | Female | |
kusekera nyengo yonse ya kusala kudya ndi kupemphera ya Ramadan yomwe asilamu achita kwa mwezi wa tunthu. Malingana ndi bungwe la Asilamu mdziko muno la Muslim Association of Malawi (MAM) | kusekera nyengo yonse ya kusala kudya ndi kupemphera ya Ramadani yomwe asilamu achita kwa mwezi wa tunthu. Malingana ndi bungwe la Asilamu mdziko muno la muzilimu asosiyeshoni ofu Malawi (Mamu) | Female | |
mwezi watsopano waoneka dzulo ndipo ichi ndi chifukwa chake mapemperowa achitike lero. Poyankhula ndi Ndirande FM, mneneri wa bungwe la MAM | mwezi watsopano waoneka dzulo ndipo ichi ndi chifukwa chake mapemperowa achitike lero. Poyankhula ndi Ndirande efuemu, mneneri wa bungwe la MAMU | Female | |
Dinala Chabulika wati pamene nyengo ya kusala kudya ndi kupemphera yatha, asilamu akuyenera kupitiliza ntchito zabwino zomwe akhala akuchita | Dinala Chabulika wati pamene nyengo ya kusala kudya ndi kupemphera yatha, asilamu akuyenera kupitiliza ntchito zabwino zomwe akhala akuchita | Female | |
Asilamu pa dziko lonse la pansi anayamba nyengo ya kusala kudya ndi kupemphera ya chaka chino pa 2 April | Asilamu pa dziko lonse la pansi anayamba nyengo ya kusala kudya ndi kupemphera ya chaka chino pa thu epulo | Female | |
Mfumu yaikulu ya Angoni a Zwangendaba, Inkosi ya Makosi Mbelwa Yachisanu, yauza Pulezidenti Lazarus Chakwera ndi boma lake la Mgwirizano wa Tonse | Mfumu yaikulu ya Angoni a ZwangendaWa, Inkosi ya Makosi Mbelwa Yachisanu, yauza Pulezidenti Lazalasi Chakwera ndi boma lake la Mgwirizano wa Tonse | Female | |
kuti liyambe ku kwaniritsa malonjezo make a pakampeni, ngati sakufuna kuti Amalawi atope ndi ulamuliro wake. Poyankhula Lachisanu, pa msonkhano wachitukuko omwe pulezidentiyu anachititsa m'boma la Mzimba | kuti liyambe ku kwaniritsa malonjezo make a pakampeni, ngati sakufuna kuti Amalawi atope ndi ulamuliro wake. Poyankhula Lachisanu, pa msonkhano wachitukuko omwe pulezidentiyu anachititsa m'boma la Mzimba | Female | |
Mbelwa anati pamene Chakwera wayamba kuopseza nduna zake kuti zichotsedwa ngati sizikwaniritsa mlingo oyikika potumikira Amalawi, iyenso akuyenera kutsatira mlingo omwewo | Mbelwa anati pamene Chakwera wayamba kuopseza nduna zake kuti zichotsedwa ngati sizikwaniritsa mlingo oyikika potumikira Amalawi, iyenso akuyenera kutsatira mlingo omwewo | Female | |
Inkosi ya Makosi Mbelwa inanena mosapsatira kuti ngati chitukuko chimene boma la Chakwera linalonjeza sichikwaniritsidwa, Amalawi sadzawona kufunikira komuvoteranso ngati mtsogoleri wa dziko | Inkosi ya Makosi Mbelwa inanena mosapsatira kuti ngati chitukuko chimene boma la Chakwera linalonjeza sichikwaniritsidwa, Amalawi sadzawona kufunikira komuvoteranso ngati mtsogoleri wa dziko | Female | |
China mwa chitukuko cholonjezedwa ndi sukulu ya Ukachenjedwe ya Mbelwa (Mbelwa University), komanso misewu ina m'bomalo | China mwa chitukuko cholonjezedwa ndi sukulu ya Ukachenjedwe ya Mbelwa (Mbelwa yunivesite), komanso misewu ina m'bomalo | Female | |
Thupi la Katswiri oyimba ndi kujambula nyimbo, Chris Kele, lifika m'dziko muno Loweruka, kuchokera Ku South Africa, kumene anamwalira | Thupi la Katswiri oyimba ndi kujambula nyimbo, khilisiKele, lifika m'dziko muno Loweruka, kuchokera Ku saufi afilika, kumene anamwalira | Female | |
Malingana ndi mkulu wake wa malemuyu, amenenso ndi mneneri wa akubanja, a Madalitso Chipwaila, thupiri lifika pa bwalo la ndege la Chileka, nthawi ya 3 koloko masana | Malingana ndi mkulu wake wa malemuyu, amenenso ndi mneneri wa akubanja, a Madalitso Chipwaila, thupiri lifika pa bwalo la ndege la Chileka, nthawi ya fili koloko masana | Female | |
Thupi la Kele, amene dzina lake lenileni anali Christopher Chipwaila, likuyembekezeka kuyikidwa mmanda Lamulungu lino, Ku mudzi kwawo kwa William Mnthumba, m'dera la Mfumu ya Ndodo Katunga, m'boma la Chikwawa | Thupi la Kele, amene dzina lake lenileni anali khilisitofa Chipwaila, likuyembekezeka kuyikidwa mmanda Lamulungu lino, Ku mudzi kwawo kwa Wiliyamu Mnthumba, m'dera la Mfumu ya Ndodo Katunga, m'boma la Chikwawa | Female | |
Iyeyu anamwalira pa 20 April, m'ziko la South Africa'lo, komwe anali ndi gulu lakelake loyimba, kudzanso malo otchuka ojambulirako nyimbo | Iyeyu anamwalira pa twente epulo, m'ziko la saufi afilika'lo, komwe anali ndi gulu lakelake loyimba, kudzanso malo otchuka ojambulirako nyimbo | Female | |
Mwa maluso ake ena, iyeyu ndi amene anajambula nyimbo imene yatchuka zedi panopa, ya Vinyo Watha, imene anayimba Mlaka Maliro | Mwa maluso ake ena, iyeyu ndi amene anajambula nyimbo imene yatchuka zedi panopa, ya Vinyo Watha, imene anayimba Mlaka Maliro | Female | |
Mpingo wa CCAP mu synod ya Nkhoma wati tsankho lakula mu ulamuliro wa boma la Tonse ndipo walangiza adindo mu mgwirizanowu kuti asiye mchitidwewu | Mpingo wa sisiepi mu sinodi ya Nkhoma wati tsankho lakula mu ulamuliro wa boma la Tonse ndipo walangiza adindo mu mgwirizanowu kuti asiye mchitidwewu | Female | |
Izi ndi malingana ndi kalata yomwe abusa a mpingowu alemba ndipo ikuwelengedwa lero m'mipingo yonse yomwe ili pansi pa Synod-yi | Izi ndi malingana ndi kalata yomwe abusa a mpingowu alemba ndipo ikuwelengedwa lero m'mipingo yonse yomwe ili pansi pa Sinodi-yi | Female | |
Kupatula nkhani ya tsankho, kalatayi yalunjikanso pa kukula kwa katangale komanso chidodo cha mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera pochita zinthu | Kupatula nkhani ya tsankho, kalatayi yalunjikanso pa kukula kwa katangale komanso chidodo cha mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera pochita zinthu | Female | |
Pamenepa, Nkhoma Synod yapempha akhilisitu ake kuti agwirane manja popemphelera chilungamo pakati pawo komanso kuti anthu wochuluka azisangalala osati kagulu ka anthu ochepa okha | Pamenepa, Nkhoma Sinodi yapempha akhilisitu ake kuti agwirane manja popemphelera chilungamo pakati pawo komanso kuti anthu wochuluka azisangalala osati kagulu ka anthu ochepa okha | Female | |
Mpingowu watulutsa kalatayi patangopita sabata zochepa nawo mpingo wa Katolika utatulutsa kalata yake yomwe inalunjikanso pa nkhani ngati zomwezi | Mpingowu watulutsa kalatayi patangopita sabata zochepa nawo mpingo wa Katolika utatulutsa kalata yake yomwe inalunjikanso pa nkhani ngati zomwezi | Female | |
Mverani Program ya Mutipo Chani lero yapa Mverani Program ya Mutipo Chani lero pa Ndirande FM kuyambira nthawi ya 5 koloko madzulowa pomwe tikhale tikukambirana nkhani yokhuza kusintha lamulo lochotsa mimba | Mverani Pulogilamu ya Mutipo Chani lero yapa Mverani Pulogilamu ya Mutipo Chani lero pa Ndirande efuemu kuyambira nthawi ya faifi koloko madzulowa pomwe tikhale tikukambirana nkhani yokhuza kusintha lamulo lochotsa mimba | Female | |
Kodi ndi koyenera kuti lamulo lomwe lilipo pano, lomwe limaloleza amayi kuchotsa pomwe ali pa chiopsezo choluza moyo, liwonjezeledwe magawo eni. Tiuzeni maganizo anu ndipo tiwelenga | Kodi ndi koyenera kuti lamulo lomwe lilipo pano, lomwe limaloleza amayi kuchotsa pomwe ali pa chiopsezo choluza moyo, liwonjezeledwe magawo eni. Tiuzeni maganizo anu ndipo tiwelenga | Female | |
Nthambi ya apolisi m'dziko muno yati yayitanitsa mkulu wa bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la ACB, Martha Chizuma | Nthambi ya apolisi m'dziko muno yati yayitanitsa mkulu wa bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la esibi, Mafa Chizuma | Female | |
kuti likamufufuze pa mawu ena omwe anafala pa masamba a mchezo omwe iye Chizuma, kudzera pa phone, anamveka akuuza munthu wina za momwe ntchito yothana ndi katangale ku ACB ikuyendera | kuti likamufufuze pa mawu ena omwe anafala pa masamba a mchezo omwe iye Chizuma, kudzera pa foni, anamveka akuuza munthu wina za momwe ntchito yothana ndi katangale ku esibi ikuyendera | Female | |
Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m'dziko muno, Harry Namwaza watsimikiza za kuyitanitsidwa kwa a Chizuma ku polisi, ponena kuti zikutsatira zomwe bwalo la milandu la Senior Resident Magistrate ku Mzuzu | Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m'dziko muno, Hale Namwaza watsimikiza za kuyitanitsidwa kwa a Chizuma ku polisi, ponena kuti zikutsatira zomwe bwalo la milandu la siniyo lezidenti majesitileti ku Mzuzu | Female | |
linalamula kuti zitero, munthu wina, Frighton Mphompho atakamang'ala ku bwalolo, ponena kuti zomwe mayi chizuma amayankhula, zinaphwanya mwa malamulo a ntchito yawo | linalamula kuti zitero, munthu wina, fulaitoni Mphompho atakamang'ala ku bwalolo, ponena kuti zomwe mayi chizuma amayankhula, zinaphwanya mwa malamulo a ntchito yawo | Female | |
Ngati njira mwa imodzi yochepesera nkhanza zomwe amayi komanso ana amasiye amakumana nazo m’dziko muno, m’modzi mwa achinyamata, Evalisto Muli Namalenga | Ngati njira mwa imodzi yochepesera nkhanza zomwe amayi komanso ana amasiye amakumana nazo m’dziko muno, m’modzi mwa achinyamata, Evalisito Muli Namalenga | Female | |
walemba buku lomwe lanyamula uthenga wozindikilitsa za kuipa kwa nkhanzazi | walemba buku lomwe lanyamula uthenga wozindikilitsa za kuipa kwa nkhanzazi | Female | |
Bukuli lomwe alikhazikitse pa 24 April mu mzinda wa Blantyre akuti likunyamulanso uthenga wolimbikitsa anthu omwe amakumana ndi nkhanza zosiyanasiyana kuti kuchitilidwa nkhanza simathero a zonse | Bukuli lomwe alikhazikitse pa twente folo epulo mu mzinda wa Bulantaya akuti likunyamulanso uthenga wolimbikitsa anthu omwe amakumana ndi nkhanza zosiyanasiyana kuti kuchitilidwa nkhanza simathero a zonse | Female | |
Malingana ndi Namalenga, mutu wa bukuli ndi Fulfiling Family Responsibilities to Eliminate Gender Based Violence | Malingana ndi Namalenga, mutu wa bukuli ndi fufiling’i famile lesiponsibilitezi tu elimineti jenda bezidi vayolensi | Female | |
Pamenepa, iye wapempha anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino kuti agule bukuli ndi cholinga chofuna kupala mfundo zomwe waziika zomwe ali ndi chikhulupiliro kuti ndi mayankho ku nkhanza zomwe anthu amachitirana | Pamenepa, iye wapempha anthu komanso mabungwe akufuna kwabwino kuti agule bukuli ndi cholinga chofuna kupala mfundo zomwe waziika zomwe ali ndi chikhulupiliro kuti ndi mayankho ku nkhanza zomwe anthu amachitirana | Female | |
Nduna ya zofalitsa nkhani, Gospel Kazako komanso Chikondi Moyo lero adalitsa ukwati wawo ku mpingo wa Lingadzi CCAP mu mzinda wa Lilongwe | Nduna ya zofalitsa nkhani, Gosipelo Kazako komanso Chikondi Moyo lero adalitsa ukwati wawo ku mpingo wa Lingadzi sisiepi mu mzinda wa Lilongwe | Female | |
ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, nduna ya zaumoyo, Mayi Khumbize Kandodo Chiponda, wachiwiri kwa nduna ya maboma aang'ono, John Bande komanso mkulu wa apolisi wakale, Lexen Kachama | ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulosi Chilima, nduna ya zaumoyo, Mayi Khumbize Kandodo Chiponda, wachiwiri kwa nduna ya maboma aang'ono, Joni Bande komanso mkulu wa apolisi wakale, Lekiseni Kachama | Female | |
Malingana ndi dongosolo la a ku banja, madzulowa kukhala madyelero a ukwatiwu ku Kambali Lodge ku mzinda omwewu pomwe malipoti akuti anthu okhawo amene ayitanidwa ndi omwe akaloleledwe kulowa | Malingana ndi dongosolo la a ku banja, madzulowa kukhala madyelero a ukwatiwu ku Kambali Loji ku mzinda omwewu pomwe malipoti akuti anthu okhawo amene ayitanidwa ndi omwe akaloleledwe kulowa | Female | |
Kafukufuku wa Afrobarometer wapeza kuti anthu 74 mwa anthu 100 aliwonse amakhulupilira kuti mdziko muno muli ufiti | Kafukufuku wa Afulobalomitar wapeza kuti anthu fote folo mwa anthu wani handiledi aliwonse amakhulupilira kuti mdziko muno muli ufiti | Female | |
Izi zili chomwechi ngakhale kuti malamulo a Malawi amanenetsa kuti ufiti kulibe ndipo munthu onena nzake kuti ndi fiti amamangidwa Tiuzeni Maganizo Anu | Izi zili chomwechi ngakhale kuti malamulo a Malawi amanenetsa kuti ufiti kulibe ndipo munthu onena nzake kuti ndi fiti amamangidwa Tiuzeni Maganizo Anu | Female | |
Kodi inu mumakhulupilira kuti ufiti ulipo kapena ayi. Chivomerezi chadutsa madera ena ozungulira boma la Blantyre.Kodi kwanuko chivomerezi chadutsa | Kodi inu mumakhulupilira kuti ufiti ulipo kapena ayi. Chivomerezi chadutsa madera ena ozungulira boma la Bulantaya.Kodi kwanuko chivomerezi chadutsa | Female | |
Osayiwala kulemba boma ndi dera lomwe muli. Mkulu wa zofalitsa nkhani ku nyumba ya boma, Sean Kampondeni | Osayiwala kulemba boma ndi dera lomwe muli. Mkulu wa zofalitsa nkhani ku nyumba ya boma, shoni Kampondeni | Female | |
wauza atolankhani lero kuti posachedwapa, alangizi a mtsogoleri wa dziko lino pa nkhani zosiyanasiyana azipezeka nawo pa misonkhano ya atolankhani yomwe nyumbayi imachititsa | wauza atolankhani lero kuti posachedwapa, alangizi a mtsogoleri wa dziko lino pa nkhani zosiyanasiyana azipezeka nawo pa misonkhano ya atolankhani yomwe nyumbayi imachititsa | Female | |
ati ndi cholinga choti azifotokozera momwe dziko lino likuchitira m'magawo osiyanasiyana. A Kampondeni ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani | ati ndi cholinga choti azifotokozera momwe dziko lino likuchitira m'magawo osiyanasiyana. A Kampondeni ayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani | Female | |
omwe akuchititsa ku nyumba ya chifumu ya Kamuzu Palace mu mzinda wa Lilongwe. Malingana ndi a Kampondeni, amalawi asaganize kuti mtsogoleriyu akugona pa ntchito | omwe akuchititsa ku nyumba ya chifumu ya Kamuzu Palesi mu mzinda wa Lilongwe. Malingana ndi a Kampondeni, amalawi asaganize kuti mtsogoleriyu akugona pa ntchito | Female | |
ndipo ichi ndi chifukwa chake nyumbayi ikuyambiranso misonkhano ya atolankhani yotere. Poyamba pa msonkhano wa lero | ndipo ichi ndi chifukwa chake nyumbayi ikuyambiranso misonkhano ya atolankhani yotere. Poyamba pa msonkhano wa lero | Female | |
mneneri wa President Lazarus Chakwera, Anthony Kasunda anayamba ndikufunira mafuno abwino a tsiku lobadwa kwa mtsogoleriyu | mneneri wa Pulezidenti Lazalasi Chakwera, Antone Kasunda anayamba ndikufunira mafuno abwino a tsiku lobadwa kwa mtsogoleriyu | Female | |
Anthu osiyanasiyana asonkhana ku mpingo wa Chingazi Catholic kwa Goliati m'boma la Thyolo komwe mwambo wa mapemphero okumbuikira moyo wa mtsogoleri wachitatu wa dziko lino, Bingu wa Mutharika ukuchitikira | Anthu osiyanasiyana asonkhana ku mpingo wa Chingazi Kafoliki kwa Goliati m'boma la Thyolo komwe mwambo wa mapemphero okumbuikira moyo wa mtsogoleri wachitatu wa dziko lino, Bingu wa Mutharika ukuchitikira | Female | |
Pa mwambowu pali mtsogoleri opuma wa dziko lino, Peter Mutharika ngati mlendo olemekeza, mkazi wawo, Gertrude, mtsogoleri wachiwiri wa dziko lino, Bakili Muluzi | Pa mwambowu pali mtsogoleri opuma wa dziko lino, Pita Mutharika ngati mlendo olemekeza, mkazi wawo, Getuludi, mtsogoleri wachiwiri wa dziko lino, Bakili Muluzi | Female | |
mwana wawo Atupele, wa pa mpando wa bungwe la Mulhakho Wa Alhomwe, Leston Muli, mkulu osutsa boma Kondwani Nankhumwa ndi anthu ena odziwika bwino | mwana wawo Atupele, wa pa mpando wa bungwe la Mulakho Wa Alomwe, Lesitoni Muli, mkulu osutsa boma Kondwani Nankhumwa ndi anthu ena odziwika bwino | Female | |
Ukatha mwambo wa mapemphero ku kachisiku, kukhalanso mwambo oyala nkhata ku Mpumulo wa bata komwe malemu Bingu anayikidwa | Ukatha mwambo wa mapemphero ku kachisiku, kukhalanso mwambo oyala nkhata ku Mpumulo wa bata komwe malemu Bingu anayikidwa | Female | |
Lero pa 5 April ndi tsiku lomwe mtsogoleri wachitatu wa dziko lino, Bingu Wa Mutharika anamwalira ali mu ofesi | Lero pa faifi epulo ndi tsiku lomwe mtsogoleri wachitatu wa dziko lino, Bingu Wa Mutharika anamwalira ali mu ofesi | Female | |
A Mutharika omwe anamwalira mchaka cha 2012, anamwalira ali ndi zaka 78, atadwala nthenda ya mtima | A Mutharika omwe anamwalira mchaka cha twente thwelofu, anamwalira ali ndi zaka sevente eiti, atadwala nthenda ya mtima | Female | |
Pakadali pano, a ku banja la a malemu motsogozedwa ndi mtsogoleri opuma wa dziko lino, Peter Mutharika lero akonza mwambo wokumbukira moyo wa malemu Bingu | Pakadali pano, a ku banja la a malemu motsogozedwa ndi mtsogoleri opuma wa dziko lino, Pita Mutharika lero akonza mwambo wokumbukira moyo wa malemu Bingu | Female | |
Mwambowu uchitikira ku Ndata m'boma la Thyolo komwe malemuwa anayikidiwa. Mwa zina, malemuwa anayambitsa chipani cha Democratic Progressive (DPP) | Mwambowu uchitikira ku Ndata m'boma la Thyolo komwe malemuwa anayikidiwa. Mwa zina, malemuwa anayambitsa chipani cha DemocDEmokilatiki pulogilesivi (Dipipi) | Female | |
kumanga bwalo la za masewero la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, sukulu ya ukachenjede ya MUST ku Thyolo komanso kukhazikitsa Nkhokwe zosungiramo chakudya mmadera osiyanasiyana a dziko lino | kumanga bwalo la za masewero la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, sukulu ya ukachenjede ya Masiti ku Thyolo komanso kukhazikitsa Nkhokwe zosungiramo chakudya mmadera osiyanasiyana a dziko lino | Female | |
Mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera mawa lolemba achititsa msonkhano wa chitukuko pa sukulu ya pulayimale ya Luchenza m'boma la Thyolo | Mtsogoleri wa dziko lino, Lazalasi Chakwera mawa lolemba achititsa msonkhano wa chitukuko pa sukulu ya pulayimale ya Luchenza m'boma la Thyolo | Female | |
Malingana ndi kalata yomwe mlembi wamkulu mu ofesi ya mtsogoleriyu ndi nduna zake, Zangazanga Chikhosi watulutsa, a Chakwera achititsa msonkhanowu | Malingana ndi kalata yomwe mlembi wamkulu mu ofesi ya mtsogoleriyu ndi nduna zake, Zangazanga Chikhosi watulutsa, a Chakwera achititsa msonkhanowu | Female | |
akazamaliza kuyendera minda ya mbewu mu ina mwa midzi ya m'bombali. Nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno ya Immigration | akazamaliza kuyendera minda ya mbewu mu ina mwa midzi ya m'bombali. Nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno ya Imigileshoni | Female | |
yati lero lachisanu iyambiranso kupanga ziphatso zoyendera maulendo a kunja Patapita miyezi ingapo nthambiyi isakupanga | yati lero lachisanu iyambiranso kupanga ziphatso zoyendera maulendo a kunja Patapita miyezi ingapo nthambiyi isakupanga | Female | |
Nthambi ya immigration inasiya kupanga ziphatsozi, boma litathetsa kontilakiti yomwe kampani imene imapeleka zipangizo zopangira ziphatsozi ya Techno Brain inali nawo m’mbuyomu Kontilakitiyi | Nthambi ya imigileshoni inasiya kupanga ziphatsozi, boma litathetsa kontilakiti yomwe kampani imene imapeleka zipangizo zopangira ziphatsozi ya tekino buleni inali nawo m’mbuyomu Kontilakitiyi | Female |
Subsets and Splits
No community queries yet
The top public SQL queries from the community will appear here once available.